Mayi Wosauka Koma Wosangalala
Kalata Yochokera ku Bolivia
Mayi Wosauka Koma Wosangalala
NDIMACHITA umishonale m’dziko la Bolivia, lomwe ndi losauka. Ndisanabwere m’dzikoli ndinali ndisanaonepo anthu osauka kwambiri. Panopa, ndimafuna mavuto onse atatha koma ndimadziwa kuti ndi Ufumu wa Mulungu wokha umene ungathetse mavutowa. Komabe, ndaonapo anthu ambiri amene amatsatira Mawu a Mulungu akusangalala ngakhale kuti amavutika. Mmodzi mwa iwo ndi mayi wina dzina lake Sabina.
Papita zaka zambiri pomwe Sabina ndi ana ake aakazi awiri anaperekeza mwamuna wake kokakwera basi paulendo wake wopita kukafuna ntchito yabwino ku dziko lina. Kwa zaka zambiri, iye wakhala akuyang’anira kunjira, koma mpaka pano kuli zii. Chichokereni mwamuna wake, Sabina amagwira ntchito mwakhama kuti asamalire ana ake awiri, Milena ndi Ghelian.
Ndinakumana koyamba ndi Sabina tsiku lina madzulo. Ndinam’peza akugulitsa m’golosale ya mchemwali wake ndipo anali atatanganidwa kwambiri, kuthandiza makasitomala. Sabina ankachita kuonekeratu kuti watopa chifukwa chogwira ntchito tsiku lonse. Ndinam’pempha kuti ndiziphunzira naye Baibulo limodzi ndi ana ake. Koma iye anayankha kuti: “Ndikanakonda mutamandiphunzitsa, koma ndimakhala wotanganidwa kwambiri. Komabe, mutha kumaphunzira ndi ana angawa.” Ndinavomera zimenezo ndipo nditayamba kuphunzira ndi atsikanawo, ndinadziwa zambiri zokhudza Sabina komanso ndinamvetsa mavuto amene ankakumana nawo.
Tsiku lililonse, Sabina amadzuka 4 koloko m’mawa, ana ake akugona m’kanyumba kawo kopanda chipinda. Iye amakoleza moto n’kuterekapo poto wa nyama yophikira samusa. Sabina amagulitsa samusayo kuti azipeza ndalama zosamalirira banja lake. Iye asanagone, amakandiratu ufa wophikira samusayo.
Kukacha, Sabina amalongedza bwinobwino zinthu zonse zofunikira mu wilibala yomwenso amachita kubwereka. Amatenga zinthu monga ambulela, sitovu yoyendera gasi, tebulo, timipando, mapoto, mafuta ophikira, nyama ndiponso ufa wokandakanda. Amatenganso zigubu za madzi azipatso amene amachita kupanga yekha.
Ikamakwana 6 kololo m’mawa, Sabina ndi ana ake amakhoma chitseko cha nyumba yawo n’kuyamba ulendo wopita kumalo awo ogulitsira samusa. Amayenda ali khumakhuma, popanda wolankhula kapena kuseka. Maganizo awo onse amakhala ali pantchito yawo. Nthawi zambiri, ndikayang’ana pawindo pa nyumba ya amishonale imene ndimakhala, ndimaona anthu akuchoka panyumba zawo m’mawa kwambiri, kukagwira ntchito ngati zimenezi. Sabina ndi mmodzi
mwa azimayi ambiri amene amachoka panyumba pawo kusanache kupita kokagulitsa zakudya ndi zakumwa m’misewu ya ku Bolivia.Ikamakwana 6:30, Sabina ndi ana ake amakhala atafika pamalo awo. Mwakachetechete, amatsitsa zinthu zawo mu wilibala ija, n’kuyamba kuphika samusa. Zikatero, kafungo konunkhira ka samusayo kamamveka pamalowo ndipo kamakopa makasitomala anjala kwambiri.
Zikatero, pamafika munthu woyamba kudzagula samusa ndipo Sabina amamufunsa kuti, “Mukufuna mungati?” Nthawi ina munthu woyamba kudzagula samusayo, yemwe ankaoneka kuti anali ali ndi tulo, anangoimika zala ziwiri. Kenako Sabina anam’patsa samusa muwiri, wopsa bwino komanso wotentha kwambiri, n’kulandira tindalama tochepa. Zimenezi n’zimene Sabina amachita kwa anthu onse omwe amabwera kudzagula samusa. Akangomaliza kugulitsa samusayo, amapakira zinthu zawo, n’kuuyambapo wa kunyumba. Ngakhale kuti Sabina amafika kunyumba miyendo ikumupweteka, iye amanyamuka kupita ku golosale ya mchemwali wake komwe amakagwiranso ntchito ina.
Patsiku loyamba limene ndinapita ku golosaleko kuti ndikaphunzire Baibulo ndi ana a Sabina, ndinapeza kuti aika kale mipando pakona kuti tikhalire. Milena ndi Ghelian, omwe anali a zaka 9 ndi 7, nthawi zonse ankasonyeza kuti akufunitsitsa kuphunzira ndipo ankakonzekera bwino phunzirolo. Pang’ono ndi pang’ono atsikanawo, omwe anali amanyazi, anayamba kundimasukira ndipo tinazolowerana. Zimenezi zinalimbikitsa kwambiri mayi awo. Kenako, nayenso Sabina anaganiza kuti aziphunzira nawo Baibulo ngakhale kuti ankakhala wotanganidwa kwambiri.
Sabina atayamba kudziwa zinthu zambiri za m’Baibulo, anayamba kukonda kwambiri Yehova Mulungu. Zimenezi zinachititsa kuti ayambe kusangalala, zomwe zinali zachilendo kwambiri kwa iye. Sabina, yemwe poyamba ankaoneka wotopa komanso wokhumudwa, anasintha kwambiri. Sankayendanso khumakhuma ndipo nkhope yake inayamba kuoneka yachimwemwe. Mchemwali wake uja anati: “Masiku ano Sabina amaoneka wosangalala, zomwe poyamba zinali zosatheka.” Anthu enanso anaona kuti Sabina ndi ana ake asintha kwambiri chifukwa chophunzira choonadi cha m’Baibulo.
Sabina ankasangalala ndi kuphunzira Baibulo koma ankalephera kufika pa misonkhano yachikhristu chifukwa chotanganidwa kwambiri. Patapita nthawi, iye anavomera kupita ku Nyumba ya Ufumu moti kungoyambira nthawi imeneyo, sajomba kumisonkhano ndipo wapeza anzake abwino mumpingo. Komanso waona kuti Yehova amasamalira anthu amene amamukonda ndiponso amene amadzipereka kumutumikira.—Luka 12:22-24; 1 Timoteyo 6:8.
Sabina ankakonda kwambiri zimene ankaphunzira moti ankafunitsitsa kuuza ena. Komabe, iye anati: “Ndinkachita mantha kwambiri ndikaganiza zolalikira.” Iye ankadziderera poganiza kuti, ‘Ndine wamanyazi ndiponso wosaphunzira, moti sindingakwanitse kuphunzitsa munthu.’ Ngakhale zinali choncho, iye anayamba kulalikira pofuna kuthokoza chifukwa choti enanso anamukomera mtima pom’phunzitsa Baibulo. Komanso anadziwa kuti moyo wake unasintha chifukwa chophunzira Baibulo. Anazindikiranso kuti ayenera kupereka chitsanzo chabwino kwa ana ake. Choncho anayamba kuuza ena uthenga wabwino ndipo nawonso ana ake anayamba kugwira nawo ntchito imeneyi.
Masiku ano, Sabina anasintha kwambiri ndipo anasiya kugwira ntchito yotopetsa komanso yosasangalatsa ija. Sikuti analemera ayi, koma wangosintha mmene amaonera zinthu pamoyo wake. Popeza kuti tsopano anabatizidwa, amagwira nawo ntchito yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu, umene udzathetseretu mavuto onse padzikoli.—Mateyo 6:10.
M’mawa uliwonse 5 koloko, Sabina amachoka panyumba pake, osati kupita kogulitsa samusa, koma kokalalikira ndi Akhristu anzake. Iye amadzipereka mlungu uliwonse kuthandiza ena ndipo zimenezi zamuthandiza kuti akhale wosangalala kwambiri. Amatseka chitseko cha nyumba yake kwinaku akumwetulira, n’kuyamba kulowera kumsewu. Koma m’malo mokankha wilibala, iye amanyamula chikwama chomwe amaikamo Baibulo, mabuku ndiponso magazini oti akagawire anthu ena. Masiku ano, Sabina akusangalala kwambiri, ndipo iye anati: “Sindinkaganiza zoti ndingathe kuuza anthu ena za m’Baibulo. Koma panopo ndimasangalala ndipo ndimaikonda kwambiri ntchito imeneyi.”