Kodi Munthu Akakhala Wosauka Ndiye Kuti Sakukondedwa ndi Mulungu?
Kodi Munthu Akakhala Wosauka Ndiye Kuti Sakukondedwa ndi Mulungu?
MULUNGU anauza Aisiraeli kuti: “Pasakhale waumphawi mwa inu.” Anawauza zimenezi chifukwa Chilamulo chimene anawapatsa chinali ndi malamulo a mmene angasamalirire anthu osauka ndiponso kukhululukira ena ngongole. (Deuteronomo 15:1-4, 7-10) Choncho, zimenezi zikanathandiza kuti pasakhale wina aliyense wosauka pakati pa Aisiraeli chifukwa Yehova anawalonjeza kuti akatero adzawadalitsa. Kuti Aisiraeliwo adalitsidwe, anafunika kumvera Chilamulo, koma iwo analephera kuchitsatira.
Komabe, zimenezi sizinatanthauze kuti Mulungu sankakonda anthu osauka komanso sizinatanthauze kuti ankakonda kwambiri olemera. Atumiki a Mulungu ambiri okhulupirika anali osauka. Mwachitsanzo, mneneri Amosi anali m’busa ndipo nthawi zina ankagwira maganyu. (Amosi 1:1; 7:14) M’nthawi ya mneneri Eliya, ku Isiraeli kutagwa chilala, Eliya ankapatsidwa chakudya ndi mzimayi wamasiye wosauka. Mzimayiyo anali ndi mafuta ndiponso ufa wochepa kwambiri koma zinthu zimenezi sizinathe m’nthawi yonse yachilalacho. Eliya ndiponso mzimayi wamasiyeyo sanakhale olemera pamoyo wawo, koma Yehova ankawapatsa zinthu zofunikira.—1 Mafumu 17:8-16.
Mavuto otigwera mwadzidzidzi akhoza kupangitsa munthu kukhala wosauka kwambiri. Ngozi ndiponso matenda zingapangitse munthu kulephera kugwira ntchito, mwina kwa kanthawi kapena kwa moyo wake wonse. Komanso imfa ikhoza kuchititsa kuti anthu ena akhale amasiye. Ngakhale munthu atakumana ndi mavuto ngati amenewa, sizitanthauza kuti sakukondedwa ndi Mulungu. Nkhani ya Naomi ndi Rute ndi chitsanzo chabwino kwambiri chosonyeza mmene Yehova amasamalirira mwachikondi anthu osauka. Ngakhale kuti Naomi ndi Rute anali osauka kwambiri chifukwa amuna awo anamwalira, Yehova Mulungu anawadalitsa poonetsetsa kuti akupeza zinthu zofunika pamoyo wawo.—Rute 1:1-6; 2:2-12; 4:13-17.
Apatu n’zoonekeratu kuti munthu akakhala wosauka sizitanthauza kuti sakukondedwa ndi Mulungu. Anthu amene ali okhulupirika kwa Yehova Mulungu, angagwirizane ndi zimene Mfumu Davide ananena kuti: “Ndinali mwana ndipo ndakalamba; ndipo sindinapenya wolungama wasiyidwa, kapena mbumba zake zilinkupempha chakudya.”—Salmo 37:25.
[Chithunzi patsamba 8]
Ngakhale kuti Naomi ndi Rute anali osauka kwambiri, Mulungu anawadalitsa ndiponso anawasamalira mwachikondi