Pankhani ya Mapemphero Amene Mulungu Amamva
Zimene Tikuphunzira kwa Yesu
Pankhani ya Mapemphero Amene Mulungu Amamva
Nthawi zambiri Yesu ankapita kwayekha kukapemphera, ndipo analimbikitsa otsatira ake kuchita zomwezo. Baibulo limati: “Anali kupemphera pamalo ena ake, atatsiriza, mmodzi wa ophunzira ake anati kwa iye: ‘Ambuye, tiphunzitseni kupemphera’ . . . Pamenepo iye anati kwa iwo: “Mukamapemphera muziti, ‘Atate, dzina lanu liyeretsedwe.”’” (Luka 5:16; 11:1, 2) Choncho Yesu anasonyeza kuti tiyenera kupemphera kwa Atate ake okha, Yehova, amene ndi Mlengi wathu ndiponso “Wakumva pemphero.”—Salmo 65:2.
Kodi Mulungu amamva mapemphero onse?
Mulungu samva mapemphero oloweza pamtima. Yesu anati: “Popemphera, usanene zinthu mobwerezabwereza.” (Mateyo 6:7) Tiyenera kulankhula ndi Atate wathu wakumwamba kuchokera mu mtima. Nthawi ina, Yesu anauza otsatira ake kuti Mulungu amamva mapemphero a munthu wochimwa amene akufunitsitsa kusintha, kusiyana ndi a munthu wonyada amene amatsatira kwambiri miyambo yachipembedzo. (Luka 18:10-14) Chotero ngati tikufuna kuti Mulungu azimva mapemphero athu, tiyenera kudzichepetsa komanso tiziyesetsa kuchita zimene amatiuza. Yesu ananenanso kuti: “Ndimalankhula zinthu izi ndendende mmene Atate anandiphunzitsira . . . Ndimachita zinthu zom’kondweretsa nthawi zonse.” (Yohane 8:28, 29) Popemphera Yesu anati: “Chifuniro chanu chichitike, osati changa.”—Luka 22:42.
Kodi tiyenera kupempha chiyani?
Popeza dzina la Mulungu lanyozedwa, Yesu anati: “Choncho inu muzipemphera motere: ‘Atate wathu wa kumwamba, dzina lanu liyeretsedwe. Ufumu wanu ubwere. Chifuniro chanu chichitike, monga kumwamba, chomwechonso pansi pano.’” (Mateyo 6:9, 10) Tiyenera kupempha Ufumu wa Mulungu kuti ubwere chifukwa ndi boma limene Mulungu adzagwiritse ntchito pokwaniritsa chifuno chake kumwamba ndi pansi pano. Yesu ananenanso kuti tizipempha “chakudya chathu cha lero.” Tikhozanso kum’pempha Yehova kuti atithandize tikamadwala, kuti tipeze ntchito, pokhala, zovala ndiponso zinthu zina. Yesu ananenanso kuti tiyenera kum’pempha Mulungu kuti atikhululukire.—Luka 11:3, 4.
Kodi tiyenera kupempherera ena?
Yesu anapempherera anthu ena. Baibulo limatiuza kuti: “Anam’bweretsera ana aang’ono, kuti awaike manja ndi kuwapempherera.” (Mateyo 19:13) Yesu anauza mtumwi Petulo kuti: “Ine ndakupempherera iwe kuti chikhulupiriro chako chisathe.” (Luka 22:32) Yesu analimbikitsa otsatira ake kupempherera anthu ena, ngakhale anthu amene amawazunza ndi kuwachitira chipongwe.—Mateyo 5:44; Luka 6:28.
N’chifukwa chiyani tiyenera kupemphera nthawi zonse?
Yesu ankakhala ndi nthawi yopemphera ndipo analimbikitsa otsatira ake ‘kupemphera nthawi zonse, osaleka.’ (Luka 18:1) Yehova amafuna kuti tisonyeze kumudalira mwa kumuuza mobwerezabwereza zinthu zimene zimatidetsa nkhawa. Yesu anati: “Pemphanibe, ndipo adzakupatsani.” Komabe zimenezi sizikutanthauza kuti Yehova safuna kuyankha mapemphero a anthu amene amamukonda ndi kumulemekeza monga Atate wawo. N’chifukwa chake Yesu ananena kuti: “Ngati inu, ngakhale muli oipa, mumadziwa kupatsa ana anu mphatso zabwino, kuli bwanji Atate wakumwamba! Iye adzapereka mowolowa manja mzimu woyera kwa amene akum’pempha.”—Luka 11:5-13.
Kuti mudziwe zambiri, onani mutu 17 wa buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? *
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 12 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.