Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

4 Musamakayikire

4 Musamakayikire

4 Musamakayikire

“Wachikhulupiriro chochepa iwe, n’chifukwa chiyani wakayikira?”​—Mateyo 14:31.

N’CHIFUKWA CHIYANI ENA AMAKAYIKIRA? Nthawi zina, ngakhalenso ophunzira a Yesu ankakayikira. (Mateyo 14:30; Luka 24:36-39; Yohane 20:24, 25) Ndipotu Baibulo limanena kuti kupanda chikhulupiriro ndi “tchimo . . . lotikola mosavuta.” (Aheberi 12:1) Mtumwi Paulo analemba kuti: “Chikhulupiriro sichikhala ndi anthu onse.” (2 Atesalonika 3:2) Lembali silikunena kuti anthu ena sangathe kukhala ndi chikhulupiriro koma likutanthauza kuti ambiri sachita khama kuti akhale nacho. Mulungu amadalitsa anthu amene amayesetsa mwakhama kuti akhale ndi chikhulupiro.

KODI MUNGATANI KUTI MUSAMAKAYIKIRE? Zindikirani zinthu zimene zimakuchititsani kuti muzikayikira. Mwachitsanzo, Tomasi yemwe anali wophunzira wa Yesu, anakayikira zoti Yesu anaukitsidwa, ngakhale kuti ophunzira anzake anali atamuuza kuti amuona. Koma Tomasi ankafuna umboni wotsimikizira kuti Yesu anali atauka ndipo Yesu anam’patsadi umboni womuthandiza kuti akhale ndi chikhulupiro cholimba.​—Yohane 20:24-29.

Kudzera m’Baibulo, Yehova Mulungu amatipatsa umboni umene ungatithandize kuti tisamakayikire. Mwachitsanzo, ena amasiya kukhulupira Mulungu chifukwa amaganiza kuti iye ndi amene amachititsa nkhondo, chiwawa ndiponso mavuto osiyanasiyana amene anthu akukumana nawo. Koma kodi Baibulo limati chiyani pa nkhaniyi?

Mulungu sakulamulira dzikoli pogwiritsa ntchito maboma a anthu. Yesu ananena kuti Satana, yemwe ndi cholengedwa chauzimu, ndi amene ‘akulamulira dzikoli.’ (Yohane 14:30) Satana anauza Yesu kuti angam’patse ulamuliro wonse padzikoli ngati atamulambira, ngakhale kamodzi kokha. Iye anati: “Ndikupatsani ulamuliro wonsewu ndi ulemerero wake wonse, chifukwa unaperekedwa kwa ine. Ndikhoza kuupereka kwa aliyense amene ndakonda kum’patsa.” Pamenepa Yesu sanatsutse zoti Satana ndiye akulamulira dzikoli. M’malomwake iye anauza Satanayo kuti: “Malemba amati, ‘Yehova Mulungu wako ndi amene uyenera kumulambira, ndipo utumiki wako wopatulika uyenera kupita kwa iye yekha basi.’” (Luka 4:5-8) Choncho, anthu ayenera kuimba mlandu Satana ndiponso maboma a anthu chifukwa ndi amene akuchititsa mavuto onse padzikoli, osati Mulungu.​—Chivumbulutso 12:9, 12.

Posachedwapa Yehova Mulungu athetsa mavuto onse. Iye wakhazikitsa kale Ufumu kapena kuti boma limene wolamulira wake ndi Mwana wake, Khristu Yesu, ndipo adzalamulira anthu padziko lapansi. (Mateyo 6:9, 10; 1 Akorinto 15:20-28) Pokwaniritsa ulosi wa m’Baibulo, uthenga wabwino wa Ufumu umenewu ukulalikidwa padziko lonse. (Mateyo 24:14) Posachedwapa Ufumu umenewu udzaononga anthu onse otsutsa ndipo udzathetseratu mavuto onse.​—Danieli 2:44; Mateyo 25:31-33, 46; Chivumbulutso 21:3, 4.

KODI TIDZAPEZA MADALITSO OTANI? Anthu amene amakayikira ali ngati mafunde a m’nyanja omwe amangotengekatengeka “ndi mphepo iliyonse ya chiphunzitso chonyenga cha anthu.” (Aefeso 4:14; 2 Petulo 2:1) Koma anthu amene amapeza mayankho ogwira mtima a mafunso awo, sakayikira ndipo amakhala ‘ochirimika m’chikhulupiriro.’​—1 Akorinto 16:13.

Anthu a Mboni za Yehova, omwe amafalitsa magazini ino angakonde kukuthandizani kupeza mayankho othandiza kuti mukhale ndi chikhulupiriro. Iwo akukulimbikitsani kuti muzisonkhana nawo n’cholinga choti mudziwe zimene amakhulupirira. Kuchita zimenezi kudzakuthandizani kukhala ndi chikhulupiriro cholimba mwa Mulungu.

Kuti mudziwe zambiri, onani buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? * mutu 8 wakuti, “Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?” ndiponso mutu 11, wakuti, “N’chifukwa Chiyani Mulungu Amalola Kuti Anthu Azivutika?”

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 10 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Chithunzi patsamba 9]

Anthu amene amapeza mayankho ogwira mtima a mafunso awo amakhala ndi maziko olimba a zimene amakhulupirira