Mafunso Ochokera kwa Owerenga
Mafunso Ochokera kwa Owerenga
Kodi n’zotheka kudziwa nthawi yeniyeni imene Yesu Khristu anapachikidwa?
Funso limeneli likubwera chifukwa chakuti zimene Maliko analemba mu uthenga wake wabwino pa nkhani ya kuphedwa kwa Yesu, zimaoneka kuti zikusiyana ndi zimene mtumwi Yohane analemba. Maliko analemba kuti: “Tsopano nthawi ili cha m’ma 9 koloko m’mawa, iwo [asilikali] anam’pachika.” (Maliko 15:25) Koma Yohane analemba kuti: “Nthawi inali cha m’ma 12 koloko masana,” pamene Pilato anapereka Yesu kwa Ayuda kuti aphedwe. (Yoh. 19:14-16) Akatswiri ofotokoza Baibulo amanena zinthu zosiyanasiyana poyesa kugwirizanitsa mavesi amenewa. Koma Malemba safotokoza mfundo zambiri zotithandiza kudziwa chifukwa chake mavesi amenewa akusiyana chonchi. Komabe kuganizira mmene anthu ankawerengera nthawi masiku amenewo, kungatithandize kumvetsa nkhaniyi.
Masiku amenewo, Ayuda ankagawa tsiku m’maola 12 ndipo ankawerengera maolawa kuchokera pamene dzuwa latuluka. (Yoh. 11:9) Ola lachitatu linkayamba m’ma 8 koloko m’mawa n’kutha cha m’ma 9 koloko ndipo ola la 6 linkatha cha m’ma 12 koloko masana. Koma popeza dzuwa linkatuluka ndiponso kulowa pa nthawi zosiyanasiyana malinga ndi nyengo, kutalika kwa tsiku kunkakhalanso kosiyana. Ndipotu anthu ankatchula nthawi pongoyang’ana pamene pali dzuwa. Izi zinkachititsa kuti azitchula nthawi yawo moyerekezera basi osati ndendende. N’chifukwa chake m’Malemba Achigiriki Achikhristu amangonena kuti nthawi inali pafupifupi 9 koloko, pafupifupi 12 koloko kapena cha m’ma 3 koloko.—Mat. 20:3, 5; Mac. 10:3, 9, 30.
Koma olemba uthenga wabwino onse analemba zofanana pa nkhani ya zimene zinachitika usiku woti Yesu aphedwa mawa lake. Onse anayi analemba kuti ansembe aakulu ndi akulu onse anakumana m’mawa kwambiri ndipo anamtenga Yesu kupita naye kwa bwanamkubwa wachiroma dzina lake Pontiyo Pilato. (Mat. 27:1; Maliko 15:1; Luka 22:66; Yoh. 18:28) Mateyu, Maliko ndi Luka analemba kuti cha m’ma 12 koloko, Yesu ali pamtengo wozunzikirapo kunagwa mdima m’dziko lonselo “mpaka 3 koloko masana.”—Mat. 27:45, 46; Maliko 15:33, 34; Luka 23:44.
Koma pali chinthu chinanso chofunika kuchikumbukira pa nkhani ya nthawi imene Yesu anaphedwa. Kukwapulidwa kunali ngati chiyambi cha kupachikidwa. Nthawi zina munthu ankakwapulidwa mwankhanza kwambiri moti mwina ankafa nthawi yomweyo. N’kutheka kuti Yesu anakwapulidwanso kwambiri moti analephera kunyamula yekha mtengo wake wozunzikirapo ndipo munthu wina ndi amene anamunyamulira. (Luka 23:26; Yoh. 19:17) Ngati anthu ankaona kuti kupachika munthu kunkayamba ndi kumukwapula, payenera kuti panadutsa nthawi ndithu kufika nthawi imene ankamukhomerera pa mtengo wozunzikirapo. Choncho anthu anganene nthawi yosiyanasiyana imene Yesu anapachikidwa malinga ndi pamene ayamba kuwerengera nthawi.
Mtumwi Yohane analemba Baibulo zaka zambiri pambuyo poti ena amene analemba Uthenga Wabwino alemba kale. Choncho zinali zotheka kuti angotengera zimene ena analembazo. N’zoona kuti Yohane analemba nthawi imene ikusiyana ndi imene analemba Maliko. Koma umenewu ndi umboni woti sikuti Yohane anangokopera zimene ena analemba kale. Onse awiri Yohane ndi Maliko anauziridwa ndi Mulungu. Ngakhale kuti Malemba sanena zinthu zina zotithandiza kudziwa chifukwa chake pali kusiyana kumeneku, mauthenga abwino olembedwa m’Baibulo ndi odalirika.