Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Angelo Ndiwo “Mizimu Yotumikira Anthu”

Angelo Ndiwo “Mizimu Yotumikira Anthu”

Angelo Ndiwo “Mizimu Yotumikira Anthu”

“Kodi onsewo si mizimu yotumikira anthu, yotumidwa kukatumikira amene adzalandira chipulumutso monga cholowa?”​—AHEB. 1:14.

1. Kodi tingalimbikitsidwe bwanji ndi lemba la Mateyo 18:10 ndi la Aheberi 1:14?

YESU KHRISTU anachenjeza anthu onse kuti asakhumudwitse otsatira ake, ponena kuti: “Samalani anthu inu kuti musanyoze mmodzi wa aang’ono awa; chifukwa ndikukutsimikizirani kuti angelo awo kumwamba amaona nkhope ya Atate wanga wa kumwamba nthawi zonse.” (Mat. 18:10) Ponena za angelo okhulupirika, mtumwi Paulo analemba kuti: “Kodi onsewo si mizimu yotumikira anthu, yotumidwa kukatumikira amene adzalandira chipulumutso monga cholowa?” (Aheb. 1:14) Mawu amenewa ndi olimbitsa mtima chifukwa akusonyeza kuti Mulungu amagwiritsira ntchito angelo pothandiza anthu. Kodi Baibulo limatiuza chiyani za angelo? Kodi amatithandiza motani? Nanga kodi tingaphunzire chiyani kwa iwo?

2, 3. Fotokozani ntchito zosiyanasiyana za angelo.

2 Kumwamba kuli angelo okhulupirika mamiliyoni ambiri. Ndipo angelo onsewa ndi “amphamvu zolimba, akuchita mawu ake, akumvera liwu la mawu ake.” (Sal. 103:20; werengani Chivumbulutso. 5:11.) Ana auzimu a Mulungu amenewa ali ndi umunthu wosiyanasiyana, amatha kusonyeza makhalidwe a Mulungu ndipo ali ndi ufulu wosankha. Iwo ali ndi maudindo apamwamba osiyanasiyana m’gulu la Mulungu ndipo mkulu wa angelo ndi Mikayeli (dzina limene Yesu amadziwika nalo kumwamba). (Dan. 10:13; Yuda 9) Mwana “woyamba kubadwa wa chilengedwe chonse” ameneyu amatchedwanso “Mawu” kapena kuti Womulankhulira Mulungu. Yehova anamugwiritsira ntchito polenga zinthu zina zonse.​—Akol. 1:15-17; Yoh. 1:1-3.

3 Pansi pa mkulu wa angeloyu pali aserafi, amene amalengeza chiyero cha Yehova ndipo amathandiza kuti anthu ake akhale oyera mwauzimu. Palinso akerubi, amene amatumikira monga ochirikiza ulamuliro wa Mulungu. (Gen. 3:24; Yes. 6:1-3, 6, 7) Angelo ena kapena kuti amithenga alinso ndi ntchito zosiyanasiyana pochita chifuniro cha Mulungu.​—Aheb. 12:22, 23.

4. Kodi angelo anamva bwanji Mulungu ataika maziko a dziko lapansi, nanga kodi anthufe tikanakhala ndi tsogolo lotani anthu oyambirira akanagwiritsa ntchito bwino ufulu wawo wosankha?

4 Angelo onse anasangalala kwambiri Mulungu ‘ataika maziko a dziko lapansi’ ndipo anasangalalanso ndi ntchito imene anapatsidwa pa nthawi imene dzikoli linkakonzedwa kuti pakhale anthu. (Yobu 38:4, 7) Yehova analenga munthu kukhala “wocheperapo kwa angelo.” Komabe, munthu analengedwa “m’chifanizo” Chake, zimene zikutanthauza kuti anthu angathe kusonyeza makhalidwe apamwamba a Mlengi. (Aheb. 2:7; Gen. 1:26) Adamu ndi Hava akanagwiritsa ntchito bwino ufulu wawo wosankha, iwo ndi ana awo akanadzasangalala ndi moyo wosatha m’paradaiso. Iwo akanakhalabe m’banja la Yehova la zolengedwa zanzeru.

5, 6. Kodi kumwamba kunachitika zinthu zotani zopandukira Mulungu, ndipo kodi Mulungu anatani?

5 N’zachidziwikire kuti angelo okhulupirika anakhumudwa kwambiri ataona kuti ena ayamba kupanduka m’banja la Mulungu. Mmodzi wa iwo sankafuna kulambira Yehova, m’malomwake ankalakalaka kuti iyeyo ndiye azilambiridwa. Izi zinam’chititsa kuti akhale Satana (kutanthauza “Wotsutsa”) chifukwa choti anatsutsa zoti Yehova ndi woyenera kulamulira ndipo anayamba kukopa zolengedwa zina kuti zipandukire ulamuliro wa Yehova pa chilengedwe chonse. Bodza loyamba la Satana lotchulidwa m’Baibulo linali lonyengerera anthu awiri oyambirira kuti apandukire Mlengi wawo wachikondi.​—Gen. 3:4, 5; Yoh. 8:44.

6 Yehova sanachedwe kupereka chiweruzo kwa Satana. Chiweruzochi anachitchula muulosi woyamba wa m’Baibulo. Iye anati: “Ndipo ndidzaika udani pakati pa iwe ndi mkaziyo, ndi pakati pa mbewu yako ndi mbewu yake; ndipo idzalalira mutu wako, ndipo iwe udzalalira chitende chake.” (Gen. 3:15) Udaniwu udzapitirira kukhalapo pakati pa Satana ndi “mkazi” wa Mulungu. Inde, Yehova amaona gulu la kumwamba la angelo okhulupirika monga mkazi wake wokondedwa. Ulosi umenewu unapereka chiyembekezo chotsimikizirika, ngakhale kuti tsatanetsatane wake anakhalabe “chinsinsi chopatulika” chomwe chinadzavumbulidwa pang’onopang’ono. Mulungu anakonza zoti mmodzi wa iwo m’gulu lake la kumwambalo adzawononge opanduka onse, ndi kuti kudzera mwa iyeyo “zinthu za kumwamba ndi zinthu za padziko lapansi” zidzasonkhanitsidwe pamodzi.​—Aef. 1:8-10.

7. Kodi angelo ena anachita zotani m’nthawi ya Nowa, ndipo zotsatira zake zinali zotani?

7 M’masiku a Nowa, angelo ena anasiya “malo awo okhala” n’kuvala matupi aumunthu n’cholinga choti adzasangalale ndi zinthu zam’dzikoli. (Yuda 6; Gen. 6:1-4) Yehova anaponya angelo opanduka amenewa mumdima wa ndiwe yani, motero iwo pamodzi ndi Satana anakhala “makamu a mizimu yoipa,” ndipo ndi adani oopsa a atumiki a Mulungu.​—Aef. 6:11-13; 2 Pet. 2:4.

Kodi Angelo Amatithandiza Motani?

8, 9. Kodi Yehova anagwiritsira ntchito bwanji angelo kuthandiza anthu?

8 Angelo anatumikirapo anthu monga Abulahamu, Yakobo, Mose, Yoswa, Yesaya, Danieli, Yesu, Petulo, Yohane komanso Paulo. Angelo olungama anapereka chiweruzo cha Mulungu, maulosi ndiponso malamulo osiyanasiyana ngakhalenso Chilamulo cha Mose. (2 Maf. 19:35; Dan. 10:5, 11, 14; Mac. 7:53; Chiv. 1:1) Popeza kuti tsopano tili ndi Baibulo lonse, lomwe ndi Mawu a Mulungu, angelo sangafunikirenso kupereka mauthenga ochokera kwa Mulungu. (2 Tim. 3:16, 17) Komabe ngakhale kuti sitiona, angelo amachita ntchito zambiri zogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu ndiponso zothandiza atumiki ake.

9 Baibulo limatiuza kuti: “Mngelo wa Yehova azinga kuwachinjiriza iwo akuopa Iye, nawalanditsa iwo.” (Sal. 34:7; 91:11) Chifukwa choti Satana anakayikira kukhulupirika kwathu, Yehova amalola kuti Satana azitibweretsera mayesero osiyanasiyana. (Luka 21:16-19) Komano, pa nkhani ya kukhulupirika kwathu kwa iye, Mulungu amadziwa pamene mayesero ayenera kulekezera. (Werengani 1 Akorinto 10:13.) Angelo amakhala tcheru kuthandizapo mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu. Iwo anapulumutsa Sadrake, Mesake, Abedinego, Danieli, ndi Petulo koma Stefano ndi Yakobe anaphedwa ndi adani. (Dan. 3:17, 18, 28; 6:22; Mac. 7:59, 60; 12:1-3, 7, 11) Zifukwa zimene zinachititsa kuti anthu ena apulumutsidwe koma ena aphedwe, zinali zosiyana. Zoterezi zinachitikanso m’ndende za chipani cha Nazi. Abale athu ena anaphedwa koma Yehova anachititsa kuti ambiri apulumuke.

10. Kuphatikiza pa thandizo la angelo, kodi tingalandire thandizo linanso lotani?

10 Malemba saphunzitsa kuti munthu aliyense padziko lapansi pano ali ndi mngelo womuteteza. Komabe, timapemphera mosakayika ngakhale pang’ono podziwa kuti “chilichonse chimene tingapemphe mogwirizana ndi chifuniro chake, [Mulungu] amatimvera.” (1 Yoh. 5:14) Yehova angathe kutumiza mngelo kuti atithandize, koma Iye amatha kuperekanso thandizo m’njira zina. Mwachitsanzo, Akhristu anzathu angagwidwe chifundo n’kutithandiza ndi kutilimbikitsa. Mwinanso Mulungu angatipatse nzeru ndi mphamvu zotithandiza kupirira “munga m’thupi” umene ukutivutitsa ngati kuti tikumenyedwa ndi “mngelo wa Satana.”​—2 Akor. 12:7-10; 1 Ates. 5:14.

Tsanzirani Yesu

11. Kodi angelo anagwiritsidwa ntchito bwanji pothandiza Yesu, ndipo Yesu anakwaniritsa chiyani pokhalabe wokhulupirika kwa Mulungu?

11 Taganizirani mmene Yehova anagwiritsira ntchito angelo pothandiza Yesu. Iwo analengeza za kubadwa kwake ndi kuuka kwake ndipo ankamuthandiza pamene anali padziko lapansi pano. Angelowo akanatha kuletsa kuti Yesu asamangidwe ndi kuphedwa mwankhanza. Koma sanachite zimenezo, m’malomwake Mulungu anatumiza mngelo kuti akamulimbikitse Yesu. (Mat. 28: 5,6; Luka 2:8-11; 22:43) Mogwirizana ndi cholinga cha Yehova, Yesu anafa imfa ya nsembe ndipo anapereka umboni wakuti munthu wangwiro angathe kukhalabe wokhulupirika kwa Mulungu ngakhale atakumana ndi mayesero aakulu kwambiri. Motero Yehova anaukitsa Yesu kuti akakhale ndi moyo wosafa kumwamba, n’kumupatsa “ulamuliro wonse” ndipo angelo onse anakhala pansi pake. (Mat. 28:18; Mac. 2:32; 1 Pet. 3:22) Motero Yesu anasonyeza kuti anali mbali yoyamba ya “mbewu” ya “mkazi” wa Mulungu.​—Gen. 3:15; Agal. 3:16.

12. Kodi tingatsanzire bwanji Yesu pa nkhani yochita zinthu ndi maganizo abwino?

12 Yesu ankadziwa kuti n’kulakwa kuti azimuyesa Yehova pochita dala zinthu zoika moyo pachiswe kuti angelo amupulumutse. (Werengani Mateyo 4:5-7.) Motero, tiyeni titsanzire Yesu pokhala “a maganizo abwino.” Tisamachite dala zinthu zoika moyo pachiswe, koma tizilimba mtima tikamazunzidwa.​—Tito 2:12.

Kodi Tingaphunzire Chiyani kwa Angelo Okhulupirika?

13. Kodi tingaphunzire chiyani pa chitsanzo cha angelo olungama chotchulidwa pa 2 Petulo 2:9-11?

13 Podzudzula anthu amene amalankhula “monyoza” atumiki a Yehova odzozedwa, mtumwi Petulo anatchulapo chitsanzo chabwino kwambiri cha angelo olungama. Ngakhale kuti iwo ali ndi mphamvu zambiri, amadzichepetsa ndipo salankhula monyoza chifukwa “amalemekeza Yehova.” (Werengani 2 Petulo 2:9-11.) Nafenso tizipewa kuweruza ena molakwika, tizilemekeza anthu amene ali ndi maudindo mumpingo, n’kusiya zonse m’manja mwa Yehova, yemwe ndi Woweruza Wamkulu.​—Aroma 12:18, 19; Aheb. 13:17.

14. Kodi angelo amatipatsa chitsanzo chotani pa nkhani ya kudzichepetsa?

14 Angelo amatipatsa chitsanzo chabwino kwambiri potumikira Yehova modzichepetsa. Angelo ena anakana kuuza anthu maina awo. (Gen. 32:29; Ower. 13:17, 18) Ngakhale kuti kumwamba kuli angelo mamiliyoni ambirimbiri, Baibulo limatchula maina a angelo awiri okha basi, Mikaeli ndi Gabrieli. N’kutheka kuti cholinga chake ndicho kutithandiza kuti tisamapatse angelo ulemu wosayenerera. (Luka 1:26; Chiv. 12:7) Mtumwi Yohane atagwada kuti alambire mngelo, anachenjezedwa kuti: “Samala! Usatero ayi! Inetu ndangokhala kapolo mnzako, ndi wa abale ako.” (Chiv. 22:8, 9) Tiyenera kulambira komanso kupemphera kwa Mulungu yekha basi.​—Werengani Mateyo 4:8-10.

15. Kodi angelo amatipatsa chitsanzo chotani pa nkhani ya kuleza mtima?

15 Angelo amaperekanso chitsanzo chabwino pa nkhani ya kuleza mtima. Ngakhale kuti amachita chidwi kwambiri kuti adziwe zinsinsi zopatulika za Mulungu, si zonse zimene amazidziwa. Baibulo limati: “M’zinthu zimenezi angelo akulakalaka kusuzumiramo.” (1 Pet. 1:12) Ndiyeno kodi amatani? Iwo amadikirira moleza mtima kuti idzafike nthawi imene “mbali zambirimbiri za nzeru ya Mulungu” zidzadziwike “kudzera mwa mpingo.”​—Aef. 3:10, 11.

16. Kodi zochita zathu zimakhudza bwanji angelo?

16 Akhristu akamayesedwa, amakhala “pachionetsero” pamaso pa angelo. (1 Akor. 4:9) Angelo amakondwera kwambiri akamaona kukhulupirika kwathu ndipo amasangalala wochimwa akalapa. (Luka 15:10) Angelo amaonanso makhalidwe auzimu a akazi achikhristu. Baibulo limasonyeza kuti “mkazi ayenera kukhala ndi chizindikiro cha ulamuliro pamutu wake chifukwa cha angelo.” (1 Akor. 11:3, 10) Inde, angelo amasangalala kuona akazi achikhristu komanso atumiki onse a Mulungu akuchita zinthu mogwirizana ndi dongosolo la Mulungu ndiponso kumvera mutu wawo. Zimenezi zimakumbutsa ana a Mulungu akumwambawa kuti nawonso azikhala omvera.

Angelo Amathandiza Kwambiri pa Ntchito Yolalikira

17, 18. N’chifukwa chiyani tinganene kuti angelo amathandiza pa ntchito yathu yolalikira?

17 Angelo amachita nawo zinthu zina zimene zikuchitika “m’tsiku la Ambuye.” Zina mwa zinthuzo ndi monga kubadwa kwa Ufumu mu 1914, ndiponso ntchito yoponya padziko Satana ndi ziwanda zake kuchokera kumwamba imene “Mikayeli ndi angelo ake” anagwira. (Chiv. 1:10; 11:15; 12:5-9) Mtumwi Yohane anaona mngelo “akuuluka mu mlengalenga chapafupi. Iye anali ndi uthenga wabwino wosatha woti aulengeze monga nkhani yosangalatsa kwa okhala padziko lapansi.” Mngeloyo anati: “Opani Mulungu ndi kum’patsa ulemerero, chifukwa ola lakuti apereke chiweruzo lafika. Chotero lambirani Iye amene anapanga kumwamba, dziko lapansi, nyanja, ndi akasupe amadzi.” (Chiv. 14:6, 7) Ngakhale kuti Mdyerekezi amalimbana kwadzaoneni ndi atumiki a Yehova, Baibulo limatitsimikizira kuti angelo amathandiza atumikiwo pa ntchito yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu, umene panopo unakhazikitsidwa.​—Chiv. 12:13, 17.

18 Masiku ano angelo satiuza mwachindunji malo amene pali anthu oona mtima monga mmene mngelo anachitira ndi Filipi kuti akakumane ndi mdindo wa ku Aitiopiya. (Mac. 8:26-29) Koma ngakhale kuti sitiwaona, pali nkhani zambiri masiku ano zimene zimatsimikizira kuti angelo amathandiza kwambiri pa ntchito yolalikira Ufumu mwa kutitsogolera kwa anthu amene ali ndi “maganizo oyenerera moyo wosatha.” * (Mac. 13:48) Motero ndi bwino kuchita khama pa ntchito yolalikira kuti tichite mbali yathu pofufuza anthu amene akufuna ‘kulambira Atate ndi mzimu ndi choonadi.’​—Yoh. 4:23, 24.

19, 20. Kodi angelo adzakhala ndi ntchito yotani “pamapeto a dongosolo lino la zinthu”?

19 Ponena za nthawi yathu ino, Yesu anati “pamapeto a dongosolo lino la zinthu” angelo ‘adzachotsa oipa pakati pa olungama.’ (Mat. 13:37-43, 49) Angelo amagwira nawo ntchito yosonkhanitsa komaliza ndiponso kuika chisindikizo chomaliza pa odzozedwa. (Werengani Mateyo 24:31; Chiv. 7:1-3) Komanso angelo adzagwira ntchito limodzi ndi Yesu ‘polekanitsa nkhosa ndi mbuzi.’​—Mat. 25:31-33, 46.

20 “Pa vumbulutso la Ambuye Yesu, kuchokera kumwamba ndi angelo ake amphamvu” anthu onse ‘osadziwa Mulungu ndi osamvera uthenga wabwino wonena za Ambuye wathu Yesu’ adzawonongedwa. (2 Ates. 1:6-10) Pofotokoza zimene anaona m’masomphenya, Yohane anati anaona Yesu pamodzi ndi magulu ankhondo a angelo kumwamba atakwera akavalo oyera kuti akachite nkhondo yolungama.​—Chiv. 19:11-14.

21. Kodi mngelo amene “ali ndi kiyi ya paphompho ndi unyolo waukulu m’dzanja lake” adzachita naye chiyani Satana ndi ziwanda zake?

21 Komanso Yohane anaona “mngelo akutsika kuchokera kumwamba ali ndi kiyi ya paphompho ndi unyolo waukulu m’dzanja lake.” Uyu si winanso ayi koma Mikaeli, mkulu wa angelo, amene adzamange Mdyerekezi ndi kum’ponya m’phompho, ndipo zikuoneka kuti adzam’ponya iyeyo pamodzi ndi ziwanda. Adzamasulidwa kwa kanthawi kochepa cha kumapeto kwa Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Khristu, pamene anthu angwiro adzayesedwe komaliza. Kenaka, Satana ndi ena onse opandukira Mulungu adzawonongedwa. (Chiv. 20:1-3, 7-10; 1 Yoh. 3:8) Moti sipadzakhalanso aliyense wopandukira Mulungu.

22. Kodi angelo adzagwira ntchito yotani posachedwapa, ndipo kodi tiyenera kuiona bwanji ntchito yawoyi?

22 Tatsala pang’ono chabe kuwomboledwa m’manja mwa dongosolo la Satana loipali. Angelo adzagwira nawo ntchito yofunika kwambiri imeneyi, yomwe idzakweze ulamuliro wa Yehova n’kukwaniritsa cholinga chimene anali nacho polenga dziko lapansi ndiponso anthu. Ndithudi, angelo olungama ndiwo “mizimu yotumikira anthu, yotumidwa kukatumikira amene adzalandira chipulumutso monga cholowa.” Motero, tizithokoza Yehova Mulungu chifukwa cha mmene amagwiritsira ntchito angelo potithandiza kuchita chifuniro chake ndi kupeza moyo wosatha.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 18 Onani buku la Chingelezi lakuti Jehovah’s Witnesses​—Proclaimers of God’s Kingdom, masamba 549 mpaka 551.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi angelo ali ndi maudindo otani?

• Kodi angelo ena anachita zotani m’nthawi ya Nowa?

• Kodi Mulungu amagwiritsira ntchito bwanji angelo potithandiza?

• Kodi angelo olungama amagwira ntchito yotani m’nthawi yathu ino?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 21]

Angelo amasangalala kuchita chifuniro cha Mulungu

[Chithunzi patsamba 23]

Monga anachitira ndi Danieli, angelo nthawi zonse amakhala tcheru kuti athandize anthu mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu

[Chithunzi patsamba 24]

Tiyenera kukhala olimba mtima, chifukwa angelo amatithandiza pa ntchito yolalikira za Ufumu

[Mawu a Chithunzi]

Globe: NASA photo