Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Yesu Sanagonje Poyesedwa

Yesu Sanagonje Poyesedwa

Zoti Achinyamata Achite

Yesu Sanagonje Poyesedwa

Malangizo: Chitani zotsatirazi muli pa malo opanda phokoso. Mukamawerenga mavesiwo, muziyerekezera kuti pamene zinthuzo zinkachitika inuyo munalipo. Yesani kuona nkhanizi m’maganizo mwanu. Yerekezerani kuti mukumva mawu a m’nkhanizi. Yesani kuganizira mmene anthu otchulidwa m’nkhaniyi ankamvera.

ONANI NKHANIYI BWINOBWINO.​—WERENGANI MATEYO 4:1-11.

Kodi mukuganiza kuti chipululu chimene Yesu anakhalako kwa masiku 40 chinali chotani?

․․․․․

Kodi mukuganiza kuti mawu a Satana ankamveka bwanji? Nanga mawu a Yesu?

․․․․․

FUFUZANI MOZAMA.

Kodi Satana anasonyeza bwanji kuti amapezerapo mwayi pa zimene zikum’chitikira munthu? (Werengani vesi 2.)

․․․․․

N’chifukwa chiyani Mdyerekezi sanangouza Yesu kuti amupatsa maufumu onse a padziko lapansi koma, kuti amupatsanso “ulemerero wawo” wonse? (Werengani vesi 8.)

․․․․․

N’chifukwa chiyani Satana anasankha kuyesa Yesu pomuuza kuti amupatsa ulamuliro?

․․․․․

(a) Tikaona mmene Satana anayesera Yesu katatu konse, kodi tinganene kuti Satana ali ndi maganizo otani? ․․․․․

(b) Nanga tinganene kuti Yesu ali ndi maganizo otani tikaona mmene anayankhira Satana pa mayesero onse? ․․․․․

GWIRITSANI NTCHITO ZIMENE MWAPHUNZIRA. LEMBANI ZIMENE MWAPHUNZIRA PONENA ZA . . .

Nthawi imene Satana amakonda kuyesa munthu.

․․․․․

Njira zosiyanasiyana zimene Satana angatiyesere.

․․․․․

Zimene tingachite kuti tisagonje poyesedwa.

․․․․․

M’NKHANIYI, KODI NDI MFUNDO ZITI ZIMENE ZAKUKHUDZANI KWAMBIRI NDIPO N’CHIFUKWA CHIYANI?

․․․․․