Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

7 Kodi Mulungu Amamva ndi Kuyankha Mapemphero?

7 Kodi Mulungu Amamva ndi Kuyankha Mapemphero?

ANTHU ambiri amafuna kudziwa yankho la funso limeneli. Baibulo limasonyeza kuti Yehova amamvetseradi mapemphero masiku ano. Komabe kuti iye amve kapena asamve mapemphero anu zimadalira inuyo.

Yesu anadzudzula atsogoleri achipembedzo amene ankapemphera mwachinyengo. Iwo ankangofuna kudzionetsera kuti ndi olungama. Iye ananena kuti anthu amenewa ‘ankalandiriratu mphoto yawo yonse.’ Zimenezi zikutanthauza kuti iwo analandira zimene ankafuna zokhazo, zimene ndi ulemu kuchokera kwa anthu. Koma Mulungu sanayankhe mapemphero awo. (Mateyu 6:5) Masiku anonso, anthu ambiri amapemphera mogwirizana ndi zofuna zawo, osati za Mulungu. Mulungu sangamve mapemphero awo chifukwa amanyalanyaza mfundo za m’Baibulo zimene takambiranazi.

Nanga inuyo bwanji? Kodi Mulungu angamve komanso kuyankha mapemphero anu? Kuti Mulungu amve ndiponso kuyankha mapemphero anu, si zidalira mtundu wanu, dziko limene mumachokera kapenanso kuti kaya ndinu olemera kapena osauka. Baibulo limatitsimikizira kuti: “Mulungu alibe tsankho. Iye amalandira munthu wochokera mu mtundu uliwonse, amene amamuopa ndi kuchita chilungamo.” (Machitidwe 10:34, 35) Kodi inuyo mumaopa Mulungu ndipo mumachita chilungamo? Ngati mumaopa Mulungu, ndiye kuti mumamulemekeza kwambiri ndipo mumaopa kumukhumudwitsa. Ndiponso ngati mumachita chilungamo, ndiye kuti mumayesetsa kuchita zimene Mulungu amanena kuti n’zolungama m’malo momangotsatira zofuna zanu kapena za anthu ena. Kodi mukufunadi kuti Mulungu azimvetsera mapemphero anu? Baibulo lingakuthandizeni kuti zimenezi zitheke. *

Komabe, anthu ambiri amafuna kuti Mulungu aziyankha mapemphero awo mozizwitsa. Koma ngakhale pa nthawi imene Baibulo linkalembedwa, Mulungu ankachita zozizwitsa mwa kamodzikamodzi. Pa zozizwitsa zimene zinalembedwa m’Baibulo, nthawi zambiri pankatha zaka zambiri kuchokera pamene chozizwitsa china chinachitika, kudzafika pa chozizwitsa china. Komanso Baibulo limasonyeza kuti nthawi yochita zozizwitsa inatha atumwi onse atatha kufa. (1 Akorinto 13:8-10) Kodi zimenezi zikutanthauza kuti Mulungu sayankhanso mapemphero masiku ano? Ayi ndithu. Taonani ena mwa mapemphero amene iye amayankha.

Mulungu amapereka nzeru. Yehova ndiye Chimake cha nzeru zenizeni. Iye amapereka nzeru zimenezi mowolowa manja kwa anthu amene amafuna kudziwa malangizo ake ndiponso amafunitsitsa kutsatira malangizowo pa moyo wawo.​—Yakobo 1:5.

Mulungu amatipatsa mzimu wake woyera pamodzi ndi madalitso amene amabwera chifukwa cha mzimuwo. Mzimu woyera ndi mphamvu ya Mulungu yogwira ntchito. Palibe mphamvu yoposa imeneyi. Mzimu woyera umenewu ungatithandize kuti tipirire mayesero. Ungatithandizenso kupeza mtendere wa mumtima tikamakumana ndi mavuto. Komanso, ungatithandize kukhala ndi makhalidwe abwino ndiponso osiririka. (Agalatiya 5:22, 23) Yesu anatsimikizira otsatira ake kuti Mulungu amapereka mphatso imeneyi mowolowa manja.​—Luka 11:13.

Mulungu amathandiza anthu amene akufuna kuti amudziwe. (Machitidwe 17:26, 27) Padziko lonse pali anthu ambirimbiri amene akufuna kudziwa choonadi. Iwo akufuna atadziwa dzina la Mulungu, cholinga chake chokhudza dziko lapansi ndiponso anthu, komanso zimene angachite kuti amuyandikire. (Yakobo 4:8) Nthawi zambiri a Mboni za Yehova amakumana ndi anthu oterewa, ndipo amasangalala kukambirana ndi anthuwa mayankho a m’Baibulo a mafunso amenewa.

Kodi inuyo mwalandira magazini ino kuti mudziwe zinthu ngati zimenezi? Kodi mukufunitsitsa mutamudziwa Mulungu? Mwina imeneyi ndi njira imene Mulungu akuyankhira mapemphero anu.

^ ndime 5 Kuti mudziwa zambiri za zimene mungachite kuti Mulungu aziyankha mapemphero anu, werengani mutu 17 wa buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.