Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mumalola Kuti Mulungu Azikulankhulani Tsiku Lililonse?

Kodi Mumalola Kuti Mulungu Azikulankhulani Tsiku Lililonse?

KODI mumadziyang’anira kangati pagalasi? Ambirife timadziyang’anira tsiku ndi tsiku, mwinanso maulendo angapo patsiku. N’chifukwa chiyani timachita zimenezi? Chifukwa timafuna kudziwa mmene tikuonekera.

Kuwerenga Baibulo kuli ngati kudziyang’anira pagalasi. (Yakobe 1:23-25) Uthenga wa m’Mawu a Mulungu uli ndi mphamvu yotithandiza kudziwa mmene tilili. Uthengawu ‘umapyoza mpaka kulekanitsa moyo ndi mzimu.’ (Aheberi 4:12) M’mawu ena, tinganene kuti uthengawu umalekanitsa kaonekedwe kathu kakunja ndi umunthu wathu wamkati. Ndipo umatithandiza kudziwa zinthu zimene tikuyenera kusintha ngati mmene timachitira tikadziyang’anira pagalasi.

Baibulo limatithandiza kudziwa zimene tikufunikira kusintha komanso mmene tingasinthire. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Malemba onse anawauzira ndi Mulungu, ndipo ndi opindulitsa pa kuphunzitsa, kudzudzula, kuwongola zinthu, kulangiza m’chilungamo.” (2 Timoteyo 3:16, 17) Onani kuti lembali likusonyeza kuti timapindula m’njira zinayi, ndipo zitatu mwa njirazi, zomwe ndi kudzudzula, kuwongola zinthu ndiponso kulangiza, zikukhudza kusintha maganizo ndiponso zochita zathu. Ngati timafunika kudziyang’anira pagalasi kawirikawiri kuti tidziwe ngati tikuoneka bwino, ndiye kuti n’kofunikanso kuti nthawi zonse tiziwerenga Baibulo, lomwe ndi Mawu a Mulungu.

Yehova Mulungu atasankha Yoswa kuti atsogolere Aisiraeli, anamuuza kuti: “Buku ili la chilamulo lisachoke pakamwa pako; koma ulingiriremo usana ndi usiku, kuti usamalire kuchita monga mwa zonse zolembedwamo; popeza ukatero udzakometsa njira yako, nudzachita mwanzeru.” (Yoswa 1:8) Choncho, kuti zinthu zizimuyendera bwino, Yoswa anafunika kuwerenga Mawu a Mulungu “usana ndi usiku,” nthawi zonse.

Buku la Masalmo limasonyezanso ubwino wowerenga Baibulo nthawi zonse, ndipo limati: “Wodala munthuyo wosayenda mu uphungu wa oipa, kapena wosaimirira m’njira ya ochimwa, kapena wosakhala pansi pa bwalo la onyoza. Komatu m’chilamulo cha Yehova muli chikondwerero chake; ndipo m’chilamulo chake amalingirira usana ndi usiku. Ndiye akunga mtengo wowoka pa mitsinje ya madzi; wakupatsa chipatso chake pa nyengo yake, tsamba lake lomwe losafota; ndipo zonse azichita apindula nazo.” (Salmo 1:1-3) N’zosakayikitsa kuti nafenso tingafune kukhala ngati munthu ameneyu.

Anthu ambiri amawerenga Baibulo tsiku lililonse. Mkhristu wina atafunsidwa kuti afotokoze chifukwa chake amawerenga Baibulo tsiku lililonse, anayankha kuti: “Ndimapemphera kwa Mulungu maulendo angapo patsiku ndipo ndimayembekezera kuti andiyankha. Choncho ndimaona kuti ndiyeneranso kumvetsera zimene Mulungu akundiuza mwa kuwerenga Mawu ake tsiku lililonse. Ngati timafuna kukhala naye paubwenzi, palibe chifukwa choti tizingomuuza zofuna zathu osamvetsera zonena zake.” Zimenezi ndi zoona, kuwerenga Baibulo kulinga ngati kumvetsera zimene Mulungu akunena chifukwa timadziwa maganizo ake pankhani zosiyanasiyana.

Kodi Mungatani Kuti Muziwerenga Baibulo Tsiku Lililonse?

Mwina munayesapo kale kukhala ndi cholinga chowerenga Baibulo tsiku lililonse. Kodi munawerengapo Baibulo lonse? Zimenezi n’zothandiza kwambiri kuti mulidziwe bwino. Komabe, ena ayesapo kangapo konse kuwerenga Baibulo lonse koma amasiyira panjira. Kodi inunso zimenezi zinakuchitikiranipo? Kodi mungatani kuti mukwanitse kuwerenga Baibulo lonse? Tayesani njira ziwiri zotsatirazi.

Khalani ndi nthawi yowerenga Baibulo tsiku lililonse. Sankhani nthawi yomwe mukuona kuti ndi yabwino kuwerenga Baibulo tsiku lililonse. Konzani zimene mungachite ngati zinazake zitakusokonezani. Mwachitsanzo, ngati mwalephera kuwerenga Baibulo panthawi imene munakonza, sankhani nthawi ina n’cholinga choti tsiku lisadutse musanawerenge Mawu a Mulungu. Mukamachita zimenezi mudzakhala mukutsatira chitsanzo cha anthu a ku Bereya. Ponena za anthuwa, Baibulo limati: “Iwowa analandira mawuwo ndi chidwi chachikulu kwambiri. Anali kufufuza Malemba mosamala tsiku ndi tsiku kuti aone ngati zinthuzo zinalidi choncho.”​—Machitidwe 17:11.

Khalani ndi cholinga. Mwachitsanzo, ngati mutamawerenga machaputala atatu mpaka asanu patsiku, ndiye kuti mungamalize Baibulo lonse m’chaka chimodzi chokha. Ndandanda yomwe ili pamasamba otsatirawa ingakuthandizeni kuchita zimenezi. Tayesani kutsatira ndandanda imeneyi. Pansi pamawu akuti “Tsiku,” lembani tsiku limene mukufuna kudzawerenga machaputala omwe mwasankha. Ndiyeno m’kabokosiko, chongani mukamaliza kuwerenga machaputalawo. Zimenezi zidzakuthandizani kuona mmene mukuchitira.

Mukamaliza kuwerenga Baibulo lonse, musasiyire pomwepo. Mungagwiritsirenso ntchito ndandanda yomweyi powerenga Baibulo chaka ndi chaka, ndipo mwina chaka chilichonse mungayambire chigawo china. Ngati mukufuna kuwerenga Baibulo pang’onopang’ono, mungawerenge masiku awiri kapena atatu machaputala oyenera kuwerenga tsiku limodzi.

Nthawi iliyonse mukawerenga Baibulo, mudzapeza zinthu zatsopano zimene mungazigwiritsire ntchito pamoyo wanu, zomwe poyamba simunkazidziwa. Tikutero chifukwa “zochitika za padzikoli zikusintha,” ndipo zochitika pamoyo wathu zikusinthanso. (1 Akorinto 7:31) Choncho, khalani ndi cholinga chowerenga Mawu a Mulungu tsiku lililonse. Ngati mumachita zimenezi, ndiye kuti mumalola kuti Mulungu azikulankhulani tsiku lililonse.​—Salmo 16:8.