Baibulo Linaneneratu za Mesiya
Baibulo Linaneneratu za Mesiya
MTUNDU wa Ayuda unayembekezera kwa nthawi yaitali kubwera kwa Mesiya chifukwa Yesaya ndi aneneri ena anali atalemba kale za kubwera kwake. Ndipotu pofika nthawi ya Yesu, Ayuda ambiri “anali kuyembekezera” kuti Mesiya afika posachedwa. (Luka 3:15) N’zochititsa chidwi kuti maulosi a m’Baibulo anafotokoza momveka bwino za moyo wa Mesiya. Palibe munthu amene akanatha kuneneratu zinthu zimenezi kapena kuchititsa kuti zikwaniritsidwe mwa Yesu.
Kuneneratu za Kubadwa kwa Mesiya. Yesaya analosera kuti Mesiya, kapena kuti Khristu, adzabadwa kwa namwali. Mateyo atafotokoza zinthu zozizwitsa zokhudza kubadwa kwa Yesu, anati: “Zonsezi zinachitika kuti zimene Yehova ananena kudzera mwa mneneri wake zikwaniritsidwe, iye anati: ‘Tamverani! Namwali adzatenga pathupi Mateyo 1:22, 23; Yesaya 7:14) Yesaya analoseranso kuti Khristu adzakhala mbadwa ya Davide, ndipo anachita kum’tchula Jese, yemwe anali bambo a Davide. Yesu analidi mbadwa yeniyeni ya Davide. (Mateyo 1:6, 16; Luka 3:23, 31, 32) Choncho, Yesu asanabadwe, mngelo Gabrieli anauza mayi a Yesu, Mariya, kuti: “Mulungu adzam’patsa mpando wachifumu wa Davide atate wake.”—Luka 1:32, 33; Yesaya 11:1-5, 10; Aroma 15:12.
ndipo adzabereka mwana wamwamuna.’” (Kuneneratu za Moyo wa Mesiya. Yesu atakula anapita ku sunagoge wa ku Nazarete ndipo anawerenga mokweza ulosi wa Yesaya, umene unali ndi mawu akuti: “Mzimu wa Yehova uli pa ine, chifukwa iye anandidzoza kuti ndilengeze uthenga wabwino kwa osauka.” Kenako posonyeza kuti ulosiwo ukukwaniritsidwa pa iye, Yesu anati: “Lero lemba ili limene mwangolimva kumeneli lakwaniritsidwa.” (Luka 4:17-21; Yesaya 61:1, 2) Yesaya ananeneratunso kuti Yesu adzakhala wokoma mtima, wodekha komanso wodzichepetsa pothandiza anthu amene akufuna kuchiritsidwa. Mateyo analemba kuti: “Anthu ambiri anam’tsatira, ndipo anawachiritsa onsewo, koma anawalamula mwamphamvu kuti asamuulule; kuti zimene zinanenedwa kudzera mwa Yesaya mneneri zikwaniritsidwe . . . ‘Sadzakangana ndi munthu kapena kufuula . . . Bango lophwanyika sadzalisansantha.’”—Mateyo 8:16, 17; 12:10-21; Yesaya 42:1-4; 53:4, 5.
Kuneneratu za Kuzunzidwa kwa Mesiya. Yesaya analosera kuti Mesiya adzakanidwa ndi Aisiraeli ambiri ndipo iye adzakhala “mwala wopunthwitsa” kwa iwo. (1 Petulo 2:6-8; Yesaya 8:14, 15) N’zoonadi kuti Yesu anachita zozizwitsa zambiri koma anthu “sanali kukhulupirira mwa iye, mwakuti mawu a Yesaya mneneri anakwaniritsidwa. Iye anati: ‘Yehova, ndani amene wakhulupirira mwa zimene ife tinamva?’” (Yohane 12:37, 38; Yesaya 53:1) Chifukwa chimodzi chimene Ayuda sanamukhulupirire n’chakuti, iwo ankaganiza molakwa kuti Mesiya akadzangofika adzawalanditsa ku ulamuliro wa Aroma, ndipo adzabwezeretsa mpando wachifumu wa Davide padziko lapansi. Koma chifukwa chakuti Yesu anazunzidwa mpaka kuphedwa, Ayuda ambiri sanakhulupirire kuti ndi Mesiya. Komatu, Yesaya anali ataneneratu kuti Mesiya adzazunzidwa asanakhale Mfumu.
Ponena za Mesiya, ulosi wa m’buku la Yesaya umati: “Ndinapereka msana wanga kwa omenya . . . Sindinabisira nkhope yanga manyazi ndi kulavuliridwa.” Mateyo anafotokoza zimene zinachitika pamene Yesu ankaimbidwa mlandu kuti: “Anayamba kumulavulira kunkhope ndi kum’menya ndi nkhonya. Ena anamuwomba mbama pankhope.” (Yesaya 50:6; Mateyo 26:67) Yesaya analemba kuti: “Iye anatsenderezedwa koma anadzichepetsa yekha osatsegula pakamwa pake.” Choncho Pilato atafunsa Yesu za zinthu zimene Ayuda ankamuneneza, “iye anangokhala duu, osanena kanthu, mwakuti bwanamkubwayo anadabwa kwambiri.”—Yesaya 53:7; Mateyo 27:12-14; Machitidwe 8:28, 32-35.
Kuneneratu za Imfa ya Mesiya. Ulosi wa Yesaya unakwaniritsidwanso pamene Yesu ankaphedwa ndiponso atafa. Yesaya ananeneratu kuti: “Anaika manda ake pamodzi ndi oipa, ndi pamodzi ndi olemera mu imfa yake.” (Yesaya 53:9) Mawu amenewa akuoneka ngati akutsutsana. Ndiyeno kodi anakwaniritsidwa bwanji? Yesu anapachikidwa pakati pa achifwamba awiri. (Mateyo 27:38) Kenako Yosefe wa ku Arimateya, yemwe anali wolemera, anakaika thupi la Yesu m’manda ake amene anawasema m’thanthwe. (Mateyo 27:57-60) Ndipo pomaliza, imfa ya Yesu inakwaniritsa mbali ina yofunika kwambiri ya ulosi wa Yesaya. Ponena za Mesiya, Yesaya anati: “Mtumiki wanga wolungama adzalungamitsa ambiri, nadzanyamula mphulupulu zawo.” Imfa ya Yesu inapereka dipo lomasula anthu onse okhulupirika ku ukapolo wa uchimo.—Yesaya 53:8, 11; Aroma 4:25.
Maulosi Osakayikitsa
Atumwi ndiponso Yesu anagwira mawu a ulosi wa Yesaya kuposa mabuku ena onse a m’Baibulo potsimikizira kuti Yesu analidi Mesiya. Komabe, sikuti ndi buku la Yesaya lokha limene linaneneratu zam’tsogolo. Maulosi enanso ambiri olembedwa m’Malemba a Chiheberi adzakwaniritsidwa kudzera mwa Yesu, Ufumu wake ndiponso zinthu zabwino zimene Ufumuwo udzachite m’tsogolo. * (Machitidwe 28:23; Chivumbulutso 19:10) N’zosakayikitsa kuti maulosi amenewa adzakwaniritsidwa. Yesu anauza Ayuda kuti: “Musaganize kuti ndinabwera kudzawononga Chilamulo kapena Zolemba za aneneri [kutanthauza, Malemba a Chiheberi]. Sindinabwere kudzawononga, koma kudzakwaniritsa; pakuti ndikukuuzani ndithu kuti kumwamba ndi dziko lapansi zingachoke mosavuta, kusiyana n’kuti kalemba kochepetsetsa kapena kachigawo kamodzi kalemba kachoke m’Chilamulo zinthu zonse zisanachitike.”—Mateyo 5:17, 18.
Yesu ananenanso za maulosi a m’Baibulo amene anakwaniritsidwa m’nthawi yake komanso amene adzakwaniritsidwe m’tsogolo. (Danieli 9:27; Mateyo 15:7-9; 24:15) Iye ndi ophunzira ake ananeneratu za zimene zidzachitike m’tsogolo mwawo ndipo zina mwa zinthuzo zikuchitika masiku ano. M’nkhani yotsatira tikambirana zinthu zimenezi ndiponso maulosi ena a m’Baibulo amene adzakwaniritsidwe m’tsogolo.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 9 Kuti mudziwe zambiri zokhudza maulosi amene anakwaniritsidwa mwa Yesu, onani buku lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova, lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? patsamba 200.
[Chithunzi patsamba 4]
“Namwali . . . adzabereka mwana wamwamuna”
[Chithunzi patsamba 5]
“Sindinabisira nkhope yanga manyazi”