Khalani Otetezeka M’gulu la Anthu a Mulungu
Khalani Otetezeka M’gulu la Anthu a Mulungu
“Ndidzakuyamikani mu msonkhano waukulu.”—SAL. 35:18.
1-3. (a) Kodi n’chiyani chingasokoneze ubwenzi wa Akhristu ena ndi Yehova? (b) Kodi anthu a Mulungu angapeze kuti chitetezo?
ALI ku tchuthi, Joe ndi mkazi wake anapita kukasambira m’nyanja ina. Malo amene ankasambirawo panali nsomba za mitundumitundu. Kenako anasambira kupita kumalo akuya kuti akaone mmene malowo alili. Atafika pamalo akuya kwambiri, mkazi wa Joe anati: “Ndikuona kuti kuno n’koopsa kwambiri.” Koma Joe anayankha kuti: “Mtima m’malo. Ndikudziwa chimene ndikuchita.” Patapita kanthawi pang’ono, Joe anangodabwa kuti nsomba zonse zathawa. Kenako anazindikira kuti nsombazo zathawa chinsomba chachikulu chotchedwa shaki. Chinsombacho chinkabwera kumene kunali Joe ndipo chinangotsala pang’ono kumuluma. Koma chitamuyandikira, chinatembenuka n’kumapita.
2 Mkhristu akhoza kutengeka ndi zinthu zokopa za m’dziko la Satanali moti sangadziwe kuti akupita kwakuya. Zinthu zimenezi ndi monga zosangalatsa, ntchito ndiponso chuma. Joe, amene ndi mkulu mumpingo, ananena kuti: “Zimene zinandichitikirazi zandithandiza kuganiziranso kuti tifunika kusamala posankha anthu ocheza nawo. Tiziyesetsa kucheza ndi anthu a mumpingo chifukwa tikatero tizikhala m’malo otetezeka ndiponso tizikhala osangalala.” Tisalole kuti zinthu za m’dzikoli zitichititse kusiyana ndi abale athu mumpingo, chifukwa kuchita zimenezi kuli ngati kusambira m’malo akuya kwambiri. Tikaona kuti tayamba kusiyana ndi abale athu mumpingo, tiyenera kubwerera msanga m’gulu la anthu a Mulungu. Tikalephera kuchita zimenezi, ubwenzi wathu ndi Yehova ukhoza kusokonekera.
3 Masiku ano, dzikoli ndi loopsa kwambiri kwa Akhristu. (2 Tim. 3:1-5) Satana akudziwa kuti nthawi yake yatsala yochepa kwambiri, choncho akufunitsitsa kudya aliyense amene sali tcheru. (1 Pet. 5:8; Chiv. 12:12, 17) Komabe chitetezo chilipo. Yehova wapatsa anthu ake malo auzimu othawirako. Malo amenewa ndi mpingo wachikhristu ndipo ndi malo otetezeka kwambiri.
4, 5. Kodi anthu ambiri amamva bwanji akaganizira za tsogolo lawo, ndipo n’chifukwa chiyani?
4 Dzikoli silipereka chitetezo chokwanira ndipo silithandiza anthu kukhala ndi mtendere wa mumtima. Anthu ambiri amakhala mwamantha chifukwa cha zinthu monga umbanda, chiwawa, kukwera mitengo kwa zinthu ndiponso kusintha kwa nyengo. Anthu onse amavutika chifukwa cha matenda ndiponso ukalamba. Ngakhale ena amene ali ndi zinthu monga ntchito yabwino, nyumba, ndalama zambiri ndiponso thanzi labwino, amada nkhawa posadziwa chimene chiwagwere mawa.
5 Ndiponso anthu ambiri alibe mtendere wa mumtima. N’zomvetsanso chisoni kuti anthu ambiri amene ankaganiza kuti zinthu ziziwayendera bwino akakhala pabanja, amakhumudwa poona kuti zomwe ankayembekezera sizikuchitika. Anthu ambiri amene amapita ku tchalitchi asokonezeka moti akusowa mtengo wogwira ndipo amakayikira ngati zinthu zimene akuphunzitsidwa zilidi zofunika. Iwo amachita zimenezi chifukwa cha khalidwe loipa la atsogoleri a zipembedzo zawo ndiponso zinthu zotsutsana ndi Malemba zimene atsogoleriwo amaphunzitsa. Choncho chifukwa chosowa chochita, anthu ambiri amaona kuti ndi bwino kumangodalira sayansi kapena zinthu zabwino zimene ena angawachitire. Ndiyetu n’zosadabwitsa kuti anthu ena amaona kuti ndi
osatetezeka ndipo safuna n’komwe kuganizira za tsogolo lawo.6, 7. (a) Kodi n’chiyani chimachititsa kuti anthu amene amatumikira Mulungu aziona zinthu mosiyana ndi amene samutumikira? (b) Kodi tikambirana chiyani?
6 Anthu amene ali mumpingo wachikhristu amaona zinthu mosiyana kwambiri ndi anthu ena. Ngakhale kuti anthu a Yehovafe timakumananso ndi mavuto amene anthu onse amakumana nawo, ifeyo timaona mavutowo mosiyana ndi mmene anthu ena amawaonera. (Werengani Yesaya 65:13, 14; Malaki 3:18.) N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa Baibulo limatiuza momveka bwino kuti nthawi imene tikukhala ino ndi yovuta ndiponso limatiuza zimene tiyenera kuchita tikakumana ndi mavuto. Zimenezi zimachititsa kuti tisamadere nkhawa kwambiri za tsogolo lathu. Popeza timalambira Yehova, timakhala otetezeka ku maganizo otsutsana ndi Malemba, makhalidwe oipa ndipo timakhalanso otetezeka ku zotsatira za zinthu zimenezi. Choncho, anthu amene ali mumpingo wachikhristu amakhala ndi mtendere umene anthu ena alibe.—Yes. 48:17, 18; Afil. 4:6, 7.
7 Pali zitsanzo zambiri zimene zingatithandize kuona kuti anthu amene amatumikira Yehova amakhala otetezeka kusiyana ndi anthu amene samutumikira. Zitsanzo zimenezi zitithandiza kuonanso bwino maganizo ndi zochita zathu kuti tidziwe ngati tikutsatira malangizo a Mulungu ndi mtima wonse. Mulungu amatipatsa malangizo amenewa n’cholinga chakuti atiteteze.—Yes. 30:21.
“Ine Ndikadagwa”
8. Kodi atumiki a Yehova nthawi zonse akhala akuchita chiyani?
8 Kuyambira kale, anthu amene amasankha kutumikira ndiponso kumvera Yehova amapewa kucheza kwambiri ndi anthu amene samutumikira. Ndipotu Yehova anasonyeza kuti padzakhala udani pakati pa olambira ake ndi anthu amene amatsatira Satana. (Gen. 3:15) Chifukwa chakuti anthu a Mulungu amatsatira mfundo zouziridwa ndi Mulungu, iwo amakhala osiyana ndi anthu ena. (Yoh. 17:15, 16; 1 Yoh. 2:15-17) Koma kuchita zimenezi sikukhala kophweka nthawi zonse. Nthawi zina atumiki ena a Yehova amakayikira ubwino wokhala moyo wodzimana.
9. Fotokozani mavuto amene wolemba Salmo 73 anakumana nawo.
Salmo 73. Wamasalmoyo anafunsa kuti n’chifukwa chiyani nthawi zambiri anthu oipa amaoneka kuti zinthu zikuwayendera bwino ndiponso amakhala osangalala, pamene anthu amene amayesetsa kutumikira Yehova amakumana ndi mavuto.—Werengani Salmo 73:1-13.
9 Atumiki a Yehova ena anakayikirapo ngati anasankha bwino ndipo mmodzi mwa anthu amenewa anali mbadwa ya Asafu. Iye ndi amene analemba10. N’chifukwa chiyani nkhani imene wamasalmo ananena ndi yofunika kwambiri kwa inuyo?
10 Kodi munayamba mwadzifunsapo mafunso ngati amene wamasalmo analembawa? Ngati ndi choncho musadziimbe mlandu poganiza kuti chikhulupiriro chanu n’chochepa. Ndipotu atumiki a Yehova ambiri kuphatikizapo amene anawagwiritsa ntchito polemba Baibulo anakhalaponso ndi maganizo amenewa. (Yobu 21:7-13; Sal. 37:1; Yer. 12:1; Hab. 1:1-4, 13) Anthu onse amene amatumikira Mulungu ayenera kupeza yankho la funso lakuti: Kodi ndi bwino kutumikira Mulungu ndiponso kumumvera? Yankho la funso limeneli limakhudza nkhani imene Satana anayambitsa m’munda wa Edene. Nkhaniyi ndi yofuna kudziwa amene ali woyenera kulamulira chilengedwe chonse. (Gen. 3:4, 5) Choncho tonsefe tifunika kuganizira bwino nkhani imene wamasalmoyu ananena. Kodi tiyenera kuchitira nsanje anthu oipa amene akuoneka kuti zinthu zikuwayendera bwino? Kodi ndi bwino kusiya kutumikira Yehova n’kumachita zimene anthuwo akuchita? Satana amafuna kuti tisiye Yehova n’kumachita zimene anthu oipawa amachita.
11, 12. (a) Kodi wamasalmo anathetsa bwanji maganizo okayikira amene anali nawo, ndipo kodi tikuphunzirapo chiyani? (b) N’chiyani chakuthandizani kuona kuti zimene wamasalmo ananena ndi zoona?
11 Kodi n’chiyani chimene chinathandiza wamasalmo kuti asiye kukayikira zimene ankachita? Ngakhale kuti anavomereza kuti anatsala pang’ono kugwa, maganizo ake anasintha iye atalowa “m’zoyera za Mulungu.” Zimenezi zikutanthauza kuti anayamba kusonkhana ndi anthu okonda zinthu zauzimu m’chihema cha Mulungu, n’kuyambanso kuganizira cholinga cha Mulungu. Kenako wamasalmo anazindikira kuti anafunika kupewa zinthu zoipa zimene zidzachitikire anthu oipa. Iye anaona kuti zochita zawozo zinawachititsa kukhala “poterera.” Wamasalmoyu anadziwa kuti anthu onse amene ankachita khalidwe lotsutsana ndi zofuna za Yehova, adzatha modzidzimutsa koma Yehova adzathandiza anthu amene amamutumikira. (Werengani Salmo 73:16-19, 27, 28.) N’zosakayikitsa kuti inuyo mwaona kuti mawu amenewa ndi oona. Munthu akamangochita zofuna zake popanda kutsatira malamulo a Mulungu amaoneka ngati zinthu zikumuyendera koma sangalephere kukumana ndi zotsatira zoipa za zochita zakezo.—Agal. 6:7-9.
12 Kodi zimene zinamuchitikira wamasalmoyu zikutiphunzitsanso chiyani? Iye anapeza chitetezo ndiponso nzeru pakati pa anthu a Mulungu. Iye anayamba kuganiza bwino atafika kumalo olambirira Yehova. Masiku anonso, tikhoza kupeza malangizo abwino ndiponso chakudya chauzimu kumisonkhano ya mpingo. Ndiyetu mpake kuti Yehova amauza atumiki ake kuti azisonkhana. Akamatero amalimbikitsidwa ndiponso amapeza nzeru.—Yes. 32:1, 2; Aheb. 10:24, 25.
Muzisankha Mwanzeru Anthu Ocheza Nawo
13-15. (a) Kodi Dina anakumana ndi zotani ndipo izi zikutiphunzitsa chiyani? (b) N’chifukwa chiyani tinganene kuti kucheza ndi Akhristu anzathu kungatiteteze?
13 Dina yemwe anali mwana wamkazi wa Yakobo ndi mmodzi mwa anthu amene anakumana ndi mavuto chifukwa chocheza kwambiri ndi anthu osalambira Mulungu woona. Nkhani ya m’buku la Genesis imasonyeza kuti iye ankakonda kucheza ndi atsikana a ku Kanani m’dera limene iye ndi makolo ake ankakhala. Akanani sankatsatira mfundo za makhalidwe abwino zimene anthu olambira Yehova ankatsatira. Zimene akatswiri ofufuza zinthu zakale apeza, zikusonyeza kuti mosiyana ndi anthu olambira Eks. 23:23; Lev. 18:2-25; Deut. 18:9-12) Taganizirani zimene zinachitikira Dina chifukwa chocheza kwambiri ndi anthu amenewa.
Yehova, zochita za Akanani zinachititsa kuti m’dziko mwawo muzichitika zinthu monga kulambira mafano, chiwerewere, kulambira milungu yawo mwa kugonana ndiponso chiwawa. (14 Munthu wina dzina lake Sekemu yemwe “anali wolemekezedwa woposa onse a pa banja la atate wake,” ataona Dina “anam’tenga nagona ndi iye, namuipitsa.” (Gen. 34:1, 2, 19) Izitu zinali zomvetsa chisoni kwambiri. Kodi mukuganiza kuti Dina ankaganiza kuti zimenezi zingamuchitikire? N’kutheka kuti iye ankangofuna kucheza ndi achinyamata achikanani, ndipo ankaona kuti panalibe vuto lililonse. Komatu maganizo a Dina amenewa anali olakwika.
15 Kodi tikuphunzira chiyani pa nkhani imeneyi. Mfundo ndi yakuti, n’zosatheka kucheza kwambiri ndi anthu osakhulupirira popanda kukumana ndi zotsatira zoipa. Malemba amati: “Mayanjano oipa amawononga makhalidwe abwino.” (1 Akor. 15:33) Koma kucheza ndi anthu omwe ndi okhulupirira, otsatira mfundo za makhalidwe abwino ndiponso okonda Yehova, kungakutetezeni. Anthu amenewa angakuthandizeni kuti mukhale anzeru.—Miy. 13:20.
“Mwasambitsidwa Kukhala Oyera”
16. Kodi mtumwi Paulo anafotokoza kuti ena mumpingo wa ku Korinto anali otani?
16 Mpingo wachikhristu wathandiza anthu ambiri kukhala oyera mwa kusiya makhalidwe oipa. M’kalata yoyamba imene mtumwi Paulo analembera mpingo wa ku Korinto, iye anayamikira Akhristuwo chifukwa chakuti anasintha n’kuyamba kukhala mogwirizana ndi mfundo za makhalidwe abwino za Mulungu. Ena mwa anthu amenewa anali adama, opembedza mafano, achigololo, amuna ogonana ndi amuna anzawo kapena akazi ogonana ndi akazi anzawo, akuba, zidakwa ndi ena otero. Paulo anawauza kuti: “Koma mwasambitsidwa kukhala oyera.”—Werengani 1 Akorinto 6:9-11.
17. Kodi kutsatira mfundo za m’Baibulo kwasintha bwanji moyo wa anthu ambiri?
17 Anthu osakhulupirira sakhala ndi mfundo zabwino zimene amatsatira. Iwo amangoyendera nzeru zawo, apo ayi amangotsatira makhalidwe oipa amene anzawo akuchita. Izi n’zimenenso anthu ena a ku Korinto ankachita asanakhale okhulupirira. (Aef. 4:14) Kudziwa molondola Mawu a Mulungu ndiponso cholinga chake, kungathandize munthu kusintha n’kukhala ndi moyo wabwino chifukwa chotsatira mfundo za m’Malemba. (Akol. 3:5-10; Aheb. 4:12) Anthu ambiri amene ali mumpingo wachikhristu masiku ano angakuuzeni kuti asanaphunzire mfundo zolungama za Yehova ndiponso asanayambe kuzitsatira pa moyo wawo, anali ndi khalidwe loipa. Koma iwo sankakhala osangalala. Anapeza mtendere wa mumtima atayamba kusonkhana ndi anthu a Mulungu ndiponso kutsatira mfundo za m’Baibulo.
18. Kodi wachinyamata wina anakumana ndi zotani, ndipo kodi zimenezi zikutiphunzitsa chiyani?
18 Koma anthu amene anachoka m’malo otetezeka omwe ndi mpingo wachikhristu panopa akunong’oneza bondo. Mlongo wina yemwe tangom’patsa dzina loti Tanya anafotokoza kuti: ‘Achibale anga anandiphunzitsa pang’ono choonadi koma kenako ndili ndi zaka 16 ndinasiya n’cholinga chakuti ndisangalale ndi zinthu za m’dzikoli.’ Zina mwa zotsatira zake zinali zoti iye anatenga mimba ndipo anachotsa mimbayo. Iye anati: “Zaka zitatu zimene ndakhala kunja kwa mpingo, zandisiyira zipsera zikuluzikulu m’maganizo mwanga. Chinthu chimene chimandipweteka kwambiri ndi chakuti ndinapha mwana wanga wosabadwa. . . . Ndikufuna kuuza achinyamata onse amene akufuna ‘kulawa’ za m’dzikoli ngakhale pang’ono chabe kuti: ‘Asayerekeze
kuchita zimenezo.’ Poyamba zingaoneke ngati ukunjoya koma zotsatira zake zimakhala zopweteka. Dzikoli silingatipatse zinthu zabwino, koma zoipa zokhazokha. Ine ndikulidziwa bwino chifukwa ndinayesapo. Ndi bwino kukhalabe m’gulu la Yehova chifukwa kuchita zimenezi n’kumene kumabweretsa chimwemwe.”19, 20. Kodi mpingo wachikhristu umatiteteza bwanji?
19 Kodi mukuganiza kuti chikanakuchitikirani n’chiyani mukanakhala kuti munachoka mumpingo wachikhristu womwe ndi malo otetezeka? Anthu ambiri safuna m’pang’ono pomwe kuganizira mmene moyo wawo unalili asanaphunzire choonadi. (Yoh. 6:68, 69) Mukhoza kukhalabe otetezeka ku zinthu zoipa ndiponso zomvetsa chisoni zomwe zafala m’dziko la Satanali, mwa kugwirizana kwambiri ndi abale ndi alongo anu achikhristu. Kucheza ndi anthu amenewa ndiponso kupezeka pamisonkhano ya mpingo nthawi zonse, kudzakuthandizani kukumbukira kuti mfundo zolungama za Yehova ndi zothandiza ndiponso kudzakuchititsani kuti muzizitsatira pa moyo wanu. Pali zifukwa zomveka zokuchititsani ‘kuyamika Yehova mu msonkhano waukulu’ ngati mmene anachitira wamasalmo.—Sal. 35:18.
20 N’zoona kuti Akhristu onse nthawi zina amavutika kuti akhalebe okhulupirika. Pa nthawi yotereyi, amafuna munthu wina atawathandiza kusankha zoyenera kuchita. Kodi inuyo ndiponso anthu ena onse mumpingo, mungawathandize bwanji Akhristu anzanu amene akukumana ndi mavuto? Nkhani yotsatira ifotokoza mmene ‘mungapitirizire kutonthoza ndiponso kulimbikitsa’ abale anu.—1 Ates. 5:11.
Kodi Mungayankhe Bwanji?
• Kodi zimene zinamuchitikira wolemba Salmo 73 zikutiphunzitsa chiyani?
• Kodi zimene zinachitikira Dina zikutiphunzitsa chiyani?
• N’chifukwa chiyani tinganene kuti mungapeze chitetezo mumpingo wachikhristu?
[Mafunso]
[Zithunzi patsamba 7]
Musachoke mumpingo chifukwa ndi malo otetezeka