Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?
Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?
KODI nkhani yaikulu ya ulaliki wa Yesu inali chiyani? Malinga ndi zimene Yesu mwiniyo ananena, inali Ufumu wa Mulungu. (Luka 4:43) Nthawi zambiri Yesu ankatchula za Ufumu umenewu polankhula ndi anthu. Kodi anthuwo ankadabwa nazo zimenezi? Kapena ankamufunsa kuti Ufumu umenewu n’chiyani? Ayi sankatero, chifukwa chakuti m’mauthenga abwino mulibe mafunso amenewa. Choncho kodi Ufumu wa Mulungu unali wodziwika kwa anthu amenewa?
Mfundo ndi yakuti, Malemba akale amene Ayuda ankawaona kuti ndi opatulika ankalongosola Ufumu umenewu momveka bwino kuti unali chiyani ndiponso zimene udzachite. Kuwerenga Baibulo masiku ano kungatithandize kuti tidziwe zambiri za Ufumu umenewu monga momwe Ayuda anachitira. Tsopano tiyeni tikambirane mfundo 7 zokhudza Ufumu zimene Baibulo limaphunzitsa. Mfundo zitatu zoyambirira zinali zodziwika kwa Ayuda a m’nthawi ya Yesu ndiponso iye asanabwere. Mfundo zina zitatuzo n’zimene Khristu ndi atumwi ake anaphunzitsa m’nthawi yawo. Ndipo mfundo yomalizayo yadziwika bwino m’nthawi yathu ino.
1. Ufumu wa Mulungu ndi boma lenileni, limene lidzakhala kosatha. Ulosi woyambirira m’Baibulo unanena kuti Mulungu adzatumiza munthu amene adzapulumutse anthu okhulupirika. Genesis 3:15) Patapita nthawi, mfumu yokhulupirika Davide inauzidwa nkhani yosangalatsa yonena za “mbewu,” kapena kuti Mesiya. Iye adzakhala wolamulira mu Ufumu wa Mulungu. Boma limeneli lidzakhala losiyana ndi ena onse ndiponso lidzakhala kosatha.—2 Samueli 7:12-14.
Iye anatchedwa kuti ndi “mbewu,” imene idzathetsa mavuto amene anayamba chifukwa cha kupanduka kwa Satana ndiponso Adamu ndi Hava. (2. Ufumu wa Mulungu udzathetsa maboma onse a anthu. Mneneri Danieli anaonetsedwa masomphenya a maufumu a mphamvu kwambiri padziko lonse amene adzalamulire motsatizana mpaka m’nthawi yathu ino. Taonani zimene zikuchitika masomphenyawo atafika pachimake: “Masiku a mafumu [omaliza] aja Mulungu wa kumwamba adzaika ufumu woti sudzawonongeka ku nthawi zonse, ndi ulamuliro wake sudzasiyidwira mtundu wina wa anthu, koma udzaphwanya ndi kutha maufumu awo onse, nudzakhala chikhalire.” Motero maufumu, kapena maboma onse a padzikoli, amene amachititsa kuti pakhale nkhondo, kuponderezana ndi katangale adzawonongedwa kotheratu. Monga mmene ulosi wa Danieli ukusonyezera, posachedwapa Ufumu wa Mulungu udzalamulira padziko lonse lapansi. (Danieli 2:44, 45) Boma limeneli ndi lenileni ndiponso ndi lokhali limene silidzatha. *
3. Ufumu wa Mulungu udzathetsa nkhondo, matenda, njala, ngakhale imfa imene. Maulosi a m’Baibulo ochititsa chidwi amasonyeza zimene Ufumu wa Mulungu udzachite padziko lapansi pano. Boma limeneli lidzachita zinthu zimene maboma onse a anthu alephera kuchita ndiponso sangachite n’komwe. Tangoganizirani zida zonse za nkhondo zitawonongedwa kotheratu. “Aletsa nkhondo ku malekezero adziko lapansi.” (Salmo 46:9) Sikudzakhalanso madokotala, zipatala, kapena matenda ena alionse. “Wokhalamo sadzanena, ine ndidwala.” (Yesaya 33:24) Sikudzakhalanso njala, kusowa chakudya, kutupikana, kapena chilala chifukwa “m’dzikomo mudzakhala dzinthu dzochuluka pamwamba pa mapiri.” (Salmo 72:16) Sitidzakhalanso ndi chisoni chifukwa sikudzakhalanso maliro, manda, kapena nyumba za chisoni. Imfa yomwe ndi mdani wathu wamkulu idzathetsedwa. Mulungu “[adzameza] imfa ku nthawi yonse; ndipo Ambuye Mulungu adzapukuta misozi pa nkhope zonse.”—Yesaya 25:8.
4. Wolamulira wa Ufumu wa Mulungu anasankhidwa ndi Mulungu. Mesiya sanadzisankhe yekha kukhala Mfumu komanso sanasankhidwe ndi anthu, koma anasankhidwa ndi Yehova Mulungu. Ndipo maina ake aulemu akuti Mesiya ndi Khristu amasonyezanso kuti anachita kusankhidwa ndi Mulungu. Maina onsewa amatanthauza kuti “Wodzozedwa.” Choncho Mfumu imeneyi ndi yodzozedwa, kapena kuti inaikidwa pampando umenewu ndi Yehova. Ponena za Mesiyayu Mulungu anati: “Tawona mtumiki wanga, amene ndim’gwiriziza; wosankhika wanga, amene moyo wanga ukondwera naye; ndaika mzimu wanga pa iye; iye adzatulutsira amitundu chiweruziro.” (Yesaya 42:1; Mateyo 12:17, 18) Ndithudi ndi Mlengi wathu yekha amene akudziwa bwino wolamulira amene anthufe tikufunikira.
5. Wolamulira wa Ufumu wa Mulungu wasonyeza kale kuti ndi woyenera kulamulira anthu. Yesu wa ku Nazarete anasonyeza kuti anali Mesiya amene analonjezedwa ndi Mulungu chifukwa anabadwira m’banja limene Mulungu analisankha. (Genesis 22:18; 1 Mbiri 17:11; Mateyo 1:1) Ali padziko lapansi, anakwaniritsa maulosi ambiri onena za Mesiya amene analembedwa zaka zambirimbiri iye asanabadwe. Mulungu ananenanso kuchokera kumwamba kuti Yesu anali Mesiya. Kodi anachita bwanji zimenezi? Mulungu analankhula kuchokera kumwamba kuti iye anali Mwana Wake. Angelo nawonso ananena kuti Yesu anali Mesiya wolonjezedwa. Ndipo Yesu iye mwini nthawi zambiri ankachita zozizwitsa pali namtindi wa anthu zomwe zinali kuonekeratu kuti anali ndi mphamvu ya Mulungu. * Yesu nthawi zambiri anasonyeza kuti adzakhala wolamulira wabwino. Iye sikuti anali ndi mphamvu zothandizira anthu chabe koma ankafunitsitsanso kuwathandiza. (Mateyo 8:1-3) Iye anali wosadzikonda, wachifundo, wolimba mtima ndiponso wodzichepetsa. Nkhani ya moyo wa Yesu padziko lapansi ili m’Baibulo kuti tonse tiziwerenga.
6. Ufumu wa Mulungu uli ndi anthu 144,000 amene adzalamulire pamodzi ndi Khristu. Yesu ananena kuti anthu ena kuphatikizapo atumwi, Luka 12:32) Kenako, mtumwi Yohane anauzidwa kuti kagulu ka nkhosa kameneka ndi ka anthu 144,000 basi. Iwowa ali ndi ntchito yosangalatsa yoti akachite kumwamba, kulamulira monga mafumu ndi kutumikira monga ansembe pamodzi ndi Khristu.—Chivumbulutso 5:9, 10; 14:1, 3.
adzalamulira naye limodzi kumwamba. Anthu amenewa anawatchula kuti “kagulu ka nkhosa.” (7. Panopa Ufumu wa Mulungu ukulamulira kumwamba ndipo watsala pang’ono kuyamba kulamulira padziko lonse lapansi. Mfundo yomalizayi ndi imodzi mwa mfundo zosangalatsa kwambiri kuziphunzira. Baibulo limapereka umboni wambiri wakuti Yesu wapatsidwa mphamvu zolamulira monga Mfumu kumwamba. Panopa, iye akulamulira kumwamba ndipo posachedwapa ayamba kulamulira padziko lonse lapansili pokwaniritsa maulosi abwino kwambiri amene takambirana kale. Koma kodi tingatsimikize bwanji kuti Ufumu wa Mulungu ukulamulira kumwamba panopa? Nanga udzayamba liti kulamulira padziko lapansili?
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 5 Ulosi ngati umenewu amasonyeza kuti Ufumu wa Mulungu si chinthu chinachake chimene chili mu mtima monga mmene anthu ena aphunzirira. Onani nkhani yakuti “Mafunso Ochokera kwa Owerenga,” patsamba 13.
^ ndime 8 Mwachitsanzo, werengani Mateyo 3:17; Luka 2:10-14; ndi Yohane 6:5-14.