Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

KALE LATHU

“Yehova Anakubweretsani ku France Kuti Muphunzire Baibulo”

“Yehova Anakubweretsani ku France Kuti Muphunzire Baibulo”

MUNTHU wina wazaka 90 dzina lake Antoine Skalecki anabadwira ku France ndipo makolo ake anali a ku Poland. Iye ali mwana, bambo ake anavulala pamene mgodi unawagumukira moti sankatha kusamalira banja lawo. Ndiyeno Antoine ankafunika kugwira ntchito mumgodi kwa maola 9 pa tsiku kuti asamalire banjalo. Iye ankayenda pa hatchi pokatenga malasha mumgodi umene unali wozama mamita 500. Nthawi ina, Antoine anangotsala pang’ono kufa pamene mgodi unagumuka.

Zipangizo zimene ankagwiritsa ntchito m’migodi ndiponso mgodi wa ku Dechy kumene Antoine Skalecki ankagwira ntchito

Pa zaka za m’ma 1920 ndi m’ma 1930, anthu ambiri ochokera ku Poland anasamukira ku France. Anachita zimenezi chifukwa chakuti chiwerengero cha anthu ku Poland chinakwera kwambiri dzikolo litalandira ufulu pambuyo pa nkhondo yoyamba ya padziko lonse. Koma ku France, amuna oposa 1 miliyoni anaphedwa pa nkhondoyo ndipo kumeneko kunkafunika anthu ambiri ogwira ntchito m’migodi. Choncho mu September 1919, akuluakulu a boma la ku France ndi Poland anagwirizana kuti anthu a ku Poland akhoza kumasamukira ku France. Pofika mu 1931, kumadera a migodi kumpoto kwa dziko la France kunali anthu 507,800 ochokera ku Poland.

Anthu amenewa ankagwira ntchito mwakhama ndipo ankatsatirabe chikhalidwe ndiponso chipembedzo cha dziko lawo. Iwo ankapita kutchalitchi Lamlungu lililonse atavala zovala zogwirizana ndi chipembedzo chawocho. Koma anthu ena a ku France osapemphera ankadana nazo. Antoine ananena kuti: “Agogo anga a Joseph ankalemekeza kwambiri Malemba Opatulika amene anaphunzitsidwa ndi abambo awo.”

Kuyambira mu 1904, Ophunzira Baibulo ankalalikira mwakhama m’dera la Nord-Pas-de-Calais ndipo anthu ambiri ochokera ku Poland anayamba kumva uthenga wabwino. Pofika mu 1915, Nsanja ya Olonda inayamba kusindikizidwa m’Chipolishi pomwe Galamukani! inayamba mu 1925. Anthu ambiri ankakonda kuwerenga magaziniwa ndiponso buku lakuti Zeze wa Mulungu.

Amalume a Antoine anapita koyamba kumisonkhano ya Ophunzira Baibulo mu 1924 ndipo anauza makolo a Antoine zimene anamva kumeneko. Chaka chomwecho, Ophunzira Baibulo anachita msonkhano wawo woyamba m’Chipolishi m’tauni ya Bruay-en-Artois. Pasanathe mwezi, Joseph F. Rutherford anabwera kuchokera kulikulu kudzachititsa msonkhano m’tauni yomweyi ndipo anthu 2,000 anasonkhana. Anthu ambiri anali ochokera ku Poland ndipo M’bale Rutherford anawauza kuti: “Yehova anakubweretsani ku France kuti muphunzire Baibulo. Tsopano, inu ndi ana anu muyenera kuthandiza anthu a ku France kuno ndipo pali ntchito yaikulu yolalikira. Koma Yehova athandiza kuti pakhale anthu ambiri ogwira ntchitoyi.”

Yehova anachitadi zimenezi. Akhristu a ku Poland amenewa ankagwira ntchito yolalikira mwakhama kwambiri ngati mmene ankachitira pogwira ntchito m’migodi. Ena mwa iwo anabwerera ku Poland kuti akaphunzitse anthu mfundo zamtengo wapatali za m’Baibulo. Anthu ena amene anachoka ku France kuti akalalikire ku Poland anali Teofil Piaskowski, Szczepan Kosiak ndi Jan Zabuda.

Koma pali anthu ena a ku Poland amene anakhalabe ku France ndipo ankalalikira mwakhama limodzi ndi abale ndi alongo akumeneko. Mu 1926, ku France kunachitika msonkhano wina. Kumbali ya chilankhulo cha Chipolishi kunali anthu 1,000 ndipo kumbali ya Chifulenchi kunali anthu 300. Buku Lapachaka la 1929 linasonyeza kuti m’chaka chimenechi anthu ochokera ku Poland okwana 332 anabatizidwa. Nkhondo yachiwiri ya padziko lonse isanayambe, ku France kunali mipingo 84 ndipo pa mipingo imeneyi, 32 inali yachipolishi.

Abale ndi alongo ochokera ku Poland ali ku France ndipo akupita ku msonkhano. Pachikwangwanicho analemba kuti “Mboni za Yehova”

Mu 1947, boma la Poland linapempha kuti anthu ake abwerere ndipo abale ndi alongo ambiri anachita zimenezi. Ngakhale zinali choncho, khama lawo komanso la Akhristu a ku France linaonekera chifukwa chakuti pa ofalitsa 100 alionse panawonjezeka ena 10. Kuyambira mu 1948 kufika mu 1950, chiwerengerochi chinachoka pa 10 kufika pa 20 kenako 23 kenako pa 40. Ndiyeno mu 1948, ofesi ya nthambi ku France inasankha abale 5 kuti akhale oyang’anira madera n’cholinga choti azithandiza Akhristu atsopanowa. Pa abalewa, 4 anali ochokera ku Poland ndipo mmodzi anali wa ku France komweko. Antoine Skalecki anali mmodzi mwa iwo.

Panopa, ku France kuli a Mboni za Yehova ambiri omwe ndi ana ndiponso zidzukulu za anthu ochokera ku Poland amene ankagwira ntchito mwakhama m’migodi komanso polalikira. Masiku ano palinso anthu ambiri ochokera m’mayiko ena amene akuphunzira Baibulo ku France. Akhristu ochokera m’mayiko enawa amabwerera kwawo koma ena amakhalabe m’dzikoli. Chosangalatsa n’chakuti onse amalalikira mwakhama ngati mmene anthu ochokera ku Poland ankachitira kalelo.—Nkhaniyi yachokera ku France.