Thandizani Ena Kuti Azichita Zonse Zimene Angathe
“Ndidzakupatsa malangizo ndi kukuyang’anira.”—SAL. 32:8.
1, 2. Kodi Yehova amaona bwanji atumiki ake a padziko lapansi?
MAKOLO akamaona ana awo akusewera nthawi zambiri amadabwa kuona luso limene anawo ali nalo. Mwina inunso mwaonapo zimenezi. Mwana wina akhoza kukhala ndi luso lothamanga kapena kudumpha pomwe wina angakhale ndi luso losewera bawo kapena lojambula. Kaya ana awo ali ndi luso lotani, makolo amasangalala kuwathandiza kuti akulitse luso lawolo.
2 Nayenso Yehova amachita chidwi kwambiri ndi ana ake a padziko lapansi. Iye amaona kuti atumiki ake padzikoli ali ngati “zinthu zamtengo wapatali zochokera ku mitundu yonse ya anthu.” (Hag. 2:7) Iwo ndi amtengo wapatali kwambiri makamaka chifukwa cha chikhulupiriro chawo ndiponso kudzipereka kwawo. Koma mwina mwaona kuti atumiki a Yehova amakhalanso ndi luso losiyanasiyana. Abale ena ali ndi luso lokamba nkhani pomwe ena ali ndi luso loyendetsa zinthu mumpingo. Alongo ena amatha kuphunzira bwino chilankhulo china kumalalikira m’chilankhulocho pamene ena amapereka chitsanzo chabwino kwambiri polimbikitsa anthu ndi kusamalira odwala. (Aroma 16:1, 12) Timayamikira kwambiri kukhala limodzi ndi Akhristu oterewa mumpingo.
3. Kodi tikambirana mafunso ati m’nkhaniyi?
3 Koma Akhristu ena, makamaka abale achinyamata kapena ongobatizidwa kumene, amafunika kuwathandiza kuti adziwe zimene angachite bwino mumpingo. Kodi tingawathandize bwanji? N’chifukwa chiyani tiyenera kutsanzira Yehova n’kumayesetsa kuona zabwino zimene angachite?
YEHOVA AMAONA ZABWINO ZIMENE ATUMIKI AKE ANGACHITE
4, 5. Kodi nkhani ya pa Oweruza 6:11-16 imasonyeza bwanji kuti Yehova amaona zimene atumiki ake angachite?
4 Nkhani zambiri za m’Baibulo zimasonyeza kuti Yehova amatha kuona zabwino zimene atumiki ake amachita komanso zimene angakwanitse kuchita. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi Gidiyoni, amene anasankhidwa kuti apulumutse anthu a Mulungu kwa Amidiyani. Iye ayenera kuti anadabwa mngelo atamuuza kuti: “Yehova ali ndi iwe, munthu wolimba mtima ndi wamphamvuwe.” Zikuonekeratu kuti umu si mmene Gidiyoni ankadzionera. Iye anasonyeza kuti ankadzikayikira ndipo ankadziona kuti ndi wachabechabe. Koma zimene anakambirana ndi mngeloyu zinasonyeza kuti Yehova ankaona Gidiyoni mosiyana kwambiri ndi mmene ankadzionera.—Werengani Oweruza 6:11-16.
5 Yehova anaona luso limene Gidiyoni anali nalo ndipo sankakayikira zoti akhoza kupulumutsa Aisiraeli. Choyamba, mngelo wa Yehova anaona Gidiyoniyo akupuntha tirigu mwamphamvu. Koma pali zinanso zimene anaona. Kalelo anthu ankapuntha tirigu pamtetete kuti mphepo iziuluza mankhusu ake. Koma Gidiyoni ankapuntha tiriguyo moponderamo mphesa kuti Amidiyani asamutulukire n’kumulanda. Yehova anazindikira kuti Gidiyoni ndi wakhama komanso wanzeru. Iye anatha kuona mmene zinthu zinalili n’kupeza njira yoti apewere mavuto. Yehova atazindikira zimene Gidiyoni angakwanitse kuchita anamuthandiza kuti achite zambiri.
6, 7. (a) Tikudziwa bwanji kuti Yehova ankaona Amosi mosiyana ndi mmene Aisiraeli ena ankamuonera? (b) N’chiyani chikusonyeza kuti Amosi sanali mbuli?
6 Zimene zinachitikira mneneri Amosi zimasonyezanso kuti Yehova amaona zimene atumiki ake angachite. Ambiri ankamuona kuti ndi munthu wamba basi ndiponso wosafunika. Ndipotu Amosi ananena kuti anali m’busa komanso woboola mtundu wina wa nkhuyu zimene anthu osauka ankadya. Koma Yehova anasankha Amosi kuti apereke chiweruzo kwa anthu okhala mu ufumu wa Isiraeli wa mafuko 10. N’kutheka kuti Aisiraeli ena ankaona kuti Mulungu sanasankhe bwino.—Werengani Amosi 7:14, 15.
7 Amosi ankachokera kumidzi koma ankadziwa bwino za miyambo komanso olamulira a m’nthawi yake. Iye ankadziwanso bwinobwino zimene zinkachitika ku Isiraeli. Mwina ankadziwanso zochitika m’mayiko ena apafupi chifukwa choti ankakumana ndi amalonda ochokera m’madera osiyanasiyana. (Amosi 1:6, 9, 11, 13; 2:8; 6:4-6) Akatswiri ena a Baibulo a masiku ano amanena kuti Amosi anali ndi luso lolemba nkhani. Iye ankagwiritsa ntchito mawu osavuta kumva komanso amphamvu. Ankathanso kugwiritsa ntchito mawuwo mwaluso komanso kuyerekezera bwino zinthu. Pa nthawi ina Amosi analankhula molimba mtima poyankha wansembe wina dzina lake Amaziya. Zimene analankhulazo zimasonyeza kuti Yehova anasankhadi munthu woyenera ndipo anaoneratu zimene anthu ena sankaona.—Amosi 7:12, 13, 16, 17.
8. (a) Kodi Yehova anamuuza chiyani Davide? (b) Kodi mawu a pa Salimo 32:8 angalimbikitse bwanji anthu amene amadzikayikira?
8 Yehova amaonadi zimene mtumiki wake aliyense angachite. Iye anauza Davide kuti adzamupatsa malangizo ndi ‘kumuyang’anira.’ (Werengani Salimo 32:8.) Kodi mfundo imeneyi ingatilimbikitse bwanji? Mwina timadzikayikira, koma Yehova angatithandize kuti tikwanitse kuchita zinthu zimene ifeyo tinkaganiza kuti sitingazikwanitse. Zimene Yehova amachita tingaziyerekezere ndi zimene bambo amachita pophunzitsa mwana wake kuyendetsa njinga. Bambo amauza mwanayo zochita n’kumayang’ana mmene akuchitira komanso kumuthandizira. Nayenso Yehova amatiyang’anitsitsa n’kumatitsogolera kuti tithe kuchita zambiri pomutumikira. Nthawi zina amagwiritsanso ntchito abale ndi alongo kuti atithandize kuchita zonse zimene tingathe. Kodi amachita bwanji zimenezi?
TIZIONA ZIMENE ANTHU ENA AMACHITA BWINO
9. Kodi tingatsatire bwanji malangizo a Paulo oti ‘tiziganizira zofuna za ena’?
9 Paulo analimbikitsa Akhristu onse kuti ‘aziganizira zofuna za anzawo.’ (Werengani Afilipi 2:3, 4.) Malangizo a Paulowa akusonyeza kuti tiyenera kuona zabwino zimene ena akuchita ndiponso kuwayamikira. Kodi timamva bwanji munthu wina akatiyamikira pamene tachita bwino zinthu zina? Nthawi zambiri zimatilimbikitsa kuti tiyesetse kuchita zinthu zina zabwino. Ifenso tikayamikira zimene anzathu akuchita timawathandiza kuti achite zambiri potumikira Yehova.
10. Kodi ndi ndani kwenikweni amene tingafunike kuwalimbikitsa?
10 Kodi ndi ndani kwenikweni amene tingafunike kuwalimbikitsa? N’zoona kuti tonsefe timafunika kulimbikitsidwa. Koma achinyamata kapena abale ongobatizidwa kumene amafunika kulimbikitsidwa kwambiri. Tiyenera kuwathandiza kudziwa kuti ndi ofunika ndipo angachite zambiri mumpingo. Mawu a Mulungu amawalimbikitsa kuyesetsa kuti azitumikira mumpingo, koma ngati sitiwalimbikitsa ndiponso kuwayamikira sangakhale ndi mtima umenewu.—1 Tim. 3:1.
11. (a) Kodi mkulu wina anathandiza bwanji mnyamata wamanyazi? (b) Kodi tikuphunzira chiyani pa nkhaniyi?
11 M’bale wina dzina lake Ludovic, yemwe ndi mkulu, anathandizidwapo ali wachinyamata. Iye anati: “Ndikalimbikitsa m’bale, amasintha mofulumira n’kuyamba kuchita zambiri.” Ludovic anafotokoza za mnyamata wina wamanyazi dzina lake Julien. Iye anati: “Nthawi zina Julien ankayesetsa kuthandiza mumpingo. Koma chifukwa chamanyazi ankadzikayikira ndipo ankachita zinthu m’njira yosamvetsetseka. Ngakhale zinali choncho, ndinatha kuona kuti anali wokoma mtima ndiponso ankafunitsitsa kuthandiza ena. Choncho m’malo momukayikira, ndinayesetsa kuganizira makhalidwe ake abwino ndipo ndinkamulimbikitsa.” Patapita nthawi, Julien anakhala mtumiki wothandiza ndipo tsopano ndi mpainiya wokhazikika.
ATHANDIZENI KUTI AZICHITA ZONSE ZIMENE ANGATHE
12. Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tithandize munthu kuchita zambiri? Perekani chitsanzo.
12 Kuti tithandize anthu kuchita zambiri, tiyenera kukhala maso kuti tione luso la ena. Nkhani ya Julien ija ikusonyeza kuti sitiyenera kuganizira kwambiri zimene ena amalakwitsa koma tiziona makhalidwe awo abwino komanso luso lawo n’kuwathandiza. Izi n’zimene Yesu anachita ndi Petulo. Nthawi zina Petulo ankaoneka ngati wosadalirika koma Yesu analosera kuti iye adzakhala wosasunthika ngati thanthwe.—Yoh. 1:42.
13, 14. (a) Kodi Baranaba anathandiza bwanji Maliko? (b) Kodi m’bale wina anathandizidwanso bwanji? (Onani chithunzi patsamba 28.)
13 Izi ndi zimenenso Baranaba anachita pothandiza Yohane Maliko. (Mac. 12:25) Pa ulendo woyamba wa umishonale, Paulo ndi Baranaba ‘ankatumikiridwa’ ndi Maliko. Koma atafika ku Pamfuliya, Maliko anawasiya n’kubwerera. Iwo anayenda okha kulowera chakumpoto kudutsa m’dera lina kumene kunkakhala achifwamba ambiri. (Mac. 13:5, 13) Koma Baranaba ayenera kuti sanaganizire kwambiri zimene Maliko anachitazo ndipo pa nthawi ina anam’tenganso kuti apitirize kumuphunzitsa. (Mac. 15:37-39) Zimenezi zinathandiza kuti Maliko akhale mtumiki wa Yehova wodalirika. Chochititsa chidwi n’chakuti pa nthawi imene Paulo anamangidwa ku Roma, Maliko anali naye limodzi ndipo onse anapereka moni m’kalata yopita kumpingo wa ku Kolose. M’kalatayo, Paulo analemba zinthu zosonyeza kuti ankaona kuti Maliko anali m’bale wabwino. (Akol. 4:10) Baranaba ayenera kuti anasangalala kwambiri pamene Paulo anaitanitsa Maliko kuti akamuthandize.—2 Tim. 4:11.
14 M’bale wina dzina lake Alexandre, yemwenso ndi mkulu, anathandizidwa ali wachinyamata. Pofotokoza mmene m’bale wina anamuthandizira iye anati: “Pamene ndinali wachinyamata, ndinkavutika kwambiri kupemphera pa gulu. Koma m’baleyo anandiuza zimene ndingachite pokonzekera komanso kuti ndisamamangike. M’malo mongosiya kundipatsa pemphero, iye ankakondabe kundiuza kuti ndipemphere pa msonkhano wokonzekera utumiki. Izi zinandithandiza kuti ndisamadzikayikire.”
15. Kodi Paulo anasonyeza bwanji kuti ankayamikira abale ake?
15 Kodi inuyo mumatani mukaona kuti m’bale kapena mlongo wina ali ndi khalidwe linalake labwino? Kodi mumamuyamikira kuchokera pansi pa mtima? M’chaputala 16 cha buku la Aroma, Paulo anatchula anthu oposa 20 n’kuyamikira kuchokera pansi pa mtima makhalidwe awo abwino. (Aroma 16:3-7, 13) Mwachitsanzo, iye ayamikira Anduroniko ndi Yuniya kuti anapirira kwambiri ponena kuti iwo anatumikira Khristu kwa nthawi yaitali kuposa iyeyo. Paulo anayamikiranso amayi a Rufu, mwina pokumbukira mmene anamuthandizira m’mbuyomo.
16. Kodi chingachitike n’chiyani ngati timayamikira achinyamata?
16 Tikamayamikira anzathu kuchokera pansi pa mtima zikhoza kuwathandiza kwambiri. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi mnyamata wina wa ku France dzina lake Rico. Iye anakhumudwa kwambiri chifukwa choti bambo ake, omwe sanali Mboni, ankamukaniza kubatizidwa. Rico anaganiza zoti angodikira kuti adzayambe kutumikira Yehova bwinobwino akadzakula. Iye ankadandaulanso chifukwa chakuti anzake kusukulu ankamuvutitsa. Mkulu wina mumpingo dzina lake Frédéric, anapemphedwa kuti aziphunzira ndi Rico ndipo anati: “Ndinamuyamikira kwambiri n’kumuuza kuti kutsutsidwako unali umboni wakuti sankabisa zimene amakhulupirira.” Zimene m’baleyu anamuuza zinamuthandiza kuti apitirize kukhala wokhulupirika komanso kuti azigwirizana ndi bambo ake. Rico anabatizidwa ali ndi zaka 12.
17. (a) Kodi tingathandize bwanji abale kuti azichita zambiri mumpingo? (b) Kodi mmishonale wina wathandiza bwanji achinyamata?
17 Tikayamikira anzathu chifukwa chokamba bwino nkhani kapena chifukwa chochita zinthu zina zabwino, timawalimbikitsa kuti achite zambiri potumikira Yehova. Mlongo wina dzina lake Sylvie, * amene watumikira ku Beteli ya ku France kwa zaka zambiri, ananena kuti nawonso alongo angachite bwino kuyamikira abale. Ananena kuti alongowo akhoza kutchula zinthu zina zimene m’bale wachita bwino zomwe akulu kapena abale ena sangazitchule. Choncho m’baleyo angalimbikitsidwe kwambiri kumva zimene abale komanso alongowo anganene. Sylvie ananenanso kuti: “Ndimaona kuti ndi udindo wanga kuyamikira ena pa zimene achita.” (Miy. 3:27) Mmishonale wina ku French Guiana, dzina lake Jérôme, wathandiza anyamata ambiri kuti ayambe umishonale. Iye anati: “Ndaona kuti kuyamikira abale achinyamata pamene achita zinthu zina zabwino mu utumiki kapena pamene apereka ndemanga yabwino kumawathandiza kuti asamadzikayikire ndiponso kuti ayambe kuchita zambiri mumpingo.”
18. Kodi kugwira ntchito limodzi ndi abale achinyamata n’kothandiza bwanji?
18 Tingathandizenso anzathu kuti achite zambiri ngati tigwira nawo ntchito zina mumpingo. Mwachitsanzo, tiyerekeze kuti mumpingo muli m’bale wachinyamata wodziwa zamakompyuta. Mkulu angamupemphe kuti asindikize nkhani zina kuchokera pa webusaiti ya jw.org zimene zingalimbikitse achikulire omwe alibe makompyuta. Mukhozanso kupempha achinyamata ena kuti muthandizane nawo ntchito zina pa Nyumba ya Ufumu. Mukamatero mudzatha kuona luso limene achinyamatawo ali nalo n’kuwayamikira ndipo zotsatira zake zidzakhala zabwino.—Miy. 15:23.
KONZEKERANI ZAM’TSOGOLO
19, 20. N’chifukwa chiyani tiyenera kuthandiza anthu ena kuchita zambiri mumpingo?
19 Yehova atasankha Yoswa kuti atsogolere Aisiraeli, anauzanso Mose kuti ‘amulimbikitse.’ (Werengani Deuteronomo 3:28.) Anthu ambiri atsopano akulowa m’gulu la Yehova padziko lonse. Choncho Akhristu onse, osati akulu okha, angathandize abale achinyamata ndiponso atsopano kuti achite zambiri mumpingo. Tikamachita zimenezi tidzathandiza anthu ambiri kuyamba utumiki wa nthawi zonse komanso kukhala “oyenerera bwino kuphunzitsa ena.”—2 Tim. 2:2.
20 Kaya tili mumpingo waukulu kapena m’kagulu, tiyeni tonsefe tizikonzekera zam’tsogolo. Kuti zimenezi zitheke, tiyenera kutsanzira Yehova yemwe nthawi zonse amaona zabwino zimene atumiki ake angachite.
^ ndime 17 Dzina lasinthidwa.