Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mulungu Ndi Amene Amapatsa Mphamvu Anthu Onse Amene Amachiritsa Mozizwitsa?

Kodi Mulungu Ndi Amene Amapatsa Mphamvu Anthu Onse Amene Amachiritsa Mozizwitsa?

Zimene Owerenga Amafunsa

Kodi Mulungu Ndi Amene Amapatsa Mphamvu Anthu Onse Amene Amachiritsa Mozizwitsa?

N’zodziwikiratu kuti Yehova Mulungu ali ndi mphamvu zochiritsa anthu komanso kuti akhoza kupereka mphamvu zimenezi kwa atumiki ake. Mwachitsanzo, m’nthawi ya atumwi, kuchiritsa mozizwitsa chinali chizindikiro chimodzi cha mphatso ya mzimu woyera. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Ntchito za mzimu zipatsidwa kwa munthu aliyense pacholinga chopindulitsa. Mwachitsanzo, mwa mzimu, wina apatsidwa mawu anzeru, . . . wina mphatso za kuchiritsa, . . . wina kunenera, . . . wina kulankhula malilime osiyanasiyana.”​—1 Akorinto 12:4-11.

Komabe, m’kalata yomweyi yopita kwa Akorinto, Paulo analembanso kuti mphatso za mzimu woyera za kuchiritsa mozizwitsa zidzatha. Iye anati: “Kaya pali mphatso za kunenera, zidzatha. Kaya kulankhula malilime, kudzatha; ngakhale mphatso ya kudziwa zinthu, idzatha.”​—1 Akorinto 13:8.

Yesu Khristu ndiponso atumwi ake ndi amene ankachiritsa anthu mozizwitsa. Panthawi imeneyo, mphatso za mzimu woyera, monga kuchiritsa anthu mozizwitsa, zinkachitika n’cholinga chopereka ulemerero kwa Mulungu. Ndiponso chinali chizindikiro chakuti Yehova akudalitsa ndi kuyanja mpingo wachikhristu umene unali utangoyambika kumene. Koma mpingowu utakula, mphatso za mzimu, monga kuchiritsa anthu mozizwitsa, sizinakhalenso chizindikiro choti Mulungu akuyanja mpingowo. M’malomwake, chikhulupiriro cholimba, chiyembekezo ndiponso chikondi ndi zimene zinakhala umboni wakuti Mulungu akuyanja mpingo. (Yohane 13:35; 1 Akorinto 13:13) Motero, pofika m’chaka cha 100 C.E., Mulungu anali atasiya kupatsa Akhristu mphamvu yochiritsa mozizwitsa. *

Koma mwina mungadzifunse kuti, ‘Nanga n’chifukwa chiyani ndimamvabe kuti anthu ena amachiritsa mozizwitsa?’ Mwachitsanzo, nyuzipepala ina inanena za munthu wina amene ankadwala matenda a khansa. Iye anali ndi zotupa m’mutu, mu impso ndiponso m’kati mwa mafupa ake. Zinali zokayikitsa kwambiri kuti munthuyo akanachira. Koma kenako, akuti Mulungu “analankhula” ndi munthuyo ndipo patapita masiku ochepa, matenda akewo anatha.

Mukamva nkhani ngati zimenezi, mungachite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi zimenezi zinachitikadi? Kodi pali umboni wa kuchipatala wotsimikizira kuti munthuyo anachiradi? Ngakhale patakhala umboni wotsimikizira kuti munthuyo anachiradi, kodi Baibulo limaphunzitsa kuti nthawi zonse Mulungu ndi amene amachiritsa anthu mozizwitsa?’

Yankho la funso lomalizali n’lofunika kwambiri. Yesu anachenjeza otsatira ake kuti: “Chenjerani ndi aneneri onyenga. . . . Ambiri adzati kwa ine patsiku limenelo, ‘Ambuye, Ambuye, kodi ife sitinanenere m’dzina lanu, ndi kutulutsa ziwanda m’dzina lanu, ndiponso kuchita zamphamvu [zozizwitsa] zambiri m’dzina lanunso?’ Koma pamenepo ine ndidzawauza mwachimvekere kuti: Sindinakudziweni konse chiyambire! Chokani pamaso panga, anthu osamvera malamulo inu.”​—Mateyo 7:15, 21-23.

Choncho, n’zodziwikiratu kuti anthu omwe amachiritsa mozizwitsa masiku ano mphamvu zawo zingachokere kwina, osati kwa Mulungu. Motero, kuti tipewe kupusitsidwa ndi anthu amene amati amachita zozizwitsa m’dzina la Mulungu, tiyenera kudziwa Mulungu molondola, kugwiritsa ntchito nzeru zimene iye anatipatsa ndiponso tiyenera kuzindikira anthu omwe akuchitadi chifuniro chake.​—Mateyo 7:16-19; Yohane 17:3; Aroma 12:1, 2.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 5 Zikuoneka kuti atumwi onse atamwalira, Mulungu anasiya kupereka mphatso za mzimu kwa Akhristu. Ndiponso mphatso zozizwitsa za mzimuwo zinatha, anthu amene anali ndi mphatsozo atamwalira.