Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

2 Kodi Tiyenera Kupemphera kwa Ndani?

2 Kodi Tiyenera Kupemphera kwa Ndani?

KODI mapemphero onse amapita kumalo amodzi, kaya wopempherayo akutchula dzina la ndani? Anthu ambiri masiku ano amaganiza choncho. Ambiri mwa anthuwa ndi amene amafuna kuti zipembedzo zonse zizichitira zinthu pamodzi. Anthu amenewa amaona kuti zipembedzo zonse n’zovomerezeka kwa Mulungu ngakhale kuti zimasiyana zochita. Koma kodi n’kutheka kuti mwina mfundo imeneyi si yoona?

Baibulo limanena kuti anthu ambiri amapemphera kwa mulungu wolakwika. Kalekale pamene Baibulo linali kulembedwa, anthu ambiri anali kupemphera kwa mafano osema. Koma nthawi zonse Mulungu anali kudzudzula khalidwe limenelo. Mwachitsanzo, pa Salimo 115:4-6, Mulungu ananena za mafano kuti: “Makutu ali nawo koma satha kumva.” Mfundo yake pamenepa ndi yakuti, si chinthu chanzeru kupemphera kwa mulungu amene saamva.

M’Baibulo muli nkhani inayake yosangalatsa yokhudza mfundo imeneyi. Mneneri woona Eliya anauza aneneri a Baala kuti apemphere kwa mulungu wawo ndipo kenako Eliyayo apempheranso kwa Mulungu wake. Iye anawauza kuti Mulungu woona ndi amene ayankhe pemphero la olambira ake, pamene mulungu wonyenga sayankha. Aneneri a Baala anavomera kuchita zimenezo, ndipo anapemphera kwa nthawi yaitali komanso mokuwa kwambiri. Koma palibe chimene chinachitika. Nkhaniyo imati: “Palibe anawayankha kapena kuwamvera.” (1 Mafumu 18:29) Nangano kodi Eliya zinamuthera bwanji?

Eliya atapemphera, Mulungu anayankha pemphero lake nthawi yomweyo mwa kutumiza moto kuchokera kumwamba. Moto umenewo unanyeketsa nsembe yonse imene Eliya anaiika paguwa. Kodi n’chiyani chinachititsa kuti pakhale kusiyana kumeneku? Pemphero la Eliya, lolembedwa pa 1 Mafumu 18:36, 37, likusonyeza chimene chinachititsa. Pempheroli ndi lalifupi ndipo m’Chiheberi choyambirira lili ndi mawu pafupifupi 30 basi. Koma m’mawu ochepa omwewo Eliya anatchula dzina la Mulungu lakuti Yehova katatu konse.

Baala anali mulungu wa Akanani ndipo mawu akuti Baala amatanthauza “mwiniwake” kapena “mbuye.” Akananiwo ankalambiranso milungu ya Baala ya mitundu yosiyanasiyana. Koma dzina lakuti Yehova ndi la Mulungu mmodzi yekha basi m’chilengedwe chonse. Mulungu ameneyu anauza anthu ake kuti: “Ine ndine Yehova. Dzina langa ndi limeneli, ndipo sindidzapereka ulemu wanga kwa wina aliyense.”​—Yesaya 42:8.

N’chifukwa chiyani pemphero la Eliya linayankhidwa pamene mapemphero a aneneri a Baala sanayankhidwe? Anthu opembedza Baala sanali kulemekeza moyo wa anthu chifukwa ina mwa miyambo ya chipembedzo chawo inkaphatikizapo kuchita uhule ngakhalenso kupereka anthu nsembe. Mosiyana ndi zimenezi, kupembedza Yehova kunachititsa anthu ake, Aisiraeli, kukhala olemekezeka chifukwa kunawateteza kuti asamachite zinthu zonyansa ngati zimene opembedza Baala ankachita. Ndiyeno taganizirani izi: Mutakhala kuti mwalembera kalata mnzanu wolemekezeka kwambiri ndiponso wakhalidwe labwino, kodi mungaitumize kwa munthu wina amene dzina lake ndi losiyana ndi la mnzanuyo, komanso khalidwe lake ndi loipa kwambiri? N’zodziwikiratu kuti simungatero.

Zimene Eliya anachita potsutsana ndi aneneri a Baala, zikusonyeza kuti si mapemphero onse amene amapita kwa Mulungu woona

Mukamapemphera kwa Yehova, ndiye kuti mukupemphera kwa Mlengi amene ndi Atate wa anthu onse. * Mneneri Yesaya popemphera ananena kuti: “Inuyo Yehova ndinu Atate wathu.” (Yesaya 63:16) Atate ameneyu ndi amene Yesu Khristu ankanena pamene anauza otsatira ake kuti: “Ine ndikukwera kwa Atate wanga ndi Atate wanu, kwa Mulungu wanga ndi Mulungu wanu.” (Yohane 20:17) Yehova ndiye Atate wake wa Yesu. Yesu ankapemphera kwa Mulungu ameneyu, ndipo anaphunzitsanso otsatira ake kuti azipemphera kwa Yehova.​—Mateyu 6:9.

Ndiyeno kodi Baibulo limanena kuti tizipemphera kwa Yesu, Mariya, oyera mtima kapena kwa angelo? Yankho ndi lakuti ayi. Tiyenera kupemphera kwa Yehova yekha basi. Chifukwa chiyani? Taganizirani zifukwa ziwiri izi: Choyamba, pemphero ndi mbali ya kulambira ndipo Baibulo limati tiyenera kulambira Yehova yekha basi. (Ekisodo 20:5) Chachiwiri, Baibulo limanena kuti Mulungu ndi “Wakumva pemphero.” (Salimo 65:2) Ngakhale kuti Yehova anapatsa ena maudindo osiyanasiyana, kumvetsera mapemphero ndi udindo wake ndipo sanaupereke kwa wina aliyense. Mulungu amalonjeza kuti iye ndi amene azimvetsera mapemphero athu.

Choncho ngati mukufuna kuti Mulungu azimva mapemphero anu, kumbukirani malangizo a m’Baibulo awa: “Aliyense woitana pa dzina la Yehova adzapulumuka.” (Machitidwe 2:21) Komabe kodi Yehova amayankha mapemphero a munthu wina aliyense zivute zitani? Kapena kodi pali chinachake chimene tiyenera kuchita kuti Yehova aziyankha mapemphero athu?

^ ndime 9 M’zipembedzo zina amanena kuti kutchula dzina la Mulungu, ngakhale popemphera, n’kulakwa. Koma dzina limenelo limapezeka maulendo pafupifupi 7,000 m’zinenero zoyambirira za Baibulo. Kawirikawiri dzinali limapezeka m’mapemphero ndi mu nyimbo zotamanda Mulungu za atumiki okhulupirika a Yehova.