Ngati Katchulidwe ka Dzina la Mulungu Sikadziwika Bwinobwino, N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuligwiritsira Ntchito?
Zimene Owerenga Amafunsa
Ngati Katchulidwe ka Dzina la Mulungu Sikadziwika Bwinobwino, N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuligwiritsira Ntchito?
Masiku ano palibe aliyense amene akudziwa mmene dzina la Mulungu linkatchulidwira m’Chiheberi chakale. Komatu dzina lenileni la Mulungu limapezeka pafupifupi nthawi 7,000 m’Baibulo. Yesu ali padziko lapansi pano anawadziwitsa anthu dzina la Mulungu, ndipo analangiza ophunzira ake kuti azipemphera kuti dzina limeneli liyeretsedwe. (Mateyo 6:9; Yohane 17:6) Motero n’zosachita kufunsa kuti m’pofunika kwambiri kuti Akhristu ayenera kugwiritsira ntchito dzina la Mulungu. Komano n’chifukwa chiyani katchulidwe koyambirira ka dzinali sikadziwika masiku ano? Pali zifukwa ziwiri zazikulu.
Chifukwa choyamba ndi choti zaka 2000 zapitazo, Ayuda ambiri anayamba kukhulupirira kuti n’kulakwa kutchula dzina la Mulungu. Moti munthu akamawerenga Baibulo n’kufika pamene pali dzinalo sankalitchula m’malomwake ankangonena kuti “Ambuye.” Chifukwa cha zimenezi anthu anasiya kugwiritsa ntchito dzina la Mulungu ndipo patapita zaka zambirimbiri katchulidwe kake kanaiwalika.
Chifukwa chachiwiri n’chakuti Chiheberi chakale chinalibe zilembo monga a, e, i, o ndi u zimene zimathandiza pa katchulidwe ka mawu m’Chichewa ndi zinenero zina. Ndiyeno munthu akamawerenga ankangokumbukira yekha kuti mawu awa akufunikira zilembo zakutizakuti kuti atchulike. M’kupita kwa nthawi, panaikidwa njira yothandiza kuti katchulidwe ka mawu a Chiheberi kasaiwalike. Njira yake inali yowonjezera zilembo zothandiza pakatchulidwe ka liwu lililonse la m’Baibulo la Chiheberi. Komano akapeza dzina la Mulungu ankangolembapo zilembo zowathandiza kutchula mawu akuti “Ambuye” kuti wowerengayo atchule mawu amenewa, apo ayi ankangosiya zilembo zoimira dzina la Mulungulo, koma osalembapo zilembo zilizonse zothandiza pa katchulidwe.
Motero panangotsala zilembo zinayi zokha zimene zimaimira dzina la Mulungu. Buku lina lofotokoza mawu linati “zilembo zinayi za Chiheberi zoimira dzina la Mulungu, zomwe nthawi zambiri zimalembedwa kuti YHWH kapena JHVH ndi zimene zimagwiritsidwa ntchito potchula dzina lenileni la Mulungu.” Apa titha kuona kuti tikalemba zilembo zimene zikusoweka pa zilembo zimenezi timapanga dzina lakuti “Yehova,” lomwe anthu ambiri amagwiritsira ntchito m’Chichewa.
Komano pali akatswiri ena amene amanena kuti ndi bwino kunena kuti “Yahweh” osati Yehova. Kodi mawu akuti Yahweh ndi amene akufanana kwambiri ndi katchulidwe koyambirira ka dzina la Mulungu? Palibe amene anganene zimenezi motsimikiza. Ndipotu pali akatswiri ena amene atchulapo mfundo zina zotsutsa katchulidwe kameneka. Komanso tikudziwa kuti katchulidwe ka mayina a m’Baibulo m’zilankhulo zathu, sikafanana m’pang’ono pomwe ndi katchulidwe ka m’Chiheberi chakale, ndipo anthu ambiri satsutsa zimenezi. Zili choncho chifukwa chakuti tazolowera kutchula mayinawo ndipo mayinawo tsopano angokhala a m’zilankhulo zathu. Izi n’zimene zachitikanso ndi dzina lakuti Yehova.
M’nthawi ya atumwi, Akhristu ankatchedwa anthu a dzina la Mulungu. Iwo ankalalikira kwa ena za dzinali ndipo ankawalimbikitsa kuitana pa dzinalo. (Machitidwe 2:21; 15:14; Aroma 10:13-15) Motero n’zosachita kufunsa kuti Mulungu amaona kuti m’pofunika kugwiritsira ntchito dzina lake m’chilankhulo chilichonse chimene timalankhula, kudziwa zimene limatanthauza ndiponso kusonyeza khalidwe logwirizana ndi tanthauzo la dzinali pamoyo wathu.
[Mawu Otsindika patsamba 31]
Dzina lenileni la Mulungu limapezeka pafupifupi nthawi 7,000 m’Baibulo