Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Zikumbutso za Yehova Zimakondweretsa Mtima Wanu?

Kodi Zikumbutso za Yehova Zimakondweretsa Mtima Wanu?

“Ndatenga zikumbutso zanu kukhala chuma changa mpaka kalekale.”—SAL. 119:111.

1. (a) Kodi anthu amachita chiyani akapatsidwa malangizo? (b) Kodi munthu wonyada amatani akapatsidwa malangizo?

ANTHU amachita zinthu zosiyanasiyana akapatsidwa malangizo. Ena amamvera malangizo mosavuta ngati akuchokera kwa munthu waudindo, koma samvera ngati akuchokera kwa munthu wamba. Anthu ena akapatsidwa malangizo amamva chisoni, amakhumudwa kapena kuchita manyazi. Pamene ena amalimbikitsidwa n’kupeza mphamvu kuti achite bwino. N’chifukwa chiyani anthu amachita zinthu zosiyanasiyana chonchi? Chifukwa chimodzi ndi kunyada. Munthu wodzikuza saganiza bwino ndipo safuna kutsatira malangizo amene angamuthandize.—Miy. 16:18.

2. N’chifukwa chiyani Akhristu enieni amayamikira akapatsidwa malangizo ochokera m’Mawu a Mulungu?

2 Koma Akhristu enieni amayamikira akapatsidwa malangizo, makamaka ngati akuchokera m’Mawu a Mulungu. Zikumbutso za Yehova zimatipatsa nzeru ndi kutithandiza kupewa misampha monga chiwerewere, kukonda kwambiri chuma, kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo komanso kuledzera. (Miy. 20:1; 2 Akor. 7:1; 1 Ates. 4:3-5; 1 Tim. 6:6-11) Tikamamvera zikumbutso za Yehova zimenezi, timasangalala “chifukwa chokhala ndi chimwemwe mumtima.”—Yes. 65:14.

3. Kodi tingachite bwino kukhala ndi maganizo ati amene wamasalimo anali nawo?

3 Kuti tikhalebe pa ubwenzi ndi Atate wathu wakumwamba, tiyenera kupitiriza kumvera malangizo a Yehova pa moyo wathu. Tingachite bwino kukhala ndi maganizo amene wamasalimo anali nawo. Iye analemba kuti: “Ndatenga zikumbutso zanu kukhala chuma changa mpaka kalekale, pakuti zimakondweretsa mtima wanga.”  (Sal. 119:111) Kodi nafenso malamulo a Yehova amatikondweretsa kapena nthawi zina timawaona ngati mtolo wolemetsa? Ngati nthawi zina timanyinyirika tikapatsidwa malangizo, tisataye mtima. Pali zinthu zina zimene zingatithandize kuti tizikhulupirira kwambiri nzeru zakuya za Mulungu. Tiyeni tione zinthu zitatu zimene zingatithandize.

PEMPHERO LINGATITHANDIZE KUTI TIZIKHULUPIRIRA KWAMBIRI YEHOVA

4. Ngakhale kuti Davide anakumana ndi mavuto ambiri pa moyo wake, kodi iye sanasiye kuchita chiyani?

4 Davide anakumana ndi mavuto ambiri pa moyo wake, koma sanasiye kukhulupirira Mlengi wake. Iye anati: “Ndapereka moyo wanga kwa inu Yehova. Inu Mulungu wanga, chikhulupiriro changa chili mwa inu.” (Sal. 25:1, 2) N’chiyani chinathandiza Davide kuti azikhulupirira kwambiri Atate wake wakumwamba?

5, 6. Kodi Mawu a Mulungu amasonyeza bwanji kuti Davide anali pa ubwenzi weniweni ndi Yehova?

5 Anthu ambiri amangopemphera kwa Mulungu akakhala m’mavuto. Kodi inuyo mungamve bwanji ngati mnzanu amangolankhula nanu pokhapokha akafuna kukupemphani ndalama kapena kuti mum’thandize zinazake? Mwinatu mukhoza kuyamba kumukayikira. Koma Davide sankangopemphera akakumana ndi mavuto. Iye anali pa ubwenzi ndi Yehova chifukwa chakuti ankamukhulupirira komanso kumukonda. Ndipo ankachita zimenezi pa mavuto ndiponso pa mtendere.—Sal. 40:8.

6 Potamanda ndi kuthokoza Yehova, Davide ananena kuti: “Inu Yehova Ambuye wathu, dzina lanu ndi lalikulu padziko lonse lapansi, inuyo ulemerero wanu ukusimbidwa kumwambamwamba!” (Sal. 8:1) Mungaone kuti Davide anali pa ubwenzi weniweni ndi Atate wake wakumwamba. Iye anatamanda Yehova “tsiku lonse” chifukwa anaona ulemerero wake.—Sal. 35:28.

7. Kodi kupemphera kwa Mulungu kumatithandiza bwanji?

7 Ifenso tiyenera kumalankhula ndi Yehova nthawi zonse kuti tizimukhulupirira. Baibulo limanena kuti: “Yandikirani Mulungu, ndipo iyenso adzakuyandikirani.” (Yak. 4:8) Kupemphera kwa Mulungu, kungatithandizenso kwambiri kuti tizilandira mzimu woyera.—Werengani 1 Yohane 3:22.

8. N’chifukwa chiyani sitiyenera kugwiritsa ntchito mawu amodzimodzi popemphera?

8 Kodi mukamapemphera, mumagwiritsa ntchito mawu amodzimodzi nthawi zonse kapena kunena mawu mobwerezabwereza? Ngati ndi choncho, muziganizira kaye zoti munene musanayambe kupemphera. Kodi mnzathu kapena wachibale wathu angasangalale ngati timagwiritsa ntchito mawu amodzimodzi polankhula naye? Mwina angasiye kutimvetsera. N’zoona kuti Yehova sangasiye kumvetsera pemphero la mtumiki wake wokhulupirika. Komabe, tingachite bwino kupewa kunena mawu amodzimodzi tikamalankhula naye.

9, 10. (a) Kodi ndi zinthu ziti zimene tinganene m’mapemphero athu? (b) Kodi tingatani kuti tizipemphera kuchokera mumtima?

9 Ngati tikufuna kuyandikira Mulungu, n’zodziwikiratu kuti mapemphero athu ayenera kukhala ochokera pansi pa mtima. Tikamauza Yehova zonse zimene zili mumtima mwathu, ubwenzi wathu umalimba ndiponso timam’khulupirira kwambiri. Koma kodi tizimuuza zotani tikamapemphera? Mawu a Mulungu akuyankha kuti: “Pa chilichonse, mwa pemphero ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu.” (Afil. 4:6) Apa mfundo ndi yakuti Yehova tingamuuze chilichonse chimene chikukhudza ubwenzi wathu ndi iye kapena utumiki wathu.

10 Kuwerenga m’Baibulo mapemphero a amuna ndi akazi okhulupirika kungatithandize pa nkhani imeneyi. (1 Sam. 1:10, 11; Mac. 4:24-31) M’buku la Masalimo muli mapemphero  ochokera pansi pa mtima komanso nyimbo zoimbira Yehova. Mapemphero ndi nyimbozi zimasonyeza mmene anthu ankamvera mumtima mwawo. Nthawi zina ankapanikizika koma nthawi zina ankasangalala kwambiri. Kuona bwinobwino mawu amene ankagwiritsa ntchito kungatithandize kuti nafenso tizipemphera kuchokera mumtima.

MUZIGANIZIRA ZIKUMBUTSO ZA YEHOVA

11. N’chifukwa chiyani tiyenera kuganizira mozama malangizo a Mulungu?

11 Davide anati: “Zikumbutso za Yehova ndi zodalirika, zimapatsa nzeru munthu wosadziwa zinthu.” (Sal. 19:7) Mwina ifenso sitidziwa zambiri koma tikhoza kukhala anzeru ngati timvera malamulo a Mulungu. Koma kuti malangizo ena a m’Baibulo atithandize, timafunika kuwaganizira mozama. Mwachitsanzo, m’Baibulo tikhoza kupeza malangizo okhudza kukhala okhulupirika kusukulu kapena kuntchito, kupewa magazi, kusalowerera ndale ndiponso kavalidwe kathu. Kudziwa maganizo a Yehova pa nkhani ngati zimenezi kungatithandize kuti mavuto ena tiziwaonera patali n’kudziwa zochita. Kuganizira zinthu zimenezi pasadakhale n’kukonzekera kungatithandize kupewa mavuto ambiri.—Miy. 15:28.

12. Kodi tiyenera kuganizira mafunso ati kuti tizimvera zikumbutso za Mulungu?

12 Kodi zimene tikuchita poyembekezera malonjezo a Yehova zimasonyeza kuti tili maso? Mwachitsanzo, kodi timakhulupiriradi kuti Babulo Wamkulu awonongedwa posachedwapa? Mwina titangoyamba kuphunzira Baibulo tinkakhulupirira kwambiri za moyo wosatha m’paradaiso padziko lapansi. Kodi ndi mmene zililinso panopa? Kodi timachitabe khama pa ntchito yolalikira kapena tayamba kutanganidwa ndi zinthu zina? Kodi timakhulupirirabe kuti akufa adzauka? Nanga maganizo athu ndi otani pa nkhani yoyeretsa dzina la Yehova ndiponso kusonyeza kuti iye ndi woyenera kulamulira? Kodi timaonabe kuti zimenezi ndi nkhani zofunika kwambiri? Kuganizira mafunso ngati amenewa kungatithandize kuti nafenso tikhale ngati wamasalimo. Pajatu iye ananena kuti: “Ndatenga zikumbutso zanu kukhala chuma changa mpaka kalekale.”—Sal. 119:111.

13. N’chifukwa chiyani Akhristu oyambirira sankamvetsa nkhani zina? Perekani chitsanzo.

13 Nkhani zina za m’Baibulo sitingazimvetse panopa chifukwa chakuti nthawi yoti Yehova atithandize kuzimvetsa sinakwane. Yesu ankauza ophunzira ake mobwerezabwereza kuti iye ayenera kuzunzidwa komanso kuphedwa. (Werengani Mateyu 12:40; 16:21.) Koma atumwiwo sankamvetsa zimene ankatanthauza. Iwo anamvetsa nkhaniyi pambuyo poti Yesu waphedwa n’kuukitsidwa. Pa nthawi imeneyi, Yesu anaonekera kwa ophunzira ake ndipo “anatseguliratu maganizo awo kuti amvetse tanthauzo la Malemba.” (Luka 24:44-46; Mac. 1:3) Otsatira a Khristu sankamvetsanso kuti Ufumu wa Mulungu udzakhazikitsidwa kumwamba. Iwo anazindikira zimenezi pambuyo poti Mulungu wawapatsa mzimu woyera pa Pentekosite mu 33 C.E.—Mac. 1:6-8.

14. Kodi kale abale ambiri anachita chiyani ngakhale kuti sankamvetsa mfundo zina zokhudza masiku otsiriza?

14 N’chimodzimodzinso m’nthawi yathu ino. Kumayambiriro kwa zaka za m’ma 1900, Akhristu oona ankayembekezera zinthu zingapo zokhudza “masiku otsiriza” zomwe sizinachitike. (2 Tim. 3:1) Mwachitsanzo, m’chaka cha 1914 ena ankaganiza kuti nthawi yoti atengedwe kupita kumwamba inali itangotsala pang’ono kukwana. Zimene ankayembekezerazo zitalephereka, anayamba kufufuza Malemba mwakhama. Izi zinawathandiza kuona kuti anali ndi ntchito yaikulu yolalikira imene ankafunika kugwira. (Maliko 13:10) Choncho mu 1922, M’bale J.  F. Rutherford, amene ankatsogolera pa ntchito yolalikira, anauza  anthu amene anafika pa msonkhano wa mayiko mumzinda wa Cedar Point, ku Ohio m’dziko la United States, kuti: “Onani, Mfumu yayamba kale kulamulira ndipo inu ndinu atumiki ake olengeza za ufumuwo. Choncho lengezani, lengezani, lengezani za Mfumu ndi ufumu wake.” Kungoyambira nthawi imeneyo, atumiki a Yehova amadziwika ndi ntchito yolalikira “uthenga wabwino wa ufumu.”—Mat. 4:23; 24:14.

15. Kodi kuganizira zimene Mulungu wachitira anthu ake m’mbuyomu kungatithandize bwanji?

15 Tikamaganizira mmene Yehova wakhala akuchitira zinthu ndi anthu ake, sitikayikira ngakhale pang’ono kuti adzakwaniritsa zolinga zake m’tsogolo. Komanso zikumbutso za Mulungu zimatithandiza kuti tizikumbukira nthawi zonse maulosi amene tikuyembekezera kuti adzakwaniritsidwa m’tsogolomu. Zimenezi zidzatithandiza kuti tizikhulupirira kuti zomwe watilonjeza zidzachitikadi.

KUTUMIKIRA MULUNGU MWAKHAMA KUNGATITHANDIZE KUTI TIZIMUKHULUPIRIRA KWAMBIRI

16. Kodi chimachitika n’chiyani tikamatumikira Mulungu mwakhama?

16 Yehova ndi Mulungu wogwira ntchito mwakhama. Wamasalimo anafunsa kuti: “Ndani ali ndi mphamvu ngati inu Ya?” Kenako ananena kuti: “Dzanja lanu ndi lamphamvu, dzanja lanu lamanja ndi lokwezeka.” (Sal. 89:8, 13) Chifukwa cha zimenezi, iye amayamikira tikamachita khama pa utumiki wathu ndipo amatidalitsa. Iye amasangalala akaona atumiki ake, kaya akhale aamuna kapena aakazi, achinyamata kapena achikulire, akugwira ntchito mwakhama osati akudya “chakudya cha ulesi.” (Miy. 31:27) Choncho tingachite bwino kutsanzira Mlengi wathu pochita utumiki mwakhama. Tikamatumikira Mulungu ndi mtima wonse timasangalala ndipo Yehova amatidalitsa.—Werengani Salimo 62:12.

17, 18. Perekani umboni wosonyeza kuti kutsatira malangizo mokhulupirika kumathandiza kuti tizikhulupirira kwambiri Yehova.

 17 Kodi kutsatira malangizo mokhulupirika kumatithandiza bwanji kuti tizikhulupirira Yehova? Taganizirani zimene zinachitika pamene Aisiraeli ankalowa m’Dziko Lolonjezedwa. Yehova anauza ansembe amene ananyamula likasa la pangano kuti akangofika mumtsinje wa Yorodano alowe m’madzi. Koma atafika, anapeza kuti mtsinjewo wasefukira chifukwa kunagwa mvula yambiri. Kodi Aisiraeliwo anatani? Kodi anakhala m’mphepete n’kumadikira kwa masiku ambiri kuti mtsinjewo uphwe? Ayi. Iwo anakhulupirira Yehova ndi mtima wonse n’kutsatira malangizo ake. Ndiyeno chinachitika n’chiyani? Nkhaniyo imati: “Onyamula Likasawo atangofika kumtsinje wa Yorodano, n’kuponda madzi a m’mphepete mwa mtsinjewo . . . , madzi a mtsinjewo anaduka . . . Ansembe onyamula likasa la pangano la Yehova anangoima chilili panthaka youma pakati pa mtsinje wa Yorodano . . . kufikira mtundu wonse unatha kuwoloka.” (Yos. 3:12-17) Kodi mukuganiza kuti Aisiraeliwo anamva bwanji ataona kuti madzi a mumtsinjewo ayamba kuima? Chikhulupiriro chawo chiyenera kuti chinalimba kwambiri. Izi zinatheka chifukwa chakuti anatsatira malangizo a Yehova.

Kodi mumakhulupirira Mulungu ngati mmene anthu a Yehova anachitira m’nthawi ya Yoswa? (Onani ndime 17 ndi 18)

18 N’zoona kuti masiku ano Yehova sachita zinthu ngati zimenezi, komabe amadalitsa anthu amene amatsatira malangizo ake mokhulupirika. Mzimu wa Yehova umathandiza anthu ake kuti agwire ntchito yolalikira uthenga wa Ufumu padziko lonse. Khristu, yemwe ndi mboni yokhulupirika, anauza ophunzira ake kuti adzakhala nawo pa ntchito yofunikayi. Iye anati: “Choncho pitani mukaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzira anga . . . Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse mpaka m’nyengo ya mapeto a nthawi ino.” (Mat. 28:19, 20) Abale ndi alongo ambiri, omwe ndi amanyazi komanso amantha, aona kuti mzimu woyera wa Mulungu wawathandiza kukhala olimba mtima. Iwo amalankhula bwinobwino ndi anthu achilendo amene amakumana nawo mu utumiki.—Werengani Salimo 119:46; 2 Akorinto 4:7.

19. Ngakhale kuti sitingachite zinthu zambiri, kodi sitiyenera kukayikira chiyani?

19 Abale ndi alongo ena sangachite zambiri potumikira Mulungu chifukwa cha matenda kapena ukalamba. Iwo sayenera kukayikira kuti ‘Tate wachifundo chachikulu, yemwenso ndi Mulungu amene amatitonthoza m’njira iliyonse,’ amamvetsa mavuto amene Mkhristu aliyense akukumana nawo. (2 Akor. 1:3) Iye amayamikira zonse zimene timachita pomutumikira. N’zoona kuti tiyenera kuchita zonse zimene tingathe potumikira Yehova. Komabe tizikumbukira kuti kukhulupirira dipo la Khristu n’kumene kungatipulumutse.—Aheb. 10:39.

20, 21. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timakhulupirira Yehova?

20 Tiyenera kuchita zonse zimene tingathe kuti tigwiritse ntchito nthawi yathu, mphamvu zathu ndiponso chuma chathu potumikira Mulungu. Tiyeni tizigwira “ntchito ya mlaliki” ndi mtima wathu wonse. (2 Tim. 4:5) Tikamagwira ntchitoyi timasangalala kwambiri chifukwa chakuti timathandiza anthu ‘kudziwa choonadi molondola.’ (1 Tim. 2:4) Timadalitsidwa kwambiri tikamalemekeza ndiponso kutamanda Yehova. (Miy. 10:22) Zimenezi zimathandiza kuti tikhale pa ubwenzi wolimba ndi Mlengi wathu komanso kuti tizimukhulupirira ndi mtima wathu wonse.—Aroma 8:35-39.

21 Taona kuti pamafunika kuchita khama kuti tizikhulupirira malangizo a Yehova. Choncho tiyeni tizidalira Yehova n’kumapemphera kwa iye. Tiziganizira zimene wachita m’mbuyomu komanso zimene adzachite m’tsogolo pokwaniritsa cholinga chake. Tiyeninso tipitirize kumutumikira mokhulupirika. Dziwani kuti zikumbutso za Yehova zidzakhalapo mpaka muyaya. Inunso mukhoza kukhala ndi moyo mpaka muyaya.