Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Yesu Anati Iye Ndi Ndani?

Kodi Yesu Anati Iye Ndi Ndani?

Kodi Yesu Anati Iye Ndi Ndani?

“N’zosakayikitsa kuti Yesu ankadziwa kuti iye anali ndani, ankadziwanso komwe anachokera, chifukwa chimene anabwerera padziko lapansi komanso kuti tsogolo lake lidzakhala lotani.”​—Anatero wolemba mabuku wina dzina lake HERBERT LOCKYER.

KUTI munthu akhulupirire zimene Yesu anaphunzitsa, ayenera kudziwa kaye zina ndi zina zokhudza iyeyo. Mwachitsanzo, kodi Yesu anali ndani kwenikweni? Kodi anachokera kuti? N’chifukwa chiyani anabwera padziko lapansi? Tingapeze mayankho a mafunso amenewa poona zimene Yesu ananena m’mabuku a Uthenga Wabwino a Mateyo, Maliko, Luka ndi Yohane.

Iye analipo kale asanabadwe padziko lapansi pano Nthawi ina Yesu ananena kuti: “Abulahamu asanakhaleko, ine n’kuti ndilipo kale.” (Yohane 8:58) Ngakhale kuti Yesu anabadwa patapita zaka 2,000 Abulahamu atamwalira, iye anali alipo Abulahamuyo asanabadwe. Ndiyeno kodi Yesu panthawiyi anali ali kuti? Iye anayankha yekha funso limeneli kuti: “Ndinatsika kuchokera kumwamba.”​—Yohane 6:38.

Mwana wa Mulungu Yehova ali ndi ana ambiri auzimu, kapena kuti angelo. Komabe, Yesu ndi mwana wapadera kwambiri. Iye anadzitchula kuti ndi “Mwana wobadwa yekha wa Mulungu.” (Yohane 3:18) Mawu amenewa akutanthauza kuti Yesu ndi yekhayo amene analengedwa ndi Mulungu popanda kuthandizidwa ndi wina aliyense. Ndipo Mulungu analenga zinthu zina zonse kudzera mwa Mwana wobadwa yekha ameneyu.​—Akolose 1:16.

“Mwana wa munthu” Yesu ankakonda kugwiritsa ntchito dzina limeneli kuposa maina ake ena onse. (Mateyo 8:20) Choncho, anasonyeza kuti iye sanali mzukwa kapena mngelo amene anangosintha kuti akhale ngati munthu. Koma iye anali munthu weniweni. Mulungu anasamutsa moyo wa Mwana wake kuchoka kumwamba kubwera padziko lino lapansi. Pogwiritsa ntchito mzimu woyera, Mulungu anachititsa kuti Mariya, amene anali namwali, akhale ndi pakati. Choncho Yesu anabadwa wangwiro, wopanda uchimo.​—Mateyo 1:18; Luka 1:35; Yohane 8:46.

Mesiya wolonjezedwa Mkazi wina wa ku Samariya anauza Yesu kuti: “Ndikudziwa kuti Mesiya akubwera.” Ndipo Yesu anati: “Ndine ndemwe, amene ndikulankhula nanune.” (Yohane 4:25, 26) Mawu akuti “Mesiya” amatanthauza “Wodzozedwa,” chimodzimodzinso ndi mawu akuti “Khristu.” Zimenezi zikutanthauza kuti Yesu anali wodzozedwa, kapena kuti anasankhidwa ndi Mulungu, kuti agwire ntchito yapadera pokwaniritsa zimene Mulungu analonjeza.

Chifukwa chachikulu chimene anabwerera padziko lapansi Nthawi ina Yesu anati: “Ndiyenera kukalengeza uthenga wabwino wa ufumu wa Mulungu ku mizinda inanso, chifukwa ndizo anandituma kudzachita.” (Luka 4:43) Ngakhale kuti Yesu anachitira anthu osauka zinthu zambiri zabwino, ntchito yake yaikulu inali kulalikira za Ufumu wa Mulungu. Tikambirana zimene iye anaphunzitsa ponena za ufumu umenewu mu imodzi mwa nkhani zotsatirazi.

Ndithudi, Yesu sanali munthu wamba. * Monga mmene tionere, moyo umene anali nawo kumwamba unathandiza kuti uthenga umene ankalalikira padziko pano ukhale wogwira mtima kwambiri. N’chifukwa chake sizodabwitsa kuti uthenga wake umakhudza mitima ya anthu ambiri padziko lonse.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 9 Kuti mudziwe zambiri zokhudza Yesu ndiponso udindo wake pokwaniritsa cholinga cha Mulungu, onani mutu 4 m’buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.