Munthu Sakhala ndi Moyo ndi Chakudya—Chokha Mmene Ndinapulumukira M’ndende za Chipani cha Nazi
Munthu Sakhala ndi Moyo ndi Chakudya—Chokha Mmene Ndinapulumukira M’ndende za Chipani cha Nazi
Yosimbidwa ndi Joseph Hisiger
Nditafunsa mkaidi wina kuti, “Ukuwerenga chiyani?” Anayankha kuti: “Ndikuwerenga Baibulo. Koma ngati ukulifuna tikhoza kusinthana ndi chakudya chako cha mlungu umodzi.”
NDINABADWA pa March 1, 1914, ku Moselle, dera lomwe panthawiyo linali mbali ya dziko la Germany. Nkhondo yoyamba ya padziko lonse itatha mu 1918, dera la Moselle linabwerera m’manja mwa dziko la France. Mu 1940, derali linalandidwanso ndi dziko la Germany. Kenaka derali linakhalanso m’manja mwa dziko la France, nkhondo yachiwiri ya padziko lonse itatha mu 1945. Nthawi zonsezi ndinkakhala nzika ya dziko limene likulamulira deralo, moti ndinaphunzira kulankhula Chifalansa ndi Chijeremani.
Makolo anga anali Akatolika olimbikira. Tsiku lililonse tisanagone, tonse m’banja mwathu tinkagwada n’kupemphera. Tinkapita kutchalitchi Lamlungu lililonse ndiponso masiku onse atchuthi. Ndinkakonda kwambiri zopemphera moti ndinali m’gulu linalake lophunzira zachikatolika.
Kuchita Khama pa Ntchito Yathu
Mu 1935, a Mboni za Yehova awiri anafika kunyumba kwathu ndipo anacheza ndi makolo anga. Anakambirana kwambiri nkhani ya zimene zipembedzo zinachita polowerera nkhondo yoyamba ya padziko lonse. Pambuyo pake, ndinayamba kuchita chidwi kwambiri ndi Baibulo moti mu 1936 ndinapempha wansembe wina kuti andipezere Baibulo. Iye anandiuza kuti Baibulo sindingalimvetse popanda kuchita kaye maphunziro a zaubusa. Zimenezi zinangowonjezera chidwi changa chofuna kupeza Baibulo n’kuyamba kuliwerenga.
Mu January 1937, mnzanga wina wakuntchito, dzina lake Albin Relewicz, yemwe anali wa Mboni, anayamba kundifotokozera zimene Baibulo limaphunzitsa. Ndiye ndinam’funsa kuti: “Ndiye kuti uli nalo Baibulo eti?” Iye anali nalodi ndipo posakhalitsa anandisonyeza dzina la Mulungu lakuti Yehova m’Baibulo la Chijeremani lotchedwa Elberfelder. Anandipatsanso Baibulolo. Ndinkaliphunzira mwakhama kwambiri ndipo ndinayamba kupita kumisonkhano ya Mboni za Yehova m’tawuni yapafupi ya Thionville.
Mu August 1937, ndinatsagana ndi Albin kumsonkhano wa mayiko wa Mboni za Yehova ku Paris. Kumeneku n’kumene ndinayambira kulalikira ku nyumba ndi nyumba. Pasanapite nthawi yaitali ndinabatizidwa ndipo kumayambiriro kwa 1939 ndinakhala m’painiya kapena kuti mlaliki wa nthawi zonse. Kenako ndinatumizidwa mumzinda wa Metz. M’mwezi wa July ndinaitanidwa kuti ndikatumikire ku ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ku Paris.
Nkhondo Inabweretsa Mavuto Ambiri
Sindinatumikire kwanthawi yaitali pa ofesi ya nthambiyi chifukwa choti mu August 1939 ndinaitanidwa kuti ndikalowe m’gulu la asilikali a ku France. Chikumbumtima changa sichinandilole
kulowa usilikali choncho ananditsekera m’ndende. M’mwezi wa May, ine ndidakali m’ndende, dziko la Germany linaukira dziko la France mwadzidzidzi. Dziko la France linagonjetsedwa mu June ndipo apa ndinakhalanso nzika ya dziko la Germany. Nditatulutsidwa m’ndende mu July 1940, ndinabwerera kwathu kukakhala ndi makolo anga.Panthawiyi chipani cha Nazi n’chimene chinkalamulira, choncho tinkaphunzira Baibulo mwakabisira. Tinkalandira magazini a Nsanja ya Olonda kudzera kwa mayi wina wa Mboni wolimba mtima, dzina lake Maryse Anasiak. Ndinkakumana naye mu shopu yogulitsira buledi ya m’bale wina. Kuyambira nthawi imeneyi mpaka mu 1941, ndinapulumuka mavuto ambiri amene Mboni za ku Germany zinkakumana nawo.
Tsiku lina wapolisi wa chipani cha Hitler anabwera kunyumba kwathu. Iye anati Mboni za Yehova n’zoletsedwa kenako anandifunsa ngati ndikufuna kupitirizabe kukhala wa Mboni za Yehova. Nditamuyankha kuti “Inde,” anandiuza kuti ndimutsatire. Mayi anga zinawakhudza kwambiri moti anakomoka. Wapolisiyo ataona zimenezi anandibweza n’cholinga choti ndisamalire mayi angawo.
Tsiku lina nditakumana ndi bwana kuntchito, sindinanena nawo mawu akuti “Hitler Mpulumutsi Wathu” popereka moni. Komanso ndinakana kukhala membala wa chipani cha Nazi, moti mawa lake ndinamangidwa ndi apolisi. Panthawi imene apolisiwa anandipanikiza ndi mafunso ndinakana kutchula mayina a Mboni zina. Choncho amene ankandifunsayo anandimenya ndi mfuti pamutu mpaka ndinakomoka. Ndinazengedwa mlandu ku khoti lina la ku Metz, lotchedwa Sondergericht, pa September 11, 1942 ndipo anandipeza ndi mlandu “wofalitsa mfundo zokopa anthu kuti akhale a Mboni za Yehova.” Choncho anandiweruza kuti ndikhale m’ndende kwa zaka zitatu.
Patatha milungu iwiri, ndinachoka kundende ya Metz kupita ku ndende ina yozunzirako anthu ku Zweibrücken. Kundendeyi ndinkagwira ntchito yokonza njanji. Tinkasintha zitsulo za njanji, kuzimangirira bwinobwino komanso kuika timiyala m’njanjizo. Koma ankangotipatsa kapu imodzi ya khofi ndi kabuledi kakang’ono m’mawa. Masana ndi madzulo ankangotipatsa supu basi. Kenako ananditumiza ku ndende ina kumene ndinkagwira ntchito yokonza nsapato. Patapita miyezi ingapo anandipititsanso kundende ya Zweibrücken ndipo panthawiyi ndinkagwira ntchito kumunda.
Sindinakhale ndi Moyo ndi Chakudya Chokha
Ndinkakhala ndi munthu wina wa ku Netherlands m’selo yanga kundendeko. Nditaphunzira pang’ono chilankhulo chake ndinatha kumufotokozera zimene ndimakhulupirira. Iye anapita patsogolo kwambiri mpaka anandipempha kuti ndimubatize mumtsinje winawake. Nditamubatiza anandikumbatira n’kunena kuti: “Joseph, tsopano ndine m’bale wako.” Koma tinasiyana panthawi imene ananditumiza kuti ndizikagwiranso ntchito yokonza njanji.
Panthawiyi ndinkakhala ndi munthu wina wa ku Germany m’selo yanga. Tsiku lina madzulo ndinamuona munthuyo akuwerenga Baibulo. Ndipo apa m’pamene ananena kuti ndizimupatsa chakudya chokwana mlungu umodzi kuti andipatse Baibulolo. Ndinamuuza kuti, “Palibe vuto.” Kupereka chakudya chokwana mlungu umodzi sinali nkhani yamasewera koma sindinadandaule ngakhale pang’ono. Ndinamvetsa tanthauzo la mawu a Yesu akuti: “Munthu asakhale ndi moyo ndi chakudya chokha, koma ndi mawu onse otuluka pakamwa pa Yehova.”—Mateyo 4:4.
Nditapeza Baibulo, vuto tsopano linali kasungidwe kake. Akaidi ena ankaloledwa kukhala ndi Baibulo koma ife Mboni za Yehova sitinkaloledwa kukhala nalo. Motero ndinkaliwerenga mobisa usiku wokhawokha nditafunda bulangete. Kukacha ndinkalisunga m’malaya anga n’kumayenda nalo kulikonse. Sindinkalisiya m’selo imene tinkagona chifukwa choti asilikali ankafufuzamo tikatuluka.
Tsiku lina nditanyamuka kuti tikayambe ntchito ndinazindikira kuti ndaiwala Baibulo langa. Madzulo ake ndinafulumira kwambiri kuti ndikaone ngati lilipo koma sindinalipeze. Nditapemphera kwa Mulungu ndinapita kwa msilikali n’kumuuza kuti wina wandibera buku langa. Iye analibe chidwi kwenikweni ndi nkhaniyi moti ndinafufuza ndekha n’kulipeza. Ndinathokoza Yehova kuchokera pansi pa mtima.
Tsiku lina anandiuza kuti ndikagwire ntchito kumalo osambira. Posintha zovala zanga ndinaika pansi Baibulo langa mochenjera. Kenako msilikali atayang’ana kumbali ndinalikankha ndi phazi kuti libisike. Choncho ndinalisunga pamalo abwino uku ndikuyeretsa malo osambirawo. Potuluka ndinalikankhanso ndi phazi kupita nalo pamalo amene panali zovala zabwino.
Zinthu Zabwino Komanso Zovuta Zimene Zinachitika Kundende
Tsiku lina m’mawa akaidi anauzidwa kuti akhale pamzere ndipo ndinamuona Albin. Nayenso anali atamangidwa. Atandiona n’kundizindikira anaika dzanja lake pamtima kusonyeza kuti ndi m’bale wanga. Kenako anandipatsa zizindikiro zosonyeza kuti andilembera kalata. Mawa lake anaponya pansi kapepala panthawi imene ankadutsa. Mwatsoka msilikali anaona ndipo anatitsekera aliyense kwa yekha kwa milungu iwiri. Ankangotipatsa buledi wakalekale ndi madzi ndipo tinkagona pamatabwa popanda chofunda.
Kenako ananditumiza kundende ya ku Siegburg komwe ndinkagwira ntchito mu shopu yokonza zinthu zachitsulo. Ntchito yake inali ya kalavulagaga koma chakudya chinali chosakwanira. Nthawi zina usiku ndinkalota ndikudya zakudya zabwino monga makeke ndi zipatso koma ndinkadzuka m’mimba mukulira komanso kukhosi kuli gwa. Ndinawonderatu koma tsiku lililonse ndinkawerenga Baibulo ndipo izi zinkandilimbikitsa kwambiri.
Kumasulidwa
Tsiku lina m’mawa mu April 1945, asilikali anathawa pandende yathu n’kusiya zitseko zili chitsegukire. Apa m’pamene tinamasuka. Koma ndinakhala nthawi ndithu ndili m’chipatala kuti ndiyambe kupeza bwino. Ndinafika kumudzi kwathu kumapeto kwa May. Achibale anga onse ankangoganiza kuti ndamwalira. Mayi anga atandiona anangoyamba kulira chifukwa cha chisangalalo. Koma pasanapite nthawi yaitali mayi ndi bambo anga anamwalira.
Ndinayambanso kupita ku mpingo wa ku Thionville. Ndinali wosangalala kwambiri kukumananso ndi abale anga auzimu. Ngakhale kuti ndinakumana ndi mayesero ambiri, ndinasangalala kumva mmene anakhalira okhulupirika. Mnzanga Albin uja anamwalira mumzinda wa Regensburg m’dziko la Germany. Kenako ndinamva zoti msuweni wanga, dzina lake Jean Hisiger, anakhalanso wa Mboni za Yehova ndipo anaphedwa chifukwa chokana kulowa usilikali. M’bale wina amene ndinkatumikira naye ku ofesi ya nthambi ya ku Paris, dzina lake Jean Queyroi, anakhalanso kundende ya ku Germany kwa zaka 5. *
Mwamsanga, ndinayambiranso kulalikira m’tawuni ya Metz. Nthawi zambiri ndinkakumana ndi banja la a Minzani. Mwana wawo Tina anabatizidwa pa November 2, 1946. Iye anali wakhama muutumiki ndipo osanama, anali wokongola. Ine ndi Tina tinakwatirana pa December 13, 1947. Tina anayamba utumiki wa nthawi zonse mu September 1967 ndipo wakhala mu utumikiwu kwa moyo wake wonse. Anamwalira mu June 2003, ali ndi zaka 98 ndipo ndimamusowa kwabasi.
Panopo ndili ndi zaka zoposa 90 ndipo ndimazindikira kuti Mawu a Mulungu ndiwo akhala akundipatsa mphamvu zoti ndipirire polimbana ndi mayesero. Ndakhalapo moyo womachita kusowa chakudya koma panthawi yonseyi mtima wanga sunakhalepo ndi njala ya Mawu a Mulungu. Yehova wakhala akundilimbikitsa kwambiri. Inde, ‘mawu ake anandipatsa moyo.’—Salmo 119:50.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 27 Kuti mumve mbiri ya moyo wa Jean Queyroi, onani Nsanja ya Olonda ya October 1, 1989 tsamba 22-26.
[Chithunzi patsamba 21]
Mnzanga Albin Relewicz
[Chithunzi patsamba 21]
Maryse Anasiak
[Chithunzi patsamba 22]
Baibulo limene ndinapeza posinthanitsa ndi chakudya changa cha mlungu umodzi
[Chithunzi patsamba 23]
Tili pa chibwenzi ndi Tina mu 1946
[Chithunzi patsamba 23]
Jean Queyroi ndi mkazi wake Titica