Ndapeza Zinthu Zambiri Zabwino
Ndapeza Zinthu Zambiri Zabwino
Yosimbidwa ndi Arthur Bonno
MU 1951, ine ndi mkazi wanga Edith tili pa msonkhano wachigawo, tinamva chilengezo chakuti pakhala msonkhano wa amene akufuna kuchita utumiki wa umishonale.
Ine ndinati, “Tiye tipite nawo.”
Koma Edith anandiyankha kuti, “Art, ife sitingakhale amishonale.”
Ine ndinati, “Edie tatiye, tikangomvetsera nawo.”
Pamapeto pa msonkhanowo anapereka mafomu a Sukulu ya Gileadi.
Ndiyeno ndinamulimbikitsa kuti, “Tiye tilembe mafomuwa.”
Koma Edie anafunsa kuti, “Art, ndiye tisiyane ndi makolo komanso achibale?”
Patapita chaka ndi hafu kuchokera pamene tinachita msonkhanowu, tinaitanidwa ku Sukulu ya Gileadi ndipo anatitumiza kukatumikira ku dziko la Ecuador, ku South America.
Mutati muone bwinobwino zokambirana zathu pa msonkhanowu, mutha kudziwa kuti ine ndinali ndi mtima wokakamiza zinthu komanso woona kuti nditha kuchita chilichonse. Koma Edith anali wodekha ndiponso wodzichepetsa. Iye anakulira m’katawuni kakang’ono ka Elizabeth, ku Pennsylvania, m’dziko la United States. Iye anali asanayendepo kutali kapena kukumana ndi munthu wochokera kudziko lina. Zinali zovuta kuti asiyane ndi achibale ake. Ngakhale zinali choncho, iye anavomera ndi mtima wonse kukatumikira kudziko lina. Tinafika ku Ecuador mu 1954 ndipo takhala tikutumikira m’dzikoli ngati amishonale mpaka pano. Pa zaka zimene takhala kuno tapeza zinthu zambiri zabwino. Kodi mungakonde kudziwa zina mwa zinthu zimenezi?
Zinthu Zosangalatsa Zimene Timakumbukira
Poyamba penipeni anatitumiza kumzinda wa Quito, womwe ndi likulu la Ecuador. Mzindawu uli pamalo okwera pa mtunda wa mamita 2,850 m’mapiri a Andes. Zinatitengera masiku awiri kuyenda pa sitima ya pamtunda ndiponso galimoto kuchokera pamzinda wa Guayaquil, womwe uli m’mphepete mwa nyanja, kupita ku Quito. Koma panopa ndi mtunda wongoyenda mphindi 30 pa ndege. Tinasangalala kutumikira ku Quito kwa zaka zinayi. Ndiyeno mu 1958 munachitika chinthu
china chosangalatsa. M’chaka chimenechi tinapemphedwa kukatumikira monga woyang’anira dera.Pa nthawiyi, m’dziko lonseli munali madera awiri okha ndipo anali ang’onoang’ono. Choncho kuwonjezera pa kuyendera mipingo, nthawi zina tinkalalikira kwa milungu ingapo m’midzi yomwe kunalibe Mboni. Nyumba zambiri m’midzi imeneyi zinali zing’onozing’ono, zopanda mawindo ndiponso zongokhala ndi bedi basi. Tinkayenda ndi chibokosi chamatabwa chimene tinkaikamo sitovu yoyendera palafini, poto, mbale, beseni, zofunda, neti yoteteza udzudzu, zovala, nyuzipepala zakale ndi zinthu zina. Tinkagwiritsa ntchito nyuzipepala zimenezi kutsekera mibowo poyesa kuteteza kuti makoswe asalowe m’nyumba.
Ngakhale kuti zipinda zake zinali za mdima ndiponso zosasamalirika, timakumbukira kuti tinkasangalala tikamacheza usiku titakhala pabedi n’kumadya kachakudya kathu kophika pa sitovu yathu yoyendera palafini ija. Chifukwa cha chibadwa changa chopupuluma, nthawi zambiri ndinkalankhula ndisanaganize. Nthawi zina tikafatsa chonchi, mkazi wanga ankandiuza mmene ndiyenera kulankhulira ndi abale amene timawachezera kuti asamakhumudwe. Ndinkamvera zonena zake ndipo izi zinkachititsa kuti pochezera abale ndiziwalimbikitsa kwambiri. Ndikamalankhula zoipa zokhudza abale, mkazi wanga sankayankhira. Izi zinandithandiza kuti ndiziona abale moyenera. Koma nthawi zambiri tinkakonda kukambirana mfundo zimene taphunzira mu Nsanja ya Olonda ndiponso zimene takumana nazo mu utumiki pa tsikulo. Ndipo tinkakumana ndi zinthu zosangalatsa kwambiri mu utumiki.
Mmene Tinamupezera Carlos
M’tawuni ya Jipijapa chakumadzulo kwa dziko la Ecuador, tinapatsidwa dzina la munthu wina wofuna kuphunzira choonadi. Dzina la munthuyo linali Carlos Mejía, koma sanatiuze komwe ankakhala. M’mawa tinanyamuka kunyumba imene tinkachita lendi n’kumangoyenda chifukwa sitinkadziwa kumene tingam’peze. Tinkayenda mosamala kwambiri chifukwa msewu wake unali wokumbikakumbika komanso wamatope popeza kuti usiku kunagwa mvula yambiri. Poyenda ine ndinkakhala patsogolo. Ndiyeno ndinangomva mkazi wanga akundiitana mofuula ndiponso mothedwa nzeru kuti, “Art!” Nditacheuka ndinangoona Edie atamira m’matope omwe anafika m’maondo. Zinali zoseketsa kwambiri moti akanakhala kuti samalira bwenzi n’tamuseka kwabasi.
Ndinamuvuula m’matopewo koma nsapato zake zinatsalira. Panali mnyamata ndi mtsikana amene ankaona izi zikuchitika ndipo ndinawauza kuti, “Mukatithandiza kutulutsa nsapatozi ndikupatsani ndalama.” Nthawi yomweyo anatulutsa nsapatozo koma Edie ankafunika kuchotsa matope. Mayi a mnyamata ndi mtsikanayo anali kuonanso zimene zinkachitika ndipo anatiitanira kunyumba kwawo. Mayiwo anathandiza mkazi wanga kuchotsa matope m’miyendo uku ana akewo akutsuka nsapato. Koma tisananyamuke panyumbayo panachitikanso chinthu china chosangalatsa. Nditafunsa mayiyo kumene Carlos Mejía ankakhala, iye anandiyang’ana modabwa kwambiri. Kenako anati: “Ndi amuna angatu amenewo.” Patapita nthawi, tinayamba kuphunzira nawo Baibulo ndipo anthu onse m’banjamo anadzabatizidwa. Patapita zaka, Carlos, mkazi wake ndi ana awo awiri anayamba kutumikira monga apainiya apadera.
Tinayenda Maulendo Ovuta Koma Tinkalandiridwa Bwino
Nthawi zina, kuyenda pochezera mipingo kunali kovuta kwambiri. Tinkayenda pa basi, pa sitima yapamtunda, pa lole, pa bwato ndiponso pa ndege zing’onozing’ono. Tsiku lina John McLenachan, yemwe anali woyang’anira chigawo, ndi mkazi wake Dorothy anatsagana nafe kukalalikira kumidzi ina ya asodzi pafupi ndi malire a dziko la Colombia. Tinayenda pa bwato limene anamangirira injini. Nsomba zoopsa zazikulu ngati bwato lathu zinali kuyenda pafupi kwambiri. Munthu amene ankatiyendetsa anachita mantha kwambiri ndi kukula kwa nsombazo
moti anakhotetsa bwatolo n’kumayenda cham’mphepete mwa nyanjayo.Mavuto amene tinkakumana nawo mu ntchito yoyang’anira dera sanali kuoneka aakulu tikaganizira zinthu zabwino zimene tinkakumana nazo. Tinkakumana ndi abale ambiri abwino ndiponso odziwa kulandira alendo. Nthawi zambiri, mabanja amene ankatisamalira ankatikakamiza kuti tizidya katatu pa tsiku pomwe iwo ankadya kamodzi kokha. Ena ankakhala ndi bedi limodzi n’kutiuza kuti tigone pabedilo, iwo n’kugona pansi. Mkazi wanga ankakonda kunena kuti, “Abale ndi alongo athu okondedwawa amandithandiza kudziwa kuti anthufe timangofunikira zinthu zochepa pa moyo wathu.”
“Sitikufuna Kuti Titaye Mwayi Uliwonse”
Mu 1960, panachitikanso chinthu china chosangalatsa kwambiri. Tinaitanidwa kukatumikira ku ofesi ya nthambi ku Guayaquil. Ine ndinkagwira ntchito mu ofesi yoyang’anira ntchito za panthambi koma Edith ankalowa mu utumiki ndi mpingo wa pafupi. Ine ndinkadziona kuti sindingakwanitse ntchito ya mu ofesi koma malinga ndi Aheberi 13:21, Mulungu amatipatsa ‘chilichonse chabwino kuti tichite chifuniro chake.’ Patapita zaka ziwiri, ndinaitanidwa ku Sukulu ya Gileadi kuti ndikaphunzire kwa miyezi 10 ku Beteli ya mumzinda wa Brooklyn, ku New York. Pa nthawi imeneyo, akazi ankauzidwa kuti atsale n’kupitiriza utumiki wawo. Mkazi wanga analandira kalata yochokera ku Brooklyn. M’kalatayo anamupempha kuganiza mofatsa kuti aone ngati angalole kuti mwamuna wake achoke kwa miyezi 10.
Poyankha kalatayo, Edith analemba kuti: “Ndikudziwa kuti si chinthu chophweka kuchichita, komabe ndikudziwanso kuti Yehova adzatithandiza pa mavuto alionse amene tingakumane nawo. . . . Sitikufuna kuti titaye mwayi uliwonse wautumiki umene tingalandire kapena wophunzira zinthu zimene zingatithandize kutumikira bwino.” Nthawi imene ndinali ku Brooklyn, mkazi wanga ankandilembera kalata mlungu uliwonse.
Kutumikira Limodzi ndi Akhristu Okhulupirika
Chifukwa cha matenda, mu 1966 ine ndi Edith tinabwerera ku Quito kukatumikiranso monga amishonale limodzi ndi abale ndi alongo a kumeneko. Iwowo anali anthu okhulupirika kwambiri.
Mlongo wina wokhulupirika anali ndi mwamuna wosakhulupirira yemwe ankakonda kumumenya. Tsiku lina cha m’ma 6 koloko m’mawa, munthu wina anatiimbira foni n’kutiuza kuti mlongoyo wamenyedwanso. Ndinathamangira kunyumba ya mlongoyo ndipo nditamuona, sindinakhulupirire. Iye anali gone pabedi thupi lonse litatupa. Mwamuna wake anali atamumenya ndi chindodo mpaka chindodocho kuthyoka. Tsiku lomwelo, nditakumana ndi mwamunayo ndinamuuza kuti wachita zopepera kwabasi. Iye anapepesa kwambiri.
Cha kumayambiriro kwa zaka za m’ma 1970, ine ndinawongokera ndipo tinayambiranso ntchito yoyang’anira dera. Mzinda wa Ibarra unali m’dera lathu. Pamene tinafika mumzindawo cha kumapeto kwa zaka za m’ma 1950, munali Mboni ziwiri zokha, mmishonale
mmodzi ndi m’bale mmodzi wa komweko. Choncho tinali ofunitsitsa kukumana ndi Akhristu atsopano omwe anali ataphunzira kumene choonadi.Pa msonkhano wathu woyamba kumeneko, M’bale Rodrigo Vaca anali ndi nkhani yokambirana ndi omvera. Iye akafunsa funso, omvera ankakuwa kuti, “Yo, yo!” (kutanthauza kuti ine, ine) m’malo mokweza mkono. Ine ndi Edith tinangoyang’anana modabwa. Ndinadzifunsa kuti, ‘Kodi chikuchitika n’chiyani?’ Kenako tinauzidwa kuti M’bale Vaca ndi wakhungu koma ankazindikira mawu a anthu mu mpingo akakuwa kuti, “Ine, Ine.” Iye ndi m’busa wodziwadi nkhosa zake. Izi zinandikumbutsa mawu a Yesu a pa Yohane 10:3, 4, 14 onena za Mbusa Wabwino amene amadziwana bwino kwambiri ndi nkhosa zake. Masiku ano, mumzindawo muli mipingo 6 ya Chisipanishi, umodzi wa Chikichuwa ndiponso wina wa chinenero cha manja. M’bale Vaca akupitiriza kutumikira mokhulupirika monga mkulu ndiponso mpainiya wapadera. *
Timayamikira Ubwino wa Yehova
Mu 1974, Yehova anatichitira chinthu chinanso chabwino. Tinaitanidwa kubwerera ku Beteli kuti ndikagwirenso ntchito yanga ya mu ofesi ija ndipo patapita nthawi ndinaikidwa mu Komiti ya Nthambi. Poyamba Edith ankagwira ntchito kukhitchini, kenako anayamba kugwira ntchito ya mu ofesi. Iye amagwirabe ntchito ya mu ofesi mpaka pano ndipo amasamalira za makalata.
Pa zaka zonsezi, takhala ndi mwayi wolandira amishonale atsopano amene amaliza maphunziro a Gilead. Iwo amathandiza mipingo chifukwa chokhala okhwima mwauzimu ndiponso akhama mu utumiki. Timalimbikitsidwanso ndi abale ndi alongo ambirimbiri amene abwera kudzatumikira kuno kuchokera kumayiko oposa 30. Timachita chidwi kwambiri ndi mtima wawo wodzipereka. Ena anagulitsa nyumba ndi mabizinezi awo n’cholinga choti akatumikire kumadera kumene kulibe ofalitsa Ufumu ambiri. Iwo agula magalimoto kuti azikalalikira kumagawo akutali, ayambitsa mipingo yatsopano ndiponso athandiza kumanga Nyumba za Ufumu. Alongo osakwatiwa ambirimbiri abweranso kuchokera kumayiko ena kudzachita upainiya. Iwo ndi akhama komanso aluso kwambiri.
Ndapeza zinthu zambiri zabwino pa zaka zonse zimene ndakhala ndikutumikira Mulungu. Chinthu choyamba ndi kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. Ndikuyamikiranso kuti Yehova wandipatsa ‘wondithandiza.’ (Gen. 2:18) Ndikaganizira za zaka 69 zimene takhala m’banja ndimakumbukira lemba la Miyambo 18:22 limene limati: “Kodi munthu wapeza mkazi wabwino? Ndiye kuti wapeza chinthu chabwino.” Ndasangalala kwambiri kukhala limodzi ndi Edith. Iye wandithandiza m’njira zambiri. Iye ankakondanso kwambiri mayi ake. Kuchokera pamene tinafika ku Ecuador, mkazi wanga ankatumizira mayi ake kalata mlungu uliwonse mpaka pamene mayi akewo anamwalira mu 1990, ali ndi zaka 97.
Panopo ndili ndi zaka 90 ndipo Edith ali ndi zaka 89. Ndife osangalala kwambiri kuti takhala ndi mwayi wothandiza anthu oposa 70 kuti adziwe Yehova. Tikuona kuti tinachita bwino kwambiri kulemba mafomu ofunsira Sukulu ya Gilead aja zaka 60 zapitazo. Kuchita zimenezo kwatithandiza kupeza zinthu zambiri zabwino pa moyo wathu.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 29 Mbiri ya moyo wa M’bale Vaca ili mu Galamukani! ya Chingelezi ya September 8, 1985.
[Chithunzi patsamba 29]
Mu 1958, tili ku Yankee Stadium ku New York limodzi ndi amishonale anzathu amene tinalowa nawo Sukulu ya Gilead
[Chithunzi patsamba 31]
Tikucheza ndi banja la Mboni pamene tinali pa ntchito yoyang’anira dera mu 1959
[Chithunzi patsamba 32]
Tili ku ofesi ya nthambi ku Ecuador mu 2002