N’chifukwa Chiyani Baibulo Lili Lothandiza Masiku Ano?
N’chifukwa Chiyani Baibulo Lili Lothandiza Masiku Ano?
“Malemba onse anawauzira ndi Mulungu, ndipo anthu angawagwiritse bwino ntchito kuti . . . aziwatsogolera pamoyo wawo.”—2 TIMOTEYO 3:16, The Jerusalem Bible.
KWA zaka zambiri, Baibulo lathandiza anthu a zikhalidwe zosiyanasiyana kusintha moyo wawo. Lemba limene lili pamwambali likusonyeza kuti Baibulo limathandiza anthu m’njira imeneyi chifukwa chakuti nzeru zake n’zochokera kwa Mulungu. Ngakhale kuti anthu ndi amene analemba Baibulo, mfundo zake n’zochokera kwa Mulungu. N’chifukwa chake limati: “Anthu analankhula mawu ochokera kwa Mulungu motsogoleredwa ndi mzimu woyera.”—2 Petulo 1:21.
Baibulo limatithandiza m’njira ziwiri. Choyamba, limatithandiza kudziwa zimene tingachite kuti tikhale ndi moyo wosangalala. Chachiwiri, lili ndi mphamvu zothandiza anthu kusintha moyo wawo. Tiyeni tikambirane mfundo ziwirizi mwatsatanetsatane.
Malangizo Amene Angatithandize Kuchita Zinthu Mwanzeru
Mulungu analonjeza kuti: “Ine ndidzakulangiza ndi kuphunzitsa iwe za njira ukayendayo; ndidzakupangira ndi diso langa lakuyang’ana iwe.” (Salmo 32:8) Lembali likusonyeza kuti Mulungu samangopereka malangizo okha, koma amaperekanso nzeru zimene zimathandiza munthu kumvetsa bwino zinthu. Tikakhala ndi nzeru zotithandiza kuchita zinthu zoyenera, sitingataye nthawi yathu pa zinthu zosathandiza.
Mwachitsanzo, anthu ambiri amafunitsitsa kukhala otchuka ndiponso olemera. Ndipo pali mabuku ambiri amene amapereka malangizo a zimene munthu angachite kuti akhale wotchuka ndiponso wolemera kuposa wina aliyense. Koma Baibulo limatiuza kuti: ‘Anansi a munthu wachuma am’chitira nsanje. Ichinso ndi chabe ndi kungosautsa mtima.’ Ndiponso limati: “Wokonda siliva sadzakhuta siliva.” (Mlaliki 4:4; 5:10) Kodi malangizo amenewa ndi othandiza masiku ano?
Kuti muone mmene malangizo a m’Baibulo amathandizira, tamvani zimene zinachitikira bambo wina wa ku Japan, dzina lake Akinori. Iye ali mnyamata, ankafunitsitsa kuti adzapite ku yunivesite inayake yotchuka, n’cholinga choti adzapeze ntchito yapamwamba. Ngakhale kuti sizinali zophweka kuti munthu apite ku yunivesiteyi, Akinori anapitadi ndipo anapeza ntchito yabwino. Zinthu zinkaoneka kuti zikumuyendera bwino. Komabe zimenezi sizinam’thandize kuti akhale wosangalala monga mmene ankaganizira poyamba. M’malo Miyambo 14:30, The Holy Bible—New International Version.
mwake iye ankakhala ndi nkhawa komanso ankatopa kwambiri, ndipo zimenezi zinkamudwalitsa. Anzake a ku ntchito sanamuthandize kuthana ndi mavutowa. Iye ankavutika maganizo kwambiri ndipo chifukwa cha zimenezi, anayamba kumwa mowa mwauchidakwa ndiponso anafika poganiza kuti angodzipha. Kenako anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Zimene ankaphunzirazo zinamuthandiza kuzindikira zinthu zimene zili zofunikadi pamoyo. Posakhalitsa matenda ake amene anabwera chifukwa chovutika maganizo anayamba kutha. Akinori sanasonyeze mtima wonyada, ndipo anavomereza zimene Baibulo limanena kuti: “Mtendere wa mu mtima ndi moyo wa thupi.”—Kodi inuyo mumaona kuti chinthu chofunika kwambiri chomwe mungachite kuti mukhale osangalala pamoyo n’chiyani? Kodi n’kukhala ndi banja labwino, kapena kukonza tsogolo labwino la ana anu? Kapena n’kukhala ndi anzanu ambiri? Zinthu zimenezi n’zofunikira ndipotu Baibulo limasonyeza kuti palibe cholakwika ndi zimenezi koma silimatiuza kuti n’zofunika kwambiri pamoyo. Baibulo limapereka malangizo anzeru onena za zimene munthu angachite kuti akhale ndi moyo wosangalala. Limati: “Opa Mulungu, musunge malamulo ake; pakuti choyenera anthu onse ndi ichi.” (Mlaliki 12:13) Tikanyalanyaza mfundo imeneyi, moyo wathu umakhala wopanda cholinga, wosasangalatsa ndiponso womvetsa chisoni. Koma Baibulo limatiuza kuti: “Wokhulupirira Yehova adala.”—Miyambo 16:20.
Mmene Baibulo Limathandizira Anthu Kusintha Moyo Wawo
Mtumwi Paulo analemba kuti: “Mawu a Mulungu ndi amoyo ndi amphamvu.” Lembali likusonyeza kuti Mawu a Mulungu ali ngati lupanga lakuthwa konsekonse ndipo amatha kulowa mumtima ndi m’maganizo a munthu. (Aheberi 4:12) Baibulo lili ndi mphamvu yosintha moyo wa anthu chifukwa limawathandiza kuti azidziona moyenerera. N’chifukwa chake anthu amene ali ndi mtima wabwino amazindikira kufunika kosintha moyo wawo. Mwachitsanzo ponena za Akhristu ena mumpingo wa ku Korinto, omwe poyamba anali akuba, zidakwa, achigololo, ndiponso ochita makhalidwe ena oipa, Paulo anati: “Ena mwa inu munali otero. Koma mwasambitsidwa kukhala oyera . . . ndi mzimu wa Mulungu wathu.” (1 Akorinto 6:9-11) Mzimu woyera wa Yehova udakali wamphamvu masiku ano ndipo umathandiza anthu kusintha moyo wawo.
Taonani chitsanzo cha bambo wina wa ku Ulaya dzina lake Mario, amene anali wokonda zachiwawa ndiponso ankasuta ndi kugulitsa chamba. Tsiku lina wapolisi atamulanda chambacho, iye analusa kwambiri moti anamenya wapolisiyo n’kumuphwanyiranso galimoto yake. Komanso Mario anali lova ndiponso anali ndi ngongole zambiri. Iye atazindikira kuti sangathetse yekha mavutowa, anavomereza kuti ayambe kuphunzira Baibulo. Pang’ono ndi pang’ono, Mario anayamba kuoneka bwino, anasiya kusuta ndi kugulitsa chamba komanso anasiya zachiwawa. Anthu ambiri amene ankamudziwa mmene analili poyamba, anadabwa kumuona atasintha, ndipo akakumana naye amam’funsa kuti: “Koma Mario uja ndiwedi?”
Kodi n’chiyani chinathandiza anthu ngati Akinori ndi Mario kusintha moyo wawo n’kuyamba kusangalala? N’zoonekeratu kuti iwo anasintha chifukwa chakuti anayamba kuphunzira Baibulo, ndipo zimenezi ziwathandiza kudziwa Mulungu molondola. Mulungu yekha ndi amene angatipatse malangizo amene angatithandize kukhala ndi moyo wosangalala panopa komanso kuti tidzakhale ndi moyo wosatha m’tsogolo. Yehova Mulungu akulankhula nafe ngati ana ake, kudzera m’Baibulo kuti: “Tamvera mwananga, nulandire mawu anga; ndipo zaka za moyo wako zidzachuluka. . . . Mapazi ako sadzaombana ulikuyenda; ukathamanga, sudzapunthwa. Gwira mwambo, osauleka; uusunge; pakuti ndiwo moyo wako.” (Miyambo 4:10-13) Kodi pangapezeke malangizo enanso abwino kwambiri kuposa amene Mlengi wathu amatipatsa?
[Bokosi/Chithunzi patsamba 7]
Malangizo Othandiza Kwambiri Masiku Ano
Baibulo lili ndi malangizo osavuta komanso othandiza omwe angatitsogolere pamoyo wathu. Tiyeni tione ena mwa malangizowa:
• Kuti tizikhala bwino ndi anthu ena
“Zinthu zonse zimene mukufuna kuti anthu akuchitireni, inunso muwachitire zimenezo.”—Mateyo 7:12.
“Aliyense wokhala ngati wamng’ono mwa inu nonse ndi amene ali wamkulu.”—Luka 9:48.
“Khalani ochereza.”—Aroma 12:13.
• Kuti tisiye makhalidwe oipa
“Ukayenda ndi anzeru udzakhala wanzeru, koma mnzawo wa opusa adzapwetekedwa.”—Miyambo 13:20.
“Usakhale mwa akumwaimwa vinyo.”—Miyambo 23:20.
“Usayanjane ndi munthu wokwiya msanga.”—Miyambo 22:24.
• Kuti tikhale ndi banja labwino
“Aliyense wa inu akonde mkazi wake monga adzikonda iye mwini; komanso mkazi akhale ndi ulemu waukulu kwa mwamuna wake.”—Aefeso 5:33.
“Valani chifundo chachikulu, kukoma mtima, kudzichepetsa, kufatsa, ndi kuleza mtima. Pitirizani kulolerana ndi kukhululukirana wina ndi mnzake ndi mtima wonse.”—Akolose 3:12, 13.
• Kuti tilere bwino ana
“Phunzitsa mwana poyamba njira yake; ndipo angakhale atakalamba sadzachokamo.”—Miyambo 22:6.
“Inunso atate, musamapsetse mtima ana anu, koma muwalere m’malango a Yehova ndi kuwaphunzitsa kalingaliridwe kake.”—Aefeso 6:4.
• Kuti tipewe mikangano
“Mayankhidwe ofatsa abweza mkwiyo; koma mawu owawitsa aputa msunamo.”—Miyambo 15:1.
“Posonyezana ulemu wina ndi mnzake, khalani patsogolo.”—Aroma 12:10.
Ngakhale anthu amene amagwirizana kwambiri, angachite bwino kusainirana pankhani za malonda kapena zilizonse zokhudza ndalama, kuti apewe mikangano. N’chifukwa chake mtumiki wa Mulungu Yeremiya analemba kuti: “Ndipo ndinalemba chikalatacho, ndichisindikiza, ndiitana mboni zambiri, ndiyesa ndalama m’miyeso.”—Yeremiya 32:10.
• Kuti tikhale ndi maganizo oyenera
“Zinthu zilizonse zoona, . . . za chikondi, zilizonse zoneneredwa zabwino, khalidwe labwino lililonse, ndi chilichonse chotamandika, pitirizani kuganizira zimenezi.”—Afilipi 4:8.
Baibulo limalimbikitsa anthu “okonda kudandaula za moyo wawo” kuti akhale ndi maganizo abwino ndipo limati: “Kondwerani ndi chiyembekezocho.”—Yuda 4, 16; Aroma 12:12.
Kugwiritsa ntchito malangizo amenewa kungatithandize kuti panopa tizisangalala komanso kungatithandize kuti tikhale oyenera kudzalandira madalitso a Mulungu m’tsogolo. Baibulo limati: “Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.”—Salmo 37:29.
[Zithunzi patsamba 5]
Akinori, panthawi imene anali pantchito (kumanzere) ndipo panopa akulalikira limodzi ndi mkazi wake