Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

1 Dalirani Baibulo

1 Dalirani Baibulo

1 Dalirani Baibulo

“Malemba onse anawauzira ndi Mulungu, ndipo ndi opindulitsa pa kuphunzitsa, kudzudzula, kuwongola zinthu.”​—2 Timoteyo 3:16.

N’CHIFUKWA CHIYANI ANTHU ENA ZIMAWAVUTA KUDALIRA MULUNGU? Anthu ambiri amaganiza kuti Baibulo ndi buku limene anthu anangolembamo maganizo awo. Ena amakhulupirira kuti mbiri yakale yomwe ili m’Baibulo si yolondola. Ndipo ena amanena kuti malangizo a m’Baibulo ndi achikale.

KODI MUNGATANI KUTI MUZIDALIRA MULUNGU? Nthawi zambiri anthu omwe amakayikira kuti Baibulo ndi lolondola ndiponso lodalirika amakhala asanafufuze okha, koma amangonena zimene anamva kwa anthu ena. Baibulo limati: “Wachibwana akhulupirira mawu onse; koma wochenjera asamalira mayendedwe ake.”​—Miyambo 14:15.

M’malo mongokhulupirira zilizonse zimene mwauzidwa, mungachite bwino kutsatira chitsanzo cha Akhristu a ku Bereya omwe anakhalapo m’nthawi ya atumwi, dera lomwe masiku ano lili kumpoto kwa Greece. Iwo sankangokhulupirira zilizonse zimene ena awauza koma ankakonda “kufufuza Malemba mosamala tsiku ndi tsiku kuti aone ngati zinthuzo zinalidi choncho.” (Machitidwe 17:11) Tiyeni tione mfundo ziwiri zotsatirazi zosonyeza zifukwa zimene muyenera kukhulupirira kuti Baibulo ndi Mawu a Mulungu owuziridwa.

Baibulo ndi lolondola pankhani zokhudza mbiri yakale. Kwa nthawi yaitali anthu akhala akutsutsa Baibulo ponena kuti maina a anthu ndiponso a malo ena otchulidwa m’Baibulo si olondola. Koma nthawi zambiri ofufuza akhala akupeza umboni wosonyeza kuti zimene anthuwa amanena n’zabodza.

Mwachitsanzo, panthawi ina akatswiri ena amaphunziro ankakayikira kuti mfumu Sarigoni ya ku Asuri, yotchulidwa pa Yesaya 20:1 inalipodi. Koma m’zaka za m’ma 1840, akatswiri a zinthu zakale zokumbidwa pansi anapeza bwinja limene panali nyumba ya mfumuyi. Masiku ano, mfumu Sarigoni ndi imodzi mwa mafumu odziwika bwino a ku Asuri.

Anthu ena otsutsa amakayikira zoti kale kunali Pontiyo Pilato, kazembe wachiroma yemwe analamula kuti Yesu aphedwe. (Mateyo 27:1, 22-24) Komabe mu 1961, akatswiri a mbiri ya zinthu zakale zokumbidwa pansi, anapeza mwala umene panalembedwa dzina la Pilato ndiponso udindo wake. Mwalawu anaupeza kufupi ndi mzinda wa Caesarea ku Israel.

Pogwirizana ndi mfundo yoti Baibulo ndi lolondola pankhani zokhudza mbiri yakale, magazini ina ya pa October 25, 1999 inanena kuti: “Masiku ano akatswiri ofufuza apeza umboni wochuluka kwambiri wotsimikizira kuti nkhani za m’Chipangano Chakale ndiponso Chipangano Chatsopano ndi zolondola. Zina mwa nkhanizi ndi zokhudza makolo akale achiisiraeli, ulendo wawo wochoka ku Iguputo, mafumu a banja la Davide ndiponso nkhani zokhudza mmene moyo unalili m’nthawi ya Yesu.” (U.S.News & World Report) Ngakhale kuti simungafunike kudalira zimene akatswiriwa apeza kuti muyambe kukhulupirira Baibulo, komabe nkhani zolondolazi zimatsimikizira kuti Baibulo ndi buku louziridwa ndi Mulungu.

Mfundo zanzeru zimene zili m’Baibulo zimathandiza anthu amitundu yonse. Anthu asanatulukire kuti tizilombo ndi timene timayambitsa matenda, Baibulo linali litapereka kale malangizo okhudza ukhondo omwe akugwirabe ntchito mpaka pano. (Levitiko 11:32-40; Deuteronomo 23:12, 13) Anthu amene amatsatira malangizo a m’Baibulo, okhudza mmene angakhalire bwino ndi ena, amakhala osangalala kwambiri pabanja pawo. (Aefeso 5:28​—6:4) Munthu yemwe amatsatira mfundo za m’Baibulo angakhale wodalirika pantchito kapenanso ngati munthuyo ndi amene walemba anzake ntchito, angathe kukhala bwana wabwino. (Aefeso 4:28; 6:5-9) Komanso munthu amene amatsatira mfundo za m’Baibulo amakhala ndi mtendere wa m’maganizo. (Miyambo 14:30; Aefeso 4:31, 32; Akolose 3:8-10) Mpake kuti mfundo zothandiza zimenezi zimachokera kwa Mlengi wathu.

KODI TINGAPEZE MADALITSO OTANI? Mfundo zanzeru zopezeka m’Baibulo zingathandize ngakhale munthu yemwe sadziwa zambiri, kuti akhale ndi nzeru. (Salmo 19:7) Komanso tikangoyamba kudalira kwambiri Baibulo kuposa buku lina lililonse, tidzakhala ndi chikhulupiriro cholimba kwambiri.

Kuti mudziwe zambiri, onani buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? * pamutu 2 wakuti, “Baibulo Ndi Buku Lochokera kwa Mulungu.”

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 12 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.