Kodi Mumaona Umboni Wakuti Mulungu Akutitsogolera?
Kodi Mumaona Umboni Wakuti Mulungu Akutitsogolera?
PAMENE Aisiraeli anali kuchoka ku Iguputo, mtambo woima njo ngati chipilala unali kuyenda nawo pafupi masana tsiku lililonse. Koma usiku panali moto woima njo ngati chipilala umene unali nawo. Aisiraeli kapenanso Aiguputo anali asanaonepo zinthu zodabwitsa ngati zimenezi. Kodi mtambo ndiponso moto zinali kuchokera kuti? Kodi cholinga cha zinthu zimenezi chinali chiyani? Ngakhale kuti papita zaka zoposa 3,500, kodi ifeyo tingaphunzire chiyani pa nkhani ya mmene Aisiraeli ankaonera “mtambo ndi moto woima njo ngati chipilala”?—Eks. 14:24.
Mawu a Mulungu amatiuza kumene mtambo ndiponso moto zinachokera komanso cholinga cha zinthu zimenezi. Amanena kuti: “Yehova anali kuyenda patsogolo pawo mumtambo woima njo ngati chipilala powatsogolera usana, ndipo usiku anali kuwatsogolera m’moto woima njo ngati chipilala kuti uziwaunikira, kuti apitirizebe ulendo usana ndi usiku.” (Eks. 13:21, 22) Yehova Mulungu anagwiritsa ntchito moto ndi mtambo kutsogolera anthu ake pochoka ku Iguputo komanso poyenda m’chipululu. Iwo ankafunika kukhala okonzeka kunyamuka n’kutsatira mtambowo. Pamene magulu ankhondo a Aiguputo anali kuwatsatira kuti aukire anthu a Mulunguwo, mtambowo unakaima pakati pa Aiguputowo ndi Aisiraeli n’cholinga choteteza Aisiraeliwo. (Eks. 14:19, 20) Ngakhale kuti mtambowo unawatsogolera panjira yozungulira popita ku Dziko Lolonjezedwa, kutsatira mtambowo inali njira yokhayo imene Aisiraeli akanafikira kudzikolo.
Mtambo ndi moto zinali kutsimikizira anthu a Mulungu kuti Yehova ali nawo. Zimenezi zinali kuimira Yehova ndipo nthawi zina iye anali kulankhula nawo kudzera mu mtambowo. (Num. 14:14; Sal. 99:7) Mtambowo unasonyezanso kuti Mose ndi amene Yehova anamusankha kuti atsogolere mtundu wa Isiraeli. (Eks. 33:9) Pa nthawi yomaliza imene mtambowo unatchulidwa m’Baibulo, unatsimikiziranso kuti Yoswa ndi amene Yehova anasankha kuti alowe m’malo mwa Mose. (Deut. 31:14, 15) Kuti zinthu ziwayendere bwino pa ulendo wawo wochoka ku Iguputo, Aisiraeli ankafunika kuona umboni wakuti Mulungu akuwatsogolera n’kumamutsatira.
Aisiraeli Anasiya Kuona Kuti Mulungu Akuwatsogolera
Aisiraeli ayenera kuti anadabwa kwambiri nthawi yoyamba imene anaona mtambowo ndiponso motowo. Koma n’zomvetsa chisoni kuti zinthu zozizwitsa zimenezi zomwe ankaziona nthawi zonse sizinawathandize kuti apitirize kukhulupirira Yehova. Nthawi zambiri iwo anali kuchita zinthu zosonyeza kuti sankadalira Mulungu. Pa nthawi imene magulu ankhondo a Aiguputo anali kuwathamangira kuti awagwire, Aisiraeli sanakhulupirire kuti Yehova ali ndi mphamvu zotha kuwapulumutsa. M’malomwake, iwo anaimba mlandu Mose yemwe anali mtumiki wa Mulungu kuti wawatenga n’cholinga choti adzawaphetse. (Eks. 14:10-12) Atapulumutsidwa pa Nyanja Yofiira, iwo anayamba kung’ung’udzira Mose, Aroni ndiponso Yehova chifukwa choganiza kuti sapeza chakudya ndi madzi. (Eks. 15:22-24; 16:1-3; 17:1-3, 7) Patapita milungu yowerengeka, iwo anaumiriza Aroni kuti awapangire mwana wa ng’ombe wa golide. Taganizirani za zimene zinachitika. Aisiraeli ali mumsasa anatha kuona moto ndi mtambo, zomwe zinali umboni wamphamvu wa amene anawatsogolera kuchokera ku Iguputo. Koma ali mumsasa momwemo anayamba kulambira fano, n’kumanena kuti: “Uyu ndiye Mulungu wanu, Aisiraeli inu, amene anakutulutsani mu Iguputo.” Ndithudi iwo anachita ‘zinthu zikuluzikulu zosalemekeza Mulungu.’—Eks. 32:4; Neh. 9:18.
Zinthu zimene Aisiraeli anachita popandukira Sal. 78:40-42, 52-54; Neh. 9:19.
Mulungu zinasonyeza kuti iwo sanafune zoti Yehova awatsogolere. Sikuti iwo anali ndi vuto la maso awo enieni, koma anali ndi vuto la maso awo auzimu. Iwo anatha kuona mtambo ndi moto woima njo ngati chipilala koma anasiya kuzindikira tanthauzo lake. Ngakhale kuti zochita zawozo ‘zinamvetsa chisoni Woyera wa Isiraeli,’ Yehova anawachitira chifundo n’kupitiriza kuwatsogolera pogwiritsa ntchito mtambo ndi moto mpaka iwo anafika m’Dziko Lolonjezedwa.—Umboni Wakuti Mulungu Akutitsogolera Masiku Ano
Yehova sanasiye Aisiraeli kuti afufuze okha njira yopita ku Dziko Lolonjezedwa. Masiku anonso iye sanasiyepo kutsogolera anthu ake. Sanatisiye kuti tizifufuza tokha njira yopita m’dziko latsopano limene watilonjeza. Yesu Khristu ndiye amene anasankhidwa kukhala Mtsogoleri wa mpingo. (Mat. 23:10; Aef. 5:23) Iye wapereka udindo wina kwa kapolo wokhulupirika, amene ndi Akhristu okhulupirika omwe ndi odzozedwa ndi mzimu. Kapolo wokhulupirika ameneyu amaika oyang’anira mu mpingo wachikhristu.—Mat. 24:45-47; Tito 1:5-9.
Kodi kapolo wokhulupirikayu, kapena kuti mtumiki woyang’anira nyumba, tingamudziwe bwanji? Taonani mmene Yesu anamufotokozera. Iye anati: “Ndani kwenikweni amene ali mtumiki woyang’anira nyumba wokhulupirika ndi wanzeru, amene mbuye wake adzamuika kuyang’anira gulu la atumiki ake, kuti aziwapatsa chakudya chokwanira pa nthawi yake? Kapolo ameneyo ndi wodala, ngati mbuye wake pobwera adzam’peze akuchita zimenezo!”—Luka 12:42, 43.
Choncho mtumiki woyang’anira nyumba ameneyu ndi “wokhulupirika.” Iye sapandukira kapena kusiya Yehova, Yesu, choonadi cha m’Baibulo ndiponso anthu a Mulungu. Mtumiki ameneyu amasonyeza kuti ndi “wanzeru” potsogolera ntchito yofunika kwambiri yolalikira ‘uthenga wabwino wa ufumu’ ndiponso yophunzitsa “anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzira.” (Mat. 24:14; 28:19, 20) Mtumikiyu amamvera Yehova mwa kupereka “pa nthawi yake” chakudya chauzimu chimene chimakhala chabwino ndiponso chopatsa thanzi mwauzimu. Yehova amasonyeza kuti amasangalala ndi mtumiki ameneyu mwa kudalitsa gulu la anthu ake m’njira zambiri. Iye amathandiza kuti gulu liwonjezeke, amalitsogolera kuti lisankhe mwanzeru zochita, amalithandiza kumvetsa bwino choonadi cha m’Baibulo, amaliteteza kuti adani awo asaliwonongeretu ndiponso amathandiza kuti anthu ake akhale ndi mtendere m’maganizo ndi mumtima.—Yes. 54:17; Afil. 4:7.
Tizitsatira Mulungu Akamatitsogolera
Kodi tingasonyeze bwanji kuti timafuna kutsogoleredwa ndi Mulungu? Mtumwi Paulo ananena kuti: “Muzimvera amene akutsogolera pakati panu ndipo muziwagonjera.” (Aheb. 13:17) Koma nthawi zina kuchita zimenezi kumakhala kovuta. Mwachitsanzo, tiyerekeze kuti munali m’gulu la Aisiraeli nthawi ya Mose. Ndipo pambuyo poyenda kwa kanthawi, mtambo waima. Kenako mukudzifunsa kuti, ‘Kodi mtambowu uima tsiku limodzi, mlungu wathunthu kapena miyezi ingapo? Kodi ndimasule katundu wanga yense?’ Mwina poyamba mukhoza kungomasula zinthu zofunika kwambiri. Ndiyeno patapita masiku angapo, mukumasula katundu yense chifukwa chotopa ndi kufufuzafufuza zinthu. Koma mutatsala pang’ono kumasula katundu yense, mukuona mtambowo ukunyamuka ndipo muyenera kulongedzanso katundu wanu. Zimenezi zingakhale zovuta. Komabe, Aisiraeli anayenera “kunyamuka nthawi yomweyo.”—Num. 9:17-22.
Kodi ife timatani tikalandira malangizo ochokera kwa Mulungu? Kodi timayesetsa kuwatsatira “nthawi yomweyo”? Kapena kodi timangopitiriza kuchita zinthu m’njira imene tinazolowera? Kodi tikudziwa bwino malangizo atsopano okhudza zinthu monga kuchititsa phunziro la Baibulo, kulalikira anthu a chinenero china ndiponso kulambira kwa pa banja nthawi zonse? Nanga kodi tikudziwa bwino malangizo okhudza kuchita zinthu mogwirizana ndi Makomiti Olankhulana ndi Achipatala ndiponso okhudza mmene tiyenera kuchitira zinthu pa misonkhano yathu yaikulu? Timasonyezanso kuti timafuna kutsogoleredwa ndi Mulungu tikamatsatira uphungu. Tikafuna kusankha zochita pa nkhani zikuluzikulu, sitidalira nzeru zathu koma timadalira Yehova
ndi gulu lake kuti atitsogolere. Mofanana ndi mwana amene amathawira kwa makolo ake kuti amuteteze kukakhala chimvula chamabingu, nafenso timathawira kwa Yehova ndi gulu lake tikakumana ndi mavuto okhala ngati chimvula chamabingu.N’zoona kuti anthu amene akutsogolera mbali ya padziko lapansi ya gulu la Mulungu si angwiro, koma nayenso Mose sanali wangwiro. Ngakhale zinali choncho, mtambowu unkapereka umboni woti Mose anasankhidwa ndi Mulungu ndipo Mulunguyo ankasangalala naye. Kumbukiraninso kuti sikuti Mwisiraeli aliyense ankasankha yekha nthawi yonyamukira. M’malomwake, anthuwo ankatsatira “malangizo a Yehova odzera kwa Mose.” (Num. 9:23) Choncho Mose, yemwe Mulungu ankamugwiritsa ntchito kuti atsogolere anthu ake, ndi amene ankanena kuti anyamuke nthawi ikakwana.
Masiku anonso, mtumiki woyang’anira nyumba, amene Yehova wamuika, ndi amene amanena pakafunika kusintha zinthu zina. Kodi mtumikiyu amachita bwanji zimenezi? Amachita zimenezi kudzera mu nkhani za mu Nsanja ya Olonda, Utumiki Wathu wa Ufumu, mabuku atsopano ndiponso nkhani za pa misonkhano ikuluikulu. Amaperekanso malangizo ku mipingo kudzera mwa oyang’anira oyendayenda, makalata kapena maphunziro amene abale amene ali ndi udindo mu mpingo amalandira.
Kodi mumatha kuona mosavuta umboni wakuti Mulungu akutitsogolera? Yehova amagwiritsa ntchito gulu lake kuti atsogolere anthu akefe poyenda “m’chipululu” cha dziko la Satana m’masiku otsiriza ano. Chifukwa cha zimenezi, timakhala ogwirizana, okondana ndiponso otetezeka.
Aisiraeli atafika m’Dziko Lolonjezedwa, Yoswa anati: “Inu mukudziwa bwino ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse, kuti pamawu onse abwino amene Yehova Mulungu wanu ananena kwa inu, palibe ngakhale amodzi omwe sanakwaniritsidwe. Onse akwaniritsidwa kwa inu.” (Yos. 23:14) Masiku anonso anthu a Mulungu adzafikadi m’dziko latsopano limene Mulungu walonjeza. Koma kuti aliyense payekha adzafike m’dziko latsopanolo, ayenera kukhala wodzichepetsa n’kumatsatira malangizo a Mulungu. Choncho tiyeni tonsefe tipitirize kuona umboni wakuti Yehova akutitsogolera.
[Zithunzi patsamba 5]
Masiku ano tikutsogoleredwa ndi gulu la Yehova
Mabuku atsopano amatulutsidwa pa misonkhano ikuluikulu
Sukulu zophunzitsa atumiki a Mulungu
Kuphunzitsidwa pa misonkhano yokonzekera utumiki