“Mudzakhala Mboni Zanga”
‘Yesu anawayankha kuti: “Mudzakhala mboni zanga mpaka kumalekezero a dziko lapansi.”’—MAC. 1:7, 8.
1, 2. (a) Kodi mboni yaikulu kwambiri ya Yehova ndi ndani? (b) Kodi dzina lakuti Yesu limatanthauza chiyani? (c) Kodi Mwana wa Mulungu anachita bwanji zinthu mogwirizana ndi dzina lake?
PAMENE Yesu Khristu ankaweruzidwa ndi bwanamkubwa wa Yudeya, ananena kuti: “Chimene ndinabadwira, ndiponso chimene ndinabwerera m’dziko, ndicho kudzachitira umboni choonadi.” (Werengani Yohane 18:33-37.) Yesu ananena mawuwa atangovomereza molimba mtima kuti ndi mfumu. Patapita zaka zambiri, mtumwi Paulo ananena za chitsanzo chimene Yesu anaperekachi kuti: “[Iye] anapereka umboni wabwino kwambiri pamaso pa Pontiyo Pilato.” (1 Tim. 6:13) Nthawi zina tiyeneranso kukhala olimba mtima kuti tikhale ‘mboni zokhulupirika ndi zoona’ m’dziko la Satanali.—Chiv. 3:14.
2 Yesu anali kale mboni ya Yehova chifukwa chakuti anali Myuda. (Yes. 43:10) Ndipotu anadzakhala mboni yaikulu kwambiri ya Mulungu kuposa wina aliyense. Yesu anaonanso kuti tanthauzo la dzina limene Mulungu anamupatsa ndi lofunika kwambiri. Mngelo anauza Yosefe, yemwe analera Yesu, kuti Mariya anatenga pakati kudzera mwa mzimu woyera. Kenako anati: “Iye adzabereka mwana wamwamuna, ndipo dzina lake udzamutche Yesu, chifukwa adzapulumutsa anthu ake ku machimo awo.” (Mat. 1:20, 21; mawu a m’munsi) Akatswiri ambiri a Baibulo amavomereza kuti dzina lakuti Yesu limachokera ku dzina lachiheberi lakuti Yesuwa. Iwo amanenanso kuti m’dzina la Yesu muli chidule cha dzina la Mulungu ndipo limatanthauza kuti “Yehova Ndiye Chipulumutso.” Mogwirizana ndi dzina lake, Yesu anathandiza anthu amene anali ngati “nkhosa zosochera za nyumba ya Isiraeli” kuti alape machimo awo n’kukhalanso pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. (Mat. 10:6; 15:24; Luka 19:10) Kuti achite zimenezi, Yesu ankalalikira mwakhama za Ufumu wa Mulungu. Maliko, yemwe analemba buku la Uthenga Wabwino, anati: “Yesu anapita ku Galileya kukalalikira uthenga wabwino wa Mulungu kuti: ‘Nthawi yoikidwiratu yakwaniritsidwa! Ufumu wa Mulungu wayandikira! Lapani anthu inu! Khulupirirani uthenga wabwino!’” (Maliko 1:14, 15) Yesu anadzudzulanso molimba mtima atsogoleri achipembedzo chachiyuda. Chimenechi ndi chifukwa china chimene chinawachititsa kuti akonze zomupha.—Maliko 11:17, 18; 15:1-15.
“ZINTHU ZAZIKULU ZA MULUNGU”
3. N’chiyani chinachitika pa tsiku lachitatu Yesu ataphedwa?
3 Koma chodabwitsa kwambiri n’chakuti pa tsiku lachitatu Yesu ataphedwa, Yehova anamuukitsa monga mzimu wokhala ndi moyo wosafa. (1 Pet. 3:18) Ndiyeno Yesu anavala thupi la munthu n’cholinga choti apereke umboni wakuti anaukitsidwadi. Pa tsikulo, anaonekera maulendo okwana 5 kwa ophunzira osiyanasiyana.—Mat. 28:8-10; Luka 24:13-16, 30-36; Yoh. 20:11-18.
4. Kodi Yesu anachita chiyani panthawi imene anaonekera kwa atumwi ndi anthu ena? (b) Kodi Yesu anathandiza ophunzira ake kumvetsa za udindo wotani?
4 Pa ulendo wa nambala 5, Yesu anaonekera kwa atumwi ake limodzi ndi ena amene anasonkhana nawo. Pa nthawi yosaiwalikayi, iye anawaphunzitsa mfundo zina za m’Mawu a Mulungu. Yesu “anatseguliratu maganizo awo kuti amvetse tanthauzo la Malemba.” Ndiyeno iwo anamvetsa kuti Malemba anali ataneneratu kuti Yesu adzaphedwa ndi adani a Mulungu komanso kuti adzaukitsidwa mozizwitsa. Pa mapeto pa msonkhanowo, Yesu anathandiza omvera ake kuti amvetse bwino udindo wawo. Anawauza kuti: “Pa maziko a dzina lake, m’mitundu yonse mudzalalikidwa za kulapa kuti machimo akhululukidwe.” Anawauzanso kuti: “Kuyambira ku Yerusalemu inu mudzakhala mboni za zimenezi.”—Luka 24:44-48.
5, 6. (a) N’chifukwa chiyani Yesu ananena kuti: “Mudzakhala mboni zanga”? (b) Kodi ophunzira a Yesu anayenera kuuza anthu zinthu zatsopano ziti?
5 Patapita masiku 40, Yesu anaonekeranso komaliza kwa atumwi ake. Pa nthawiyi, iwo ayenera kuti anamvetsa bwino lamulo la Yesu lakuti: “Mudzakhala mboni zanga mu Yerusalemu, ku Yudeya konse ndi ku Samariya, mpaka kumalekezero a dziko lapansi.” (Mac. 1:8) N’chifukwa chiyani Yesu anati: “Mudzakhala mboni zanga,” osati mboni za Yehova? Iye ananena zimenezi chifukwa chakuti anthu amene ankawalankhulawo anali Aisiraeli ndipo anali kale mboni za Yehova.
6 Ophunzira a Yesu anali ndi udindo wouza anthu zinthu zatsopano zokhudza cholinga cha Yehova. Zinthuzo zinali zazikulu kwambiri kuposa kupulumuka kwa Aisiraeli ku ukapolo wa ku Iguputo komanso ku Babulo. Imfa ndiponso kuuka kwa Yesu Khristu zinachititsa kuti anthu akhale ndi mwayi womasuka ku ukapolo wozunza kwambiri wa uchimo ndi imfa. Ophunzira a Yesu atangodzozedwa pa Pentekosite mu 33 C.E., anauza anthu “zinthu zazikulu za Mulungu.” Anthu masauzande ambiri analapa n’kuyamba kukhulupirira nsembe ya Yesu. Choncho Yesu atabwerera kumwamba, Yehova anali kumugwiritsa ntchito populumutsa anthu masauzande padzikoli.—Mac. 2:5, 11, 37-41.
‘DIPO LOWOMBOLA ANTHU AMBIRI’
7. Kodi zimene zinachitika pa Pentekosite mu 33 C.E. zinapereka umboni wotani?
7 Zimene zinachitika pa Pentekosite mu 33 C.E. zinapereka umboni wakuti Yehova wavomereza kuti nsembe ya moyo wa Yesu iphimbe uchimo. (Aheb. 9:11, 12, 24) Paja Yesu ananena kuti “sanabwere kudzatumikiridwa, koma kudzatumikira ndi kudzapereka moyo wake dipo kuwombola anthu ambiri.” (Mat. 20:28) Mu lembali mawu akuti “anthu ambiri” sanena za Ayuda okha amene analapa. Tikutero chifukwa Mulungu amafuna kuti “anthu, kaya akhale a mtundu wotani, apulumuke” ndipo dipo linaperekedwa kuti ‘lichotse uchimo wa dziko!’—1 Tim. 2:4-6; Yoh. 1:29.
8. Kodi ophunzira a Yesu anachitira umboni mpaka kufika pati, ndipo n’chiyani chinawathandiza?
8 Kodi Akhristu oyambirirawo anapitiriza kulimba mtima n’kukhalabe mboni za Yesu? Inde, koma osati mwa mphamvu zawo zokha. Mzimu woyera wa Yehova unawapatsa mphamvu kuti apitirizebe kuchitira umboni. (Werengani Machitidwe 5:30-32.) Pafupifupi zaka 27 pambuyo pa Pentekosite mu 33 C.E., tinganene kuti “choonadi cha uthenga wabwino” chinali chitalengezedwa kwa Ayuda ndiponso anthu a mitundu ina “m’chilengedwe chonse cha pansi pa thambo.”—Akol. 1:5, 23.
9. Malinga ndi ulosi, kodi n’chiyani chinachitikira mpingo wachikhristu woyambirira?
9 Koma n’zomvetsa chisoni kuti patapita nthawi mpingo wachikhristu woyambirirawu unasokonezedwa. (Mac. 20:29, 30; 2 Pet. 2:2, 3; Yuda 3, 4) Yesu anasonyeza kuti “woipayo,” kapena kuti Satana, adzachititsa kuti mpatuko uyambe mumpingo ndipo udzakula mpaka kusokoneza Chikhristu choona. Iye ananena kuti zimenezi zidzachitika mpaka “mapeto a nthawi ino.” (Mat. 13:37-43) Baibulo linasonyezanso kuti Yehova adzaika Yesu monga Mfumu ya anthu a padzikoli. Zimenezi zinachitikadi mu October 1914 ndipo pa nthawiyi “masiku otsiriza” a dziko loipa la Satanali anayamba.—2 Tim. 3:1.
10. (a) Kodi Akhristu odzozedwa ankaneneratu za nthawi iti? (b) N’chiyani chinachitika mu October 1914 ndipo n’chiyani chakhala chikuonekera kuyambira nthawiyo?
10 Kutatsala zaka 30 kuti mwezi wa October mu 1914 ufike, Akhristu odzozedwa ankaneneratu kuti zinthu zapadera zidzachitike pa nthawiyo. Ankanena zimenezi chifukwa cha ulosi wa Danieli wonena za mtengo waukulu umene unadulidwa ndipo unayambiranso kukula patadutsa “nthawi zokwanira 7.” (Dan. 4:16) Mu ulosi wonena za kukhalapo kwake ndiponso “mapeto a nthawi ino,” Yesu anatchula “nthawi zokwanira 7” zimenezi. Koma anagwiritsa ntchito mawu akuti ‘nthawi zoikidwiratu za anthu a mitundu ina.’ Kuyambira mu 1914, “chizindikiro cha kukhalapo [kwa Khristu]” monga Mfumu yatsopano ya dziko lapansi chikuonekera kwambiri. (Mat. 24:3, 7, 14; Luka 21:24) Choncho kuyambira nthawi imeneyo, “zinthu zazikulu za Mulungu” zikuphatikizapo zimene Yehova anachita poika Yesu monga Mfumu ya anthu a padzikoli.
11, 12. (a) Kodi Mfumu yatsopano ya dziko lapansi inayamba kuchita chiyani mu 1919? (b) N’chiyani chinayamba kuonekera kuyambira cha m’ma 1935? (Onani chithunzi patsamba 28.)
11 Monga Mfumu yatsopano ya dziko lapansi, Yesu Khristu anayamba kumasula otsatira ake odzozedwa ku ukapolo wa “Babulo Wamkulu.” (Chiv. 18:2, 4) Mu 1919, nkhondo yoyamba ya padziko lonse itatha, Akhristu anali ndi mwayi woti ayambe kuchitira umboni padziko lonse. Ankalalikira za njira ya Mulungu yotipulumutsira ndiponso za uthenga wabwino wa Ufumu umene unakhazikitsidwa. Iwo anagwira ntchitoyi mwakhama kwambiri. Izi zinachititsa kuti anthu ena ambiri aphunzire Baibulo ndipo anadzozedwa kuti adzakalamulire ndi Khristu.
12 Kuyambira cha m’ma 1935, zinaonekeranso kuti Khristu wayamba kusonkhanitsa mamiliyoni a “nkhosa zina” kuti adzakhale mu “khamu lalikulu” la anthu amitundu yosiyanasiyana. A khamu lalikuluwa amatsogoleredwa ndi Akhristu odzozedwa ndipo amatsatira chitsanzo cha Yesu podziwitsa anthu kuti chipulumutso chawo chimachokera kwa Mulungu ndi Khristu. Iwo akapitiriza kuchitira umboni ndiponso kukhulupirira nsembe ya dipo ya Khristu, adzapulumuka pa ‘chisautso chachikulu,’ chomwe chidzawononga dziko la Satanali.—Yoh. 10:16; Chiv. 7:9, 10, 14.
TIZILIMBA MTIMA KUTI TILALIKIRE UTHENGA WABWINO
13. (a) Kodi tiyenera kuyesetsa kuchita chiyani? (b) Kodi tingatani kuti tikhalebe odzipereka kwa Yehova?
13 Tiyeni tipitirize kuyamikira mwayi wathu wochitira umboni “zinthu zazikulu” zomwe Yehova Mulungu wachita ndiponso zimene walonjeza kuchita m’tsogolo. N’zoona kuti nthawi zina kuchitira umboni si kophweka. Abale athu ambiri amalalikira m’madera kumene anthu safuna kumvetsera, amawanyoza kapenanso kuwazunza kumene. Koma tikhoza kuchita zimene mtumwi Paulo ndi anzake anachita. Iye anati: “Tinalimba mtima mothandizidwa ndi Mulungu wathu ndipo tinalankhula kwa inu uthenga wabwino wa Mulungu movutikira kwambiri.” (1 Ates. 2:2) Choncho tisataye mtima koma tiziyesetsa kukhalabe odzipereka kwa Mulungu pamene dziko la Satanali likuwonongedwa n’kukhala bwinja. (Yes. 6:11) Sitingathe kuchita zimenezi mwa mphamvu zathu zokha koma mofanana ndi Akhristu oyambirira, tiyenera kupempha Yehova kuti atipatse mzimu wake ndiponso “mphamvu yoposa yachibadwa.”—Werengani 2 Akorinto 4:1, 7; Luka 11:13.
14, 15. (a) Kodi anthu ankaona bwanji Akhristu m’nthawi ya atumwi? (b) Kodi mtumwi Petulo anati chiyani ponena za Akhristuwa? (c) Kodi tizikumbukira chiyani tikamatsutsidwa chifukwa chokhala Mboni za Yehova?
14 Masiku ano, anthu mamiliyoni ambiri amati ndi Akhristu ‘koma amakana Mulungu ndi zochita zawo chifukwa ndi onyansa ndi osamvera, ndipo ndi osayenerera ntchito iliyonse yabwino.’ (Tito 1:16) Tingachite bwino kukumbukira kuti anthu ambiri ankadana ndi Akhristu oona m’nthawi ya atumwi. M’pake kuti mtumwi Petulo analemba kuti: “Ngati anthu akukunyozani chifukwa cha dzina la Khristu, ndinu odala chifukwa . . . mzimu wa Mulungu . . . wakhazikika pa inu.”—1 Pet. 4:14.
15 Kodi tingagwiritsenso ntchito mawu amenewa ponena za a Mboni za Yehova masiku ano? Inde tikhoza kutero chifukwa chakuti iwo amachitira umboni za Ufumu wa Yesu. Choncho anthu akamatinyoza chifukwa chodziwika ndi dzina la Yehova ndiye kuti ‘akutinyozanso chifukwa cha dzina la [Yesu] Khristu.’ Paja iye anauza anthu omutsutsa kuti: “Ndabwera m’dzina la Atate wanga, ndipo simunandilandire.” (Yoh. 5:43) Ndiyetu ngati mungatsutsidwenso pamene mukulalikira, muzilimba mtima. Muzikumbukira kuti kutsutsidwako ndi umboni wakuti Mulungu akusangalala nanu ndiponso kuti mzimu wake “wakhazikika pa inu.”
16, 17. (a) Kodi a Mboni za Yehova m’madera ambiri akukumana ndi zotani? (b) Kodi inuyo mumafunitsitsa kuchita chiyani?
16 Koma tisaiwale kuti m’madera ambiri padziko lapansi anthu ambiri akubwera m’gulu la Yehova. Ngakhale m’madera amene timalalikiramo kwambiri, timapezabe anthu amene akufuna kumva uthenga wathu wa chipulumutso. Tiyenera kuchita khama pobwereranso kwa anthu n’cholinga choti tiziphunzira nawo Baibulo. Tikatero tingawathandize kuti afike podzipereka kwa Yehova ndiponso kubatizidwa. Muyenera kuti mumamva mofanana ndi mlongo wina wa ku South Africa dzina lake Sarie. Iye wakhala akugwira ntchito yolalikira kwa zaka zoposa 60, ndipo anati: “Ndikuyamikira kwambiri kuti chifukwa cha nsembe ya dipo ya Yesu, ndimatha kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova, yemwe ndi Wolamulira Wamkulu wa chilengedwe chonse. Ndine wosangalalanso kuti ndili ndi mwayi wodziwitsa anthu dzina la Mulungu laulemerero.” Mlongoyu limodzi ndi mwamuna wake, dzina lake Martinus, athandiza ana awo atatu komanso anthu ambiri kuti ayambe kulambira Yehova. Sarie ananenanso kuti: “Palibenso ntchito ina imene imasangalatsa kuposa imeneyi ndipo kudzera mwa mzimu wake woyera, Yehova amatipatsa mphamvu zotithandiza kupitiriza kugwira ntchito yopulumutsa anthuyi.”
17 Kaya ndife Akhristu obatizidwa kapena tili ndi cholinga chobatizidwa m’tsogolomu, tonse tili ndi zifukwa zambiri zotichititsa kuyamikira mwayi wathu wokhala mumpingo wa padziko lonse wa Mboni za Yehova. Choncho tiyeni tipitirize kuchitira umboni mokwanira ndiponso kuyesetsa kuti tisadetsedwe ndi dziko la Satanali. Tikamachita zimenezi tidzalemekeza Atate wathu wachikondi yemwe timadziwika ndi dzina lake laulemerero.