Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mapiri Ofika M’mitambo

Mapiri Ofika M’mitambo

Kalata Yochokera ku Papua New Guinea

Mapiri Ofika M’mitambo

TSIKU lina ine ndi mkazi wanga tinali pa ulendo wokayendera kagulu ka Mboni za Yehova ka ku Lengbati, mudzi wa kuphiri la Rawlinson lomwe lili m’dera lotchedwa Morobe Province. Panthawiyi tinkakhala ku Lae, mzinda wina wa konkuno ku Papua New Guinea (PNG). Tsikuli linali Lachiwiri ndipo tinayamba kukonzekera ulendo wathu 5 koloko m’mawa. Kunja kunkatentha ngakhale kuti kunalibe dzuwa.

Tinayenda pa ndege yaing’ono yokwera anthu anayi okha. Nthawi zambiri timayenda ulendowu kwa mphindi pafupifupi 30 basi. Pa maulendo amenewa, ine ndimakonda kukhala moyandikana ndi woyendetsa ndegeyi. Chifukwa cha phokoso la injini ya ndegeyi, timacheza pogwiritsira ntchito makina olankhulira. Titanyamuka patsikuli, woyendetsa ndegeyo anandilozera mabatani oyendetsera ndegeyo n’kundifotokozera ntchito zake ndipo moseka, anandiuza kuti ngati chinachake chitamuchitikira, ineyo ndiyendetse ndegeyo. Zimenezi zinandikumbutsa zomwe zinam’chitikira mtumiki wina woyendera mipingo ya Mboni za Yehova konkuno ku PNG. Woyendetsa ndege yawo anakomoka ndege ili m’malere ndipo ndegeyo inkangozungulira yokha mpaka woyendetsayo anatsitsimuka n’kuiteretsa. Mwamwayi, ifeyo sitinakumane ndi vuto lililonse pa ulendo wathuwu.

Titayenda kwakanthawi, tinayamba kudutsa pamwamba pa mapiri ambiri ogundizana, kenako tinangoona kuti tatuluka m’mitambo ndipo tinadutsa pafupi kwambiri ndi phiri lina. Panangotsala mamita pafupifupi 100 kuti tikhudze nsonga ya phirili. Kutsogolo kwathu tinaona nyumba zambiri zaudzu zomangidwa ndi mitengo ndiponso matabwa. Kumeneku n’kumene tinkapita, ku mudzi wa Lengbati. Woyendetsa ndege uja anayamba wayang’ana pabwalo la ndegeyo kuti aone ngati panali bwinobwino ndiponso ngati panalibe ana osewera mpira komanso timayenje timene nkhumba zimakonda kufukula. Kenako anazungulira n’kunena kuti, “Zili bwino, tiyese kutera.” Ndegeyo inayenda mozungulira n’kuyamba kutsika kuti itere. Anthu am’derali anakonza okha bwalo loti ndege zing’onozing’ono zizitera. Bwaloli lili m’mphepete mwa phiri ndipo analikonza poswa miyala pamalopo n’kusalazapo bwinobwino. Panthawi imene timafikayi n’kuti atangopankonzanso kumene. Iwo anaswerapo miyala ya laimu imene anaswa m’phiri lina lapafupi.

Ndikabwera kuno ndimachita chidwi ndi mapiri a miyala ya laimu ndipo ndimadzifunsa kuti, ‘Kaya mapiri amenewa atha zaka zingati kaya?’ Poyamba, miyala yambiri imene inapanga mapiri amenewa inali pansi pa nyanja. Koma kenako inakankhidwa mwamphamvu kwambiri moti inasuntha kufika kumtunda n’kupanga mapiri ogundizana aatali pafupifupi makilomita anayi. Ndege yathu itatera tinatsika n’kuponda nthaka ya kuderali kumene ine ndimangokutchula kuti kumapiri ofika m’mitambo.

Monga mwachizolowezi, anthu a m’mudziwu anathamanga n’kubwera atamva phokoso la ndege yathu. Woyendetsa ndegeyo ataizimitsa, munthu wina, dzina lake Zung, anatuluka m’gulu la anthuwo n’kubwera pafupi ndi ndegeyo. Iye ndi mmodzi mwa anthu amene anasankhidwa kuti azitsogolera misonkhano ya Mboni za Yehova m’derali. Pamisonkhanoyi amaphunzira Baibulo ndipo imachitikanso padziko lonse lapansi mlungu uliwonse. Anthu kumeneku amati Zung ndi wakhalidwe labwino, woona mtima ndiponso wodalirika. Koma mwiniwakeyo amati poyamba sanali wotere, anachita kusintha chifukwa chotsatira mfundo za m’Baibulo pa moyo wake. Titapatsana moni, tinatsika phirili limodzi ndi Zung komanso Mboni zina zimene zinadzatichingamira. Ana ankabwera m’mbuyo mwathu akukanganirana kunyamula zikwama zathu zoberekera.

Titatsetsereka pang’ono, tinafika panyumba ina yamatabwa imene inamangidwa ndi Mboni za m’derali kuti atumiki oyendera mipingo azifikiramo. Atumikiwa amayendera mipingo ya Mboni za Yehova kamodzi pa miyezi 6 iliyonse. Dziko la PNG lili m’dera lotentha, komabe kumapiri kuno kumazizira kwambiri. Kukada timayatsa nyali za palafini ndipo nthawi zambiri mitambo imadutsa m’timipata ta matabwa a pansi pa nyumba yathu n’kulowa m’nyumbamo. Masana, mitamboyi imakhala m’madera otsika ndipo kukamada imayenda pang’onopang’ono kubwera kumtunda kuno. Zochitika zake zimaseketsa pang’ono chifukwa munthu ukakhala m’mphepete mwa nyanja umachita kusamba thukuta chifukwa cha kutentha koma ukangokwera kumtunda kuno si kuzizira kwake, moti umafunika chovala cha mphepo kuti uzitenthedwa.

Cha m’ma 1980, munthu wina wa m’derali anapita kumzinda wa Lae ndipo anakakumana ndi Mboni za Yehova zomwe zinam’phunzitsa Baibulo. Atabwerako, iye limodzi ndi anzake angapo anamanga nyumba yaing’ono kuti azisonkhanamo. Koma kenako m’busa wina wa tchalitchi cha Lutheran chakumeneku anabwera limodzi ndi nkhosa zake n’kudzawotcha nyumba yochitira misonkhanoyo. Anthu ankhanzawa ananena moyerekedwa kuti derali ndi la tchalitchi cha Lutheran chokha basi. Anthu ena a m’mudziwu anapitirizabe kudana ndi Mboni za Yehova, komabe a Mboniwa anamanganso malo ena ochitira misonkhano yawo ndipo chiwerengero chawo chakhala chikukula moti panopa kuli anthu pafupifupi 50 amene amafalitsa uthenga wabwino nthawi zonse. Ena mwa anthu amene poyamba ankadana ndi ntchito ya Mboni, panopo nawonso ndi Mboni za Yehova ndipo akugwira nawo ntchitoyi mwakhama.

Masiku ano, anthu a m’derali nthawi zambiri amalola kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Ngakhale kuti ndi anthu ochepa chabe amene amatha kuwerenga m’mudziwu, a Mboni za Yehova ambiri aphunzira kuwerenga kuti aziphunzitsa ena uthenga wa m’Baibulo. Mlungu uliwonse anthu oposa 200 amabwera kumisonkhano yawo yomwe imachitikira ku Nyumba ya Ufumu.

M’mudziwu mulibe magetsi. Choncho madzulo timasonkhana m’khitchini n’kukhala mozungulira moto. Timadyera limodzi kwinaku tikukamba nkhani zathu n’kumaseka. Moto ukawalira nkhope za anthuwa, amaoneka kuti akusangalala kwambiri chifukwa chotumikira Yehova. Kenako, kunja kukada kwambiri, ena amafumula matsatsa a kanjedza pamotopo kuti aunikire njira yakwawo.

Ifenso tikubwerera kunyumba komwe tinafikira, tinachita chidwi kuona kuti kunja kunangoti zii, moti phokoso lokha lomwe linkamveka linali la tizilombo tosiyanasiyana. Tisanagone, tinayang’ananso nyenyezi kumwamba ndipo zinali zochititsa chidwi kwambiri kuona kuchuluka kwa nyenyezi zimene zimaoneka m’dera la mapiri lino.

Posakhalitsa Lamlungu linafika ndipo tinali titangotsala ndi tsiku limodzi lokha tili kumudziwu. Tsiku lotsatira ndege ija inabwera kudzatitenga ndipo tinabwerera ku Lae.