Udindo wa Mariya Pokwaniritsa Cholinga cha Mulungu
Udindo wa Mariya Pokwaniritsa Cholinga cha Mulungu
NTHAWI ina Yesu akuphunzitsa anthu, mayi wina pagululo anakuwa kuti: “Ngosangalala mayi amene mimba yake inanyamula inu ndi kuyamwa mawere ake!” Yesu akanafuna kuti mayi ake azipatsidwa ulemu wapadera, akanayamikira mayiyu chifukwa cha zimene ananenazo. Koma iye sanatero, m’malomwake anati: “Ayi, koma, Osangalala ndi amene akumva mawu a Mulungu ndi kuwasunga!”—Luka 11:27, 28.
Yesu sanapatse mayi ake ulemu uliwonse wapadera kapena kuuza ophunzira ake kuti azitero. Ndiyeno kodi n’zoyenera kuti anthu azipatsa Mariya ulemu wapadera? Tiyeni tione ngati ziphunzitso zotchuka zokhudza mayi a Yesu n’zogwirizana ndi Malemba.
“Wodzala Chisomo,” “Wodala Mwa Akazi Onse”
Pouza Mariya za udindo umene anali nawo pokwaniritsa cholinga cha Mulungu, mngelo Gabrieli anayamba ndi kunena kuti: “Mtendere ukhale nawe, wodalitsika koposatu iwe, Yehova ali nawe.” (Luka 1:28) M’Mabaibulo ena lembali analimasulira kuti: “Tamandani, wodzala chisomo, Ambuye ali nanu.” Nthawi inanso, Elizabeti analonjera Mariya ndi mawu ofanana ndi amenewa kuti: “Wodalitsika ndiwe mwa akazi onse, n’chodalitsikanso chipatso cha mimba yako!” (Luka 1:42) Kodi mawu amenewa akusonyeza kuti tiyenera kum’patsa ulemu wapadera?
Ayi. Ngakhale kuti mawuwa ali m’pemphero limene Akatolika amanena kwa Mateyo 6:9.
Mariya, Baibulo silinena kuti tizipemphera kwa iye. Mngelo Gabrieli komanso Elizabeti analemekeza Mariya chifukwa cha udindo wake wobereka Mesiya, koma Malemba sanena kuti tizipemphera kwa iye. Ophunzira a Yesu atam’pempha kuti awaphunzitse kupemphera, iye anawauza kuti azipemphera kwa Atate ake. N’chifukwa chake pemphero lachitsanzo la Yesu limayamba ndi mawu akuti: “Atate wathu wa kumwamba.”—Ali M’gulu la Anthu Olamulira
Chiphunzitso chinanso chotchuka chokhudza Mariya n’chakuti iye ndi “Mfumukazi Yakumwamba.” Koma Baibulo silisonyeza kuti iye ali ndi udindo umenewu. Zimene Baibulo limanena n’zakuti iye ali ndi udindo wapadera m’boma la kumwamba. Kodi iye wapatsidwa udindo wotani?
Yesu ananena kuti ena mwa ophunzira ake okhulupirika adzalamulira naye mu Ufumu wake. (Luka 22:28-30) Yesu wapatsa anthu amenewa udindo wokhala “ansembe kwa Mulungu wathu, mwakuti adzalamulira dziko lapansi monga mafumu.” (Chivumbulutso 5:10) Baibulo limasonyeza kuti Mariya ali m’gulu la anthu amene apatsidwa udindo wapaderawu. Kodi tikudziwa bwanji zimenezi?
Mungakumbukire kuti Yesu atamwalira, Mariya “analimbika kupemphera” pamodzi ndi ophunzira komanso abale ake a Yesu. Pa anthu okwana 120, amene anasonkhana kuti apemphere, panalinso “azimayi.” (Machitidwe 1:12-15) Baibulo limati: “Tsiku la chikondwerero cha Pentekosite lili mkati, onse anali chisonkhanire pa malo amodzi.” Ndipo onsewo anadzazidwa ndi mzimu wa Mulungu n’kuyamba kulankhula zinenero zosiyanasiyana.—Machitidwe 2:1-4.
Mariya anadalitsidwa nawo tsiku limeneli, ndipo zimenezi zikusonyeza kuti iye ndi amayi ena amene analandira mzimu woyera, anasankhidwa kuti akalamulire ndi Yesu mu Ufumu wake wakumwamba. Choncho, sitikukayikira kuti Mariya ali limodzi ndi Yesu mu ulemerero wakumwamba. (Aroma 8:14-17) Mariya ndiponso anthu ena amene adzalamulire ndi Yesu adzagwira ntchito zina pokwaniritsa cholinga cha Mulungu.
Adzagwira Ntchito Imene Idzabweretse Madalitso Osatha
Buku la Chivumbulutso limanena kuti anthu 144,000 adzaukitsidwa ndi kupita kumwamba kukatumikira pamodzi ndi Yesu monga ansembe, oweruza ndi mafumu. (Chivumbulutso 14:1, 4; 20:4, 6) Monga ansembe, iwo adzachititsa kuti nsembe ya Yesu igwire ntchito kwa anthu onse omvera ndipo anthuwo adzakhala angwiro mwauzimu ndi mwa kuthupi. (Chivumbulutso 21:1-4) Nthawi imeneyi idzakhala yosangalatsa kwambiri kwa atumiki onse a Yehova okhulupirika. *
Yehova anagwiritsira ntchito Mariya ndipo akumugwiritsirabe ntchito pokwaniritsa cholinga chake. Mariya ndi chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani ya kudzichepetsa, kukhulupirika, kumvera, kusamalira banja ndiponso kupirira mavuto. Tiyenera kumulemekeza chifukwa chobereka Mesiya komanso chifukwa chogwira ntchito imene idzabweretse madalitso osatha.
Komabe, chinthu chofunika kwambiri chimene timaphunzira kwa Mariya ndiponso kwa atumiki onse a Yehova okhulupirika n’chakuti iwo salambira mulungu wina, koma Yehova yekha basi. Mariya ndiponso anthu ena amene adzalamulira ndi Khristu kumwamba amatamanda Mulungu kuti: “Kwa Iye wokhala pampando wachifumu[Yehova Mulungu] ndi kwa Mwanawankhosa [Yesu Khristu] kukhale chitamando, ulemu, ulemerero, ndi mphamvu, kwa muyaya ndi muyaya.”—Chivumbulutso 5:13; 19:10.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 13 Kuti mudziwe zambiri zokhudza madalitso amenewa, onani mutu 8 m’buku la Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
[Mawu Otsindika patsamba 10]
Mariya ndi chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani ya kudzichepetsa, kukhulupirika, ndiponso kumvera