NSANJA YA OLONDA (YOPHUNZIRA) March 2014

Magazini ino ikufotokoza zimene zingatithandize kukhalabe ndi mtima wodzipereka komanso kuti tisamadzione ngati achabechabe. Mulinso nkhani yomwe ikufotokoza zimene tingachite posamalira Akhristu anzathu komanso achibale okalamba.

Kodi Tingathandize Bwanji Achibale Omwe Si Mboni?

Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Yesu anachitira achibale ake? Kodi tingalalikire bwanji kwa achibale athu amene ali m’chipembedzo china kapena amene sapembedza n’komwe?

Kodi Tingatani Kuti Tikhalebe ndi Mtima Wodzipereka?

Tili ndi mdani amene angatilepheretse mwaukathyali kusonyeza mtima wodzipereka. Nkhaniyi ikunena za mdani ameneyu komanso mmene tingamugonjetsere pogwiritsa ntchito Baibulo.

Kodi Tingatani Kuti Tikhalebe Osangalala?

N’chifukwa chiyani anthu ambiri sasangalala? Nkhaniyi ikusonyeza kuti Baibulo lingatithandize kuti tisamadzione ngati achabechabe.

Kulambira kwa Pabanja Kuzikhala Kosangalatsa

Werengani nkhaniyi kuti mudziwe mmene abale ena amachitira Kulambira kwa Pabanja m’mayiko osiyanasiyana kuti nanunso muone zimene mungamachite.

Muzilemekeza Anthu Achikulire

Werengani nkhaniyi kuti muone mmene Mulungu amaonera anthu achikulire. Kodi ana amene ali ndi makolo okalamba ali ndi udindo wotani? Kodi mpingo ungasonyeze bwanji kuti umalemekeza achikulire?

Kodi Achikulire Tingawasamalire Bwanji?

Makolo achikulire ayenera kukambirana ndi ana awo zimene angachite pokonzekera “masiku oipa.” Kodi angathane bwanji ndi mavuto obwera chifukwa cha ukalamba?

Mawu Anu “Asakhale Inde Kenako Ayi”

Akhristu ayenera kuchita zimene alonjeza osati kunena kuti “inde kenako ayi.” Koma bwanji ngati pachitika zinthu zina ndipo tifunika kusintha pulogalamu? Tiyenera kutsanzira Paulo pa nkhani imeneyi.