Kodi Ufumu wa Mulungu Udzabwera Liti?
Kodi Ufumu wa Mulungu Udzabwera Liti?
ATUMWI ankafunitsitsa kudziwa kuti Yesu adzayamba liti kulamulira. N’chifukwa chake anafunsa kuti: “Ambuye, kodi mubwezeretsa ufumu kwa Isiraeli panthawi ino?” (Machitidwe 1:6) Tikunena pano papita zaka zoposa 2,000, koma anthu akufunitsitsabe kudziwa kuti: Kodi Ufumu wa Mulungu udzabwera liti?
Muyenera kuti mukuganiza kuti Yesu anayankha funso limeneli chifukwa nkhani yaikulu ya ulaliki wa wake inali yonena za Ufumu. Ndipo iye anayankhadi. Nthawi zambiri iye ankafotokozera anthu za nyengo imene anaitchula kuti nthawi ya “kukhalapo” kwake. (Mateyo 24:37) Nthawi imeneyi ndi yogwirizana kwambiri ndi kukhazikitsidwa kwa Ufumu wa Mesiya. Kodi nthawi ya kukhalapo kwake imeneyi n’chiyani? Tsopano tiyeni tikambirane mfundo zinayi za m’Baibulo zimene zimalongosola za nthawi ya kukhalapo kwa Khristu.
1. Khristu atamwalira, panadutsa nthawi yaitali kwambiri kuti nthawi ya kukhalapo kwake ifike. Yesu anafotokoza fanizo limene iye anadziyerekezera ndi munthu amene “anapita kudziko lakutali kuti akalandire ufumu.” (Luka 19:12) Kodi fanizo la ulosili linakwaniritsidwa bwanji? Yesu atamwalira, anaukitsidwa ndipo anapita “kudziko lakutali,” kumene ndi kumwamba. Mogwirizana ndi ulosi umene Yesu anafotokoza mu fanizo lofanana ndi limeneli, ‘padzapita nthawi yaitali’ kuti adzabwere ali mfumu.—Mateyo 25:19.
Patapita zaka zingapo Yesu atakwera kumwamba, mtumwi Paulo analemba kuti: “Koma munthu ameneyu [Yesu] anapereka nsembe imodzi ya machimo kwa muyaya, nakhala pansi kudzanja lamanja la Mulungu. Kuyambira pamenepo, akuyembekeza mpaka pamene adani ake adzaikidwa kukhala Aheberi 10:12, 13) Choncho Yesu atapita kumwamba anadikira nthawi yaitali kuti akhale mfumu. Kudikirako kunatha pamene Yehova Mulungu anaika Mwana wakeyu kukhala Mfumu ya Ufumu wa Mesiya umene analonjeza kalekale. Apa m’pamene panayambira nthawi ya kukhalapo kwake. Kodi anthu padziko lapansi anaona ndi maso awo zimenezi?
chopondapo mapazi ake.” (2. Kukhalapo kwake ndi kosaoneka ndi maso athu. Kumbukirani kuti Yesu anafotokoza za chizindikiro cha kukhalapo kwake. (Mateyo 24:3) Ngati kukhalapo kwake kukanakhala kooneka ndi maso athu, kodi chizindikiro chikanafunika? Mwachitsanzo: Yerekezerani kuti muli paulendo wokaona nyanja. Mwachionekere mudzapeza zikwangani zokusonyezani kumene kuli nyanjayo. Koma mukangofika kunyanjako, mwina tinene kuti mwaima m’mphepete mwa nyanjayo, kodi mungayembekezere kuona chikwangwani chokulozerani kuti nyanja ndi iyi? Zimenezo sizingatheke. N’kuikiranji chikwangwani pa zinthu zimene mukuziona ndi maso anu?
Yesu pofotokoza chizindikiro cha kukhalapo kwake, sankanena zinthu zimene anthu angazione ndi maso awo, koma ankawathandiza kuti adzazindikire kuti kumwamba kukuchitika zinazake. N’chifukwa chake Yesu anati: “Ufumu wa Mulungu sudzabwera mwa maonekedwe ochititsa chidwi ayi.” (Luka 17:20) Ndiyeno kodi anthu amene ali padziko lapansi adzazindikira bwanji kuti nthawi ya kukhalapo kwa Khristu yayamba?
3. Nthawi ya kukhalapo kwa Yesu idzadziwika ndi mavuto aakulu padziko lapansi lino. Yesu ananena kuti anthu padziko lapansi adzazindikira kuti nthawi ya kukhalapo kwake monga Mfumu kumwamba yayamba chifukwa padzakhala nkhondo, njala, zivomezi, milili, ndi kusamvera malamulo. (Mateyo 24:7-12; Luka 21:10, 11) Kodi n’chiyani chidzachititsa mavuto onsewa? Baibulo limafotokoza kuti Satana yemwe ndi “wolamulira wa dzikoli” ali ndi mkwiyo waukulu chifukwa akudziwa kuti panopa nthawi yake yatsala yochepa kwambiri popeza kuti nthawi ya kukhalapo kwa Khristu monga Mfumu inayamba kale. (Yohane 12:31; Chivumbulutso 12:9, 12) Zinthu zimene Satana akuchita posonyeza mkwiyo wake ndiponso zizindikiro za kukhalapo kwa Khristu ndi zochuluka masiku ano. Makamaka kuyambira mu 1914 zizindikiro zimenezi zakhala zochuluka kwambiri padziko lonse kuposa kale ndipo chaka chimenechi n’chimene akatswiri ambiri yakale amati m’pamene panasinthira zinthu kwambiri padziko lonse.
Zimenezi ndi zinthu zosangalatsa ngakhale kuti zikuoneka ngati ndi zinthu zoipa. Tikutero chifukwa zikusonyeza kuti tsopano Ufumu wa Mesiya ukulamulira kumwamba. Posachedwapa boma limeneli lidzalamulira padziko lonse lapansi lino. Nangano anthu angadziwe bwanji za Ufumu umenewu n’cholinga choti avomereze boma limeneli ndi kukhala nzika zake?
4. Nthawi ya kukhalapo kwa Yesu idzadziwika ndi ntchito yolalikira imene idzachitike padziko lonse. Yesu anati nthawi ya kukhalapo kwake idzakhala ngati “masiku a Nowa.” * (Mateyo 24:37-39) Nowa anamanga chingalawa komanso anali “mlaliki wa chilungamo.” (2 Petulo 2:5) Nowa anachenjeza anthu kuti chiweruzo cha Mulungu chinali pafupi kuchitika. Yesu ananena kuti otsatira ake adzachita zofanana ndi zimenezi padziko lapansi mu nthawi ya kukhalapo kwake. Iye analosera kuti: “Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukakhale umboni ku mitundu yonse; kenako mapeto adzafika.”—Mateyo 24:14.
Monga taonera m’nkhani yapitayi, Ufumu wa Mulungu udzawononga maboma onse a dzikoli. Ntchito yolalikira imachenjeza anthu kuti posachedwapa Ufumu wa kumwambawu udzawononga anthu oipa. Ntchitoyi imaperekanso mwayi woti anthu adzapulumuke chiwonongeko chimene chikubwerachi ndi kukhala nzika za Ufumuwu. Komano funso lofunika kuliganizira n’loti, Kodi inuyo mudzachita chiyani?
Kodi Inuyo Mudzakhalamo mu Ufumu wa Mulungu?
Uthenga umene Yesu analalikira umathandiza anthu kukhala ndi chiyembekezo choposa china chilichonse. Anthu atapanduka mu Edeni zaka zambiri zapitazo, Yehova Mulungu anakhazikitsa boma limene lidzakonzenso zinthu. Boma limeneli lidzakwaniritsa cholinga chimene Mulungu anali nacho poyamba choti anthu okhulupirika akhale ndi moyo wosatha m’paradaiso pompano padziko lapansi. N’zosangalatsa kwabasi kudziwa kuti ufumu umene unalonjezedwa kalekale tsopano ukulamulira kumwamba. Ndipotu ufumu umenewu si chinthu chinachake chosadziwika bwinobwino, koma ndi weniweni ndipo ulipo.
Tsopano Mfumu imene Mulungu anaisankha ikulamulira pakati pa adani ake. (Salmo 110:2) M’dziko loipa lino limene anthu ake amachita zimene Mulungu amadana nazo, Mesiya akuchita zimene Atate ake akufuna zofufuza anthu amene ali ndi chidwi chofuna kudziwadi Mulungu ndi kum’lambira mu “mzimu ndi choonadi.” (Yohane 4:24) Anthu a mitundu yonse, a msinkhu uliwonse, ndiponso ochokera malo osiyanasiyana angakhale ndi chiyembekezo chodzakhala ndi moyo wosatha mu Ufumu wa Mulungu. (Machitidwe 10:34, 35) Tikukulimbikitsani kuti mulandire mwayi umene muli nawo panopa. Phunzirani za Ufumu wa Mulungu n’cholinga choti mudzasangalale kosatha mu Ufumu wolungama umenewu.—1 Yohane 2:17.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 10 Mawu a Yesu amenewa akutithandiza kuchotsa maganizo olakwika a mmene Mabaibulo ena anamasulirira mawu akuti “kukhalapo.” Mabaibulo ena anamasulira mawuwa kuti “kubwera,” kapena “kubweranso,” zimene zimatanthauza zochitika za kanthawi kochepa. Komano, onani kuti Yesu sanayerekezere nthawi ya kukhalapo kwake ndi Chigumula cha m’tsiku la Nowa, chomwe chinangochitika kamodzi, koma anayerekezera ndi “masiku a Nowa,” omwe anali nthawi yaitali. Mofanana ndi nthawi ya kale imeneyi, kukhalapo kwa Khristu ndi nthawi yaitali imene anthu adzakhala otanganidwa kwambiri ndi zinthu zochitika tsiku ndi tsiku moti sadzatha kulabadira chenjezo.
[Zithunzi pamasamba 8, 9]
Nkhani zoipa zimene timamva tsiku ndi tsiku ndi umboni woti zinthu zabwino zili pafupi
[Mawu a M’munsi]
Antiaircraft gun: U.S. Army photo