Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Tingathandize Bwanji Anthu Ena?

Kodi Tingathandize Bwanji Anthu Ena?

M’BALE wina dzina lake François amene ndi mkulu kudziko lina anati: “Anthu amene anakana zotsatira za chisankho anayambitsa chipolowe ndipo abale ndi alongo ambirimbiri anathawa m’nyumba zawo. Chakudya ndi mankhwala zinayamba kusowa ndipo zimene zinkapezeka zinali zodula kwambiri. Mabanki anatsekedwa ndipo makina otapira ndalama anasiya kugwira ntchito.”

Mwamsanga abale ochokera ku ofesi ya nthambi anayamba kupereka ndalama ndiponso zinthu zina zofunika kwa abale ndi alongo amene anathawira ku Nyumba za Ufumu. Magulu amene ankalimbanawo anatseka misewu. Koma ankalola magalimoto ochokera kunthambi kudutsa chifukwa ankadziwa kuti a Mboni salowerera ndale.

François anati: “Pamene tinkapita ku Nyumba ya Ufumu ina, anthu anayamba kuwombera galimoto yathu. Zipolopolo zinkadutsa pafupi kwambiri koma mwamwayi sanatiwombere. Kenako tinaona msilikali wonyamula chida akutithamangira. Nthawi yomweyo tinatembenuza galimoto n’kubwerera kunthambi. Tinathokoza Yehova kuti tinapulumuka. Tsiku lotsatira abale ndi alongo 130 amene anali m’Nyumba ya Ufumu imeneyo anathawa n’kukabisala kwina. Ena anabwera ku ofesi ya nthambi ndipo tinawathandiza komanso kuwalimbikitsa mpaka pamene mavutowo anatha.”

François ananenanso kuti: “Abale ambiri anatumiza makalata oyamikira kwambiri zimene abale awo anachita powathandiza. Kuona abale ochokera kwina akuwathandiza kunawalimbikitsa kukhulupirira kwambiri Yehova.”

Pakagwa mavuto, sitimangouza abale ndi alongo ovutika kuti “mupeze zovala ndi zakudya za tsiku lililonse.” (Yak. 2:15, 16) Koma timayesetsa kuwathandiza kupeza zinthu ngati zimenezi. Umu ndi mmene zinalili m’nthawi ya atumwi. Ophunzira atamva kuti kudzakhala njala, “anatsimikiza mtima kutumiza thandizo lililonse limene akanatha kwa abale okhala ku Yudeya.”—Mac. 11:28-30.

Atumiki a Yehovafe timafunitsitsa kuthandiza anthu ovutika. Koma anthu amakhalanso ndi zosowa zauzimu. (Mat. 5:3) Pofuna kuthandiza anthu kudziwa ndiponso kupeza zosowa zawo zauzimu, Yesu analamula otsatira ake kuti aziphunzitsa anthu. (Mat. 28:19, 20) Tonse timayesetsa kugwiritsa ntchito nthawi yathu, mphamvu zathu ndiponso chuma chathu kuti tigwire ntchito imeneyi. Gulu lathu limagwiritsa ntchito ndalama zina pothandiza anthu ovutika. Koma zopereka zambiri zimagwiritsidwa ntchito pothandiza kuti tilalikire uthenga wabwino. Pochita zimenezi timasonyeza kuti timakonda Mulungu ndiponso anzathu.—Mat. 22:37-39.

Anthu amene amapereka ndalama zothandiza pa ntchito yapadziko lonse ya Mboni za Yehova ayenera kudziwa kuti ndalamazo zikugwiritsidwa ntchito moyenera. Kodi inuyo mungathandize abale anu amene akuvutika? Kodi mumafunitsitsa kuthandiza pa ntchito yolalikira? Ngati zili choncho, ‘musalephere kuchitira zabwino anthu amene akufunikira zabwinozo, pamene dzanja lanu lingathe kuchita zimenezo.’—Miy. 3:27.