Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mulungu Amavomereza Kulambira Kwina Kulikonse?

Kodi Mulungu Amavomereza Kulambira Kwina Kulikonse?

Kodi Mulungu Amavomereza Kulambira Kwina Kulikonse?

Ambiri amanena kuti:

▪ “Zipembedzo zonse zili ngati njira yopita kwa Mulungu.”

▪ “Zilibe kanthu kuti umakhulupirira chiyani malinga ngati uli woona mtima.”

Kodi Yesu anati chiyani?

▪ “Lowani pa chipata chopapatiza; chifukwa msewu waukulu ndi wotakasuka ukupita ku chiwonongeko, ndipo anthu ambiri akuyenda mmenemo; koma chipata cholowera kumoyo n’chopapatiza komanso msewu wake ndi wopanikiza, ndipo amene akuupeza ndi owerengeka.” (Mateyo 7:13, 14) Yesu sankakhulupirira kuti zipembedzo zonse ndi zovomerezeka kwa Mulungu.

▪ “Ambiri adzati kwa ine patsiku limenelo, ‘Ambuye, Ambuye, kodi ife sitinanenere m’dzina lanu, ndi kutulutsa ziwanda m’dzina lanu, ndiponso kuchita zamphamvu zambiri m’dzina lanunso?’ Koma pamenepo ine ndidzawauza mwachimvekere kuti: Sindinakudziweni konse chiyambire! Chokani pamaso panga, anthu osamvera malamulo inu.” (Mateyo 7:22, 23) Yesu salandira onse amene amanena kuti amamutsatira.

ANTHU ambiri opemphera amakonda zikhulupiriro ndi miyambo yawo. Koma kodi chimachitika n’chiyani ngati zimene amakhulupirirazo si zochokera m’Mawu a Mulungu, Baibulo? Yesu anasonyeza vuto lotsatira miyambo ya anthu pamene anauza atsogoleri achipembedzo a m’nthawi yake kuti: “Mwasandutsa mawu a Mulungu kukhala opanda pake chifukwa cha mwambo wanu.” Ndiyeno anabwereza mawu a Mulungu akuti: “Anthu awa amandilemekeza ndi milomo yokha, koma mtima wawo uli kutali ndi ine. Amandilambira ine pachabe, chifukwa amaphunzitsa malamulo a anthu monga ziphunzitso za Mulungu.”​—Mateyo 15:1-9; Yesaya 29:13.

Khalidwe labwino ndi lofunika kwambiri, osati chikhulupiriro chokha. Kwa anthu amene amati amalambira Mulungu, Baibulo limati: “Amanena poyera kuti amadziwa Mulungu, koma amam’kana ndi ntchito zawo.” (Tito 1:16) Ndipotu za anthu ambiri a m’nthawi ino Baibulo limanena kuti: ‘Adzakhala okonda zosangalatsa, m’malo mokonda Mulungu, ooneka ngati odzipereka kwa Mulungu koma mphamvu ya kulambira Mulungu siitha kuwasintha; anthu amenewa, uwapewe.’​—2 Timoteyo 3:4, 5.

Pali zinthu zinanso zofunika kuwonjezera pa kuona mtima. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa munthu akhoza kukhala woona mtima koma pa zinthu zolakwika. Motero, kudziwa zolondola ponena za Mulungu n’kofunika. (Aroma 10:2, 3) Kuphunzira zinthu zimenezi ndi kutsatira zimene Baibulo limanena kudzatithandiza kuti tikondweretse Mulungu. (Mateyo 7:21) Choncho, chipembedzo cholondola chifunika kukhala ndi zolinga zabwino, zikhulupiriro zolondola, ndiponso kuchita zinthu zolondola. Ndipo kuchita zinthu zolondola kumeneku kumatanthauza kuchita zimene Mulungu amafuna tsiku lililonse.​—1 Yohane 2:17.

Ngati mungafune kudziwa zambiri zokhudza Mulungu zimene Baibulo limanena, pemphani a Mboni za Yehova kuti aziphunzira nanu Baibulo kwaulere kunyumba kwanu.

[Mawu Otsindika patsamba 9]

Chipembedzo cholondola chifunika kukhala ndi zolinga zabwino, zikhulupiriro zolondola, ndiponso kuchita zinthu zolondola