Lolani Kuti Yehova Azikuumbani Ndi Malangizo Ake
“Mudzanditsogolera ndi malangizo anu, ndipo pambuyo pake mudzanditenga ndi kundipatsa ulemerero.”—SAL. 73:24.
1, 2. (a) Kodi ndi zinthu ziti zimene zingatithandize kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova? (b) Kodi kuphunzira zimene anthu ena anachita atapatsidwa malangizo ndi Mulungu kutithandiza bwanji?
WAMASALIMO ananena mawu osonyeza kuti ankakhulupirira kwambiri Mulungu. Iye anati: “Koma kwa ine kuyandikira kwa Mulungu ndi chinthu chabwino. Yehova Ambuye Wamkulu Koposa ndiye pothawirapo panga.” (Sal. 73:28) Kodi n’chiyani chinam’chititsa kuti anene mawu amenewa? Poyamba, wamasalimoyu anakhumudwa kwambiri ataona kuti anthu oipa akukhala mwamtendere. Choncho iye anadandaula kuti: “Ndayeretsa mtima wanga pachabe, ndipo ndasamba m’manja mwanga pachabe posonyeza kuti ndine wopanda cholakwa.” (Sal. 73:2, 3, 13, 21) Koma atalowa “m’malo opatulika aulemerero a Mulungu,” anasintha maganizo ake n’kuyambanso kukonda kwambiri Mulungu. (Sal. 73:16-18) Wamasalimoyu, yemwe anali munthu woopa Mulungu, anaphunzirapo kanthu chifukwa chopezeka m’malo opatulika. Iye anazindikira kuti kupezeka pakati pa anthu a Mulungu, kulandira malangizo ndiponso kuwagwiritsa ntchito kumathandiza kwambiri kuti munthu akhale pa ubwenzi wabwino ndi Yehova.—Sal. 73:24.
2 Ifenso timafunitsitsa kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu woona ndiponso wamoyo. Kuti zimenezi zitheke, m’pofunika kwambiri kuti tizimulola kutiumba pogwiritsa ntchito malangizo kapena chilango chake. Izi zingathandize kuti iye azisangalala nafe. Kale, Mulungu anapereka mwayi kwa anthu ndi mitundu yosiyanasiyana kuti asankhe kumvera malangizo ake. Zimene iwo anachita atapatsidwa mwayi umenewu zinalembedwa m’Baibulo kuti “zitilangize” komanso “zitichenjeze ifeyo amene mapeto a nthawi zino atifikira.” (Aroma 15:4; 1 Akor. 10:11) Kukambirana nkhani zimenezi kutithandiza kudziwa bwino Yehova ndiponso mmene amatithandizira akamatiumba.
KODI YEHOVA AMAUMBA BWANJI ANTHU?
3. Kodi lemba la Yesaya 64:8 ndiponso Yeremiya 18:1-6 limasonyeza bwanji mphamvu zimene Yehova ali nazo? (Onani Chithunzi patsamba 24.)
3 Lemba la Yesaya 64:8 limafotokoza fanizo losonyeza mphamvu zimene Yehova ali nazo pa munthu aliyense ndiponso pa mitundu ya anthu. Lembali limati: “Inu Yehova, inu ndinu Atate wathu. Ife ndife dongo ndipo inu ndinu Wotiumba. Tonsefe ndife ntchito ya manja anu.” Woumba amakhala ndi ufulu wonse pogwiritsa ntchito dongo kuti aumbe chinthu chimene akufuna, ndipo dongolo silingakane. Munthunso ali ngati dongo m’manja mwa Mulungu. Choncho n’zosamveka kuti munthu azikana zimene Mulungu akumuuza.—Werengani Yeremiya 18:1-6.
4. Kodi Mulungu amangosankha kuumba anthu kuti akhale abwino kapena oipa? Fotokozani.
4 Zimene Yehova ankachita ndi Aisiraeli zimasonyeza kuti iwo anali ngati dongo m’manja mwake. Koma pali kusiyana pakati pa zimene Yehova ankachita ndi zimene woumba amachita. Woumba amangosankha chinthu chimene akufuna kuumba, n’kuchiumba. Ndiye funso ndi lakuti, kodi Yehova amangosankha kuti aumbe anthu ena kukhala abwino, ena kukhala oipa? Baibulo limasonyeza kuti sachita zimenezo. Iye anapatsa anthu ufulu wosankha ndipo imeneyi ndi mphatso yamtengo wapatali. Ngakhale kuti Yehova ndi Wolamulira wa Chilengedwe Chonse, iye akamachita zinthu saphwanyira anthu ufulu umenewu. Anthu amafunika kusankha okha kuti aumbidwe ndi Mlengi wawo, Yehova.—Werengani Yeremiya 18:7-10.
5. Kodi Yehova amatani ngati anthu akana kuti iye awaumbe?
5 Nanga chingachitike n’chiyani ngati anthu akana kuumbidwa ndi Mulungu? Taganizirani zimene woumba amachita akaona kuti chinthu chimene akuumba sichikuumbika bwino. Iye angasankhe kuumba chinthu china kapena akhoza kungotaya dongolo. Nthawi zambiri kuti dongo lifike powonongeka, vuto limakhala ndi woumbayo. Koma si mmene zilili ndi Mulungu. (Deut. 32:4) Ngati munthu wina akukanika kuumbidwa ndi Yehova, nthawi zonse vuto limakhala ndi munthuyo. Yehova akamaumba anthu amasintha mogwirizana ndi zimene anthuwo akuchita. Anthu amene amalola kuumbidwa, iye amawaumba kuti akhale anthu abwino. Mwachitsanzo, Akhristu odzozedwa ndi “ziwiya zachifundo” omwe aumbidwa kukhala ‘ziwiya zolemekezeka.’ Koma anthu amene amakana kuti Mulungu awaumbe amakhala “ziwiya za mkwiyo zoyenera kuwonongedwa.”—Aroma 9:19-23.
6, 7. Kodi Mfumu Davide anachita chiyani atapatsidwa uphungu? Nanga Mfumu Sauli anatani?
6 Yehova amatha kuumba anthu popereka uphungu kapena malangizo. Tiyeni tione mmene amaumbira anthu poona nkhani ya Sauli ndiponso Davide, omwe anali mafumu oyambirira a Isiraeli. Davide atachita chigololo ndi Bati-seba, tchimo lakelo linabweretsa mavuto kwa iyeyo ndiponso kwa anthu ena. Ngakhale kuti Davide anali mfumu, Yehova anam’patsabe uphungu wamphamvu. Iye anatumiza mneneri Natani kuti akapereke uphunguwo. (2 Sam. 12:1-12) Kodi Davide anatani atapatsidwa uphungu? Zinam’khudza kwambiri ndipo analapa. Choncho Mulungu anamuchitira chifundo.—Werengani 2 Samueli 12:13.
7 Koma Sauli anachita zinthu mosiyana kwambiri ndi Davide. Kudzera mwa mneneri Samueli, Yehova anapereka lamulo lomveka bwino kwa Sauli lakuti akawononge Aamaleki onse ndi ziweto zawo. Koma Sauli sanamvere lamulo lochokera kwa Mulungu limeneli. Iye sanaphe Agagi, yemwe anali mfumu, ndipo anasiyanso ziweto zabwino kwambiri. N’chifukwa chiyani anachita zimenezi? Chifukwa chimodzi chinali chakuti ankafuna kuti anthu azimulemekeza. (1 Sam. 15:1-3, 7-9, 12) Atapatsidwa uphungu, Sauli akanachita bwino kumvera n’kulola kuti aumbidwe ndi Mulungu. Koma anakana n’kuyamba kupereka zifukwa zodzikhululukira. Iye ananena kuti anachita bwino chifukwa chakuti ziwetozo akanazigwiritsa ntchito popereka nsembe. Komanso anapeputsa uphungu wa Samueli. Izi zinachititsa kuti Yehova akane Mfumu Sauli moti ubwenzi wake ndi Mulungu woona unatheratu.—Werengani 1 Samueli 15:13-15, 20-23.
MULUNGU ALIBE TSANKHO
8. Kodi tingaphunzire chiyani pa zimene zinachitikira Aisiraeli?
8 Yehova amapatsanso mitundu ya anthu ufulu womumvera kapena wokana kumumvera. Aisiraeli atamasulidwa ku Iguputo mu 1513 B.C.E., Yehova anachita nawo pangano. Iwo anali mtundu wake wosankhidwa ndipo anali ndi mwayi woumbidwa ndi Mulunguyo. Koma anthuwo ankangochitabe zimene Yehova amadana nazo ndipo anayamba kulambira milungu ya anthu a mitundu ina. Yehova ankatumiza aneneri ake mobwerezabwereza kuti akawalangize koma Aisiraeli sanawamvere. (Yer. 35:12-15) Chifukwa cha zimenezi, iwo anayenera kulangidwa ndipo anali ngati ziwiya zoyenera kuwonongedwa. Ufumu wakumpoto wa mafuko 10 unawonongedwa ndi Asuri ndipo ufumu wakum’mwera wa mafuko awiri unawonongedwa ndi Ababulo. Limeneli ndi chenjezo lamphamvu kwa ifeyo. Yehova akhoza kutiumba pokhapokha ngati talola kuti atiumbe.
9, 10. Kodi anthu a ku Nineve anatani atachenjezedwa ndi Mulungu?
9 Yehova anaperekanso chenjezo kwa anthu a mumzinda wa Nineve, womwe unali likulu la Asuri. Iwo anali ndi ufulu woti amvere kapena ayi. Yehova anauza Yona kuti: “Nyamuka upite kumzinda waukulu wa Nineve. Kumeneko ukadzudzule anthu a mumzindawo ndi kuwauza kuti ine ndaona zoipa zimene akuchita.” Mzinda wa Nineve unali woyenera kuwonongedwa.—Yona 1:1, 2; 3:1-4.
10 Koma Yona atawachenjeza, “anthu a ku Nineve anayamba kukhulupirira Mulungu ndipo anayamba kulengeza kuti aliyense, popanda wotsala, asale kudya ndipo avale ziguduli.” Mfumu yawo “inanyamuka pampando wake wachifumu ndi kuvula chovala chake chachifumu. Ndiyeno inavala chiguduli ndi kukhala paphulusa.” Anthu a ku Nineve analola kuumbidwa ndi Yehova ndipo analapa. Chifukwa cha zimenezi, Yehova sanawononge mzindawu.—Yona 3:5-10.
11. Kodi zimene Yehova anachita ndi Aisiraeli komanso anthu a ku Nineve zikusonyeza kuti iye ndi wotani?
11 Ngakhale kuti Aisiraeli anali mtundu wosankhidwa, Yehova anawalangabe. Koma anthu a ku Nineve sanali pa ubwenzi wapadera ndi Mulungu. Ngakhale zinali choncho, Yehova anawachenjeza ndipo anawachitira chifundo pamene iwo analola kuumbidwa. Zitsanzo ziwirizi zikusonyeza bwinobwino kuti Yehova Mulungu wathu “alibe tsankho.”—Deut. 10:17.
YEHOVA NDI WOLOLERA KOMANSO WOKONZEKA KUSINTHA
12, 13. (a) N’chifukwa chiyani Yehova amasintha maganizo anthu akalolera kuumbidwa? (b) Kodi Yehova anasintha bwanji maganizo ake pa nkhani ya Sauli? Nanga pa nkhani ya Nineve?
12 Zimene Yehova amachita poumba anthu zimasonyeza kuti iye ndi wololera komanso wokonzeka kusintha. Yehova akaweruza mwachilungamo kuti anthu akufunika kuwonongedwa, iye amatha kusintha maganizo ngati anthuwo amvera chenjezo lake. Mwachitsanzo, Baibulo limatiuza kuti anthu a ku Nineve atalapa n’kusiya machimo awo, “Mulungu woona anasintha maganizo ake pa tsoka limene ananena kuti awabweretsera, moti sanawabweretsere.” (Yona 3:10) Ponena za mfumu yoyamba ya Isiraeli, Yehova anati: “Ndikumva chisoni kuti ndinaika Sauli kukhala mfumu.”—1 Sam. 15:11.
13 Mawu achiheberi amene anawamasulira kuti ‘kumva chisoni,’ amatanthauza kusintha maganizo kapena kusintha zimene ukufuna kuchita. Yehova anasankha Sauli kukhala mfumu koma anasintha maganizo n’kumukana. Sikuti Yehova analakwitsa posankha Sauli koma Sauliyo ndi amene anasiya kumvera Mulungu. Yehova anasinthanso maganizo pa nkhani yofuna kuwononga anthu a ku Nineve. N’zolimbikitsa kudziwa kuti Yehova akamatiumba, amakhala wololera komanso wokonzeka kusintha. Iye ndi wachifundo ndipo amasintha maganizo ngati munthu wochimwa walapa.
TISAKANE MALANGIZO A YEHOVA
14. (a) Kodi Yehova amatiumba bwanji masiku ano? (b) Kodi tizitani Mulungu akamatiumba?
14 Masiku ano, Yehova amatiumba pogwiritsa ntchito Mawu ake ndiponso gulu lake. (2 Tim. 3:16, 17) Choncho tiyenera kumvera malangizo amene timalandira kudzera m’njira zimenezi. Kaya tinabatizidwa liti kapena tili ndi udindo wotani m’gulu la Mulungu, tonsefe tiyenera kupitiriza kumvera malangizo a Yehova. Tikatero, iye adzatiumba kukhala ziwiya zolemekezeka.
15, 16. (a) Kodi nthawi zina munthu angamve bwanji ngati wapatsidwa chilango n’kuchotsedwa pa udindo winawake? Perekani chitsanzo. (b) N’chiyani chingatithandize kuti tisamadandaule kwambiri tikapatsidwa chilango?
15 Nthawi zina Yehova amatiumba potipatsa malangizo kapena uphungu. Koma nthawi zina angatiumbe potipatsa chilango ngati talakwitsa zinazake. Mwina tingachotsedwe pa udindo winawake mu mpingo. Mwachitsanzo, m’bale wina dzina lake Dennis, * amene anali mkulu, anadzudzulidwa chifukwa sanachite zinthu mwanzeru pa nkhani ya bizinezi yake. Kodi Dennis anamva bwanji pamene chilengezo chinaperekedwa kuti iye sakutumikiranso monga mkulu? Iye anati: “Ndinkadziona kuti ndine wachabechabe. Pa zaka 30 zapitazi, ndakhala ndi mwayi wotumikira Yehova m’njira zosiyanasiyana. Ndachitapo upainiya, kutumikira pa Beteli, kukhala mtumiki wothandiza ndipo kenako mkulu. Ndinalinso nditangokamba nkhani yanga yoyamba pa msonkhano wachigawo. Koma zonse zinatha mwadzidzidzi. Ndinachita manyazi kwambiri komanso ndinkaona kuti Yehova sangandigwiritsenso ntchito m’gulu lake.”
16 N’zoona kuti Dennis anayenera kupatsidwa chilango. Koma n’chiyani chinamuthandiza kuti asamadandaule kwambiri? Iye anafotokoza kuti: “Ndinatsimikiza mumtima mwanga kuti ndisasiye kuchita zinthu zimene zingalimbitse ubwenzi wanga ndi Yehova. Ndinalimbikitsidwanso ndi abale ndi alongo mu mpingo komanso powerenga mabuku athu. Nkhani yakuti ‘Ngati Munatumikirapo pa Udindo Wina Mumpingo, Kodi Mungatumikirenso?’ mu Nsanja ya Olonda ya August 15, 2009, inandithandiza kwambiri. Zinali ngati Mulungu walembera ineyo poyankha mapemphero anga. Malangizo amene anandifika kwambiri pa mtima anali akuti: ‘Nthawi imene mwasiya kutumikira mumpingo, muyenera kuchita khama kuti moyo wanu wauzimu ulimbe.’” Kodi chilango chimene Dennis anapatsidwa chamuthandiza bwanji? Patapita zaka zingapo, iye anati: “Yehova wandidalitsa ndi mwayi wotumikiranso monga mtumiki wothandiza.”
17. Kodi kuchotsa munthu mu mpingo kumathandiza bwanji munthuyo kuti akonzenso ubwenzi wake ndi Yehova? Perekani chitsanzo.
17 Kuchotsa munthu mu mpingo ndi njira ina imene Yehova amagwiritsa ntchito poumba anthu ake. Kumatetezera mpingo komanso kungathandize kuti munthu wolakwayo alape. (1 Akor. 5:6, 7, 11) Mwachitsanzo, Robert anachotsedwa n’kukhala kunja kwa gulu kwa zaka pafupifupi 16. Pa zaka zonsezi, makolo ake pamodzi ndi achibale ake anatsatira mokhulupirika malangizo a m’Mawu a Mulungu akuti asamayanjane ndi anthu ochimwa, ngakhale kuwapatsa moni. Zaka zingapo zapitazo, Robert anabwezeretsedwa mu mpingo ndipo akuchita bwino. Atafunsidwa kuti afotokoze chimene chinamuthandiza kuti abwerere kwa Yehova pambuyo pa zaka zambiri, ananena kuti zimene makolo ndi achibale ake ankachita zinamuthandiza kwambiri. Iye ananena kuti: “Iwo akanayesa kundilankhulitsa, ngakhale pang’ono pokha, ndikanasangalala kwambiri. Mwina zimenezi zikanachititsa kuti ndisakhale ndi mtima wofuna kubwerera m’gulu la Mulungu kuti ndizicheza ndi abale.”
18. Kodi Yehova akamatiumba, tiyenera kukhala dongo lotani?
18 Mwina ifeyo sitingafunikire kupatsidwa chilango. Koma kodi Yehova akamatiumba, timasonyeza kuti ndife dongo lotani? Kodi timatani tikapatsidwa malangizo kapena uphungu? Kodi timakhala ngati Davide kapena Sauli? Yehova Mulungu, yemwe amatiumba, ndi Atate wathu. Nthawi zonse tizikumbukira kuti “Yehova amadzudzula munthu amene amam’konda, monga momwe bambo amadzudzulira mwana amene amakondwera naye.” Choncho, ‘tisamakane malangizo a Yehova kapena kunyansidwa ndi kudzudzula kwake.’—Miy. 3:11, 12.
^ ndime 15 Mayina asinthidwa.