Tiyenera Kukhala Aulemu Popeza Ndife Atumiki a Mulungu
Tiyenera Kukhala Aulemu Popeza Ndife Atumiki a Mulungu
“Khalani otsanzira Mulungu.”—AEF. 5:1.
1, 2. (a) N’chifukwa chiyani ulemu uli wofunika? (b) Kodi mu nkhani ino tikambirana chiyani?
PONENA za ulemu, mayi wina wolemba mabuku, dzina lake Sue Fox, analemba kuti: “Palibe nthawi imene tiyenera kusiya kaye kukhala aulemu. Ulemu umafunika kulikonse ndiponso nthawi iliyonse.” Anthu akakhala ndi chizolowezi chochita zinthu mwaulemu, mavuto amene amakhala nawo ndi anthu ena amachepa kapena amatheratu kumene. Koma kuchitira anthu mwano kumayambitsa mkangano, chidani, ndi mkwiyo.
2 Anthu mumpingo woona wachikhristu ndi aulemu. Komabe, tiyenera kusamala kuti tisatengere khalidwe lopanda ulemu limene lili lofala m’dzikoli masiku ano. Tiyeni tione mmene kutsatira
mfundo za m’Baibulo pa nkhani ya ulemu kungatitetezere m’dzikoli ndiponso mmene kungakopere anthu ku chipembedzo choona. Kuti timvetse bwino kuti ulemu n’chiyani, tiyeni tiganizire chitsanzo cha Yehova Mulungu ndi Mwana wake.Yehova ndi Mwana Wake Anatipatsa Chitsanzo cha Mmene Tingakhalire Aulemu
3. Kodi Yehova Mulungu watipatsa chitsanzo chotani cha ulemu?
3 Yehova Mulungu ndi chitsanzo chabwino kwambiri cha mmene tingakhalire aulemu. Ngakhale kuti iye ali ndi udindo wapamwamba kwambiri monga Wolamulira Wamkulu wa chilengedwe chonse, amakomera mtima kwambiri anthu ndiponso amawachitira ulemu. Polankhula ndi Abulahamu ndiponso Mose m’Chiheberi chomwe ndi chilankhulo chimene analembera Baibulo, Yehova anagwiritsa ntchito mawu amene amasonyeza kuti munthu akupempha mwaulemu, osati kulamula. (Gen. 13:14; Eks. 4:6) Atumiki ake akalakwa, Yehova amakhala “wansoni ndi wachisomo, wosapsa mtima msanga, ndi wochulukira chifundo ndi choonadi.” (Sal. 86:15) Iye ndi wosiyana kwambiri ndi anthu amene amakwiya kwambiri anthu ena akapanda kuchita zinthu mmene iwowo akufunira.
4. Kodi tingatsanzire bwanji Yehova anthu ena akamalankhula nafe?
4 Ulemu wa Mulungu umaonekeranso m’njira imene amamvetsera anthu akamalankhula. Pamene Abulahamu anafunsa mafunso osiyanasiyana okhudza anthu a ku Sodomu, Yehova anayankha funso lililonse moleza mtima. (Gen. 18:23-32) Mulungu sanaone kuti Abulahamu akumutayitsa nthawi ndi zinthu zimene anali kuda nazo nkhawa. Yehova amamva mapemphero a atumiki ake ndiponso kulira kwa anthu ochimwa amene alapa. (Werengani Salmo 51:11, 17.) Kodi ifeyo sitikuyenera kutsanzira Yehova pomvetsera anthu ena akamalankhula nafe?
5. Kodi kutsanzira ulemu wa Yesu kungatithandize bwanji kuti tizikhala bwino ndi anthu?
5 Ulemu n’chimodzi mwa zinthu zambiri zimene Yesu Khristu anaphunzira kwa Atate wake. Nthawi zina pochita utumiki wake, Yesu ankathera nthawi yake yambiri mu utumikiwo ndiponso ankatopa kwambiri. Koma nthawi zonse iye anali woleza mtima ndiponso wokoma mtima. Anthu akhate, akhungu amene ankadalira kupempha, ndi ena ofunika kuthandizidwa, ankaona kuti Yesu analidi kufuna kuwathandiza ndi mtima wake wonse. Iye sanawanyalanyaze, ngakhale kuti iwo anabwera kwa iye popanda kumudziwitsa kaye kuti akubwera. Nthawi zambiri iye ankasiya zimene akuchita kuti athandize munthu amene akuvutika. Yesu ankamvera chisoni kwambiri anthu amene anali kumukhulupirira. (Maliko 5:30-34; Luka 18:35-41) Akhristufe timatsatira chitsanzo cha Yesu mwa kukhala okoma mtima ndi ofuna kuthandiza anthu ena. Achibale athu, anthu oyandikana nawo nyumba, ndi ena, amaona zimene timachitazi. Komanso, khalidwe labwino lotereli limachititsa anthu kulemekeza Yehova ndipo limatichititsa ifeyo kukhala achimwemwe.
6. Kodi Yesu anapereka chitsanzo chotani chokhala waulemu ndi waubwenzi kwa anthu?
6 Yesu anasonyezanso ulemu kwa anthu chifukwa chakuti powaitana ankagwiritsa ntchito mayina awo. Koma atsogoleri achipembedzo achiyuda sankalemekeza anthu mwanjira imeneyi. Iwo ankaona kuti anthu amene sanali kudziwa Chilamulo anali ‘otembereredwa’ ndipo ankawachitira zinthu ngati kuti anali otembereredwadi. (Yoh. 7:49) Koma Mwana wa Mulungu sanachite zimenezo. Iye anaitana Marita, Mariya, Zakeyu, ndi anthu ena ambiri pogwiritsa ntchito mayina awo. (Luka 10:41, 42; 19:5) Ngakhale kuti mmene timaitanira anthu zimadalira chikhalidwe chathu ndi zochitika za kwathuko, atumiki a Yehova amayesetsa kukhala aubwenzi. * Iwo salola kuti tsankho liwachititse kukhala opanda ulemu kwa Akhristu anzawo kapena kwa anthu ena.—Werengani Yakobe 2:1-4.
7. Kodi mfundo za m’Baibulo zimatithandiza bwanji kuchitira anthu ulemu kulikonse?
7 Chisomo cha Mulungu ndi Mwana wake kwa anthu a mitundu yonse ndiponso a mafuko onse, chimasonyeza kuti amalemekeza anthuwo ndipo izi zimakopa anthu okonda choonadi. N’zoona kuti zimene anthu amaona kuti ndi ulemu zimasiyanasiyana malinga ndi madera. Chotero tilibe m’ndandanda wa malamulo okhudza ulemu.
M’malomwake timatsatira mfundo za m’Baibulo zimene zimatithandiza kusintha kuti tithe kuchitira ulemu anthu kulikonse. Tiyeni tione mmene kuchitira anthu ulemu kungatithandizire kuti utumiki wathu wachikhristu ukhale waphindu.Kupatsa Anthu Moni ndi Kulankhula Nawo
8, 9. (a) Kodi ndi chizolowezi chotani chimene anthu angachione ngati mwano? (b) N’chifukwa chiyani tiyenera kutsatira mawu a Yesu olembedwa pa Mateyo 5:47 tikakumana ndi anthu?
8 M’madera ambiri masiku ano, anthu amakhala otanganidwa kwambiri moti nthawi zambiri anthu amangodutsana osapatsana moni. N’zoona kuti palibe amene angayembekezere kuti tizipereka moni kwa munthu aliyense wodutsa mumsewu mmene anthu ali pikitipikiti. Koma nthawi zambiri, zimakhala zoyenera ndiponso zabwino kupereka moni kwa anthu. Kodi inuyo muli ndi chizolowezi chopatsa anthu moni? Kapena kodi nthawi zambiri mumangowadutsa anthu osawamwetulira kapena kunena chilichonse? Ngati munthu sasamala, akhoza kuyamba chizolowezi chimenechi, chimene kwenikweni ndi mwano.
9 Yesu anatikumbutsa nkhani imeneyi pamene anati: “Ngati mupatsa moni abale anu okha, kodi n’chiyani chachilendo chimene mukuchita? Kodi anthu a mitundu nawonso sachita zimenezo?” (Mat. 5:47) Pa nkhani imeneyi, bwana wina dzina lake Donald Weiss, analemba kuti: “Anthu sasangalala ndi munthu amene akungowanyalanyaza ngati sakuwaona. Palibe chifukwa chomveka chimene mungapereke chomwe chingakhutiritse munthu amene munangomunyalanyaza. Njira yabwino ndi yakuti: Muzipereka moni kwa anthu. Muzilankhula nawo.” Tikapewa kunyada ndiponso tikamacheza ndi anthu, zinthu zimatiyendera bwino.
10. Kodi kukhala aulemu kungatithandize bwanji kukhala ndi utumiki waphindu? (Onani bokosi lakuti “Yambani ndi Kumwetulira.”)
10 Taganizirani za m’bale ndi mlongo wina, Tom ndi Carol, amene amakhala mumzinda wina waukulu ku North America. Nthawi zonse akakhala mu utumiki, amachezako pang’ono ndi anthu amene amakumana nawo. Kodi amachita bwanji zimenezi? Iwo amatsatira lemba la Yakobe 3:18. Tom anati: “Timayesetsa kukhala ochezeka ndiponso amtendere ndi anthu ena. Timapita kukalankhula ndi anthu amene ali panja pa nyumba zawo ndiponso amene akugwira ntchito m’dera lathu. Timawamwetulira ndi kuwapatsa moni. Timacheza nawo nkhani zimene ali nazo chidwi, monga zokhudza ana awo, agalu awo, nyumba zawo ndiponso ntchito zawo. Pakapita nthawi, amayamba kutiona kuti ndife anzawo.” Carol akupitiriza kuti: “Pa ulendo wotsatira, timawauza mayina athu ndi kuwafunsa mayina awo. Timawauza zimene tikuchita m’deralo koma sitilankhula zambiri. Kenako timatha kuwalalikira.” Tsopano Tom ndi Carol ali ndi anzawo ambiri m’deralo. Angapo alandira mabuku ofotokoza Baibulo, ndipo ena asonyeza chidwi chofuna kuphunzira choonadi.
Kukhala Aulemu Ngakhale Zinthu Zitavuta
11, 12. N’chifukwa chiyani tiyenera kuyembekezera kuchitiridwa chipongwe tikamalalikira uthenga wabwino, ndipo tiyenera kutani anthu akatichitira chipongwe?
11 Nthawi zina anthu amatichitira chipongwe tikamalalikira uthenga wabwino. Timayembekezera zimenezi, chifukwa Khristu Yesu anachenjezeratu ophunzira ake kuti: “Ngati anazunza ine, adzakuzunzani inunso.” (Yoh. 15:20) Koma kubwezera chipongwe n’kosathandiza ngakhale pang’ono. Kodi tiyenera kutani m’malomwake? Mtumwi Petulo analemba kuti: “Pangani Khristu kukhala woyera m’mitima mwanu, monga Ambuye. Khalani okonzeka nthawi zonse kuyankha aliyense wofuna kudziwa chifukwa cha chiyembekezo chimene muli nacho, koma ayankheni ndi mtima wofatsa ndi mwa ulemu waukulu.” (1 Pet. 3:15) Tikamachita zinthu mwaulemu ndiponso kuyankha modekha anthu amene atichitira chipongwe, tikhoza kufewetsa mtima wawo.—Tito 2:7, 8.
12 Kodi pali chilichonse chimene tingachite kuti tikonzekere kuchita zimene zingasangalatse Mulungu, munthu wina akatinenera mawu achipongwe? Inde. Paulo anatilimbikitsa kuti: “Nthawi zonse mawu anu azikhala achisomo, okoleretsa ndi mchere, kuti mudziwe mmene mungayankhire wina aliyense.” (Akol. 4:6) Ngati titakhala ndi chizolowezi chosonyeza ulemu kwa anthu a m’banja mwathu, anzathu akusukulu, anzathu akuntchito, anthu akumpingo, ndi anthu am’dera limene timakhala, ndiye kuti tingakhale okonzeka kuchita zinthu zoyenera Mkhristu, anthu ena akatichitira zinthu zachipongwe.—Werengani Aroma 12:17-21.
13. Perekani chitsanzo cha mmene ulemu ungafewetsere mtima wa anthu otsutsa.
13 Kukhala aulemu ngakhale zinthu zikavuta kumathandiza kuti zinthu ziyende bwino. Mwachitsanzo, m’bale wina ku Japan ananyozedwa ndi anthu awiri amene anawapeza panyumba ina ndipo mmodzi mwa anthuwo anali mlendo panyumbapo. M’baleyo anangochokapo mwaulemu. Akupitiriza kulalikira m’deralo, iye anaona mlendo uja akumuyang’anitsitsa ataima chapatali. M’baleyo anapita pamene panali mlendoyo, ndipo mlendo uja anati: “Pepani chifukwa cha zimene zinachitika zija. Ngakhale kuti tinakunenerani
zinthu zoipa, ndinadabwa kuona kuti munapitirizabe kumwetulira. Kodi ndingatani kuti inenso ndikhale wotero?” Popeza mwamunayo ntchito inali itamuthera ndipo mayi ake anali atangomwalira kumene, analibe chiyembekezo chilichonse choti angakhalenso wosangalala. M’baleyo anapempha mwamunayo kuti aziphunzira naye Baibulo, ndipo anavomera. Pasanapite nthawi, anayamba kuphunzira Baibulo kawiri pamlungu.Njira Yabwino Kwambiri Yophunzirira Ulemu
14, 15. Kodi atumiki a Yehova m’nthawi za m’Baibulo ankaphunzitsa bwanji ana awo?
14 Makolo oopa Mulungu m’nthawi za m’Baibulo ankayesetsa kuphunzitsa ana awo ulemu kunyumba. Taonani mmene Abulahamu ndi mwana wake Isake analankhulirana mwaulemu pa Genesis 22:7. Nayenso Yosefe anasonyeza kuti anaphunzitsidwa bwino ndi makolo ake. Ataikidwa m’ndende, Yosefe ankalankhula mwaulemu ngakhale kwa akaidi anzake. (Gen. 40:8, 14) Mawu amene Yosefe analankhula kwa Farao anasonyezanso kuti iye anaphunzitsidwa mmene angalankhulire mwaulemu kwa munthu waudindo wapamwamba.—Gen. 41:16, 33, 34.
15 Malamulo Khumi amene ana a Isiraeli anapatsidwa anaphatikizapo lamulo ili: “Uzilemekeza atate wako ndi amako; kuti achuluke masiku ako m’dziko limene Yehova Mulungu wako akupatsa iwe.” (Eks. 20:12) Njira imodzi imene ana akanalemekezera makolo awo, inali kukhala aulemu panyumba. Mwana wamkazi wa Yefita anasonyeza ulemu waukulu kwa bambo ake pochita zinthu mogwirizana ndi lumbiro la bambo akewo, ngakhale kuti linali lovuta kwambiri kulitsatira.—Ower. 11:35-40.
16-18. (a) Kodi makolo angachite chiyani kuti aphunzitse ana ulemu? (b) Kodi phindu lophunzitsa ana ulemu n’lotani?
16 Kuphunzitsa ana athu kuti akhale aulemu n’kofunika kwambiri. Kuti ana akadzakula azidzakhala bwino ndi anzawo, ayenera kuphunzira kupereka moni mwaulemu kwa alendo ndiponso kudya mwaulemu ndi anthu ena. Ayenera kuphunzira kuti m’pofunika kuti azichoka pampando kuti munthu wamkulu akhalepo, azithandiza anthu okalamba ndi odwala, ndiponso akaona anthu atanyamula katundu wolemera aziwalandira. Ayenera kumvetsetsa kufunika kolankhula mwaulemu popempha zinthu, kulandira alendo mwaulemu, kunena kuti “zikomo” ndiponso “pepani.”
17 Kuphunzitsa ana kukhala aulemu kukhoza kuchitika m’njira yosavuta. Njira yabwino kwambiri ndiyo kuwapatsa chitsanzo chabwino. Kurt, amene ali ndi zaka 25 ananena zotsatirazi, pofotokoza mmene iyeyo ndi achimwene ake atatu anaphunzirira kukhala aulemu. Iye anati: “Tinkayang’anitsitsa ndi kumvetsera mwachidwi mayi ndi bambo akamalankhulana mwaulemu komanso akamachitira anthu zinthu mokoma mtima
ndiponso mosonyeza kuti akuwaganizira. Ku Nyumba ya Ufumu, bambo ankanditenga akamacheza ndi abale ndi alongo achikulire misonkhano isanayambe ndiponso ikatha. Ndinkamva mmene ankaperekera moni ndiponso kuona mmene ankalemekezera achikulirewo.” Kurt akupitiriza kuti: “M’kupita kwa nthawi, ndinaphunzira kukhala waulemu ngati bambo angawo. Kuchitira anthu ulemu kumangokhala ngati chibadwa chako. Umayamba kuchita ulemu chifukwa chakuti ukufuna kutero, osati chifukwa chakuti ukuyenera kutero.”18 Kodi nthawi zambiri chimachitika n’chiyani makolo akaphunzitsa ana awo ulemu? Anawo akakula, savutika kupeza anzawo ndiponso amakhala mwamtendere ndi anthu ena. Amakhala okonzeka bwino kugwira ntchito ndi mabwana ndi antchito anzawo. Komanso, ana aulemu, akhalidwe labwino, ndi olongosoka, amasangalatsa makolo awo chifukwa makolowo amaona kuti ntchito yonse imene anagwira pophunzitsa ana awo ulemu, sinapite pachabe.—Werengani Miyambo 23:24, 25.
Ulemu Umatisiyanitsa ndi Dzikoli
19, 20. N’chifukwa chiyani tiyenera kuyesetsa kutsanzira Mulungu wathu wachisomo ndi Mwana wake?
19 Paulo analemba kuti: “Khalani otsanzira Mulungu, monga ana okondedwa.” (Aef. 5:1) Kuti titsanzire Yehova Mulungu ndi Mwana wake, tiyenera kugwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo, ngati zimene takambirana mu nkhani ino. Tikamachita zimenezi, tidzapewa kusonyeza ulemu wachiphamaso pongofuna kukondedwa ndi munthu waudindo wapamwamba kapena pongofuna kupezapo kenakake.—Yuda 16.
20 Masiku ano, pamene tili m’masiku otsiriza a ulamuliro woipa wa Satana, iye akufunitsitsa kuthetseratu makhalidwe abwino amene Yehova wakhazikitsa. Koma Mdyerekezi sangakwanitse kuthetsa ulemu umene Akhristu oona ali nawo. Tiyeni tonsefe tiyesetse kutsanzira Mulungu wathu wachisomo ndi Mwana wake. Tikatero, zolankhula ndi zochita zathu nthawi zonse zidzakhala zosiyana ndi za anthu amwano. Tidzalemekeza dzina la Mulungu wathu waulemu, Yehova, ndipo zimenezi zidzathandiza kuti anthu oona mtima akopeke ndi chipembedzo chake choona.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 6 M’zikhalidwe zina, anthu amaona kuti ndi mwano kuitana munthu wachikulire pomutchula dzina lake loyamba, pokhapokha ngati munthu wachikulireyo atanena kuti palibe vuto kutero. Akhristu ayenera kulemekeza zikhalidwe zoterozo.
Kodi Mukukumbukira?
• Kodi Yehova ndi Mwana wake akutiphunzitsa chiyani pa nkhani yopereka ulemu?
• N’chifukwa chiyani kupatsa anthu moni mwansangala kumapereka chithunzi chabwino cha Akhristufe?
• Kodi ulemu umatithandiza bwanji kuti utumiki wathu ukhale waphindu?
• Kodi makolo ali ndi udindo wotani pophunzitsa ana awo ulemu?
[Mafunso]
[Bokosi patsamba 27]
Yambani ndi Kumwetulira
Anthu ambiri amakayikira kuyamba kucheza ndi munthu amene sakumudziwa. Koma chifukwa chokonda Mulungu ndiponso anthu, Mboni za Yehova zimayesetsa kuphunzira kucheza ndi anthu kuti zizitha kuwaphunzitsa choonadi cha m’Baibulo. Kodi n’chiyani chingakuthandizeni kuti muzichita bwino kwambiri zimenezi?
Pa Afilipi 2:4 tikupezapo mfundo yofunika kwambiri yakuti: “Musasamale zofuna zanu zokha, koma musamalenso zofuna za ena.” Taganizirani mawu amenewa motere: Mukakumana ndi munthu winawake koyamba, iye amakuonani ngati munthu wachilendo. Kodi mungachite chiyani kuti munthuyo amasuke? Kumumwetulira ndi kumupatsa moni mwansangala kungathandize. Koma pali zinanso zimene muyenera kuganizira.
Poyamba kulankhula ndi munthuyo, mwina mwamusokoneza zimene anali kuganiza. Mukayamba kulankhulana naye zimene zili m’maganizo mwanu popanda kuganizira zimene iye akuganizira, mwina sangasangalale nanu. Choncho, ngati pali njira yodziwira zimene munthu winayo akuganiza, bwanji osagwiritsa ntchito zimenezo monga poyambira kucheza kwanu? Yesu anachita zimenezo atakumana ndi mkazi wina pachitsime ku Samariya. (Yoh. 4:7-26) Maganizo a mkaziyo anali pa kutunga madzi. Yesu anayamba kucheza naye nkhani yokhudza madzi omwewo. Ndipo kenako anatha kukambirana naye zinthu zambiri zauzimu.
[Zithunzi patsamba 26]
Kukhala womasuka ndi anthu kungathandize kuti muwalalikire uthenga wabwino
[Chithunzi patsamba 28]
Ulemu ndi wofunika nthawi zonse