Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Tizipereka Nsembe kwa Yehova ndi Moyo Wathu Wonse

Tizipereka Nsembe kwa Yehova ndi Moyo Wathu Wonse

“Chilichonse chimene mukuchita, muzichichita ndi moyo wanu wonse ngati kuti mukuchitira Yehova.”​—AKOL. 3:23.

1-3. (a) Kodi imfa ya Yesu pamtengo wozunzikirapo inachititsa kuti Yehova asafunenso nsembe zilizonse kwa ife? Fotokozani. (b) Kodi tingafunse funso liti pa nkhani yopereka nsembe masiku ano?

NTHAWI ya atumwi, Yehova anaululira anthu ake kuti nsembe ya dipo imene Yesu anapereka inafafaniza Chilamulo cha Mose. (Akol. 2:13, 14) Yehova sankafunanso kuti anthu azipereka nsembe zimene Ayuda anakhala akupereka kwa zaka zambirimbiri. Chilamulo chinali chitamaliza ntchito yake ‘yotsogolera anthu kuwafikitsa kwa Khristu.’​—Agal. 3:24.

2 Apa sizikutanthauza kuti Akhristu samaperekanso nsembe. Mtumwi Petulo ananena kuti Akhristu ayenera kupereka “nsembe zauzimu zovomerezeka pamaso pa Mulungu kudzera mwa Yesu Khristu.” (1 Pet. 2:5) Ndipotu mtumwi Paulo ananena kuti chilichonse chimene Mkhristu amachita pa moyo wake chikhoza kuonedwa kuti ndi “nsembe.”​—Aroma 12:1.

3 Choncho, Mkhristu amapereka nsembe kwa Yehova akamapatsa Yehova zinthu kapena akamadzimana zinthu chifukwa chofuna kumusangalatsa. Malinga ndi zimene takambirana pa nkhani ya nsembe zimene Aisiraeli ankapereka, kodi tingadziwe bwanji ngati nsembe zathu zili zovomerezeka kwa Yehova?

NSEMBE ZIMENE TIMAPEREKA TSIKU LILILONSE

4. Kodi tiyenera kukumbukira chiyani pochita zinthu za tsiku ndi tsiku?

4 Mwina zingativute kumvetsa mmene zochita zathu za tsiku lililonse zimakhudzira nsembe zimene timapereka kwa Yehova. Zinthu monga ntchito zapakhomo, sukulu, ntchito zolembedwa ndiponso kugula zinthu zingaoneke ngati sizikhudzana ndi zinthu zauzimu. Koma ngati mwadzipereka kwa Yehova kapena ngati mukufuna kudzipereka m’tsogolomu, muyenera kuona bwino mmene mumachitira zinthu za tsiku ndi tsiku. Tiyenera kukumbukira kuti ndife Akhristu nthawi zonse. Choncho tizitsatira mfundo za m’Malemba pochita chilichonse pa moyo wathu. N’chifukwa chake Paulo ananena kuti: “Chilichonse chimene mukuchita, muzichichita ndi moyo wanu wonse ngati kuti mukuchitira Yehova, osati anthu.”​—Werengani Akolose 3:18-24.

5, 6. Kodi tiyenera kuganizira zinthu ziti posankha zovala kapena pochita zinthu zina pa moyo wathu?

5 Sikuti zimene Mkhristu amachita tsiku ndi tsiku ndi mbali ya utumiki wake wopatulika. Koma mawu a Paulo akuti ‘tizichita zinthu ndi moyo wathu wonse ngati kuti tikuchitira Yehova’ ayenera kutichititsa kuonanso bwino zimene timachita tsiku ndi tsiku. Kodi tingagwiritse ntchito bwanji mfundo imeneyi pa moyo wathu? Kodi khalidwe ndiponso kavalidwe kathu kamasonyeza nthawi zonse kuti ndife Akhristu? Kapena kodi nthawi zina tingachite manyazi kuuza anthu kuti ndife Mboni za Yehova chifukwa cha khalidwe lathu kapena kavalidwe kathu pamene tikuchita zinthu za tsiku ndi tsiku? Tisalole zimenezi kuchitika. Anthu a Yehova ayenera kupewa zinthu zilizonse zimene zinganyozetse dzina la Mulungu.​—Yes. 43:10; 2 Akor. 6:3, 4, 9.

6 Tiyeni tione mmene mtima wofuna ‘kuchita zinthu ndi moyo wathu wonse ngati kuti tikuchitira Yehova’ ungakhudzire mbali zosiyanasiyana za moyo wathu. Pamene tikukambirana mfundo zimenezi tiyenera kukumbukira kuti nsembe zonse zimene Aisiraeli ankapereka kwa Yehova zinayenera kukhala zabwino kwambiri.​—Eks. 23:19.

NSEMBE ZIMENE MUMAPEREKA ZIMAKHUDZA MOYO WANU

7. Kodi kudzipereka kwa Mulungu kumatanthauza chiyani?

7 Pamene munkadzipereka kwa Yehova, muyenera kuti munachita zimenezo ndi mtima wanu wonse. Zimenezi zikutanthauza kuti muziika Yehova patsogolo pa zochita zanu zonse. (Werengani Aheberi 10:7.) Pamenepatu munasankha bwino kwambiri. Mosakayikira mwadzionera nokha kuti munthu akatsatira zimene Yehova amaphunzitsa pa nkhani zosiyanasiyana zotsatira zake zimakhala zabwino. (Yes. 48:17, 18) Anthu a Mulungu ndi oyera ndiponso osangalala chifukwa amatsanzira Yehova amene amawaphunzitsa.​—Lev. 11:44; 1 Tim. 1:11.

8. Kodi kukumbukira kuti nsembe za Aisiraeli zinali zopatulika kwa Yehova kungatithandize bwanji?

8 Yehova ankaona kuti nsembe zimene Aisiraeli ankapereka zinali zopatulika. (Lev. 6:25; 7:1) Mawu achiheberi amene anawamasulira kuti “kupatulika” amanena za chinthu chimene n’chosiyana kwambiri ndi zina, chapadera kapena choyenera Mulungu yekha. Kuti Yehova alandire nsembe zathu, nsembezo ziyenera kukhala zosadetsedwa ndi zinthu za m’dzikoli. Sizingatheke kukonda zinthu zimene Yehova amadana nazo. (Werengani 1 Yohane 2:15-17.) Zimenezi zikutanthauza kuti tiyenera kupewa anthu kapena zinthu zimene zingatichititse kukhala odetsedwa pamaso pa Mulungu. (Yes. 2:4; Chiv. 18:4) Zikutanthauzanso kuti sitingalole kuyang’anitsitsa zinthu zoipa kapena kuziganizira kwambiri.​—Akol. 3:5, 6.

9. Kodi zimene timachitira ena n’zofunika bwanji?

9 Paulo anauza Akhristu anzake kuti: “Musaiwale kuchita zabwino ndi kugawana zinthu ndi ena, pakuti nsembe zotero Mulungu amakondwera nazo.” (Aheb. 13:16) Choncho ngati ndife anthu abwino ndipo timachitira ena zabwino, Yehova amaona kuti zimenezi ndi nsembe zovomerezeka. Kukonda anzathu n’kumene kumasiyanitsa Akhristu oona ndi anthu ena.​—Yoh. 13:34, 35; Akol. 1:10.

NSEMBE ZIMENE TIMAPEREKA POLAMBIRA

10, 11. Kodi Yehova amaona bwanji ntchito yathu yolalikira komanso kulambira kwathu ndipo zimenezi ziyenera kutilimbikitsa kuchita chiyani?

10 Njira imodzi imene Akhristu amachitira anthu ena zabwino ndiyo “kulengeza poyera chiyembekezo chathu.” Kodi mumayesetsa kuchitira umboni pa mpata uliwonse umene wapezeka? Pofotokoza za ntchito yofunika kwambiri ya Akhristu imeneyi, Paulo ananena kuti: “Tizitamanda Mulungu. Tizichita zimenezi monga nsembe imene tikupereka kwa Mulungu, yomwe ndi chipatso cha milomo yathu. Timagwiritsa ntchito milomo imeneyi polengeza dzina lake kwa anthu ena.” (Aheb. 10:23; 13:15; Hos. 14:2) Ndi bwino kuganizira kuchuluka kwa nthawi imene timalalikira ndiponso njira zimene timagwiritsa ntchito polalikira. Mbali zambiri mu Msonkhano wa Utumiki zimatithandiza kuchita zimenezi. Utumiki wakumunda ndiponso kulalikira mwamwayi ndi ‘nsembe zotamanda Mulungu.’ Popeza ndi mbali ya kulambira kwathu, nsembe zimenezi ziyenera kukhala zabwino kwambiri. Zochitika pa moyo wa anthufe zimakhala zosiyana koma kawirikawiri nthawi imene timagwiritsa ntchito polalikira uthenga wabwino imasonyeza mmene timakondera zinthu zauzimu.

11 Yehova amafuna kuti Akhristu azipeza nthawi yolambira Mulungu kunyumba kwawo ndiponso ku mpingo. N’zoona kuti sititsatiranso malamulo okhudza Sabata kapena kupita kukachita zikondwerero ku Yerusalemu. Koma zinthu zimene zinkachitika kalezi n’zofanana ndi zinthu zina zimene Akhristu amachita masiku ano. Mulungu amafunanso kuti tizisiya zinthu zakuthupi n’kumaphunzira Mawu ake, kupemphera ndiponso kupezeka pa misonkhano. Akhristu omwe ndi mitu ya mabanja amaonetsetsa kuti akuchita kulambira kwa pabanja. (1 Ates. 5:17; Aheb. 10:24, 25) Pa nkhani yotumikira Mulungu, tiyenera kudzifunsa kuti, ‘Kodi pali zinthu zina zimene ndiyenera kusintha pa nkhani yolambira Yehova?’

12. (a) Kodi zofukiza zimene Aisiraeli ankapereka tingaziyerekeze ndi chiyani? (b) Kodi kudziwa zimenezi kuyenera kukhudza bwanji zimene timanena m’mapemphero athu?

12 Mfumu Davide inaimbira Yehova kuti: “Pemphero langa likhale lokonzedwa ngati zofukiza pamaso panu.” (Sal. 141:2) Taganizirani mapemphero amene mumapereka kwa Yehova. Kodi mumapemphera kawirikawiri, nanga mumatchula zinthu zotani? Buku la Chivumbulutso limayerekezera “mapemphero a oyera” ndi zofukiza. Limatero chifukwa chakuti mapempherowo amakhala ovomerezeka kwa Yehova ngati zofukiza zonunkhira bwino. (Chiv. 5:8) Aisiraeli ankaonetsetsa kuti zofukiza zimene ankapereka pa guwa la Yehova zikhale zokonzedwa bwino kwambiri. Yehova ankazivomereza kokha ngati zaperekedwa motsatira malangizo amene iye anapereka. (Eks. 30:34-37; Lev. 10:1, 2) Ngati tisankha bwino mawu oti tinene, Yehova adzavomereza pemphero lathu.

KUPATSA NDIPONSO KULANDIRA

13, 14. (a) Kodi Epafurodito ndi anthu a mu mpingo wa ku Filipi anathandiza bwanji Paulo ndipo mtumwiyu anamva bwanji ndi zimene anamuchitira? (b) Kodi tingatsanzire bwanji Epafurodito ndi anthu a mu mpingo wa Filipi?

13 Ndalama zimene timapereka kuti zithandize pa ntchito ya padziko lonse yolalikira tingaziyerekezere ndi nsembe kaya zikhale zochepa kapena zambiri. (Maliko 12:41-44) M’nthawi ya atumwi, anthu a mu mpingo wa ku Filipi anatumiza Epafurodito ku Roma kuti akapereke zinthu zina kwa Paulo. Zikuoneka kuti mpingo wa ku Filipi unamupatsira ndalama. Aka sikanali koyamba kuti Afilipi apereke zinthu kwa Paulo. Iwo ankafuna kuti Paulo asamavutike pa nkhani ya ndalama n’cholinga choti azichita mokwanira utumiki wake. Kodi Paulo anaona bwanji mphatso imeneyi? Iye ananena kuti mphatsoyi inali ngati “fungo lonunkhira bwino ndiponso nsembe yovomerezeka yosangalatsa kwa Mulungu.” (Werengani Afilipi 4:15-19.) Paulo anayamikira kwambiri kuwolowa manja kwa Afilipi ndipo Yehova anayamikiranso.

14 Masiku anonso, Yehova amayamikira kwambiri zinthu zimene timapereka kuti zithandize pa ntchito ya padziko lonse. Iye amatilonjezanso kuti ngati tiika patsogolo zinthu za Ufumu, adzatisamalira mwauzimu ndiponso mwakuthupi.​—Mat. 6:33; Luka 6:38.

MUZIYAMIKIRA

15. Kodi inuyo mumayamikira Yehova pa zifukwa ziti?

15 Pali zifukwa zambirimbiri zimene ziyenera kutichititsa kuyamikira Yehova. Tsiku lililonse tiyenera kumuyamikira kuti watipatsa moyo. Iye amatipatsanso zinthu zofunika pa moyo monga chakudya, zovala, malo ogona ndiponso mpweya umene timapuma. Tikadziwa zinthu molondola n’kukhala ndi chikhulupiriro, timakhalanso ndi chiyembekezo. Tiyeneradi kulambira Yehova ndiponso kupereka nsembe zomutamanda chifukwa cha mmene iye alili komanso zimene watichitira.​—Werengani Chivumbulutso 4:11.

16. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timayamikira nsembe ya dipo ya Khristu?

16 Malinga ndi zimene takambirana m’nkhani yapita ija, mphatso yamtengo wapatali imene Mulungu wapatsa anthu ndi nsembe ya dipo ya Khristu. Popereka nsembe imeneyi Mulungu anasonyeza kuti amatikonda kwambiri. (1 Yoh. 4:10) Kodi mphatso imeneyi iyenera kutilimbikitsa kuchita chiyani? Paulo anati: “Chikondi chimene Khristu ali nacho chimatikakamiza, chifukwa tatsimikiza kuti munthu mmodzi anafera anthu onse . . . Iye anaferanso onse kuti amene ali moyo asakhale moyo wongodzisangalatsa okha, koma akhale moyo wosangalatsa amene anawafera n’kuukitsidwa.” (2 Akor. 5:14, 15) Apa Paulo ankatanthauza kuti ngati timayamikira kukoma mtima kwa Mulungu tidzagwiritsa ntchito moyo wathu kuti tilemekeze Iyeyo limodzi ndi Mwana Wake. Timasonyeza kuti timakonda ndiponso kuyamikira Mulungu ndi Khristu tikamawamvera ndiponso kukhala ndi mtima wofunitsitsa kulalikira ndi kuphunzitsa anthu.​—1 Tim. 2:3, 4; 1 Yoh. 5:3.

17, 18. Kodi anthu ena awonjezera bwanji nsembe zawo zotamanda Yehova? Perekani chitsanzo.

17 Kodi pali zinthu zina zimene muyenera kusintha pa nsembe zotamanda Mulungu zimene mumapereka? Anthu ambiri ataganizira bwinobwino zimene Yehova wawachitira aona kuti ndi bwino kuwonjezera nthawi imene amagwira ntchito yolalikira za Ufumu komanso ntchito zina m’gulu la Yehova. Ena amachita upainiya wothandiza mwezi umodzi kapena ingapo pa chaka. Ena akuchita upainiya wokhazikika. Ndipo ena akugwira nawo ntchito zomangamanga m’gulu la Yehova. Onsewatu amasonyeza kuti akuyamikira kwambiri zimene Yehova wawachitira. Munthu akamachita zimenezi ali ndi zolinga zoyenera, zomwe ndi kuyamikira Yehova, utumiki wake wopatulikawo umakhala wovomerezeka pamaso pa Mulungu.

18 Akhristu ambiri amayamikira Yehova ndipo amaona kuti ayenera kumuchitira zinthu zina. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi Morena. Iye anakulira m’banja lachikatolika ndipo anayesetsa kuti apeze mayankho a mafunso amene anali nawo. Anafufuzanso mayankho m’zinthu zimene anthu a ku Asia amakhulupirira ndipo sanapeze mfundo zogwira mtima. Koma atayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova, ludzu lake lauzimu linathetsedwa. Iye anapeza mayankho ochokera m’Malemba ndiponso anaona mmene mayankhowo anamuthandizira pa moyo wake. Izi zinamuchititsa kuyamikira kwambiri Yehova ndipo anafuna kusonyeza kuti amayamikira pogwiritsa ntchito moyo wake wonse mu utumiki. Iye atangobatizidwa ankachita upainiya wothandiza pafupipafupi ndipo kenako ataona kuti zinthu zili bwino anadzayamba upainiya wokhazikika. Morena wakhala akuchita utumiki wa nthawi zonse kwa zaka 30 tsopano.

19. Kodi mungawonjezere bwanji nsembe zimene mumapereka kwa Yehova?

19 N’zoona kuti pali atumiki a Yehova okhulupirika ambiri amene sangachite upainiya chifukwa cha zinthu zina pa moyo wawo. Koma zilizonse zimene tonsefe tingakwanitse kuchita potumikira Yehova zikhoza kukhala nsembe zauzimu zovomerezeka kwa Iye. Tsiku lililonse khalidwe lathu liyenera kusonyeza kuti timatsatira mfundo zolungama za Yehova ndipo tiyenera kukumbukira kuti timaimira Yehova nthawi zonse. Tiyenera kukhala ndi chikhulupiriro ndipo tisamakayikire zoti zolinga za Yehova zizikwaniritsidwa. Ntchito zathu zabwino zimathandiza kuti tifalitse uthenga wabwino. Popeza timayamikira kwambiri zonse zimene Yehova watichitira, tiyeni tipitirize kupereka nsembe kwa Yehova ndi moyo wathu wonse.

[Mafunso]

[Mawu Otsindika patsamba 25]

Kodi mumafuna kuchita chiyani mukaganizira zinthu zabwino zimene Yehova wakuchitirani?

[Chithunzi patsamba 23]

Kodi mumayesetsa kuchitira umboni pa mpata uliwonse umene wapezeka?