Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Khalani Odzipereka pa Kulambira Koona

Khalani Odzipereka pa Kulambira Koona

Khalani Odzipereka pa Kulambira Koona

“Zokolola n’zochuluka, koma antchito ndi ochepa.”​—MAT. 9:37.

1. Kodi n’chiyani chimene chingachititse munthu kuchita changu?

TIYEREKEZE kuti munthu wina wadwala kwambiri, kodi mungachite chiyani? Mungapite naye kuchipatala “MWACHANGU.” Tiyerekezenso kuti mukupita kumsonkhano wofunika kwambiri koma mwachedwa, kodi mungachite chiyani? Mungachite zinthu “MWACHANGU.” N’zoonadi, ngati pali zinthu zina zoti muchite koma nthawi ikutha mumapanikizika ndiponso mumada nkhawa. Mumayamba kupumira m’mwamba ndipo mumachita zinthu mwachangu kwambiri komanso mwakhama.

2. Kodi ndi ntchito iti imene Akhristu masiku ano ayenera kuigwira mwachangu kwambiri?

2 Kwa Akhristu oona masiku ano, ntchito yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu ndi kuphunzitsa anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzira a Yesu, ndi yofunika kuigwira mwachangu kwambiri. (Mat. 24:14; 28:19, 20) Pofotokoza zimene Yesu ananena, Maliko yemwe anali wophunzira wa Yesu analemba kuti ntchito imeneyi iyenera kuchitika “choyamba” mapeto asanafike. (Maliko 13:10) Umu ndi mmene ziyenera kukhalira. Yesu anati: “Zokolola n’zochuluka, koma antchito ndi ochepa.” Munthu sasiya zokolola m’munda kuopera kuti zingawonongeke.​—Mat. 9:37.

3. Kodi anthu ambiri achita chiyani atadziwa kuti ntchito yolalikira ndi yofunika kuigwira mwachangu?

3 Popeza ntchitoyi ndi yofunika kwambiri kwa ife tiyenera kutherapo nthawi, mphamvu ndiponso kuikirapo mtima mmene tingathere. Chosangalatsa n’chakuti anthu ambiri akuchita zimenezi. Ena ayamba kukhala moyo wosalira zambiri n’cholinga choti ayambe utumiki wa nthawi zonse monga upainiya, umishonale kapena kukatumikira pa Beteli. Iwo ndi otanganidwa kwambiri. Abale ndi alongo amenewa alolera kudzimana zinthu zambiri komanso amakumana ndi mavuto osiyanasiyana. Ngakhale zili choncho, iwo adalitsidwa kwambiri ndi Yehova. Timawanyadira kwambiri anthu amenewa. (Werengani Luka 18:28-30.) Abale ndi alongo ena sangakwanitse kuchita utumiki wa nthawi zonse koma amayesetsa kuchita zonse zimene angathe pothandiza anthu kuti apulumuke ndipo ena mwa anthu amene amawathandiza ndi ana athu.​—Deut. 6:6, 7.

4. Kodi n’chiyani chingachititse anthu ena kuiwala kuti afunika kukhala achangu?

4 Malinga ndi zimene takambiranazi, ntchito yofunika kuigwira mwachangu imakhala ndi malire ake. Panopa tikukhala m’masiku otsiriza ndipo pali umboni wa zimenezi. Baibulo komanso zochitika m’dzikoli zimatsimikizira zimenezi. (Mat. 24:3, 33; 2 Tim. 3:1-5) Komabe palibe munthu amene akudziwa tsiku limene mapeto adzafike. Pofotokoza “chizindikiro” cha “mapeto a nthawi ino,” Yesu ananena kuti: “Kunena za tsikulo ndi ola lake, palibe amene akudziwa, ngakhale angelo akumwamba kapenanso Mwana, koma Atate yekha.” (Mat. 24:36) Chifukwa cha zimenezi, ena angalephere kuchita zinthu mwachangu, makamaka ngati akhala akutumikira Mulungu kwa nthawi yaitali. (Miy. 13:12) Kodi inunso mumamva choncho nthawi zina? Kodi n’chiyani chingatithandize kukhala ndi mtima wachangu ndiponso kupitiriza kukhala ndi mtima umenewu pa ntchito imene Yehova Mulungu ndi Yesu Khristu atipatsa.

Muziganizira za Yesu Amene Anatipatsa Chitsanzo

5. Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti anali wachangu pa utumiki wake?

5 Pa anthu onse amene anatumikira Yehova mwachangu, Yesu Khristu ndi chitsanzo chabwino kwambiri. Chifukwa china chimene chinamuchititsa kuti akhale wachangu chinali kuchuluka kwa ntchito yoti agwire pa zaka zitatu ndi hafu. Komabe Yesu anachita zambiri zogwirizana ndi kulambira koona kuposa zimene wina aliyense anachitapo. Iye anathandiza anthu kudziwa dzina ndiponso cholinga cha Atate wake. Analalikira uthenga wabwino wa Ufumu, anauza anthu poyera za chinyengo ndiponso ziphunzitso zabodza za atsogoleri a chipembedzo ndipo anasonyeza kuti ali ku mbali ya ulamuliro wa Yehova mpaka pamene anafa. Iye anayesetsa kuyendayenda m’dziko kuti aphunzitse, kuthandiza ndiponso kuchiritsa anthu. (Mat. 9:35) Palibe munthu aliyense amene anachita zinthu zambiri chonchi pa nthawi yochepa ngati mmene anachitira Yesu. Yesu anagwira ntchito mwakhama kwambiri kuposa munthu wina aliyense.​—Yoh. 18:37.

6. Kodi Yesu ankaganizira kwambiri za chiyani pa moyo wake?

6 Kodi n’chiyani chinalimbikitsa Yesu kugwira ntchito mwakhama pa utumiki wake wonse? Mosakayikira Yesu ankadziwa kuchokera mu ulosi wa Danieli, nthawi imene Yehova anakonza kuti iye agwire ntchito yake. (Dan. 9:27) Malinga ndi ulosiwu, utumiki wake unayenera kutha cha “pakatikati pa mlunguwo” kapena kuti patatha zaka zitatu ndi hafu. Atangolowa mu Yerusalemu kumayambiriro kwa chaka cha 33 C.E., Yesu anati: “Nthawi yafika yakuti Mwana wa munthu alemekezedwe.” (Yoh. 12:23) Ngakhale kuti Yesu ankadziwa kuti imfa yake yayandikira, iye sankangoganizira zimenezi ndipo izi si zimene zinkamuchititsa kugwira ntchito mwakhama. Iye ankafuna kugwiritsa ntchito mpata uliwonse pochita chifuniro cha Atate wake ndiponso kusonyeza kuti amakonda anthu anzake. Chifukwa cha chikondi chimenechi, iye ankasonkhanitsa ophunzira ake n’kuwaphunzitsa kenako ankawatumiza kuti akalalikire. Yesu ankachita zimenezi n’cholinga choti ophunzirawo apitirize ntchito imene iye anaiyamba ndipo iwo anali kudzachita zambiri kuposa zimene Yesuyo anachita.​—Werengani Yohane 14:12.

7, 8. Kodi ophunzira a Yesu anamva bwanji Yesu atayeretsa kachisi, nanga n’chifukwa chiyani Yesu anachita zimenezi?

7 Zimene Yesu anachita nthawi ina zinasonyeza bwino kuti iye anali wodzipereka kwambiri. Anachita zimenezi chakumayambiriro kwa utumiki wake pa nyengo ya Pasika mu 30 C.E. Yesu ndi ophunzira ake atafika m’kachisi ku Yerusalemu anapeza “ogulitsa ng’ombe, nkhosa ndi nkhunda komanso osintha ndalama ali m’kachisi atakhala m’mipando yawo.” Kodi Yesu anachita chiyani ataona zimenezi, nanga ophunzira ake anamva bwanji ndi zimene Yesu anachitazi?​—Werengani Yohane 2:13-17.

8 Zimene Yesu anachita ndiponso kulankhula pa nthawi imeneyi zinakumbutsa ophunzira ake mawu aulosi opezeka mu salimo la Davide akuti: “Pakuti kudzipereka kwambiri panyumba yanu kwandidya.” (Sal. 69:9) N’chifukwa chiyani zinali choncho? Chifukwa chakuti zimene Yesu anachita zikanamuika pa ngozi. Ndipotu akuluakulu a pakachisipo monga ansembe, alembi ndi anthu ena ndi amene ankalimbikitsa anthu kuchita malondawa pakachisi. Choncho zimene Yesu anachita pouza anthu poyera chinyengo cha atsogoleri achipembedzo komanso kusokoneza mapulani awo kukanachititsa kuti adane naye kwambiri. Ophunzira ake anazindikira kuti iye anachita zimenezi chifukwa chakuti anali ‘wodzipereka kwambiri panyumba ya Mulungu’ kapena kuti pa kulambira koona. Koma kodi mawu akuti kudzipereka kwambiri amatanthauza chiyani? Kodi ndi osiyana ndi mawu akuti changu?

Kudzipereka N’kosiyana ndi Changu

9. Kodi kudzipereka kumatanthauza chiyani?

9 Buku lina limati kudzipereka kumatanthauza kukhala ndi mtima wofunitsitsa kuchita chinthu chinachake ndipo n’kofanana ndi khama. Yesu analidi wakhama ndipo ankafunitsitsa kutumikira. N’chifukwa chake Baibulo lina limamasulira mawuwa kuti: “Kudzipereka kwambiri pa nyumba yanu kukuyaka ngati moto mumtima mwanga.” (Today’s English Version) Chochititsa chidwi n’chakuti m’zinenero za m’madera ena a ku Asia, mawu akuti kudzipereka amatanthauza “kutentha kwa mu mtima” ngati kuti muli moto. Mpake kuti ophunzira anakumbukira mawu a Davide ataona zimene Yesu anachita pakachisi. Kodi n’chiyani chinachititsa mtima wa Yesu kuyaka ndiponso kuchita zinthu mwanjira imeneyi?

10. Kodi m’Baibulo mawu akuti “kudzipereka” amatanthauza chiyani?

10 M’salimo la Davide, mawu akuti “kudzipereka” ndi ochokera ku mawu achiheberi omwe nthawi zambiri amamasuliridwa kuti “nsanje” m’mavesi ena a m’Baibulo. Mu Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika mawu amenewa nthawi zina amamasuliridwa kuti ‘kufuna kuti anthu azidzipereka kwa iye yekha.’ (Werengani Eksodo 20:5; 34:14; Yoswa 24:19.) Buku lina lomasulira mawu a m’Baibulo limati: “Mawu amenewa kawirikawiri amagwiritsidwa ntchito pa nkhani ya ukwati . . . Mwamuna kapena mkazi wansanje amafuna kuti iye yekha azikondedwa choncho Mulungu amafuna kuti anthu Ake azilambira Iye yekha.” Choncho m’Baibulo mawu akuti kudzipereka samangotanthauza khama kapena kutengeka maganizo pochita zinazake ngati mmene anthu okonda masewera enaake amachitira. Kudzipereka kwa Davide kunali nsanje yoyenera. Iye sankafuna kuti anthu apanduke kapena kukhala onyoza ndipo ankafunitsitsa kuteteza dzina labwino komanso kukonza zinthu zimene zinalakwika.

11. Kodi n’chiyani chinachititsa Yesu kukhala wodzipereka kwambiri?

11 Ophunzira a Yesu sanalakwitse pogwirizanitsa mawu a Davide ndi zimene anaona Yesu akuchita pakachisi. Yesu ankachita khama kwambiri osati chifukwa chakuti ankadziwa kuti ntchito yake ili ndi malire, koma chifukwa choti anali wodzipereka kwambiri kapena kuti ankachitira nsanje dzina la Atate wake ndiponso kulambira koona. Iye ataona kuti anthu akunyoza dzina la Mulungu anachita nsanje ndipo anadzipereka kwambiri kuti akonze zimene zinalakwikazo. Yesu ataona kuti anthu osauka akuponderezedwa ndiponso kudyeredwa masuku pamutu ndi atsogoleri achipembedzo, iye anadziperekanso kuti athandize anthuwo ndiponso kutsutsa mwamphamvu atsogoleri achipembedzo oponderezawo.​—Mat. 9:36; 23:2, 4, 27, 28, 33.

Khalani Odzipereka pa Kulambira Koona

12, 13. Kodi atsogoleri a Matchalitchi Achikhristu achita chiyani ndi (a) dzina la Mulungu? (b) Ufumu wa Mulungu?

12 Zochitika m’zipembedzo za masiku ano n’zofanana ndi zimene zinkachitika m’nthawi ya Yesu ndipo panopa zaipa kwambiri. Mwachitsanzo, kumbukirani kuti chinthu choyamba chimene Yesu anaphunzitsa otsatira ake kuti azipempherera ndi dzina la Mulungu. Iye anawauza kuti azipemphera kuti: “Dzina lanu liyeretsedwe.” (Mat. 6:9) Kodi atsogoleri achipembedzo masiku ano, makamaka Matchalitchi Achikhristu amaphunzitsa anthu kuti adziwe dzina la Mulungu ndiponso kuti aliyeretse kapena kuti kulilemekeza? Ayi ndithu. M’malomwake iwo amaphunzitsa anthu zinthu zabodza monga zoti pali Mulungu atate, mwana ndi mzimu woyera, zoti moyo wa munthu sufa, ndiponso zoti oipa akawotchedwa. Izi zimachititsa anthu kuganiza kuti Mulungu ndi wosamvetsetseka, wankhanza ndiponso wozunza anthu. Iwo amanyozetsa Mulungu chifukwa cha zinthu zoipa zimene amachita komanso chinyengo chawo. (Werengani Aroma 2:21-24.) Iwo akuyesetsa mmene angathere kuti anthu asagwiritse ntchito dzina lenileni la Mulungu ndipo afika polichotsa m’Baibulo. Chifukwa cha zimenezi, iwo amalepheretsa anthu kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu.​—Yak. 4:7,8.

13 Yesu anaphunzitsanso otsatira ake kuti azipempherera Ufumu wa Mulungu. Iye anawauza kuti azipemphera kuti: “Ufumu wanu ubwere. Chifuniro chanu chichitike, monga kumwamba, chimodzimodzinso pansi pano.” (Mat. 6:10) Ngakhale kuti atsogoleri a Matchalitchi Achikhristu amanena mobwerezabwereza pemphero limeneli, iwo amalimbikitsa anthu kuti azichita nawo zandale ndiponso kuchirikiza magulu ena a anthu. Kuwonjezera pamenepa, iwo amanyoza anthu amene amalalikira ndi kuchitira umboni za Ufumuwu. Zotsatira zake n’zakuti anthu ambiri amene amati ndi Akhristu sakonda kukambirana za Ufumu wa Mulungu ndipo saukhulupirira n’komwe.

14. Kodi atsogoleri a Matchalitchi Achikhristu achita zotani ndi Mawu a Mulungu?

14 Popemphera kwa Mulungu, Yesu ananena kuti “Mawu anu ndiwo choonadi.” (Yoh. 17:17) Asanapite kumwamba, Yesu ananena kuti adzaika “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” yemwe azidzapereka chakudya kwa anthu ake. (Mat. 24:45) Atsogoleri a Matchalitchi Achikhristu amanena kuti iwo ndi atumiki a Mawu a Mulungu. Koma kodi iwo asonyeza kuti ndi okhulupirika pogwira ntchito ya Mbuye wawo? Ayi. M’malomwake iwo amanena kuti nkhani za m’Baibulo ndi zongopeka. M’malo mopereka chakudya chauzimu kwa nkhosa, kuzilimbikitsa komanso kuzithandiza kukhala zozindikira, atsogoleriwa amangouza anthu zinthu zowakomera m’khutu zomwe ndi nzeru za anthu. Kuwonjezera pamenepa, iwo saphunzitsa mfundo za Mulungu za makhalidwe abwino kwa anthu awo poopa kuti angawakhumudwitse.​—2 Tim. 4:3, 4.

15. Kodi mumamva bwanji ndi zimene atsogoleri achipembedzo achita m’dzina la Mulungu?

15 Chifukwa cha zinthu zimene ena amachita m’dzina la Mulungu, anthu ambiri a mitima yabwino agwiritsidwa mwala ndipo ena sakhulupiriranso Mulungu ndi Baibulo. Anthu amenewa agwera m’manja mwa Satana ndi dongosolo loipali. Kodi inuyo mukamaona ndiponso kumva zinthu zoterezi zikuchitika tsiku ndi tsiku mumamva bwanji? Popeza ndinu mtumiki wa Yehova, kodi mukaona anthu akunyoza dzina la Mulungu sizikuchititsani kufunitsitsa kukonza zolakwikazo? Kodi mukaona anthu a mtima wabwino akunamizidwa ndiponso kudyeredwa masuku pamutu sizikuchititsani kufunitsitsa kulimbikitsa anthu oponderezedwa? Yesu ataona anthu a “onyukanyuka ndi otayika ngati nkhosa zopanda m’busa,” sanangowamvera chisoni koma “anayamba kuwaphunzitsa zinthu zambiri.” (Mat. 9:36; Maliko 6:34) Choncho tili ndi zifukwa zokhalira odzipereka kwambiri pa kulambira koona ngati mmene Yesu anachitira.

16, 17. (a) Kodi n’chiyani chiyenera kutilimbikitsa kuchita khama kwambiri mu utumiki? (b) Kodi tidzakambirana chiyani m’nkhani yotsatira?

16 Tikamaona utumiki wathu mwa njira imeneyi, timamvetsa tanthauzo la mawu a mtumwi Paulo opezeka pa 1 Timoteyo 2:3, 4. (Werengani.) Timachita khama mu utumiki osati kokha chifukwa chakuti tikukhala m’masiku otsiriza, koma chifukwa chakuti tikudziwa kuti ndi cholinga cha Mulungu. Iye amafuna kuti anthu adziwe choonadi molondola. Izi zingawathandize kuti aphunzire kulambira Mulungu, kumutumikira ndiponso kuti adalitsidwe. Timafunitsitsa kuchita zonse zimene tingathe mu utumiki osati chifukwa choti nthawi yatsala yochepa koma chifukwa chakuti timafuna kulemekeza dzina la Mulungu ndiponso kuthandiza anthu kuti adziwe chifuniro chake. Ndifedi odzipereka pa kulambira koona.​—1 Tim. 4:16.

17 Anthu a Yehovafe tadalitsidwa kwambiri chifukwa tikudziwa choonadi pa nkhani ya cholinga cha Mulungu kwa anthu ndiponso dziko lapansi. Tingathe kuthandiza anthu kukhala osangalala komanso kuyembekezera zinthu zabwino m’tsogolo. Tingawasonyeze njira imene ingawathandize kuti adzapulumuke pamene dongosolo la Satanali lizidzawonongedwa. (2 Ates. 1:7-9) M’malo mokhumudwa kapena kutaya mtima chifukwa choona ngati kuti tsiku la Yehova likuchedwa, tiyenera kusangalala podziwa kuti tidakali ndi nthawi yosonyeza kuti ndife odzipereka pa kulambira koona. (Mika 7:7; Hab. 2:3) Kodi tingatani kuti tikhaledi odzipereka? Tidzakambirana zimenezi m’nkhani yotsatira.

Kodi Mungafotokoze?

• N’chiyani chinathandiza Yesu kugwira ntchito mwakhama pa utumiki wake wonse wa padziko lapansi?

• Kodi m’Baibulo mawu akuti “kudzipereka,” amatanthauza chiyani?

• Tchulani zinthu zimene zikuchitika masiku ano zomwe zingatilimbikitse kukhala odzipereka pa kulambira koona.

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 8]

Yesu ankafunitsitsa kuchita chifuniro cha Atate wake ndiponso kusonyeza chikondi kwa anthu anzake

[Chithunzi patsamba 10]

Tili ndi zifukwa zabwino zokhalira odzipereka pa kulambira koona