Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Kubadwanso Ndiyo Njira Yopezera Chipulumutso?

Kodi Kubadwanso Ndiyo Njira Yopezera Chipulumutso?

Kodi Kubadwanso Ndiyo Njira Yopezera Chipulumutso?

KODI mungayankhe bwanji munthu atakufunsani kuti: “Kodi ndinu wobadwanso?” Anthu ambiri akhoza kuyankha mosakaika kuti, “Inde.” Iwo amakhulupirira kuti Akhristu onse oona ayenera kubadwanso kapena kuti kubadwa mwatsopano ndipo amati imeneyi ndi njira yokhayo yopezera chipulumutso. Iwo amagwirizana ndi mawu a katswiri wina wamaphunziro a zaumulungu, dzina lake Robert C. Sproul, yemwe analemba kuti: “Ngati munthu sanabadwenso, . . . ndiye kuti si Mkhristu.”

Kodi inunso mumakhulupirira kuti kubadwa mwatsopano ndiyo njira imene ingakupezetseni chipulumutso? Ngati zili choncho, ndiye kuti mungafune kuthandiza abale anu ndiponso anzanu kuti nawonso apeze njirayo n’kuyamba kuyendamo. Komabe, kuti iwo achite zimenezi, ayenera kumvetsa bwino kusiyana kwa munthu amene anabadwanso ndi wosabadwanso. Ndiyeno, kodi mungawafotokozere bwanji tanthauzo la kubadwanso?

Anthu ambiri amakhulupirira kuti munthu wobadwanso ndi amene analonjeza ndi mtima wonse kuti adzatumikira Mulungu ndi Khristu, ndipo chifukwa cha zimenezi, amasintha khalidwe lake loipa n’kuyamba ntchito zabwino.

Koma mukhoza kudabwa kwambiri mutadziwa kuti Baibulo siligwirizana ndi maganizo amenewa. Kodi mungakonde kudziwa zimene Mawu a Mulungu amanena pa nkhani ya kubadwanso? Kunena zoona, mungapindule kwambiri ngati mutafufuza mozama nkhaniyi m’Baibulo chifukwa kudziwa tanthauzo la kubadwanso kungakhudze kwambiri moyo wanu ndiponso chiyembekezo chanu.

Kodi Baibulo Limati Chiyani Pankhaniyi?

M’Baibulo lonse, mawu akuti “kubadwanso” amapezeka pa Yohane 3:1-12 pokha. Mavesi amenewa amafotokoza nkhani yochititsa chidwi imene Yesu ndi mtsogoleri wina wachipembedzo ku Yerusalemu anakambirana. Nkhani imeneyi ili m’bokosi limene lili patsamba lotsatirali. Tikukulimbikitsani kuwerenga nkhaniyi mosamala.

M’nkhaniyi, Yesu anafotokoza mbali zosiyanasiyana za “kubadwa mwatsopano.” * Ndipotu zimene Yesu ananena zikutithandiza kupeza mayankho a mafunso ofunika kwambiri awa:

Kodi kubadwa mwatsopano n’kofunika motani?

Kodi munthu amachita kusankha yekha kuti abadwe mwatsopano?

▪ Kodi cholinga cha kubadwa mwatsopano n’chiyani?

Kodi chimachitika n’chiyani kuti munthu abadwe mwatsopano?

▪ Kodi zimenezi zimathandiza munthu kuti akhale paubwenzi ndi Mulungu?

Tiyeni tione mafunso amenewa, lililonse palokha.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 8 Mawu akuti ‘kubadwa mwatsopano’ amapezeka pa 1 Petulo 1:3, 23, ndipo ndi ofanana ndi mawu akuti “kubadwanso.” Mawu awiri onsewa anachokera ku mawu a Chigiriki akuti, gen·naʹo.

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 4]

“Anthu Inu Muyenera Kubadwanso”

“Panali Mfarisi wina dzina lake Nikodemo, mmodzi wa olamulira a Ayuda. Iyeyu anabwera kwa Yesu usiku ndi kumuuza kuti: ‘Rabi, tikudziwa kuti inu ndinu mphunzitsi wochokera kwa Mulungu; chifukwa munthu sangathe kuchita zizindikiro zimene inu mumachita ngati Mulungu sali naye.’ Poyankha Yesu anati kwa iye: ‘Ndithudi ndikukuuza, Munthu sangathe kuona ufumu wa Mulungu atapanda kubadwanso.’ Nikodemo anati kwa iye: ‘Munthu angabadwe bwanji ali wamkulu kale? Kodi angathe kulowa m’mimba mwa mayi wake ndi kubadwanso?’ Yesu anayankha nati: ‘Ndithudi ndikukuuza, Munthu sangathe kulowa mu ufumu wa Mulungu atapanda kubadwa mwa madzi ndi mzimu. Chobadwa mwa thupi n’chanyama, ndipo chobadwa mwa mzimu n’chauzimu. Usadabwe chifukwa ndakuuza kuti, Anthu inu muyenera kubadwanso. Mphepo imawombera kumene ikufuna, ndipo munthu amamva mkokomo wake, koma sadziwa kumene ikuchokera ndi kumene ikupita. N’chimodzimodzinso aliyense wobadwa mwa mzimu.’ Poyankha Nikodemo anati kwa iye: ‘Zimenezi zingatheke bwanji?’ Yesu anamuyankha nati: ‘Kodi iwe sudziwa zinthu zimenezi, chikhalirecho ndiwe mphunzitsi wa Isiraeli? Ndithudi ndikukuuza, Zimene ife timadziwa timazilankhula, ndipo zimene taona timazichitira umboni, koma anthu inu simulandira umboni umene timapereka. Ngati ndakuuzani zinthu za padziko lapansi koma inu osakhulupirira, mudzakhulupirira bwanji ndikakuuzani zinthu za kumwamba?’”​—Yohane 3:1-12.