Kodi Mulungu ndi Munthu Weniweni?
Kodi Mulungu ndi Munthu Weniweni?
Ambiri amanena kuti:
▪ “Ali paliponse ngati mphepo.”
▪ “Iye ndi nzeru kapena mphamvu inayake yosadziwika bwino.”
Kodi Yesu anati chiyani?
▪ “M’nyumba ya Atate wanga alimo malo ambiri okhalamo.” (Yohane 14:2) Yesu anafotokoza kuti Mulungu ali ndi nyumba yophiphiritsa, kapena kuti malo okhala.
▪ “Ndinachokera kwa Atate ndipo ndinabwera m’dziko. Tsopano ndikuchoka m’dziko kupita kwa Atate.” (Yohane 16:28) Yesu ankakhulupirira kuti Mulungu ndi Munthu weniweni ndipo ali ndi malo enieni okhala.
YESU samuona Mulungu ngati mphamvu chabe. Iye ankalankhula ndi Mulungu ndiponso ankapemphera kwa iye. Nthawi zambiri ankamutchula Yehova kuti Atate wake wakumwamba, mawu amene akusonyeza kuti anali paubwenzi wabwino ndi Mulungu.—Yohane 8:19, 38, 54.
N’zoona kuti “palibe munthu anaonapo Mulungu ndi kale lonse” ndiponso kuti “Mulungu ndiye Mzimu.” (Yohane 1:18; 4:24) Koma zimenezi sizikutanthauza kuti alibe thupi. Baibulo limatiuza kuti: “Ngati pali thupi la nyama, palinso lauzimu.” (1 Akorinto 15:44) Ndiye kodi Yehova ali ndi thupi lauzimu?
Inde, ali ndi thupi lauzimu. Yesu ataukitsidwa, “analowa kumwamba kwenikweniko. Anatero kuti tsopano aonekere pamaso pa Mulungu mwiniyo kaamba ka ife.” (Aheberi 9:24) Apa tikuphunzirapo mfundo ziwiri zofunika zonena za Mulungu. Mfundo yoyamba ndi yakuti ali ndi malo amene amakhala. Yachiwiri ndi yakuti ndi Munthu osati mphamvu yosadziwika bwino imene imapezeka paliponse.
Nanga zimatheka bwanji kuti Mulungu azitha kulamulira zinthu kulikonse? Mulungu angatumize mzimu wake woyera, kapena kuti mphamvu yake yogwira ntchito, kulikonse padziko lapansili. Mofanana ndi atate yemwe amagwiritsa ntchito dzanja lake kuti athandize mwana wake, Mulungu amagwiritsa ntchito mzimu wake woyera kuti akwaniritse zolinga zake.—Salmo 104:30; 139:7.
Chifukwa choti Mulungu ndi Munthu, iye ali ndi zinthu zimene amakonda komanso zimene amadana nazo. Baibulo limatiuza kuti Mulungu amakonda anthu, amasangalala ndi ntchito yake, amadana ndi kulambira mafano ndiponso amavutika mu mtima anthu akamachita zoipa. (Genesis 6:6; Deuteronomo 16:22; 1 Mafumu 10:9; Salmo 104:31) Pa 1 Timoteyo 1:11, amamutchula kuti ndi “Mulungu wa chisangalalo.” N’chifukwa chake Yesu ananena kuti tingam’konde Mulungu ameneyu ndi mtima wathu wonse.—Maliko 12:30. *
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 12 Kuti mumve zambiri pankhani imeneyi, onani mutu 1 m’buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
[Mawu Otsindika patsamba 5]
Mofanana ndi atate yemwe amagwiritsa ntchito dzanja lake kuti athandize mwana wake, Mulungu amagwiritsa ntchito mzimu wake woyera kuti akwaniritse zolinga zake