Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

1 Kodi N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kupemphera?

1 Kodi N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kupemphera?

PEMPHERO ndi imodzi mwa nkhani zochepa zimene zimachititsa chidwi kwambiri anthu. Mwachitsanzo, taganizirani mafunso 7 amene tikambirane m’nkhani zino, onena za pemphero, amene anthu amafunsa kawirikawiri. Kenako tifufuzire limodzi mayankho ake m’Baibulo. Nkhani zimenezi zakonzedwa kuti zikuthandizeni pa nkhani ya pemphero. Zikuthandizani kuti muyambe kupemphera kapena zikuthandizani kuti mapemphero anu azikhala ochokera mumtima.

PADZIKO lonse lapansi anthu azikhalidwe ndiponso zipembedzo zosiyanasiyana amapemphera. Iwo amapemphera pa okha kapena pagulu. Amapemphera m’tchalitchi, m’kachisi, m’sunagoge mumzikiti kapenanso pamalo olambirira mizimu ya makolo. Popemphera, ena amagwada pakansalu kopemphererapo, kapena amagwiritsa ntchito kolona. Enanso amagwiritsa ntchito chinthu chozungulira chimene mkati mwake amaikamo timapepala timene alembapo mapemphero. Ena amawerenga mapemphero awo m’mabuku, kapena amawalemba patimatabwa timene amatipachika penapake.

Anthu okha ndiwo amapemphera ndipo palibe zolengedwa zinanso padziko lapansi pano zimene zimapemphera. N’zoona kuti anthufe timafanana ndi nyama pa zinthu zambiri. Mwachitsanzo, nyama zimafunika chakudya, mpweya, ndiponso madzi. N’chimodzimodzinso anthufe. Mofanana ndi nyama, ifenso timabadwa, timakhala ndi moyo ndipo kenako timafa. (Mlaliki 3:19) Koma mosiyana ndi nyama, anthu amapemphera. Kodi n’chifukwa chiyani zili choncho?

Mwina yankho lachidule n’lakuti tiyenera kupemphera. Anthu ambiri amaona kuti pemphero ndi njira yolankhulirana ndi munthu kapena chinthu chinachake chauzimu chimene amachiona kuti ndi chopatulika, choyera komanso chosatha. Baibulo limasonyeza kuti tinalengedwa ndi mtima wofuna kupemphera. (Mlaliki 3:11) Pa nthawi ina Yesu Khristu anati: “Odala ndi anthu amene amazindikira zosowa zawo zauzimu.”​—Mateyu 5:3.

Anthu amanga nyumba zopemphereramo zambirimbiri ndipo amatha maola ambiri akupemphera. Zimenezi zikusonyeza kuti anthu alidi ndi ‘zosowa zauzimu.’ Ena amaona kuti okha angathe kupeza zosowa zawo zauzimu kapena munthu wina akhoza kuwapatsa zimenezo. Koma anthu sangatipatse zosowa zathu zauzimu. Anthufe tili ndi mphamvu zochepa, moyo wathu ndi waufupi ndipo sitingadziwe zonse za m’tsogolo. Pakufunika winawake wanzeru ndiponso wamphamvu kwambiri, amenenso moyo wake ndi wautali kwambiri kuti azitipatsa zimene tikufunikira. Zosowa zauzimu n’zimene zimatichititsa kuti tizifuna kupemphera. Koma kodi zosowa zauzimu zimenezi n’chiyani?

Taganizirani mfundo iyi: Kodi mumalakalaka winawake atamakutsogolerani, kukupatsani nzeru kapena kukuthandizani kupeza mayankho a mafunso amene munthu sangathe kuwayankha? Kodi nthawi ina munalakalaka wina atakulimbikitsani chifukwa cha chisoni chimene munali nacho mutaferedwa? Kapena munalakalaka wina atakutsogolerani kuti musankhe zinthu mwanzeru pa nkhani inayake imene inakuvutitsani maganizo kwambiri? Kapena kodi nthawi ina munalakalaka mutakhululukidwa tchimo linalake limene linakuvutitsani maganizo kwambiri?

Baibulo limanena kuti zonsezi ndi zifukwa zabwino zopempherera. Baibulo ndi buku lothandiza kwambiri pa nkhani ya pemphero, ndipo lili ndi mapemphero amene amuna ndi akazi ambiri okhulupirika anapemphera. Anthu amenewo anapemphera pofuna kulimbikitsidwa, kutsogoleredwa komanso kupeza mayankho a mafunso ovuta kwambiri.​—Salimo 23:3; 71:21; Danieli 9:4, 5, 19; Habakuku 1:3.

Ngakhale kuti mapemphero amenewo ndi osiyana kwambiri, anthu amene anapemphera mapemphero amenewa anafanana pa chinthu chimodzi. Iwo ankadziwa chimene chimafunika kuti pemphero liyankhidwe. Onse ankadziwa kuti ayenera kupemphera kwa ndani. Koma anthu ambiri masiku ano sadziwa mfundo imeneyi kapenanso amainyalanyaza.