Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Baibulo Limasintha Anthu

Baibulo Limasintha Anthu

Baibulo Limasintha Anthu

Mnyamata wina wa ku Mexico, amene poyamba anali m’gulu la achinyamata lotchedwa Ana a Satana, anasintha n’kukhala munthu woona mtima komanso wolimbikira ntchito. Kodi n’chiyani chinamuthandiza kuti asinthe? Nanga n’chiyani chinachititsa mayi wina wa bizinesi ku Japan kuti asiye moyo wongokhalira kufunafuna chuma? Ndipo kodi panopa akumva bwanji chifukwa cha kusintha kumeneku? N’chiyani chinachititsa munthu wina wa ku Russia kusiya kuchita malonda ozembetsa zida zankhondo amene ankamupangira ndalama zambiri? Tamvani zimene eniakewo ananena.

ZA MUNTHUYU

DZINA: ADRIAN PEREZ

ZAKA: 30

DZIKO: MEXICO

POYAMBA: ANALI M’GULU LA ZIGAWENGA

KALE LANGA: Ndili ndi zaka 13 banja lathu linasamukira ku Ecatepec de Morelos m’dziko la Mexico. Panthawiyi kuderali kunali anyamata ambiri olowerera ndipo anthu ambiri ankasakaza zinthu komanso kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo. Nanenso ndinayamba kuledzera, kusakaza zinthu komanso chiwerewere.

Kenako tinabwerera kwathu ku tawuni ya San Vicente. Koma nakonso kunali anthu ambiri amene ankagwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo. M’derali sizinali zachilendo kuona anyamata atafa, ali kwala pamsewu. Ndinalowa m’gulu la achinyamata lotchedwa Ana a Satana. Tinkakonda kuba ndiponso kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo. Chifukwa cha zimenezi, nthawi zambiri sindinkazindikira mmene ndafikira kunyumba ndipo nthawi zina ndinkagona panjira. Anzanga ambiri anamangidwa chifukwa cha kuba ndiponso kupha anthu.

Ngakhale kuti ndinkachita zonsezi, ndinkakhulupirira Mulungu. Pofuna kuti chikumbumtima chisamandivutitse, sabata loyera likafika, ndinkachita nawo miyambo ina yachipembedzo monga njira ya mtanda. Pamapeto pa mwambo umenewu tonse kuphatikizapo amene ankayerekezera kukhala Khristu pamwambowo, tinkasangalala mpaka kufika poledzera.

MMENE BAIBULO LINASINTHIRA MOYO WANGA: Ndili pafupi kukwanitsa zaka 20, ndinayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Ndinazindikira kuti ndinalibe cholinga chenicheni pamoyo ndipo ndinaona kuti ngati sindisintha, zinthu sizindiyendera bwino. Mawu a pa Agalatiya 6:8 ndi amene anandigwira mtima kwambiri. Lembalo limati: “Iye amene akufesera thupi lake adzakolola chivundi kuchokera m’thupi lakelo, koma iye amene akufesera mzimu adzakolola moyo wosatha ku mzimuwo.” Mawu amenewa anandithandiza kuona kuti ndifunika kufesa moganizira zam’tsogolo kuti zinthu zindiyendere bwino.

Nditayamba kuphunzira Baibulo ndinazindikira kuti Yehova ndi Mulungu wamoyo ndipo amandiganizira ineyo pandekha. Ndinazindikiranso kuti ndi wokonzeka kundikhululukira machimo anga akale. Ndinaphunzira kuti iye amamva ndi kuyankha mapemphero.

Kusintha moyo wanga sinali nkhani yamasewera. Ndinavutika kuti ndisiyane ndi gulu lija. Gululo linali ndi malire a dera lake ndipo panali madera ena amene sindinkayerekeza kufikako ngakhale kuti ndinachoka m’gululo. Nthawi zina ndikaona anzangawo ndinkabisala chifukwa ankafuna kuti ndibwerere m’gululo n’kuyambiranso zomwe ndinkachita.

Koma nditayamba kusonkhana ndi Mboni ku Nyumba ya Ufumu ndinaona kuti ndi mpingo wachikondi kwambiri. Ndinachita chidwi kuona kuti anthuwo anali ndi chikhulupiriro cholimba kwambiri ndipo ankachita zimene amaphunzitsa. Zinali zosiyana kwambiri ndi zimene ndinkachita poyamba.

PHINDU LIMENE NDAPEZA: Panopo ndinabatizidwa ndipo ndakhala wa Mboni za Yehova kwa zaka 10 tsopano. Ndimayesetsa kwambiri kutsatira zimene Baibulo limaphunzitsa. Chifukwa cha zimenezi, anthu a m’banja lathu amandilemekeza. Akuona kuti panopo ndine munthu wakhama pantchito ndipo ndimawapatsa thandizo la ndalama. Mayi anga anayamba kuphunzira Baibulo ndipo anabatizidwa n’kukhala wa Mboni za Yehova. Nawonso bambo anga anayamba kusintha moyo wawo. Abale anga ambiri si a Mboni za Yehova koma chifukwa choona mmene ndasinthira, amavomereza kuti Baibulo limasinthadi munthu n’kukhala wabwino kwambiri.

ZA MUNTHUYU

DZINA: YAYOI NAGATANI

ZAKA: 50

DZIKO: JAPAN

POYAMBA: ANALI MAYI WA BIZINESI YAPAMWAMBA

KALE LANGA: Ndinakulira mumzinda wina wa anthu ansangala. Bambo anga anali ndi sitolo yaikulu ndipo anali ndi antchito 10. Nyumba yathu inali pafupi ndi sitoloyo moti ngakhale kuti bambo ndi mayi ankatanganidwa kwambiri, ine sindinkasowa ocheza nawo.

M’banja lathu muli ana aakazi atatu ndipo ine ndi woyamba kubadwa. Makolo anga anandiphunzitsa kuyendetsa bizinesi yathu. Ndinakwatiwa ndidakali wamng’ono. Ndipo mwamuna wanga anasiya ntchito yomwe ankagwira ku banki n’cholinga choti azithandizira kuyendetsa bizinesi yathu. Pa zaka zochepa chabe tinali ndi ana atatu. Mayi anga ndi amene ankasamalira ana angawo komanso kugwira ntchito zapakhomo ndipo ine ndinkagwira ntchito m’sitoloyo kuyambira m’mawa mpaka usiku. Ngakhale zinali choncho, tinkakhala ndi nthawi yopuma n’kumacheza monga banja.

Kenako chuma cha m’deralo chinalowa pansi ndipo zimenezi zinakhudza bizinesi yathu. Zitatero tinaganiza zomanga sitolo yogulitsira zipangizo zomangira nyumba pafupi ndi msewu waukulu. Koma kutangotsala tsiku limodzi kuti ntchito yomanga sitoloyo iyambe, bambo anga omwe anali mkulu wa kampaniyo, anayamba kudwala matenda okhudza ubongo. Kuyambira pamenepo sankatha kulankhula bwinobwino ndipo udindo wonse woyang’anira sitolo yatsopanoyo unali m’manja mwanga. Mwamuna wanga anapitirizabe kuyang’anira sitolo yoyamba ija moti moyo wathu unali wopanikiza kwambiri.

Malonda ankayenda bwino kwambiri m’sitolo yathu yatsopanoyo. Ndinkanyadira kwambiri ndikaganizira mmene ndinathandizira kuti bizinesiyo itukuke ndipo sindinkagona mokwanira pofuna kuti iziyenda. Ngakhale kuti ndinkakonda kwambiri ana anga, maganizo anga onse anali pa ntchito basi. Ndinalibe nthawi yocheza bwino ndi mwamuna wanga ndipo tikati tilankhulane tinkangokhalira kukangana. Pofuna kuchepetsa nkhawa ndinkapita kukamwa mowa ndi anzanga komanso anthu amene ndinkagwira nawo ntchito. Ndinkachita zimenezi pafupifupi usiku uliwonse. Pamoyo wanga, ndinkangokhalira kugwira ntchito, kumwa mowa ndi kugona basi. Sindinkadziwa chifukwa chimene ndinkakhalira wosasangalala ngakhale kuti ndinkapeza ndalama zambiri.

MMENE BAIBULO LINASINTHIRA MOYO WANGA: Nditayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova, panali malemba atatu amene anandigwira mtima kwambiri. Ndinalira nditamvetsa tanthauzo la mawu a pa Mateyo 5:3. Lembalo limati: “Osangalala ali iwo amene amazindikira zosowa zawo zauzimu, popeza ufumu wa kumwamba ndi wawo.” Mawu amenewa anandithandiza kudziwa chifukwa chake sindinali wosangalala ngakhale kuti ndinali ndi ndalama zambiri komanso ndinkapatsidwa ulemu ndi anzanga. Ndinaphunzira kuti ndingakhale wosangalala ngati nditazindikira zosowa zanga zauzimu n’kuzikwaniritsa.

Panthawi imeneyi n’kuti chuma cha dziko la Japan chitalowa pansi ndipo ndinaona kuti mawu a pa 1 Timoteyo 6:9 akukwaniritsidwa pa anzanga. Palembali pali mawu akuti: “Anthu ofunitsitsa kulemera, amagwera m’mayesero ndi mu msampha, ndi m’zilakolako zambiri zopanda nzeru ndi zopweteka, zimene zimaponya anthu ku chiwonongeko chotheratu.” Ndinaonanso kuti mawu a Yesu pa Mateyo 6:24 akundikhudza ndipo ndiyenera kusintha. Mawuwo amati: “Simungathe kutumikira Mulungu ndi Chuma nthawi imodzi.”

Ndinazindikiranso kuti ndinkanyalanyaza makolo anga, mwamuna wanga ndiponso ana anga. Ndinaonanso kuti khalidwe langa linasinthiratu. Ndinkachita makani kwambiri. Sindinali woleza mtima ndi anthu ndipo sindinkachedwa kukwiya. Poyamba ndinkaganiza kuti sindingasinthe n’kukhala Mkhristu. Komabe, ndinkakonda kwambiri ana anga ndipo ndinaona kuti pamene ndinayamba kutsatira malangizo a m’Baibulo posamalira banja langa, ana anga anayambanso kusangalala. Ndinkapeza nthawi yocheza nawo komanso ndinkawatengera ku misonkhano yachikhristu.

PHINDU LIMENE NDAPEZA: Panopo ndine wosangalala kwambiri chifukwa ndili ndi cholinga chabwino pamoyo, ndikutumikira Mulungu, ndiponso ndimachita zinthu zokondweretsa Mulungu. Sindinyalanyazanso banja langa chifukwa cha ntchito ndipo masiku ano anthu ayambanso kundipatsa ulemu.

Mayi anga ataona kuti moyo wanga wasintha chifukwa chotsatira mfundo za m’Baibulo anayambanso kuphunzira ndipo panopo ndi Mkhristu. Chosangalatsa n’chakuti bambo anga ndiponso mwamuna wanga satsutsa zimene tinasankha. Masiku ano ndimagwirizana kwambiri ndi ana anga ndipo banja lathu lonse ndi losangalala.

ZA MUNTHUYU

DZINA: MIKHAIL ZUYEV

ZAKA: 51

DZIKO: RUSSIA

POYAMBA: ANKACHITA MALONDA OZEMBETSA ZIDA ZA NKHONDO

KALE LANGA: Mumzinda wa kwathu wotchedwa Krasnogorsk muli mitengo yambiri yobiriwira moti midzi ya kumpoto ndi kumadzulo sioneka chifukwa cha mitengoyo. Chakum’mwera kwa mzindawu kuli mtsinje wa Moscow.

Ndili wamng’ono, ndinkakonda kuchita masewera a nkhonya komanso kuseweretsa zida zankhondo. Nthawi zambiri ndinkangokhalira kuchita masewero olimbitsa thupi. Ndinkapanganso mfuti, zipolopolo ndi mipeni. M’kupita kwanthawi ndinayamba kugulitsa zida zankhondo zimene ndinkapanga. Ndinkachita zinthu mosamala pogulitsa zida kwa zigawenga ndipo malonda anga ankayenda bwino kwambiri.

MMENE BAIBULO LINASINTHIRA MOYO WANGA: Chakumayambiriro kwa m’ma 1990 ndinakumana ndi Mboni za Yehova, koma poyamba ndinkawakayikira. Ndinkaona kuti akundipanikiza ndi mafunso.

Tsiku lina wa Mboni wina anabweranso n’kundiwerengera lemba la Aroma 14:12 lomwe limati: “Aliyense wa ife adzadziyankhira yekha kwa Mulungu.” Ndinadzifunsa kuti kodi ndidzayankha chiyani kwa Mulungu? Lemba limeneli linandichititsa kuti ndiyambe kuphunzira zimene Mulungu amafuna kuti ndizichita.

Ndinayesetsa kutsatira malangizo a m’Baibulo opezeka pa Akolose 3:5-10 onena kuti: “Choncho chititsani ziwalo za thupi lanu pa dziko lapansi kukhala zakufa ku dama, chonyansa, chilakolako cha kugonana, chikhumbo choipa, ndi kusirira kwa nsanje, kumene ndiko kulambira mafano. Chifukwa cha zinthu zimenezi, mkwiyo wa Mulungu ukubwera. . . . Zonsezo muzitaye kutali ndi inu, mkwiyo, kupsa mtima, kuipa, ndi mawu achipongwe; ndipo pakamwa panu pasatuluke nkhani zotukwana. Musamanamizane wina ndi mnzake. Vulani umunthu wakale pamodzi ndi ntchito zake, ndipo muvale umunthu watsopano.”

Sizinali zophweka kuti ndisinthe chifukwa anzanga amene ndinkachita nawo bizinesi ankandipatsabe ndalama n’cholinga choti ndiwapatse zida. Ngakhale kuti zinkandipweteka kwambiri akamandinyoza, ndinawononga zida zonse zimene ndinali nazo. Ndinayamba kukonda kwambiri Mulungu ndi Khristu chifukwa chophunzira kuti iwonso amandikonda. Ndinapitiriza kuphunzira Baibulo pandekha, kupita kumisonkhano yampingo ndipo ndinkapemphera kwa Mulungu kuti andithandize.

PHINDU LIMENE NDAPEZA: Kusintha kunali kovuta kwambiri komabe mothandizidwa ndi abale achikhristu, ndinasintha khalidwe langa. Ndinasangalala kwambiri kudziwa kuti Yehova Mulungu amatisamalira ndipo amakondanso ngakhale athu amene anamwalira. (Machitidwe 24:15) Ndimasangalala kuona kuti Mboni za Yehova ndi anthu omasuka ndiponso oona mtima. Ndimayamikira kwambiri chifukwa chakuti iwo anasonyeza kuti amandikonda ndipo ndi okhulupirika kwa Mulungu.

Poyamba, abale anga ndiponso anzanga ankatsutsa chikhulupiriro changa chatsopanocho. Komabe anaona kuti ndi bwino kuti ndizichita zinthu zachipembedzo m’malo mopitiriza kuthandiza anthu achiwembu. Ndipo panopo ndine wosangalala chifukwa sindigulitsanso zida zankhondo koma ndimachita khama kuthandiza anthu kudziwa Mulungu wamtendere.

[Chithunzi patsamba 27]

Kuti chikumbumtima chisamandivutitse ndinkachita nawo miyambo ina yachikatolika

[Chithunzi patsamba 28]

Ndinkapeza ndalama zambiri koma sindinkasangalala