Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi ‘Tingayankhe Bwanji Wina Aliyense’?

Kodi ‘Tingayankhe Bwanji Wina Aliyense’?

“Nthawi zonse mawu anu azikhala achisomo, . . . kuti mudziwe mmene mungayankhire wina aliyense.”—AKOL. 4:6.

1, 2. (a) Perekani chitsanzo chosonyeza kuti kufunsa mafunso abwino kumathandiza. (Onani chithunzi pamwambapa.) (b) N’chifukwa chiyani sitiyenera kuopa kukambirana ndi anthu nkhani zina zovuta?

ZAKA zingapo zapitazo, mlongo wina ankakambirana mfundo za m’Baibulo ndi mwamuna wake yemwe poyamba anali membala wa tchalitchi chinachake. Pokambiranapo, mwamunayo ananena kuti amakhulupirira Utatu. Mlongoyu atazindikira kuti mwina iye sakudziwa bwinobwino tanthauzo la Utatu, anamufunsa kuti: “Kodi ndiye kuti mumakhulupirira zoti Mulungu ndi Mulungu, Yesu ndi Mulungu, mzimu woyera ndi Mulungu koma Mulunguyo ndi mmodzi osati itatu?” Mwamunayo atamva anadabwa n’kukana kuti: “Ayi! Ine sindikhulupirira zimenezo.” Izi zinachititsa kuti ayambe kukambirana bwinobwino nkhani zokhudza Mulungu.

2 Zimene zinachitikazi zikusonyeza kuti kufunsa mwaulemu mafunso abwino kumathandiza kuti tikambirane bwino ndi anthu. Zikusonyezanso kuti sitiyenera kuopa kukambirana ndi anthu amene amakhulupirira zinthu monga Utatu, zoti oipa akawotchedwa komanso zoti kulibe Mulungu. Ngati tidalira Yehova komanso zimene amatiphunzitsa, tikhoza kupereka mayankho ogwira  mtima kwa anthu. (Akol. 4:6) Tiyeni tsopano tikambirane zimene ofalitsa aluso amachita pokambirana ndi anthu nkhani ngati zimenezi. Tikambirana mfundo zitatu izi: (1) Tizifunsa mafunso kuti timve maganizo a anthu. (2) Tizikambirana nawo zimene Malemba amanena. (3) Tizigwiritsa ntchito mafanizo kuti amvetse.

MUZIWAFUNSA MAFUNSO KUTI MUMVE MAGANIZO AWO

3, 4. N’chifukwa chiyani kufunsa mafunso kuti tidziwe zimene munthu amakhulupirira ndi kofunika? Perekani chitsanzo.

3 Kufunsa mafunso kumatithandiza kuti tidziwe zimene munthu amakhulupirira. N’chifukwa chiyani zimenezi zili zofunika? Lemba la Miyambo 18:13 limati: “Munthu aliyense woyankhira nkhani asanaimvetsetse n’ngopusa, ndipo amachita manyazi.” Choncho tisanayambe kukambirana zimene Baibulo limanena pa nkhani inayake, tingachite bwino kudziwa kaye zimene munthuyo amakhulupirira. Ngati sitidziwa zimene amakhulupirira tikhoza kuwononga nthawi pokambirana naye zinthu zimene sakhulupirira n’komwe.—1 Akor. 9:26.

4 Mwachitsanzo, tiyerekeze kuti tikukambirana ndi munthu zimene zimachitikira anthu oipa. Si onse amene amakhulupirira kuti oipa amapita kumalo enaake kumene kuli moto. Choncho, tingachite bwino kunena kuti: “Anthu amakhulupirira zinthu zosiyanasiyana pa nkhani ya zimene zimachitikira anthu oipa. Kodi inuyo mumakhulupirira zotani?” Ndiyeno munthuyo akafotokoza maganizo ake, tikhoza kumuthandiza bwinobwino kuti adziwe zimene Baibulo limanena pa nkhaniyi.

5. Kodi mafunso angatithandize bwanji kudziwa chifukwa chake munthu amakhulupirira zinazake?

5 Kufunsa mafunso mwanzeru kungatithandizenso kudziwa chifukwa chake munthu amakhulupirira zinazake. Mwachitsanzo, kodi tingakambirane bwanji ndi munthu amene wanena kuti sakhulupirira zoti kuli Mulungu? Mwina tingafulumire kuganiza kuti munthuyo akutengera maganizo a anthu, monga akuti zinthu zinangokhalapo zokha. (Sal. 10:4) Komabe anthu ena asiya kukhulupirira Mulungu chifukwa cha mavuto amene awachitikira iwowo kapena anthu ena. Mwina amaona kuti pakanakhala Mulungu wachikondi, si bwenzi zonsezi zikuchitika. Choncho tingachite bwino kufunsa munthu amene amakayikira zoti kuli Mulungu kuti: “Kodi munayamba liti kukhulupirira zimenezi?” Kenako tingamufunse kuti: “N’chiyani chinachititsa kuti muyambe kuzikhulupirira?” Tikamva zimene munthuyo anganene tikhoza kudziwa mmene tingamuthandizire.—Werengani Miyambo 20:5.

6. Kodi tiyenera kuchita chiyani tikafunsa funso?

6 Tikafunsa funso, tiyenera kumvetsera bwino zimene munthuyo akunena komanso kusonyeza kuti tamvetsa maganizo ake. Mwachitsanzo, munthu angafotokoze kuti vuto lalikulu limene wakumana nalo lamuchititsa kuyamba kukayikira zoti kuli Mulungu. Tisanayambe kupereka umboni woti kuli Mulungu, tingachite bwino kusonyeza kuti tikumumvera chisoni chifukwa cha vuto lakelo. Tiyeneranso kumuuza kuti sakulakwa pofuna kudziwa chifukwa chake anthufe timavutika. (Hab. 1:2, 3) Tikamakambirana naye moleza mtima komanso mwachikondi iye angafune kuphunzira zambiri. *

MUZIKAMBIRANA ZIMENE MALEMBA AMANENA

Kodi kuti tiphunzitse mogwira mtima, zimadalira chiyani? (Onani ndime 7)

7. Kodi kuti tiwafike anthu pa mtima zimadalira chiyani?

7 Tsopano tiyeni tione njira zimene tingatsatire pokambirana ndi anthu zimene Malemba amanena. Akhristufe tikakhala mu utumiki, timagwiritsa ntchito kwambiri Baibulo. Limatithandiza kuti tikhale ‘oyenerera bwino ndi okonzeka mokwanira kuchita ntchito iliyonse  yabwino.’ (2 Tim. 3:16, 17) Koma kuti tiwafike anthu pa mtima, sizidalira kuchuluka kwa malemba amene timawerenga, koma mmene timafotokozera malembawo pokambirana. (Werengani Machitidwe 17:2, 3.) Tiyeni tione zitsanzo zitatu zotsimikizira mfundoyi.

8, 9. (a) Kodi munthu amene amakhulupirira zoti Yesu ndi Mulungu mungakambirane naye bwanji? (b) Fotokozani njira zina zokambirana ndi anthu oterewa zimene inuyo mwapeza kuti n’zothandiza.

8 Chitsanzo 1: Tiyerekeze kuti takumana ndi munthu amene amakhulupirira kuti Yesu ndi Mulungu. Kodi tingagwiritse ntchito malemba ati pokambirana naye? Mwina tingawerenge naye Yohane 6:38 pamene Yesu ananena kuti: “Ndinatsika kuchokera kumwamba kudzachita chifuniro cha iye amene anandituma, osati chifuniro changa.” Kenako tingamufunse kuti: “Ndiyeno ngati Yesu ndi Mulungu, kodi amene anamutumayo ndi ndani? Kodi sizikutanthauza kuti wotumayo ndi wamkulu kuposa Yesu? Pajatu wamkulu ndi amene amatuma wamng’ono, si choncho?”

9 Mwina tingawerengenso Afilipi 2:9 n’kuona zimene Paulo ananena. Ponena zimene zinachitika Yesu ataukitsidwa, iye anati: “Mulungu anamukweza [Yesu] n’kumuika pamalo apamwamba. Ndipo anamukomera mtima n’kumupatsa dzina loposa lina lililonse.” Ndiyeno pokambirana ndi munthuyo tikhoza kumufunsa kuti: “Ngati Yesu ndi Mulungu, kodi udindo umene anapatsidwa ataukitsidwa unali wapamwamba kuposa wa ndani? Kodi pali udindo winanso wapamwamba kuposa wa Mulungu?” Ngati munthuyo amalemekeza Mawu a Mulungu komanso ali ndi maganizo abwino akhoza kuona kuti m’pofunika kuiganizira bwino nkhaniyi.—Mac. 17:11.

10. (a) Kodi munthu amene amakhulupirira kuti anthu oipa adzawotchedwa mungakambirane naye bwanji? (b) Fotokozani njira zina zokambirana ndi anthu oterewa zimene inuyo mwapeza kuti n’zothandiza.

10 Chitsanzo 2: Tiyerekeze kuti takumana ndi munthu amene amakhulupirira kuti anthu oipa adzawotchedwa kwamuyaya. N’kutheka kuti amakhulupirira zimenezi chifukwa chofuna kuti oipa alangidwe. Kodi munthu wotereyu tingakambirane naye bwanji? Choyamba, tiyenera kumutsimikizira kuti anthu oipa adzalangidwadi. (2 Ates. 1:9) Kenako tingamupemphe kuti awerenge lemba la Genesis 2:16, 17, limene limasonyeza kuti chilango cha uchimo ndi imfa. Tingamufotokozerenso kuti tchimo la Adamu linachititsa kuti tonsefe tibadwe ochimwa. (Aroma 5:12) Koma tikhoza kumuuzanso kuti pa lembali Mulungu sananene chilichonse chokhudza kulangidwa kumoto. Kenako tingamufunse kuti: “Kodi za motozi zikanakhala zoona, chikanakhala chilungamo kubisira Adamu ndi Hava zimenezi?” Ndiyeno tingawerenge  lemba la Genesis 3:19 limene limafotokoza chilango chimene Adamu ndi Hava analandira atachimwa koma limene silitchulanso za moto. Pa lembali, Adamu anauzidwa kuti adzabwerera kufumbi. Kenako tingafunse kuti: “Kodi chikanakhala chilungamo kuuza Adamu kuti adzabwerera kufumbi pamene kwenikweni adzapita kumoto?” Ngati munthuyo ndi wofunitsitsa kudziwa choonadi, funso ngati limeneli likhoza kumuchititsa kuganizira bwino nkhaniyi.

11. (a) Kodi munthu amene amakhulupirira kuti anthu onse abwino amapita kumwamba mungakambirane naye bwanji? (b) Fotokozani njira zina zokambirana ndi anthu oterewa zimene inuyo mwapeza kuti n’zothandiza.

11 Chitsanzo 3: Tiyerekeze kuti takumana ndi munthu amene amakhulupirira kuti anthu onse abwino amapita kumwamba. Chikhulupiriro chimenechi chimachititsa kuti anthu azimva uthenga wa m’Baibulo m’njira ina. Tinene kuti mukukambirana ndi munthu wotereyu lemba la Chivumbulutso 21:4. (Werengani.) Munthuyo akhoza kuganiza kuti zinthu zabwino zimene zikufotokozedwa pa lembali ndi za kumwamba. Kodi ndiye tingakambirane naye bwanji? Mwina m’malo momutsegulira lemba lina, tingachite bwino kukambirana naye mfundo za mu lemba lomweli. Mwachitsanzo, lembali likuti: “Imfa sidzakhalaponso.” Ndiye tikhoza kukambirana ndi munthuyo kuti: “Kodi munthu akati chakutichakuti sichidzakhalaponso amanena za chinthu chimene chinalipo kapena panalibe?” Mosakayikira ayankha kuti chimene chinalipo. Ndiyeno munganene kuti: “Mukudziwa zoti imfa imachitika padziko lapansi pokha osati kumwamba eti? Choncho lemba la Chivumbulutso 21:4 liyenera kuti limanena zimene zidzachitike padziko lapansi osati kumwamba.”—Sal. 37:29.

MUZIGWIRITSA NTCHITO MAFANIZO KUTI AMVETSE

12. N’chifukwa chiyani Yesu ankagwiritsa ntchito mafanizo?

12 Pamene Yesu ankalalikira, ankagwiritsa ntchito mafunso komanso mafanizo. (Werengani Mateyu 13:34, 35.) Mafanizo ake ankathandiza kuti anthu asonyeze zimene zili mumtima mwawo. (Mat. 13:10-15) Ankachititsanso kuti uthenga wake uzikhala wogwira mtima komanso wosaiwalika. Kodi tingatani kuti nafenso tizigwiritsa ntchito mafanizo pophunzitsa?

13. Kodi tingagwiritse ntchito chitsanzo chiti posonyeza kuti Mulungu ndi wamkulu kuposa Yesu?

13 Zimakhala bwino kugwiritsa ntchito mafanizo osavuta kumva. Mwachitsanzo, pofotokozera munthu kuti Mulungu ndi wamkulu kuposa Yesu tinganene kuti: “Mulungu ankatchula Yesu kuti Mwana wake ndipo Yesu ankanena kuti Mulungu ndi Atate wake.” (Luka 3:21, 22; Yoh. 14:28) Ndiyeno tingamufunse munthuyo kuti: “Kodi inuyo mutati mufotokoze za anthu am’banja limodzi ofanana msinkhu mungagwiritse ntchito mawu ati?” Mwina angayankhe kuti: “Ndinganene kuti anthuwo ndi mapasa.” Kenako munganene kuti: “Choncho ngati Yesu, yemwe ndi Mphunzitsi Waluso, akanafuna kusonyeza kuti iye ndi wofanana ndi Mulungu, kodi akanamutchula kuti Atate?” Munthuyo akhoza kuyankha kuti: “Ayi akananena za mapasazo.” Ndiyeno tinganene kuti: “Choncho ponena kuti Mulungu ndi Atate wake, anasonyeza kuti Mulungu ndi wamkulu kuposa iye ndipo udindo wake ndi wapamwamba kuposa wake.”

14. Perekani fanizo losonyeza kuti Mulungu sangagwiritse ntchito Mdyerekezi kuti alange anthu oipa kumoto.

14 Tiyeni tione chitsanzo china. Anthu ena amakhulupirira kuti Satana ndi amene amayang’anira malo owotchera anthu oipa. Tingagwiritse ntchito fanizo lothandiza munthu kuona kuti Mulungu sangatume Mdyerekezi kuti awotche anthu. Tikhoza kunena kuti: “Tiyerekeze kuti muli ndi mwana wovuta amene akuchita zinthu zambiri zoipa. Kodi mungachite chiyani?” Munthuyo akhoza kunena  kuti: “Ndingayesetse kumuthandiza kuti asinthe.” (Miy. 22:15) Tsopano tingamufunse zimene angachite ngati mwanayo akungopitiriza kuchita zoipazo. Makolo ambiri angayankhe kuti akhoza kumulanga. Kenako tingafunse kuti: “Kodi mungatani mutamva kuti munthu wina woipa kwambiri ndi amene akusokoneza mwana wanuyo?” Akhoza kuyankha kuti: “Munthuyo ndingadane naye kwambiri.” Ndiyeno tingathandize munthuyo kumvetsa mfundo yathu pofunsa kuti: “Kodi mungapereke mwana wanuyo kwa munthu woipayo kuti akulangireni?” N’zosachita kufunsa kuti ayankha kuti ayi. Pomaliza munganene kuti: “Choncho n’zoonekeratu kuti Mulungu sangagwiritse ntchito Satana kuti alange anthu omwe anawasokoneza ndi iyeyo.”

MUZIONA ZINTHU MOYENERA

15, 16. (a) N’chifukwa chiyani sitiyenera kuyembekeza kuti aliyense adzamvetsera uthenga wa Ufumu? (b) Kodi n’zotheka kuphunzitsa mogwira mtima ngakhale kuti si ife aluso kwambiri? Fotokozani. (Onaninso bokosi lakuti, “ Nkhani Zotithandiza Kuyankha Aliyense.”)

15 Timadziwa kuti anthu ena amene timawalalikira sangafune kumvetsera uthenga wa Ufumu. (Mat. 10:11-14) Zimenezi zikhoza kuchitika ngakhale titakambirana nawo mwaluso komanso kugwiritsa ntchito mafunso ndi mafanizo abwino kwambiri. Tisaiwale kuti ndi anthu ochepa okha amene anatsatira Yesu ngakhale kuti iye anali Mphunzitsi waluso kwambiri.—Yoh. 6:66; 7:45-48.

16 Tiyenera kudziwanso kuti ngakhale kuti si ife aluso kwambiri tikhoza kumaphunzitsa mogwira mtima. (Werengani Machitidwe 4:13.) Paja Mawu a Mulungu amatitsimikizira kuti ‘anthu onse amene ali ndi maganizo abwino owathandiza kupeza moyo wosatha’ adzalandira uthenga wabwino. (Mac. 13:48) Choncho sitiyenera kudzikayikira kapena kukhumudwa ngati anthu ena sakufuna kumva uthenga wabwino wa Ufumu. Polalikira, tiyeni tizigwiritsa ntchito mfundo zimene Yehova amatiphunzitsa ndipo tisamakayikire kuti zitithandiza ifeyo komanso anthu amene angamvetsere. (1 Tim. 4:16) Yehova akhoza kutithandiza kuti tidziwe ‘mmene tingayankhire munthu aliyense.’ M’nkhani yotsatira tidzaona kuti zinthu zingatiyenderenso bwino mu utumiki ngati titsatira mfundo ina yofunika kwambiri imene Yesu anaitchula.

^ ndime 6 Onani nkhani yakuti “Kodi N’zotheka Kuyamba Kukhulupirira Mlengi?” mu Nsanja ya Olonda ya October 1, 2009.