Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Samalani Kuti Musanyengedwe

Samalani Kuti Musanyengedwe

Samalani Kuti Musanyengedwe

DON QUIXOTE ndi munthu wa m’nthano yodziwika bwino kwambiri m’mayiko ena. Nthanoyi inalembedwa ndi Miguel de Cervantes wa ku Spain wa m’zaka za m’ma 1500. Don Quixote ankawerenga kwambiri nkhani zopeka zokhudza anthu olimba mtima amene anapulumutsa atsikana amene moyo wawo unali pangozi. Chifukwa chowerenga kwambiri nkhani zoterozo, Don Quixote anayamba kunyengeka n’kudziona kuti iyenso ndi munthu wolimba mtima komanso wolemekezeka. Nthawi ina, iye analimbana ndi makina oyendera mphepo poganiza kuti ndi ziphona zoopsa kwambiri. Iye ankaganiza kuti angakondweretse Mulungu atapha ziphonazo, koma zimenezo zinali zopanda nzeru moti nkhani yake inatha mochititsa manyazi kwambiri makinawo atamukankha ndi kumugwetsa chagada.

Nkhani ya Don Quixote ndi yopeka, koma ikungosonyeza kuti munthu akanyengedwa amatha kuchita zinthu zimene zingamubweretsere mavuto aakulu. Mwachitsanzo, taganizani za munthu amene amamwa mowa mwauchidakwa. Iye angaganize kuti atha kumwa mowa mmene akufunira. Koma pa mapeto pake angathe kudwala matenda aakulu ndiponso banja lake lingathe kusokonekera. Taganizaninso za mtsikana amene sadya mokwanira chifukwa choopa kunenepa. Iye angaganize kuti akudya chakudya chopatsa thanzi koma sadziwa kuti angathe kufa chifukwa cha zimenezi.

Kodi nafenso tinganyengedwe ndi zinthu zinazake? N’zomvetsa chisoni kuti yankho la funso limeneli ndi lakuti inde, tonsefe tikhoza kunyengedwa pa zinthu zosiyanasiyana. Tikhozanso kunyengedwa pa nkhani ya zimene timakhulupirira m’chipembedzo chathu, ndipo zotsatirapo zake zingakhale zoopsa kwambiri. N’chifukwa chiyani zili choncho? Kodi mungatani kuti musanyengedwe?

Kunyengedwa N’koopsa

Dikishonale ina imanena kuti mawu akuti kunyenga amatanthauza “kuchititsa munthu kukhulupirira zinthu zabodza.” Amatanthauzanso “kuchita zinthu zolepheretsa munthu kudziwa zinthu n’cholinga choti asokonezeke ndiponso azilephera kuchita zinthu zina payekha.” Mawu amenewa, komanso mawu ena ofanana nawo monga akuti “kupusitsa,” kwenikweni amatanthauza kusocheretsa munthu mwachinyengo. Choncho munthu amene sakudziwa kuti anthu ena akumusocheretsa mwadala n’cholinga chomusokoneza kuti ‘asadziwe bwinobwino zinthu zinazake kapena kuti azilephera kuchita zinthu payekha’ ali pangozi yaikulu.

Chomvetsa chisoni kwambiri ndi chakuti munthu amene wanyengedwa kapena kusocheretsedwayo amakakamirabe zimene anauzidwazo ngakhale patakhala umboni wamphamvu wosonyeza kuti zimenezo ndi zabodza. Mwina zimakhala chifukwa chakuti amakonda kwambiri zimene anauzidwazo moti amangotseka maso ndi makutu ake kuti asaone kapena kumva china chilichonse chotsutsana ndi zimene amakhulupirirazo.

Kodi Aliyense Angathe Kunyengedwa?

Mwina mungaganize kuti, ‘N’zosatheka kuti aliyense anganyengedwe pa nkhani ya chipembedzo.’ Koma dziwani kuti Satana Mdyerekezi, amene Yesu anamutchula kuti ndi “tate wake wa bodza,” akufunitsitsa kwambiri kutinyenga ndiponso kutisocheretsa. (Yohane 8:44) Baibulo limanenanso kuti Satana ndi “mulungu wa dongosolo lino la zinthu,” ndipo kuyambira kale iye wakhala ‘akuchititsa khungu maganizo’ a anthu ambiri. (2 Akorinto 4:4) Ngakhale panopa iye “akusocheretsa dziko lonse lapansi kumene kuli anthu.”​—Chivumbulutso 12:9.

Satana anayamba kunyenga anthu kuyambira kale kwambiri. Mwachitsanzo, iye ananyenga Hava kuti akhulupirire kuti akanatha kukhala wosangalala popanda kumvera malamulo a Mlengi wake. Hava anayambanso kukhulupirira kuti ‘angafanane ndi Mulungu pa nkhani ya kudziwa zabwino ndi zoipa,’ kapena kuti akanatha kudziwa yekha zabwino ndi zoipa popanda kuthandizidwa ndi Mulungu. (Genesis 3:1-5) Chimenechi chinali chinyengo choyamba ndiponso chachikulu kwambiri chimene Satana anachita. Ngakhale kuti anthufe tinapatsidwa ufulu wosankha zimene tikufuna kuchita, sitinalengedwe kuti tizitha kudziwa tokha chabwino kapena choipa. Mulungu yekha, amene ndiye Mlengi ndiponso Ambuye Wamkulu Koposa, ndi amene ali ndi ufulu ndiponso mphamvu yochita zimenezo. (Yeremiya 10:23; Chivumbulutso 4:11) Munthu amene amakhulupirira kuti ufulu wosankha kuchita chabwino kapena choipa umatanthauza kuti munthu angathe kudziwa yekha chabwino ndi choipa popanda thandizo la Mulungu ndiye kuti wasocheretsedwa. Koma n’zomvetsa chisoni kuti umenewu ndi msampha umene anthu ochimwafe timakodwa nawo kawirikawiri.

Kodi Zimenezi Zakuchitikirani Inuyo?

N’kutheka kuti zimene mumakhulupirira zinayamba kale kwambiri, mwinanso n’zimene makolo anu ndiponso makolo awo ankakhulupirira. Koma umenewu si umboni wosonyeza kuti zimene mumakhulupirirazo n’zoona. Chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa chakuti Baibulo limasonyeza kuti atumwi a Khristu atafa onse, anthu achinyengo analowa mu mpingo wachikhristu ndipo anayamba kuphunzitsa zinthu “zopotoka kuti akanganule ophunzira aziwatsatira.” (Machitidwe 20:29, 30) Iwo mochenjera anasocheretsa anthu “ndi mfundo zokopa” komanso “mwa nzeru za anthu ndi chinyengo chopanda pake, malinga ndi miyambo ya anthu.”​—Akolose 2:4, 8.

Kodi masiku ano zinthu zasintha? Ayi ndithu. Mtumwi Paulo anatichenjeza kuti zinthu zidzaipa kwambiri “m’masiku otsiriza” ano. Iye analemba kuti: “Anthu oipa ndi onyenga adzaipiraipirabe, kusocheretsa ena ndi kusocheretsedwa.”​—2 Timoteyo 3:1, 13.

Choncho ndi nzeru kumvera chenjezo la mtumwi Paulo lakuti: “Ndiye chifukwa chake iye amene akuyesa kuti ali chilili asamale kuti asagwe.” (1 Akorinto 10:12) N’zoona kuti palembali Paulo ankanena za ubwenzi wathu ndi Mulungu, komabe ngati munthu amaganiza kuti Satana sangamunyenge, ndiye kuti wasocheretsedwa kale. Aliyense angathe kunyengedwa ndi “machenjera a Mdyerekezi.” (Aefeso 6:11) N’chifukwa chake mtumwiyu anadera nkhawa Akhristu anzake ndipo anawauza kuti: “Mwina, monga njoka inanyenga Hava mwa machenjera ake, maganizo anunso angapotozedwe kuti musakhalenso oona mtima ndi oyera, monga muyenera kukhalira kwa Khristu.”​—2 Akorinto 11:3.

Kodi Mungatani Kuti Musanyengedwe?

Choncho kodi mungatani kuti musanyengedwe ndi Satana? Nanga mungachite chiyani kuti ‘muzilambira Mulungu ndi mzimu ndi choonadi?’ (Yohane 4:24) Gwiritsani ntchito nzeru zimene Yehova Mulungu wakupatsani. Iye wakupatsani “nzeru” zimene zingakuthandizeni kusiyanitsa zoona ndi zonama. (1 Yohane 5:20) Yehova angakuthandizeninso kudziwa njira za Satana zofuna kutisokoneza. (2 Akorinto 2:11) Ndipotu iye wakupatsani chilichonse chimene mungafunikire kuti mulimbane ndi mayesero a Satana ofuna kukusocheretsani.​—Miyambo 3:1-6; Aefeso 6:10-18.

Kuposa zonse, Mulungu wakupatsani njira yodalirika kwambiri imene mungadzitetezere. Kodi njira imeneyi ndi iti? Ndi yofanana ndi imene mtumwi Paulo anauza Timoteyo kuti azitsatira pa nkhani ya chikhulupiriro. Atapereka chenjezo lokhudza “anthu oipa ndi onyenga,” mtumwi Paulo anauza Timoteyo kuti azipewa anthu oterewa mwa kuonetsetsa kuti chilichonse chimene amakhulupirira n’chochokera “m’malemba opatulika,” kapena kuti Baibulo lomwe ndi Mawu a Mulungu.​—2 Timoteyo 3:15.

Anthu ena anganene kuti munthu aliyense amene amakhulupirira Mulungu ndiponso kukhulupirira kuti Baibulo ndi Mawu a Mulungu ouziridwa, ndiye kuti wasocheretsedwa. Koma zoona n’zakuti anthu amene asocheretsedwa ndi amene amakana kuti kuli Mlengi ndiponso amene amakana kuti Baibulo ndi Mawu a Mulungu ouziridwa. *​—Aroma 1:18-25; 2 Timoteyo 3:16, 17; 2 Petulo 1:19-21.

M’malo monyengedwa ndi “zimene ena monama amati ndiko ‘kudziwa zinthu,’” muyenera kuwerenga Mawu a Mulungu kuti mudziwe choonadi. (1 Timoteyo 6:20, 21) Mukhale ngati amuna ndi akazi anzeru amene mtumwi Paulo anawalalikira ku Bereya. Iwo “analandira mawuwo ndi chidwi chachikulu kwambiri.” Iwo sanangokhulupirira zimene mtumwi Paulo anaphunzitsa, koma “anali kufufuza Malemba mosamala tsiku ndi tsiku kuti aone ngati zinthuzo zinalidi choncho.”​—Machitidwe 17:11.

Mofanana ndi anthu a ku Bereya, musaope kuunikanso zimene mumakhulupirira. Baibulo limatilimbikitsa kuti ‘tizitsimikizira zinthu zonse’ tisanayambe kuzikhulupirira. (1 Atesalonika 5:21) Chaka cha 100 C.E. chitatsala pang’ono kukwana, mtumwi Yohane analimbikitsa Akhristu anzake kuti: “Okondedwa, musamakhulupirire mawu alionse ouziridwa, koma yesani mawu ouziridwawo kuti muone ngati ali ochokera kwa Mulungu.” (1 Yohane 4:1) Ngakhale kuti chipembedzo china chingamaphunzitse mfundo inayake yooneka ngati ‘youziridwa’ kapena yochokera kwa Mulungu, tingachite bwino kufufuza m’Malemba tisanayambe kukhulupirira mfundoyo.​—Yohane 8:31, 32.

Tsatirani Zimene Mwaphunzira

Koma palinso chinthu chimene muyenera kuchita. Yakobe, yemwe anali wophunzira wa Yesu, analemba kuti: “Khalani ochita zimene mawu amanena, osati ongomva chabe, ndi kudzinyenga ndi malingaliro onama.” (Yakobe 1:22) Kungodziwa zimene Baibulo limaphunzitsa sikokwanira. Muyeneranso kuchita zimene Baibulo limanena. Kodi mungachite bwanji zimenezi? Muzitsatira malamulo a Mulungu ndipo muzipewa kuchita zimene iye amaletsa.

Mwachitsanzo, tangoganizirani mmene makhalidwe abwino alowera pansi. Kodi zimenezi sizikusonyeza kuti Satana akunyengadi anthu kuti aziganiza kuti palibe vuto kuphwanya malamulo a Mulungu okhudza makhalidwe abwino? N’chifukwa chake mtumwi Paulo anachenjeza Akhristu mosapita m’mbali kuti: “Musanyengedwe: Mulungu sapusitsika. Chilichonse chimene munthu wafesa, adzakololanso chomwecho.”​—Agalatiya 6:7.

Musakhale ngati “munthu wopusa” amene Yesu ananena kuti ‘amamva’ zimene Yesuyo akunena koma ‘sachita.’ Mofanana ndi Don Quixote, amene anadzinyenga ndi maganizo ake mu nthano yolembedwa ndi Cervantes ija, munthu wopusayo ananyengedwa poganiza kuti akhoza kumanga nyumba yolimba pamchenga. Koma, khalani ngati munthu amene “anamanga nyumba yake pathanthwe.” Yesu ananena kuti munthu wotereyu ndi “wochenjera” chifukwa anamva mawu a Yesu ndi “kuwachita.”​—Mateyo 7:24-27.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 18 Kuti mudziwe zambiri, onani buku lakuti, Baibulo​—Kodi Ndilo a Mulungu Kapena a Munthu? komanso lachingelezi lakuti, Is There a Creator Who Cares About You? Mabukuwa ndi ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 12, 13]

Maonekedwe Apusitsa

M’ma 1930, katswiri wina wojambula zithunzi wa ku Sweden, dzina lake Oscar Reutersvärd, anajambula zinthu zosiyanasiyana koma zosonyeza zinthu zosatheka. Chitsanzo cha zithunzi zimenezi ndi chimene chili kumanzereku. Kungochiona chithunzichi, munthu angaganize kuti chili bwinobwino. Koma mukachiyang’anitsitsa kwambiri, mutha kuzindikira kuti zimene mukuonazo n’zosatheka koma kungoti chithunzicho anachijambula m’njira yoti munthu aziona ngati chili bwinobwino.

Mofanana ndi zithunzi zoterezi, palinso zinthu zina zimene zimaoneka mopusitsa. Zaka 2,000 zapitazo, Baibulo linachenjeza kuti: “Samalani: mwina wina angakugwireni ngati nyama, mwa nzeru za anthu ndi chinyengo chopanda pake, malinga ndi miyambo ya anthu, malinga ndi mfundo zimene zili maziko a moyo wa m’dzikoli, osati malinga ndi Khristu.”​—Akolose 2:8.

Chochititsa chidwi kwambiri ndi chenjezo limeneli n’chakuti amene analilemba anali atanyengedwapo m’mbuyomo. Iye anaphunzitsidwa ndi mmodzi mwa atsogoleri otchuka kwambiri achipembedzo pa nthawiyo, ndiponso ankadziwana ndi akuluakulu ena. Ankaoneka ngati wozindikira woti sangapusitsike ndi chilichonse.​—Machitidwe 22:3.

Munthu ameneyu anali Saulo wa ku Tariso. Iye ananyengedwa moti anayamba kuona kuti aliyense amene ankakhulupirira zosiyana ndi zimene iye ankakhulupirira, anali woyenera kulangidwa. Saulo anapatsidwa mphamvu ndi atsogoleri achipembedzo achiyuda zolanga aliyense amene ankachita zosiyana ndi chipembedzo chachiyuda. Ankachita zimenezi poganiza kuti akuchita chifuniro cha Mulungu. Iye anathandiza nawo kupha Myuda mnzake, yemwe ananamiziridwa kuti wachitira mwano Mulungu.​—Machitidwe 22:4, 5, 20.

Kenako Saulo anathandizidwa kuti azitha kusiyanitsa chabwino ndi choipa komanso kuti azitha kudziwa zimene Mulungu amakonda ndi zimene amadana nazo. Saulo atazindikira kuti sankachita bwino, anasiya kuchita zoipa ndipo anayamba kudziwika kuti Paulo, mtumwi wa Yesu Khristu. Pa nthawiyi, Paulo sankanyengedwanso chifukwa anapeza chipembedzo choona.​—Machitidwe 22:6-16; Aroma 1:1.

Mofanana ndi Paulo, anthu ambiri ofunitsitsa kudziwa choonadi ananyengedwapo ndi ziphunzitso zina zomveka ngati zabwinobwino, pamene kwenikweni sizogwirizana ndi Mawu a Mulungu. (Miyambo 14:12; Aroma 10:2, 3) Koma kenako, anathandizidwa kuzindikira kuti zikhulupiriro zawozo sizinali zoona komanso kuti ntchito za chipembedzo chawo zinali zoipa. (Mateyo 7:15-20) Atayamba kumvetsa zimene Baibulo limanena, anasiya zikhulupiriro zawo ndi makhalidwe awo oipa n’cholinga chakuti Mulungu aziwakonda.

Kodi mungakonde kutsatira chitsanzo cha mtumwi Paulo, n’kufufuza kuti muone ngati zimene mumakhulupirira zimagwirizana ndi Mawu a Mulungu, Baibulo? Mboni za Yehova zingakuthandizeni kuchita zimenezi.

[Mawu a Chithunzi patsamba 10]

Engravings by Doré