Kodi Kubadwa Mwatsopano Kumachitika Motani?
Kodi Kubadwa Mwatsopano Kumachitika Motani?
POLANKHULA ndi Nikodemo za kubadwa mwatsopano, Yesu sanangonena za kufunika kwake, kapena za cholinga chake koma anamuuzanso chimene chimachititsa kuti munthu abadwenso. Iye anati: “Munthu sangathe kulowa mu ufumu wa Mulungu atapanda kubadwa mwa madzi ndi mzimu.” (Yohane 3:5) Choncho, munthu amabadwanso akabatizidwa mwa madzi ndi mzimu. Koma kodi mawu akuti “madzi ndi mzimu” akutanthauza chiyani?
Tanthauzo la “Kubadwa mwa Madzi ndi Mzimu”
N’zosakayikitsa kuti Nikodemo, yemwe anali mtsogoleri wachipembedzo cha Chiyuda, ankadziwa bwino tanthauzo la mawu akuti “mzimu wa Mulungu” m’Malemba a Chiheberi. Iye ankadziwa kuti mzimu umenewu ndi mphamvu yogwira ntchito ya Mulungu, imene ingachititse munthu kuchita zozizwitsa. (Genesis 41:38; Eksodo 31:3; 1 Samueli 10:6) Choncho, pamene Yesu anagwiritsa ntchito mawu akuti “mzimu,” Nikodemo ayenera kuti anadziwa tanthauzo limeneli.
Nanga Yesu ankatanthauza chiyani pamene ananena za madzi? Taonani zimene zinalembedwa, Yesu ndi Nikodemo asanayambe kukambirana ndiponso atangomaliza kukambirana. Zimenezi zimasonyeza kuti Yohane Mbatizi ndiponso ophunzira a Yesu ankabatiza anthu ndi madzi. (Yohane 1:19, 31; 3:22; 4:1-3) Ubatizo wa madzi unali wodziwika kwambiri ku Yerusalemu. Motero, pamene Yesu anatchula za madzi, Nikodemo ayenera kuti anadziwa kuti iye sankatanthauza madzi aliwonse, koma ubatizo wa madzi. *
Kubatizidwa “ndi Mzimu Woyera”
Ngati “kubadwa mwa madzi” kukutanthauza kubatizidwa ndi madzi, nanga “kubadwa mwa . . . mzimu” kukutanthauza chiyani? Yesu asanakambirane ndi Nikodemo, Yohane Mbatizi anali atanena kale kuti madzi ndiponso mzimu n’zofunika kwambiri paubatizo. Iye anati: “Ine ndakubatizani m’madzi, koma iye [Yesu] adzakubatizani ndi mzimu woyera.” (Maliko 1:7, 8) Nayenso Maliko, yemwe analemba nawo mabuku a uthenga wabwino anafotokoza nthawi yoyamba imene ubatizo wotere unachitika. Iye analemba kuti: “M’masiku amenewo, Yesu anabwera kuchokera ku Nazarete wa ku Galileya ndipo anabatizidwa ndi Yohane mu Yorodano. Ndipo atangovuuka m’madzimo, anaona kumwamba kukutseguka, ndiyeno mzimu ukutsika ngati nkhunda kudzatera pa iye.” (Maliko 1:9, 10) Yesu atamizidwa mumtsinje wa Yorodano, anabatizidwa ndi madzi. Koma panthawi imene analandira mzimu kuchokera kumwamba, anabatizidwa ndi mzimu woyera.
Patapita zaka pafupifupi zitatu Yesu atabatizidwa, iye anauza ophunzira ake kuti: “Pasanathe masiku ambiri mudzabatizidwa ndi mzimu woyera.” (Machitidwe 1:5) Kodi zimenezi zinachitika liti?
Ophunzira a Yesu pafupifupi 120 anasonkhana m’nyumba inayake ku Yerusalemu pa Pentekosite mu 33 C.E. Baibulo limati: “Mwadzidzidzi kumwamba kunamveka mkokomo ngati wa mphepo yamphamvu, ndipo unadzaza nyumba yonseyo imene iwo anakhalamo. Pamenepo iwo anaona malawi ooneka ngati malilime a moto. . . . Ndipo onsewo anadzazidwa ndi mzimu woyera.” (Machitidwe 2:1-4) Tsiku lomwelo, mtumwi Petulo analimbikitsa anthu enanso ku Yerusalemu kuti abatizidwe ndi madzi. Iye anauza gulu la anthulo kuti: “Lapani, ndipo aliyense wa inu abatizidwe m’dzina la Yesu Khristu kuti machimo anu akhululukidwe. Pamenepo mudzalandira mphatso yaulere ya mzimu woyera. Choncho amene analandira mawu akewo ndi mtima wonse anabatizidwa, moti tsiku limenelo anthu pafupifupi 3,000 anawonjezedwa.”—Machitidwe 2:38, 41.
Ubatizo wa Mbali Ziwiri
Kodi ubatizo wa madzi ndi mzimu ukusonyeza chiyani za kubadwa mwatsopano? Ukusonyeza kuti kubadwa mwatsopano kumachitika m’njira ziwiri. Kumbukirani kuti choyamba, Yesu anabatizidwa ndi madzi ndipo kenako analandira mzimu woyera. Mofanana ndi zimenezi, ophunzira oyambirira nawonso ankayamba kubatizidwa ndi madzi (ena anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi), ndipo kenako ankalandira mzimu woyera. (Yohane 1:26-36) Ndiponso anthu 3,000 amene anakhulupirira, choyamba anabatizidwa ndi madzi ndipo kenako analandira mzimu woyera.
Poganizira ubatizo umene unachitika pa Pentekosite mu 33 C.E., kodi masiku ano munthu amabadwa mwatsopano m’njira yotani? M’njira yofanana ndi mmene atumwi a Yesu ndiponso ophunzira ake oyambirira anachitira. Choyamba, munthu amalapa machimo ake, kusiya njira zake zoipa n’kudzipereka kwa Yehova. Munthu amachita zimenezi kuti azilambira ndi kutumikira Mulungu. Ndiponso amasonyeza poyera kuti anadzipereka kwa Yehova pobatizidwa m’madzi. Kenako, ngati Mulungu angasankhe munthuyo kuti akalamulire mu Ufumu wake, amamudzoza ndi mzimu woyera. Mbali yoyamba ya ubatizowu (kubatizidwa ndi madzi) ndi imene munthu amachita kusankha yekha, pamene mbali yachiwiri (kubatizidwa ndi mzimu), amasankha ndi Mulungu. Choncho, munthu akabatizidwa mwa madzi ndi mzimu, m’pamene amabadwa mwatsopano.
Nanga n’chifukwa chiyani Yesu pokambirana ndi Nikodemo anagwiritsa ntchito mawu akuti “kubadwa mwa madzi ndi mzimu”? N’chifukwa chakuti ankafuna kutsindika mfundo yakuti moyo wa munthu amene wabatizidwa mwa madzi ndi mzimu umasintha kwambiri. Tikambirana mfundo imeneyi m’nkhani yotsatirayi.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 5 Panthawi inayake ya ubatizo, mtumwi Petulo ananena kuti: “Kodi pali munthu akhoza kuletsa madzi?”—Machitidwe 10:47.
[Chithunzi patsamba 9]
Yohane ankabatiza Aisiraeli olapa ndi madzi