Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Khalanibe Otetezeka M’chigwa cha Yehova

Khalanibe Otetezeka M’chigwa cha Yehova

“Yehova adzapita kukamenyana ndi anthu a mitundu inawo ngati mmene anachitira pomenyana ndi adani ake m’mbuyomu.”—ZEK. 14:3.

1, 2. Kodi ndi nkhondo iti imene yatsala pang’ono kuchitika? Nanga atumiki a Mulungu sadzayenera kuchita chiyani pa nkhondoyi?

PA October 30, 1938, anthu ambirimbiri ku United States anali kumvetsera sewero la pa wailesi. Sewerolo linali lochokera m’buku la nkhani yopeka yonena za nkhondo ya pakati pa dziko lapansi ndi la Mars. Ngakhale kuti analengeza kuti ndi sewero, anthu ambiri ankaganiza kuti ndi zenizeni ndipo ankachita mantha. Choncho anthu ambiri anayesetsa kuchita zinthu zoti adziteteze.

2 Koma pali nkhondo yeniyeni imene yatsala pang’ono kuchitika. Ngakhale zili choncho, anthu ambiri sakuikonzekera. Nkhondo imeneyi imafotokozedwa m’Baibulo, limene ndi Mawu a Mulungu, osati m’buku la nkhani zongopeka. Nkhondo imeneyi imatchedwa Aramagedo ndipo pa nkhondoyi Mulungu adzawononga dziko loipali. (Chiv. 16:14-16) Atumiki a Mulungu sadzayenera kudziteteza kwa adani ochokera kudziko lina. Koma adzaona Mulungu akuwapulumutsa m’njira yodabwitsa kwambiri.

3. Kodi tikambirana ulosi uti? N’chifukwa chiyani ulosiwu ndi wofunika kwambiri kwa ife?

3 Ulosi wopezeka pa Zekariya 14 umanena za nkhondo ya Aramagedo. Ngakhale kuti unalembedwa zaka zoposa 2,500 zapitazo, ndi wofunika kwambiri kwa ife. (Aroma 15:4) Umafotokoza zimene zinachitikira anthu a Mulungu kuyambira mu 1914 pamene Ufumu wa Mesiya unakhazikitsidwa kumwamba komanso zinthu zochititsa chidwi zimene zichitike posachedwapa. Ulosiwu umanena za kukonzedwa kwa “chigwa chachikulu kwambiri” ndiponso kutuluka kwa “madzi amoyo.” (Zek. 14:4, 8) M’nkhaniyi, tiona kuti chigwachi n’chofunika kwambiri kuti anthu a Yehova atetezedwe. Tionanso tanthauzo la madzi amoyo ndipo tikamvetsa tanthauzo  lake, tidzazindikira kufunika kwa madziwo komanso tidzakhala ndi mtima wofuna kuwamwa. Choncho n’kofunika kwambiri kuti tiganizire mozama ulosi umenewu.—2 Pet. 1:19, 20.

“TSIKU LA YEHOVA” LINAYAMBA

4. (a) Kodi “tsiku la Yehova” linayamba liti? (b) Kodi atumiki a Yehova analengeza za chiyani kwa zaka zambiri chisanafike chaka cha 1914? Nanga atsogoleri a dzikoli anatani atamva?

4 Chaputala 14 cha buku la Zekariya chimayamba ndi mawu onena za “tsiku la Yehova.” (Werengani Zekariya 14:1, 2.) Kodi tsiku limeneli ndi liti? Ndi “tsiku la Ambuye” limene linayamba pamene “ufumu wa dziko” unakhala “ufumu wa Ambuye wathu ndi wa Khristu wake.” (Chiv. 1:10; 11:15) Tsiku limeneli linayamba mu 1914, pamene Ufumu wa Mesiya unakhazikitsidwa kumwamba. Chakachi chisanafike, atumiki a Yehova analengeza kwa zaka zambiri kwa anthu a mitundu yonse kuti mapeto a ‘nthawi zoikidwiratu za anthu a mitundu ina’ adzafika mu 1914. (Luka 21:24) Ananenanso kuti m’chakachi, dziko lidzalowa m’nyengo ya mavuto aakulu kuposa kale lonse. Kodi anthu anatani atamva zimenezi? M’malo momvera chenjezo la pa nthawi yake limeneli, atsogoleri andale ndiponso achipembedzo anayamba kunyoza ndiponso kuzunza odzozedwa amene ankalalikira mwakhamawa. Pochita zimenezi, iwo ankanyozanso Mulungu Wamphamvuyonse. Tikutero chifukwa chakuti akazembe odzozedwa a Ufumuwa ankaimira “Yerusalemu wakumwamba.” Mawu oti “Yerusalemu wakumwamba” akutanthauza Ufumu wa Mesiya ndipo odzozedwawa ndi mbali ya Ufumuwo.—Aheb. 12:22, 28.

5, 6. (a) Kodi anthu a mitundu anachitira chiyani “mzindawu” ndi “nzika” zake? (b) Kodi “anthu otsala” akuimira ndani?

5 Pofotokoza zimene anthu a mitundu adzachite, Zekariya anati: “Mzindawu [Yerusalemu] udzalandidwa.” “Mzindawu” ukuimira Ufumu wa Mulungu. Akhristu odzozedwa amene atsala padzikoli ndi “nzika” za Ufumuwu. (Afil. 3:20) ‘Mzindawu unalandidwa’ pa nthawi ya nkhondo yoyamba ya padziko lonse pamene abale ena omwe ankayang’anira mbali ya padziko lapansi ya gulu la Yehova anamangidwa. Iwo anaikidwa m’ndende mumzinda wa Atlanta ku Georgia, ku United States. Anthu okhulupirika ankachitiridwa zinthu zopanda chilungamo komanso zankhanza. Analetsedwa kufalitsa mabuku ndiponso kulalikira za Ufumu. Apa zinali ngati ‘katundu wa m’nyumba watengedwa.’

6 Adani anali ambiri ndipo ananamizira anthu a Mulungu nkhani zambiri, kuwatsutsa ndiponso kuwazunza. Koma kulambira koona sikunathetsedwe. Panali “anthu otsala” kapena kuti odzozedwa okhulupirika ena amene sanalolere ‘kuchotsedwa mumzindawu.’

7. Kodi chitsanzo cha Akhristu odzozedwa chimathandiza bwanji atumiki a Yehova masiku ano?

7 Kodi ulosiwu unangokwaniritsidwa pa nthawi ya nkhondo yoyamba ya padziko lonse basi? Ayi. Odzozedwawa limodzi ndi anzawo okhulupirika amene akuyembekezera kudzakhala padziko lapansi anapitiriza kuzunzidwa. (Chiv. 12:17) Mwachitsanzo, anazunzidwa kwambiri pa nthawi ya nkhondo yachiwiri ya padziko lonse. Chitsanzo cha Akhristu odzozedwa okhulupirikawa chimathandiza atumiki a Mulungu masiku ano  kupirira mayesero. Chifukwa cha chikhulupiriro chawo, iwo amakumana ndi mayesero monga kunyozedwa ndi achibale komanso anzawo akuntchito kapena akusukulu. (1 Pet. 1:6, 7) Kulikonse kumene amakhala, atumiki a Yehova akuyesetsa kwambiri ‘kulimbikira mu mzimu umodzi’ ndipo ‘sachita mantha ndi owatsutsa.’ (Afil. 1:27, 28) Koma kodi anthu a Yehova angapeze kuti chitetezo m’dziko limene limadana nawo?—Yoh. 15:17-19.

YEHOVA ANAKONZA “CHIGWA CHACHIKULU KWAMBIRI”

8. (a) Kodi m’Baibulo nthawi zina mapiri amaimira chiyani? (b) Kodi “phiri la mitengo ya maolivi” likuimira chiyani?

8 Popeza kuti Yerusalemu, kapena kuti “mzindawu,” akuphiphiritsira Yerusalemu wakumwamba ndiye kuti ‘phiri la mitengo ya maolivi limene lili moyang’anizana ndi Yerusalemu’ ndi lophiphiritsanso. Kodi phirili likuimira chiyani? Kodi “kugawanika pakati” kwa phirili n’kukhala mapiri awiri kumatanthauza chiyani? Nanga n’chifukwa chiyani Yehova amanena kuti onsewa ndi ‘mapiri ake’? (Werengani Zekariya 14:3-5.) M’Baibulo, nthawi zina mapiri amaimira maufumu kapena kuti maboma. Baibulo limanenanso kuti madalitso ndiponso chitetezo zimachokera kuphiri la Mulungu. (Sal. 72:3; Yes. 25:6, 7) Choncho phiri la mitengo ya maolivi limene Mulungu amaima chakum’mawa kwa Yerusalemu likuimira ulamuliro wa Yehova wa chilengedwe chonse, kapena kuti ulamuliro wake wapamwamba kwambiri.

9. Kodi kugawanika kwa “phiri la mitengo ya maolivi” kumatanthauza chiyani?

9 Kodi kugawanika kwa phiri la mitengo ya maolivi kumatanthauza chiyani? Phirili, lomwe lili kum’mawa kwa Yerusalemu, linagawanika pamene Yehova anakhazikitsa ulamuliro wina wocheperapo. Ulamuliro wocheperapowu ndi Ufumu wa Mesiya ndipo wolamulira wake ndi Yesu Khristu. N’chifukwa chake Yehova amanena kuti mapiri onse awiriwa, amene anapangika “phiri la mitengo ya maolivi” litagawanika, ndi ake. (Zek. 14:4) Mapiri onsewa ndi a Yehova.

10. Kodi “chigwa chachikulu kwambiri” cha pakati pa mapiri awiriwa chikuimira chiyani?

10 Phiri lophiphiritsali litagawanika, hafu imodzi inapita kumpoto ndipo hafu ina inapita kum’mwera. Koma mapazi a Yehova anapondabe mapiri awiriwa. Ndiyeno pakati pa mapiri amene Yehova akupondawa, panapangika “chigwa chachikulu kwambiri.” Chigwachi chikuimira chitetezo chochokera kwa Mulungu chimene atumiki a Yehova amapeza akamagonjera ulamuliro wa Yehova wa chilengedwe chonse ndiponso Ufumu wa Mesiya. Izi zikusonyeza kuti Yehova adzaonetsetsa kuti kulambira koona kusathetsedwe. Kodi phirili linagawanika liti? Linagawanika pamene Ufumu wa Mesiya unakhazikitsidwa mu 1914. Awa anali mapeto a ‘nthawi za anthu a mitundu ina.’ Nanga atumiki a Mulungu anayamba liti kuthawira kuchigwa chophiphiritsachi?

ANTHU A YEHOVA ANAYAMBA KUTHAWIRA KUCHIGWACHI

11, 12. (a) Kodi anthu a Yehova anayamba liti kuthawira kuchigwa chophiphiritsa? (b) N’chiyani chikusonyeza kuti Yehova akuteteza anthu ake ndi dzanja lake lamphamvu?

11 Yesu anachenjeza otsatira ake kuti: “Mitundu yonse idzadana nanu chifukwa cha dzina langa.” (Mat. 24:9) Chidani chimenechi chakula kwambiri m’masiku omaliza a dziko loipali, kuyambira mu 1914. Ngakhale kuti adaniwo anaukira kwambiri odzozedwa amene anatsala padziko lapansi pa nthawi ya nkhondo yoyamba ya padziko lonse, odzozedwa okhulupirikawo sanatheretu. Mu 1919, iwo anamasulidwa mu ukapolo wa Babulo Wamkulu, yemwe akuimira zipembedzo zonse zonyenga padziko lapansi. (Chiv. 11:11, 12) * Pa nthawiyi, m’pamene anthu a  Yehova anayamba kuthawira kuchigwa cha pakati pa mapiri ake.

12 Kuyambira mu 1919, chigwa cha Yehova chikupitiriza kuteteza atumiki ake padziko lonse. Kwa zaka zambiri, mayiko osiyanasiyana akhala akuletsa ntchito yolalikira ndiponso kufalitsa mabuku othandiza kuphunzira Baibulo a Mboni za Yehova. Zimenezi zikuchitikabe m’mayiko ena. Koma kaya ayesetse bwanji, sangathetse kulambira koona. Yehova adzateteza anthu ake ndi dzanja lake lamphamvu.—Deut. 11:2.

13. N’chiyani chingatithandize kukhalabe m’chigwa choteteza cha Yehova? N’chifukwa chiyani tifunika kukhalabe m’chigwachi panopa kuposa kale lonse?

13 Tikamapitiriza kukhala okhulupirika kwa Yehova n’kukhalabe m’choonadi, Yehova ndiponso Yesu Khristu adzatiteteza. Palibe amene ‘angatitsomphole m’dzanja la Mulungu.’ (Yoh. 10:28, 29) Yehova ndi wofunitsitsa kutithandiza m’njira iliyonse imene tingafunikire kuti tizimumvera monga Wolamulira wa Chilengedwe Chonse ndiponso kugonjera Ufumu wa Mesiya. Tifunika kukhalabe m’chigwa cha chitetezo chifukwa chigwachi chidzathandiza kwambiri atumiki a Yehova pa chisautso chachikulu chimene changotsala pang’ono kuyamba.

YEHOVA AMENYANA NDI ADANI AKE POSACHEDWAPA

14, 15. Kodi anthu amene ali kunja kwa chigwa zidzawathera bwanji pamene Mulungu azidzamenya nkhondo?

14 Pamene mapeto a dzikoli akuyandikira, Satana aziukira kwambiri atumiki a Yehova. Koma ulendo wina umene iye adzaukira anthu a Yehova, adzaona zakuda. Yehova adzamenyana ndi adani ake n’kuwawononga. Pa nthawi imeneyo, Wolamulira Chilengedwe Chonse adzasonyeza kuposa kale lonse kuti ndi wamphamvu pa nkhondo.—Zek. 14:3.

15 Kodi anthu amene ali kunja kwa “chigwa chachikulu” zidzawathera bwanji pamene Mulungu azidzamenya nkhondo? Iwo sadzakhala ndi “kuwala kwapadera” kochokera kwa Mulungu. Pa nthawi imeneyo, “mahatchi, nyulu, ngamila, abulu amphongo ndi chiweto cha mtundu uliwonse” zidzazizidwa kwambiri moti sizingachite chilichonse. Nyama zimenezi zikuimira zida za nkhondo za anthu. Choncho zikusonyeza kuti zidazo zidzakhala zopanda ntchito. Yehova adzawagwetseranso “mliri.” Kaya mliriwu udzakhala weniweni kapena ayi, adani a Mulungu sadzakhalanso oopsa. Baibulo limanena kuti: ‘Maso awo adzawola ndiponso lilime lawo lidzawola.’ Izi zikutanthauza kuti azidzamenya nkhondo ngati anthu akhungu ndipo adzasowa chonena kuti atsutse Mulungu. (Zek. 14:6, 7, 12, 15.) Anthu ambirimbiri adzakhala kumbali ya Satana. Koma palibe mbali iliyonse ya dziko loipali imene idzapulumuke. (Chiv. 19:19-21) Baibulo limati: “Pa tsiku limenelo padzakhala anthu ophedwa ndi Yehova kuchokera kumalekezero a dziko lapansi kufikanso kumalekezero ena a dziko lapansi.”—Yer. 25:32, 33.

16. Pamene tikuyembekezera nthawi imene Mulungu adzamenye nkhondo, kodi tiyenera kuganizira mafunso ati? Nanga tiyeneranso kuchita chiyani?

16 Nthawi zonse anthu amavutika pa nkhondo ngakhale amene amapambana. Chakudya chimasowa ndipo katundu amawonongeka. Zinthu zimasokonekera komanso ufulu umachepa. Kodi ifeyo tidzatani ngati zoterezi zitatigwera? Kodi tidzachita mantha mpaka kufika posiya kukhala okhulupirika kwa Mulungu? Kodi tidzataya mtima n’kumaona kuti palibe mtengo wogwira? Pa nthawi ya chisautso chachikulu, tidzafunika kudalirabe kuti Yehova adzatipulumutsa ndiponso kukhalabe m’chigwa chake cha chitetezo.—Werengani Habakuku 3:17, 18.

 “MADZI AMOYO ADZATULUKA”

17, 18. (a) Kodi “madzi amoyo” n’chiyani? (b) Kodi ‘nyanja ya kum’mawa’ ndiponso ‘nyanja ya kumadzulo’ zikuimira chiyani? (c) Kodi inuyo mukufunitsitsa kuchitabe chiyani?

17 Aramagedo ikadzatha, “madzi amoyo” azidzayenda mosalekeza kuchokera ku mpando wachifumu wa Mesiya. “Madzi amoyo” amenewa akuimira zonse zimene Yehova watipatsa kuti tikhale ndi moyo wosatha. ‘Nyanja ya kum’mawa’ ikuimira Nyanja Yakufa ndipo ‘nyanja ya kumadzulo’ ikuimira nyanja ya Mediterranean. Nyanja zonsezi zikutchulidwa pofotokoza za anthu. Nyanja Yakufa ikuimira anthu amene ali m’manda a anthu onse. Popeza kuti nyanja ya Mediterranean ili ndi zamoyo zambiri, ikuimira “khamu lalikulu” limene lidzapulumuke Aramagedo. (Werengani Zekariya 14:8, 9; Chiv. 7:9-15) Choncho magulu onse awiriwa adzamasulidwa ku imfa imene anatengera kwa Adamu. Izi zidzachitika akamadzamwa madzi ophiphiritsa ochokera ‘mumtsinje wa madzi a moyo.’—Chiv. 22:1, 2.

Yesetsani kukhalabe otetezeka m’chigwa cha Yehova

18 Ife tidzatetezedwa ndi Yehova kuti tipulumuke mapeto a dziko loipali n’kulowa m’dziko latsopano lachilungamo. Ngakhale kuti dzikoli limadana nafe, tiziyesetsa kukhalabe nzika zokhulupirika za Ufumu wa Mulungu. Tiziyesetsanso kukhalabe otetezeka m’chigwa cha Yehova.

^ ndime 11 Onani buku lakuti Mapeto Osangalatsa a Masomphenya a M’buku la Chivumbulutso Ayandikira, tsamba 169 mpaka 170.