Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Khalani Okonzeka

Khalani Okonzeka

Khalani Okonzeka

“Khalani okonzeka, chifukwa pa ola limene simukuliganizira, Mwana wa munthu adzabwera.”​—MAT. 24:44.

1, 2. (a) Kodi Baibulo linalosera zinthu ziti zimene zikufanana ndi kuukira kwa nyama yofanana ndi kambuku? (b) Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tipulumuke pamene Khristu azidzawononga oipa?

KWA zaka zambiri munthu wina ankasangalatsa anthu posewera bwinobwino ndi nyama zofanana ndi akambuku koma zokulirapo. Iye anati: “Munthu akazolowerana ndi nyama, zimakhala ngati wapatsidwa mphatso yapamwamba kwambiri padziko lapansi.” Koma pa October 3, 2003, zinthu zinavuta. Mosayembekezereka imodzi mwa nyamazi, yomwe inali yolemera makilogalamu 172, inaukira munthuyu. Iye sanayembekezere kuti nyamayi ingamuukire choncho sanali wokonzeka.

2 Chochititsa chidwi n’chakuti Baibulo linaneneratu za kuukira kwa “chilombo,” ndipo chifukwa cha zimenezi tiyenera kukhala okonzeka. (Werengani Chivumbulutso 17:15-18.) Kodi chilombo chimenechi chidzaukira ndani? Zinthu zidzasintha mwadzidzidzi ndipo dziko la Mdyerekezili lidzagawikana. Chilombo chimenechi, chomwe ndi chofiira kwambiri, chimaimira bungwe la United Nations ndipo “nyanga 10” zimaimira maulamuliro onse andale. Chilombo ndi nyanga 10 zimenezi zidzaukira ndi kusakaza hule, kapena kuti Babulo Wamkulu, yemwe ndi zipembedzo zonyenga zonse pamodzi. Kodi zimenezi zidzachitika liti? Sitikudziwa tsiku kapena ola lake. (Mat. 24:36) Koma chimene tikudziwa n’chakuti zidzachitika pa ola limene sitikuliganizira ndiponso kuti nthawi imene yatsala kuti zimenezi zichitike yafupika. (Mat. 24:44; 1 Akor. 7:29) Choncho m’pofunika kuti tikhale okonzeka mwauzimu kuti pamene zimenezi zizidzachitika komanso pamene Khristu azidzabwera kudzawononga oipa, adzatipulumutse. (Luka 21:28) Kuti tikhaledi okonzeka, tingaphunzire kwa atumiki okhulupirika a Mulungu amene anakhala okonzeka ndipo anaona ndi maso awo kukwaniritsidwa kwa malonjezo a Mulungu. Kodi tidzatengeradi chitsanzo cha anthu amenewa?

Khalani Okonzeka Ngati Nowa

3. Kodi ndi mavuto ati amene Nowa anakumana nawo pamene ankatumikira Mulungu mokhulupirika?

3 Nowa anakhalabe wokonzeka kuti aone kukwaniritsidwa kwa malonjezo a Mulungu. Iye anatero ngakhale kuti pa nthawi imeneyo zinthu zinali zoipa kwambiri padziko lapansi. Taganizirani mavuto amene Nowa anakumana nawo pamene angelo opanduka anavala matupi a anthu n’kudzakhala padziko kuti azigona ndi akazi okongola. Kugonana kwa anthu ndi angelo kumeneku kunachititsa kuti kubadwe anthu amphamvu kwambiri kapena kuti “ziphona,” zimene zinagwiritsa ntchito mphamvu zawo pozunza anthu. (Gen. 6:4) Ndiye taganizirani mmene zinthu zinaipira pamene ziphonazi zinkachita chiwawa kulikonse kumene zinkapita. Izi zinachititsa kuti kuipa kuwonjezeke kwambiri ndipo maganizo ndi makhalidwe a anthu anaipiratu. Pamenepo Ambuye Wamkulu Yehova anaika nthawi yoti awononge anthu oipa amenewa.​—Werengani Genesis 6:3, 5, 11, 12. *

4, 5. Kodi zochitika masiku ano zikufanana bwanji ndi masiku a Nowa?

4 Yesu ananeneratu kuti masiku athu ano zinthu zidzakhala zofanana ndi mmene zinalili masiku a Nowa. (Mat. 24:37) Mwachitsanzo, mizimu yoipa ikuvutitsanso anthu masiku ano. (Chiv. 12:7-9, 12) M’masiku a Nowa, ziwanda zimenezi zinavala matupi a anthu koma masiku ano anazichotsera mphamvu yochita zimenezi. Ngakhale zili choncho, zimayesetsa kuti zizilamulira achinyamata ndi achikulire omwe. Ziwanda zachiwerewerezi zimasangalala zikaona anthu amene zawasokoneza maganizo akuchita zinthu zoipa ndiponso zochititsa manyazi.​—Aef. 6:11, 12.

5 Mawu a Mulungu amafotokoza Mdyerekezi kuti ndi “wopha anthu” ndiponso kuti ali ndi “njira yobweretsera imfa.” (Yoh. 8:44; Aheb. 2:14) Komabe, iye ali ndi mphamvu zochepa zopha anthu mwachindunji. Ngakhale zili choncho, Satana yemwe ndi wankhanza amanyenga ndiponso kukopa anthu kuti achite zofuna zake. Iye amachititsa anthu kukhala ndi mtima komanso maganizo achiwembu. Mwachitsanzo, mwana mmodzi mwa ana 142 obadwa ku United States adzaphedwa ndi achiwembu. Popeza Yehova ankaona zimene zinkachitika masiku a Nowa, kodi sakuonanso zinthu zankhanza zimene zafala kwambiri masiku ano? Ndiye kodi sadzachitapo kanthu?

6, 7. Kodi Nowa ndi banja lake anasonyeza bwanji kuti anali ndi chikhulupiriro ndiponso ankaopa Mulungu?

6 Patapita nthawi, Mulungu anauza Nowa kuti akufuna kubweretsa chigumula padziko lapansi kuti awononge chamoyo chilichonse. (Gen. 6:13, 17) Yehova anauzanso Nowa kuti amange chingalawa chooneka ngati chibokosi chachikulu ndipo Nowa ndi banja lake anayamba kugwira ntchito imeneyi. Kodi n’chiyani chimene chinawathandiza kumvera Yehova ndiponso kukhala okonzeka pamene Mulungu ankapereka chiweruzo?

7 Nowa ndi banja lake anachita zimene Mulungu anawalamula chifukwa chokhala ndi chikhulupiriro champhamvu ndiponso chifukwa choopa Mulungu. (Gen 6:22; Aheb. 11:7) Monga mutu wa banja, Nowa anakhalabe tcheru mwauzimu ndipo sankachita nawo zinthu zoipa zimene anthu ena ankachita. (Gen 6:9) Iye ankadziwa kuti banja lake linafunika kusamala kuti lisatengere khalidwe lachiwawa ndiponso mtima wosamvera wa anthu owazungulira. Iwo sanafunike kutengeka ndi zochitika za tsiku ndi tsiku. M’malomwake, Mulungu anali atawapatsa ntchito yoti agwire ndipo iwo anafunika kuika patsogolo ntchitoyo.​—Werengani Genesis 6:14, 18.

Nowa ndi Banja Lake Anali Okonzeka

8. N’chiyani chikusonyeza kuti anthu a m’banja la Nowa anali odzipereka pa kulambira Mulungu?

8 Nkhani ya m’Baibuloyi imafotokoza kwambiri za Nowa popeza anali mutu wa banja, koma mkazi wake ndi ana ake aamuna ndiponso akazi awo ankalambiranso Yehova. Mneneri Ezekieli anatsimikiziranso zimenezi. Iye ananena kuti Nowa akanakhalapo m’nthawi ya Ezekieliyo, ana ake sakanapulumutsidwa chifukwa cha chilungamo cha bambo wawo. Anawo anali aakulu moti akanasankha okha kumvera kapena ayi. Choncho, mwana aliyense payekha anasonyeza kuti ankakonda Mulungu ndiponso njira zake. (Ezek. 14:19, 20) Anthu a m’banja la Nowa ankamvera malangizo ake, ankakhulupirira zimene iyeyo ankakhulupirira ndiponso sanalole kuti anthu ena awasokoneze pa ntchito imene Mulungu anawapatsa.

9. Kodi ndani akutsanzira chikhulupiriro cha Nowa masiku ano?

9 Masiku ano, m’gulu la abale padziko lonse muli mitu ya mabanja imene ikuyesetsa kwambiri kutsanzira Nowa. Zimenezi n’zolimbikitsa kwambiri. Iwo amadziwa kuti kungopezera banja lawo chakudya, zovala, nyumba ndi maphunziro si kokwanira. Koma ayenera kusamaliranso banja lawo mwauzimu. Akamachita zimenezi, amasonyeza kuti akukonzekera zimene Yehova adzachita posachedwapa.

10, 11. (a) Kodi Nowa ndi banja lake ayenera kuti anamva bwanji ali m’chingalawa? (b) Kodi tingachite bwino kudzifunsa funso liti?

10 Zikuoneka kuti Nowa, mkazi wake, ana ake ndiponso akazi awo anagwira ntchito yomanga chingalawa kwa zaka pafupifupi 50. Pamene anali kumanga chingalawacho ayenera kuti ankalowa ndi kutulukamo maulendo ambirimbiri. Iwo anachimata ndi phula, kuikamo chakudya chokwanira ndiponso kulowetsamo nyama. Taganizirani zimene zinachitika tsiku lalikulu litafika pa tsiku la 17 la mwezi wachiwiri wa chaka cha 2370 B.C.E. Iwo analowa m’chingalawa. Yehova anatseka chitseko ndipo mvula inayamba kugwa. Koma imeneyi sinali mvula wamba. Madzi a kumwamba, amene anali ngati nyanja yaikulu, anayamba kugwa ndipo aliyense m’chingalawa ankamva phokoso la chimvula chadzaoneni chimene chinkagwacho. (Gen. 7:11, 16) Anthu amene anali kunja kwa chingalawa anali kuphedwa koma amene anali mkati anali kupulumutsidwa. Kodi mukuganiza kuti Nowa ndi banja lake ankamva bwanji? Ayenera kuti anathokoza kwambiri Mulungu. Mosakayikira ankaganiza kuti, ‘Tinachita bwino kwambiri kuyenda ndi Mulungu woona ndiponso kukhala okonzeka.’ (Gen. 6:9) Taganizirani mmene nanunso mungamvere mutapulumuka pa Armagedo. Kodi simungayamikire Mulungu ndi mtima wonse?

11 Palibe chimene chingaletse Wamphamvuyonse kukwaniritsa lonjezo lake lothetsa dongosolo la Satanali. Ndiyeno dzifunseni kuti, ‘Kodi ndimakhulupirira ndi mtima wonse kuti Mulungu sadzalephera ngakhale pang’ono kukwaniritsa lonjezo lililonse pa nthawi yake yoyenera?’ Ngati ndi choncho, khalani okonzeka ndipo muzikumbukira nthawi zonse kuti “tsiku la Yehova” lili pafupi.​—2 Pet. 3:12.

Mose Anakhalabe Tcheru

12. Kodi n’chiyani chikanalepheretsa Mose kuona zinthu mwauzimu?

12 Tiyeni tikambirane chitsanzo china. Anthu angaone kuti Mose ankakhala moyo wabwino kwambiri ku Iguputo. Popeza ankaleredwa ndi mwana wamkazi wa Farao, n’zodziwikiratu kuti ankapatsidwa ulemu, kudya chakudya chabwino, kuvala zovala zapamwamba ndiponso kukhala malo abwino kwambiri. Iye anaphunzira maphunziro apamwamba. (Werengani Machitidwe 7:20-22.) N’kuthekanso kuti akanapatsidwa chuma chambiri.

13. Kodi n’chiyani chinathandiza Mose kupitirizabe kudalira malonjezo a Mulungu?

13 N’zosakayikitsa kuti Mose ali wamng’ono anaphunzitsidwa ndi makolo ake kuipa kwa kulambira mafano kumene Aiguputo ankachita. (Eks. 32:8) Maphunziro a ku Iguputo komanso chuma cha kunyumba ya mfumu sizinachititse Mose kusiya kulambira koona. Iye ayenera kuti ankaganizira kwambiri zimene Yehova analonjeza makolo ake akale ndipo ankayesetsa kukhala wokonzeka kuchita chifuniro cha Mulungu. Ndipotu Mose anauza ana a Isiraeli kuti: “Yehova . . . Mulungu wa Abulahamu, Mulungu wa Isaki ndi Mulungu wa Yakobo, wandituma kwa inu.”​—Werengani Ekisodo 3:15-17.

14. Kodi chikhulupiriro ndiponso kulimba mtima kwa Mose zinayesedwa bwanji?

14 Mose ankaona kuti Yehova, yemwe ndi Mulungu woona, ndi weniweni ndipo ndi wosiyana ndi mafano amene ankaimira milungu yopanda moyo ya ku Iguputo. Pa moyo wake ankakhala ngati akuona “Wosaonekayo.” Mose ankakhulupirira kuti anthu a Mulungu adzamasulidwa ku ukapolo koma sankadziwa nthawi yake. (Aheb. 11:24, 25, 27) Umboni wakuti ankafunitsitsa kwambiri Aheberi atamasulidwa ndi wakuti anateteza kapolo wina wachiisiraeli amene ankazunzidwa. (Eks. 2:11, 12) Koma iyi sinali nthawi imene Yehova ankafuna kuwamasula, choncho Mose anathawira kudera lina lakutali. N’zosachita kufunsa kuti iye anavutika pamene moyo wake unasintha kuchoka kumalo abwino kwambiri kunyumba ya mfumu ku Iguputo, n’kupita kukakhala kuchipululu. Koma Mose ankakhala tcheru kuti amvere malangizo onse a Yehova. Choncho atakhala ku Midiyani zaka 40, Mulungu anamugwiritsa ntchito kuti akapulumutse abale ake. Mulungu atamuuza kuti abwerere ku Iguputo, Mose anamvera. Tsopano nthawi inali itafika yoti Mose agwire ntchito ya Mulungu m’njira imene Mulunguyo ankafunira. (Eks. 3:2, 7, 8, 10) Atabwerera ku Iguputo, Mose yemwe anali “munthu wofatsa kwambiri kuposa anthu onse” anafunika chikhulupiriro ndiponso kulimba mtima kuti akakumane ndi Farao. (Num. 12:3) Sikuti anangopita kukakumana ndi Farao kamodzi kokha ayi. Koma pa nthawi iliyonse imene miliri inkachitika ankakumana naye ndipo iye sankadziwa kuti akumana nayenso kangati.

15. Ngakhale kuti Mose ankakumana ndi zokhumudwitsa, kodi n’chiyani chinamulimbikitsa kuti ayesetse kupeza mipata yolemekezera Atate wake wakumwamba?

15 Pa zaka 40 zotsatira, kuchokera mu 1513 B.C.E. mpaka 1473 B.C.E., Mose anakumana ndi zinthu zokhumudwitsa. Koma iye ankayesetsa kupeza mipata yolemekezera Yehova ndipo ankayesetsa ndi mtima wonse kulimbikitsa Aisiraeli anzake kuti azichitanso chimodzimodzi. (Deut. 31:1-8) N’chifukwa chiyani ankachita zimenezi? Chifukwa chakuti m’malo mokonda dzina lake, iye ankakonda dzina la Yehova ndiponso ulamuliro wake. (Eks. 32:10-13; Num. 14:11-16) Nafenso sitiyenera kusiya kukhala ku mbali ya ulamuliro wa Mulungu ngakhale kuti timakumana ndi zinthu zokhumudwitsa kapena zofooketsa. Tisamakayikire zoti nthawi zonse Mulungu amachita zinthu mwanzeru, mwachilungamo ndiponso m’njira yabwino kuposa wina aliyense. (Yes. 55:8-11; Yer. 10:23) Kodi inuyo mumaona choncho?

Khalani Tcheru

16, 17. N’chifukwa chiyani tinganene kuti kumvetsa mfundo ya pa Maliko 13:35-37 n’kofunika kwambiri kwa inuyo?

16 “Khalani maso, khalani tcheru, pakuti simukudziwa pamene nthawi yoikidwiratu idzafika.” (Maliko 13:33) Yesu anapereka chenjezo limeneli pamene ankafotokoza za chizindikiro cha mapeto a nthawi yoipa ino. Taonani mawu omaliza a ulosi waukulu umene Yesu ananena. Maliko analemba kuti: “Choncho khalani maso, pakuti simukudziwa nthawi yobwera mwininyumba. Simukudziwa ngati adzabwere madzulo, pakati pa usiku, atambala akulira, kapena m’mawa, kuti akadzafika mwadzidzidzi, asadzakupezeni mukugona. Koma zimene ndikuuza inuzi ndikuuza onse, Khalani maso.”​—Maliko 13:35-37.

17 Malangizo amene Yesu anaperekawa ndi ofunika kuwaganizira bwino. Iye anatchula za maulonda anayi a usiku. Ulonda womaliza umakhala wovuta kwambiri kuti munthu akhale maso chifukwa umayambira 3 koloko m’mawa mpaka kutuluka kwa dzuwa. Akatswiri pa nkhani zankhondo amanena kuti nthawi imeneyi ndi yabwino kwambiri kuukira adani chifukwa mukhoza kuwapeza ‘akugona.’ N’chimodzimodzinso ndi nthawi yathu ino. Dzikoli lili m’tulo tofa nato mwauzimu ndipo zingakhale zovuta kuti tikhalebe maso. Choncho tisamakayikire zoti tiyenera ‘kukhala tcheru,’ ndiponso ‘kukhala maso’ podikira mapeto komanso chipulumutso chathu zimene zinaloseredwa.

18. Kodi Mboni za Yehovafe tili ndi mwayi wosaneneka uti?

18 Munthu wosewera ndi zinyama amene tamutchula kumayambiriro kwa nkhani ino uja anapulumuka pamene nyama ija inamuukira. Koma maulosi a m’Baibulo amasonyeza bwinobwino kuti chipembedzo chonyenga ndiponso mbali zina zonse za dongosolo loipali sizidzapulumuka mapeto amene ayandikirawa. (Chiv. 18:4-8) Choncho, atumiki a Mulungu onse, kaya achinyamata kapena achikulire, ayenera kuona kuti m’pofunika kwambiri kukonzekera tsiku la Yehova ngati mmene anachitira Nowa ndi banja lake. Tikukhala m’dziko losalemekeza Mulungu ndipo aphunzitsi azipembedzo zonyenga ndiponso anthu amene amakayikira kapena kutsutsa zoti kuli Mulungu, amanena zinthu zonyoza Mlengi. Koma tisalole kuti anthu amenewa atisokoneze maganizo. Tiyeni tizitsatira zitsanzo zimene takambiranazi ndi kukhala maso kuti tipeze mipata yolemekeza ndiponso yosonyeza kuti tili ku mbali ya Yehova yemwe ndi “Mulungu wa milungu” komanso “Mulungu wamkulu, wamphamvu ndi woopsa.”​—Deut. 10:17.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Kuti mumvetse nkhani ya “zaka 120” zotchulidwa pa Genesis 6:3, onani Nsanja ya Olonda ya December 15, 2010, tsamba 30.

Kodi Mukukumbukira?

• N’chifukwa chiyani Nowa anafunika kuika patsogolo zosowa zauzimu za banja lake?

• Kodi nthawi yathu ino ikufanana bwanji ndi masiku a Nowa?

• Ngakhale kuti Mose ankakumana ndi zokhumudwitsa, n’chiyani chinamuthandiza kudalirabe malonjezo a Yehova?

• Kodi ndi maulosi a m’Baibulo ati amene amakulimbikitsani kukhalabe tcheru mwauzimu?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 25]

Nowa ndi banja lake sanalole kuti chilichonse chiwasokoneze pa ntchito ya Yehova

[Chithunzi patsamba 26]

Malonjezo odalirika a Mulungu anathandiza Mose kukhalabe tcheru