Kodi Timamvetsa Tanthauzo Lake?
“Anatseguliratu maganizo awo kuti amvetse tanthauzo la Malemba.”—LUKA 24:45.
1, 2. Kodi Yesu analimbikitsa bwanji ophunzira ake pa tsiku limene anauka?
TSIKU limene Yesu anaukitsidwa, ophunzira ake awiri ankapita kumudzi wina. Mudziwu unali pa mtunda wa pafupifupi makilomita 11 kuchokera ku Yerusalemu. Iwo sankadziwa kuti Yesu wauka choncho anali ndi chisoni kwambiri. Kenako Yesu anatulukira n’kuyamba kuyenda nawo limodzi. Iye anawalimbikitsa kwambiri ‘powatanthauzira zinthu zokhudza iyeyo m’Malemba onse, kuyambira ndi Zolemba za Mose ndi za aneneri zonse.’ (Luka 24:13-15, 27) Iwo anakhudzidwa kwambiri mumtima chifukwa Yesu ‘ankawafotokozera Malemba momveka bwino.’—Luka 24:32.
2 Tsiku lomwelo, ophunzira awiriwa anabwerera ku Yerusalemu. Iwo anafufuza atumwi n’kuyamba kuwauza zimene zinachitika. Ali mkati mofotokoza, Yesu anatulukiranso ndipo onse anamuona. Atumwiwo anaopa kwambiri ndipo ankakayikira kuti ndi Yesudi. Kodi Yesu anawalimbikitsa bwanji? Baibulo limati: “Anatseguliratu maganizo awo kuti amvetse tanthauzo la Malemba.”—Luka 24:45.
3. (a) Kodi tingakumane ndi mavuto ati mu utumiki? (b) N’chiyani chingatithandize kuti tizisangalala ndi utumiki?
3 Ifenso nthawi zina tikhoza kukhala osasangalala. Mwina 1 Akor. 15:58) Kapena mwina anthu amene timawaphunzitsa sakusintha. Mwinanso ena amene tinkawaphunzitsa asiya kuphunzira. Kodi tingatani kuti tizisangalalabe ndi utumiki? Chinthu chimodzi chimene chingatithandize ndi kumvetsa bwino tanthauzo la mafanizo a Yesu. Tiyeni tikambirane mafanizo atatu n’kuona zimene tikuphunzirapo.
tikugwira ntchito yolalikira mwakhama koma takhumudwa chifukwa anthu safuna kumvetsera. (FANIZO LA WOFESA MBEWU AMENE AMAGONA
4. Kodi fanizo la wofesa mbewu amene amagona limatanthauza chiyani?
4 Werengani Maliko 4:26-29. Kodi fanizoli limatanthauza chiyani? Munthu wotchulidwa mu fanizoli akuimira munthu aliyense amene amalalikira za Ufumu. Mbewuzo zikuimira uthenga wa Ufumu umene timalalikira kwa anthu amtima wabwino. Mofanana ndi munthu wina aliyense, mlimiyu “amagona usiku n’kumadzuka kukacha.” Ndiyeno pang’ono ndi pang’ono, “mbewuzo zimamera ndi kukula” mpaka nthawi yokolola. Mbewuzo zimakula ‘pazokha’ n’kumasintha. Ndi mmene zimakhaliranso ndi anthu amene timaphunzitsa. Amasintha mwapang’onopang’ono. Ndiyeno akafika pofunitsitsa kutumikira Mulungu, amadzipereka kwa iye ndiponso kubatizidwa. Apa tsopano zimakhala ngati akubala zipatso.
5. N’chifukwa chiyani Yesu ananena fanizo la wofesa mbewu amene amagona?
5 N’chifukwa chiyani Yesu ananena fanizoli? Anachita zimenezi pofuna kutithandiza kudziwa kuti Yehova ndi amene amakulitsa uthenga wa Ufumu mumtima wa munthu wa “maganizo abwino.” (Mac. 13:48; 1 Akor. 3:7) N’zoona kuti timabzala ndiponso kuthirira koma sitingathe kukulitsa mbewuzo kapena kuzichititsa kuti zikule mwachangu. Mofanana ndi munthu wa mu fanizo lija, sitidziwa mmene mbewuzo zimakulira. Timangochita zinthu zathu za tsiku ndi tsiku mwina osaona mmene munthu akusinthira. Koma pakapita nthawi, timaona kuti munthuyo akubala zipatso ndipo amayamba kutithandiza pa ntchito yokolola.—Yoh. 4:36-38.
6. Kodi tiyenera kuzindikira chiyani tikamaphunzitsa anthu?
6 Kodi tikuphunzira chiyani pa fanizoli? Choyamba, tiyenera kuvomereza kuti tilibe mphamvu yochititsa munthu kusintha kapena kuyamba kukonda Mulungu. Tiyenera kukhala ozindikira n’kumapewa kukakamiza anthu kuti abatizidwe. Tizingoyesetsa kuthandiza anthu n’kuvomereza modzichepetsa kuti udindo wodzipereka kwa Yehova ndi wawo. Munthu ayenera kudzipereka kwa Mulungu chifukwa chomukonda osati pa zifukwa zina. Tikutero chifukwa chakuti zifukwa zinazo sizingasangalatse Yehova.—Sal. 51:12; 54:6; 110:3.
7, 8. (a) Kodi tikuphunziranso chiyani pa fanizo la Yesu la wofesa mbewu amene amagona? Perekani chitsanzo. (b) Kodi fanizoli likutiphunzitsa chiyani za Yehova ndi Yesu?
7 Chachiwiri, kumvetsa tanthauzo la fanizoli kungatithandize kuti tisakhumudwe ngati panopa sitikuona zotsatira za ntchito yathu. Tiyenera kukhala oleza mtima. (Yak. 5:7, 8) Ngati ifeyo tachita zonse zimene tingathe pothandiza munthu, koma munthuyo osasintha, tisaganize kuti zachitika chifukwa chakuti ndife osakhulupirika. Yehova amakulitsa mbewu za Ufumu mumtima mwa anthu odzichepetsa okha amene amalolera kusintha. (Mat. 13:23) Choncho tisamaganize kuti kusintha kwa anthu n’kumene kumasonyeza kuti utumiki wathu ukuyenda bwino. Yehova amaona kuti tikuchita bwino ngati tikuchita khama polalikira, ngakhale kuti anthu amene tikuwaphunzitsawo sakusintha.—Werengani Luka 10:17-20; 1 Akorinto 3:8.
8 Chachitatu, nthawi zina sitiona mmene uthenga wabwino ukusinthira munthu. Mmishonale wina ankaphunzitsa Baibulo banja lina. Tsiku lina banjalo linauza mmishonaleyo kuti likufuna kukhala ofalitsa osabatizidwa. Ndiyeno mmishonaleyo anawauza kuti ayenera kusiya kaye kusuta fodya. Koma anadabwa kumva banjalo likunena kuti linasiya kusutako miyezi ingapo m’mbuyomo chifukwa chozindikira kuti Yehova akhoza kuwaona akusuta. Popeza Yehova amadana ndi chinyengo, iwo anaona kuti ngati akufuna kusuta asamabisire mmishonaleyo, apo ayi angosiyiratu. Popeza anayamba kukonda kwambiri Yehova, anasankha kuti angosiyiratu kusuta. Mmishonaleyu sanadziwe kuti anthuwo asintha mpaka kufika pamenepa.
FANIZO LA KHOKA
9. Kodi fanizo la khoka limatanthauza chiyani?
9 Werengani Mateyu 13:47-50. Kodi fanizoli likutanthauza chiyani? Yesu anayerekezera kulalikira uthenga wa Ufumu kwa anthu onse ndi kuponya khoka lalikulu m’nyanja. Khoka likaponyedwa m’nyanja limakokolola “nsomba zamitundumitundu.” Tikamalalikira timakopanso anthu osiyanasiyana. (Yes. 60:5) Umboni wa zimenezi ndi anthu ambirimbiri amene amafika pa misonkhano yathu ikuluikulu komanso pa chikumbutso chaka chilichonse. Ena mwa anthu amenewa ali ngati nsomba “zabwino” ndipo amasonkhanitsidwa mumpingo wachikhristu. Koma ena amene amasonkhanitsidwa sachita zimene Yehova amafuna ndipo ali ngati nsomba “zosafunika.”
10. N’chifukwa chiyani Yesu ananena fanizo la khoka?
10 N’chifukwa chiyani Yesu ananena fanizoli? Kulekanitsa nsombazi sikuimira chiweruzo chomaliza chimene chidzachitike pa chisautso chachikulu. Koma kumaimira zimene zikuchitika m’masiku otsiriza ano. Yesu anasonyeza kuti anthu ena amene amakopeka ndi uthenga wabwino sadzafuna kutumikira Yehova. Anthu ambiri amasonkhana nafe ndiponso amavomera kuphunzira koma safuna kudzipereka kwa Yehova. (1 Maf. 18:21) Palinso anthu ena amene achoka mumpingo wachikhristu. Ndiyeno pali achinyamata ena amene abadwira m’banja la Mboni koma safuna kutsatira mfundo za Yehova. Yesu anasonyeza kuti munthu aliyense ayenera kusankha yekha kutumikira Yehova kapena ayi. Yehova amaona anthu amene asankha kumutumikira kukhala ‘amtengo wapatali.’—Hag. 2:7.
11, 12. (a) Kodi tikuphunzira chiyani pa fanizo la khoka? (b) Kodi fanizoli likutiphunzitsa chiyani za Yehova ndi Yesu?
11 Kodi tikuphunzira chiyani pa fanizo la khoka? Kumvetsa mfundo ya fanizoli kungatithandize kuti tisamakhumudwe kwambiri ngati munthu amene tikuphunzira naye kapena mwana wathu sakufuna kutumikira Yehova. Zimenezi zikhoza kuchitika ngakhale kuti tachita khama kwambiri powaphunzitsa. Sikuti munthu akavomera kuphunzira Baibulo kapena akabadwira m’banja la Mboni ndiye kuti adzakhala mtumiki wa Yehova. Ngati munthu sakufuna kumvera Yehova, sangakhale mtumiki wake.
Anthu ena amene amakopeka ndi uthenga wathu adzayamba kutumikira Yehova (Onani ndime 9 mpaka 12)
12 Kodi zimenezi zikutanthauza kuti anthu amene achoka mumpingo sangabwererenso? Kapena kodi ngati munthu sakudzipereka kwa Yehova ndiye kuti Mal. 3:7) Mfundoyi imaonekera bwino m’fanizo lina la Yesu la mwana wolowerera.—Werengani Luka 15:11-32.
azingokhalabe ngati nsomba ‘yosafunika’? Ayi. Anthu oterewa adakali ndi nthawi yosintha chisautso chachikulu chisanayambe. Zili ngati Yehova akuwauza kuti: “Bwererani kwa ine ndipo ine ndibwerera kwa inu.” (FANIZO LA MWANA WOLOWERERA
13. Kodi fanizo la mwana wolowerera limatanthauza chiyani?
13 Kodi fanizoli limatanthauza chiyani? Bambo wokoma mtima wotchulidwa m’fanizoli akuimira Yehova, yemwe ndi Atate wathu wachikondi. Mwana amene anapempha kuti apatsidwe chuma chake kenako n’kuchisakaza akuimira anthu onse amene amachoka m’gulu la Yehova. Akachoka zimakhala ngati apita ‘kudziko lakutali’ chifukwa amakhala m’dziko la Satana lomwe ndi lotalikirana ndi Yehova. (Aef. 4:18; Akol. 1:21) Koma ena nzeru zimawabwerera ndipo amayesetsa mwakhama kuti akhalenso m’gulu la Yehova. Yehova amalandira bwino anthu oterewa ndipo amawakhululukira.—Yes. 44:22; 1 Pet. 2:25.
14. N’chifukwa chiyani Yesu ananena fanizo la mwana wolowerera?
14 N’chifukwa chiyani Yesu ananena fanizoli? Iye ankafuna kusonyeza kuti Yehova amafuna kuti anthu amene asochera abwerere. Bambo wotchulidwa m’fanizoli sanasiye kuyembekezera kuti mwana wake adzabwerera. Ndiyeno ataona mwanayo akubwera “chapatali” anamuthamangira n’kumulandira. Fanizoli likulimbikitsa kwambiri anthu amene achoka m’gulu la Yehova kuti abwerere mwamsanga. Iwo amakhala atafooka ndipo akhoza kuona kuti kubwerera n’kovuta komanso n’kochititsa manyazi. Koma zoyenera kuchita ndi zomwezo chifukwa kumwamba kumakhala chisangalalo chachikulu anthu oterewa akabwerera.—Luka 15:7.
15, 16. (a) Kodi tikuphunzira chiyani pa fanizo la Yesu la mwana wolowerera? Perekani zitsanzo. (b) Kodi fanizoli likutiphunzitsa chiyani za Yehova ndi Yesu?
15 Kodi tikuphunzira chiyani pa fanizo la mwana wolowerera? Tiyenera kutsanzira Yehova. Si bwino kukhala ‘olungama mopitirira muyezo’ n’kumakana kulandira anthu ochimwa amene alapa chifukwa tikatero tikhoza Mlal. 7:16) Koma pali phunziro linanso. Munthu amene wachoka mumpingo tiyenera kumuona monga “nkhosa yosochera” osati munthu wokanika. (Sal. 119:176) Choncho tikapeza munthu amene anasochera, tiyenera kumuthandiza kuti abwerere. Chofunika n’kuuza akulu kuti apite kukamuthandiza moyenerera. Kutsatira zimene taphunzira mu fanizo la Yesu la mwana wolowerera kungatithandize kuti tichite zimenezi.
kuwononga ubwenzi wathu ndi Yehova. (16 Pali Akhristu ena omwe anali ngati mwana wolowerera ndipo amayamikira kwambiri chifundo cha Yehova komanso thandizo limene analandira mumpingo. Mwachitsanzo, m’bale wina anachotsedwa ndipo panapita zaka 25 asanabwezeretsedwe. Iye anati: “Kuyambira nthawi imene ndinabwezeretsedwa, ndikusangalala kwambiri. Ndikuona kuti ‘nyengo zotsitsimutsa’ zabwera kuchokera kwa Yehova. (Mac. 3:19) Aliyense mumpingo amandikonda ndiponso kundithandiza. Ndikuona kuti panopa ndili m’banja labwino kwambiri.” Chitsanzo china ndi cha mlongo amene anasochera n’kubwerera patapita zaka 5. Iye atabwerera anati: “Kunena zoona, chikondi chimene Yesu ankanena chija ndikuchiona bwinobwino panopa. Kukhala m’gulu la Yehova ndi mwayi wamtengo wapatali kwambiri.”
17, 18. (a) Kodi taphunzira chiyani m’mafanizo atatu amene takambirana? (b) Kodi tiyenera kuyesetsa kuchita chiyani?
17 Kodi taphunzira chiyani m’mafanizo atatuwa? Choyamba, tiyenera kukumbukira kuti sitingakulitse mbewu za uthenga wabwino. Yehova ndi amene angathe kuchita zimenezi. Chachiwiri, tiyenera kukumbukira kuti si onse amene amasonkhana nafe kapena kuphunzira omwe adzayambe kutumikira Yehova. Pomaliza, taona kuti sitiyenera kusiya kuyembekezera kuti anthu amene anachoka m’gulu la Yehova adzabwerera. Ndipo anthu oterewa akabwerera, tiyenera kutsanzira Yehova n’kuwalandira bwino.
18 Tiyeni tonse tiziyesetsa kudziwa zinthu, kumvetsa zinthuzo komanso kusonyeza kuti ndife anzeru. Tikamawerenga mafanizo a Yesu tizidzifunsa kuti: Kodi fanizoli limatanthauza chiyani? N’chifukwa chiyani linalembedwa m’Baibulo? Kodi tikuphunzira chiyani pa fanizoli? Nanga likutiphunzitsa chiyani za Yehova ndi Yesu? Tikamatero, tidzamvetsa tanthauzo la mawu a Yesu.