Maulendo Okafika Kumalekezero a Dziko Lapansi
Moyo wa Akhristu Oyambirira
Maulendo Okafika Kumalekezero a Dziko Lapansi
“Tsiku lotsatira iye pamodzi ndi Baranaba anachoka ndi kupita ku Debe. Atalengeza uthenga wabwino mumzinda umenewo ndi kuphunzitsa anthu angapo kuti akhale ophunzira, anabwerera ku Lusitara, ku Ikoniyo ndi ku Antiokeya.”—MACHITIDWE 14:20, 21.
KUNJA kudakali m’mawa ndipo kukuwomba kamphepo kayaziyazi. Munthu wina amene akuoneka wotopa akuvala nsapato zake zakutha pokonzekera kuyenda ulendo wapansi tsiku linanso lathunthu.
Iye akuyamba ulendo wake dzuwa likungotuluka kumene ndipo akuyenda mumsewu wafumbi wodutsa m’munda wa mpesa. Akudutsanso minda ya maolivi ndipo akuyamba kuyenda kukweza chitunda chachitali. M’njiramo akukumana ndi anthu ena apaulendo monga alimi amene akupita ku minda yawo, amalonda atanyamulitsa nyama zosiyanasiyana katundu wambiri komanso anthu opita ku Yerusalemu kukapemphera. Munthu uja limodzi ndi anzake amene ali nawo pa ulendowu akucheza ndi aliyense amene akukumana naye. Kodi n’chifukwa chiyani akuchita zimenezi? Iwo akuchita zimenezi ndi cholinga chokwaniritsa ntchito imene Yesu anawapatsa yolalikira za iye “mpaka kumalekezero a dziko lapansi.”—Machitidwe 1:8.
Munthu wapaulendo ameneyu angakhale mtumwi Paulo kapena Baranaba kapena wina aliyense mwa amishonale akhama amene ankatumikira m’nthawi ya atumwi. (Machitidwe 14:19-26; 15:22) Anthu amenewa anali olimba mtima komanso akhama kwambiri. Kuyenda ulendo m’nthawi imeneyo kunali kovuta. Pofotokoza mavuto amene anakumana nawo pa nyanja, mtumwi Paulo analemba kuti: “Chombo chinandiswekerapo katatu. Kamodzi ndinakhala pamadzi akuya usiku ndi usana wonse.” Ulendo wapamtunda unalinso wovuta. Paulo ananena kuti kawirikawiri ankakumana ndi “zoopsa za m’mitsinje,” ndi “zoopsa za achifwamba pamsewu.”—2 Akorinto 11:25-27.
Kodi munthu ankakumana ndi zotani akayenda ndi amishonale amenewa? Kodi patsiku ankayenda ulendo wautali bwanji? Kodi ankafunika kutenga chiyani pa ulendo ngati umenewu ndipo ankagona malo otani?
Ulendo Wapansi: Pomafika m’nthawi ya atumwi, Aroma anali atamanga misewu ikuluikulu yomwe inkalumikiza matawuni akuluakulu a mu ufumuwu. Misewu imeneyo inali yomangidwa mwaluso ndiponso yolimba kwambiri. Ina mwa misewu imeneyi inali yaikulu kupitirira mamita anayi ndipo inali yomangidwa ndi miyala. M’mphepete mwake ankaika zotchinga kuti isagumuke komanso ankalembamo zinthu zosonyeza kutalika kwa ulendo. Pamisewu yotereyi, amishonale ngati Paulo ankatha kuyenda ulendo wa makilomita 32 pa tsiku.
Komabe misewu yambiri ku Palesitina inali yoopsa komanso yamatope kwambiri. Inali yoyandikana kwambiri ndi minda ndipo m’mphepete mwake munali maphompho. Nthawi zina munthu akamayenda m’misewu imeneyi ankakumana ndi nyama zakutchire kapena achifwamba kapenanso ankapeza msewu utatchingika ndi zinthu zina.
Ndiyeno kodi munthu amene ali pa ulendo ankatenga chiyani? Zina mwa zinthu zofunika kwambiri pa ulendo zinali ndodo yodzitetezera (1), kabedi (2), kachikwama ka ndalama (3), nsapato zina (4), chikwama cha zakudya (5), ndi zovala zosinthira (6). Iye ankatenganso kabaketi kachikopa kotungira madzi kamene ankatha kukapinda bwinobwino (7), botolo la madzi (8) komanso chikwama chachikulu chachikopa chimene ankaikamo zinthu zina zofunika pa ulendowu (9).
Amishonale amenewa ankadziwa kuti pa ulendo wawowu akumana ndi anthu amalonda amene akupititsa katundu wawo ku misika yosiyanasiyana. Amalondawa ankanyamula katundu wawo pa abulu. Abulu sagwa chisawawa ndipo panalibe nyama imene inkayenda bwino m’misewu yotsetsereka ndiponso yamiyala yotereyi kuposa abuluwo. Anthu ena amanena kuti bulu wamphamvu ankatha kuyenda ulendo wa makilomita 80 pa tsiku atanyamula katundu wambiri. Koma ngolo zokokedwa ndi ng’ombe zinkayenda pang’onopang’ono kwambiri moti pa tsiku zinkangoyenda makilomita pakati pa 8 ndi 20 basi. Koma ngakhale kuti ng’ombe zinkayenda ulendo waufupi, zinkanyamula katundu wambiri kuposa abulu. Munthu wapaulendo ankatha kudutsananso ndi gulu la ngamila kapena abulu atanyamula katundu wolemera wochokera m’madera osiyanasiyana padziko lapansi. Ankakumananso ndi anthu ena okwera pa mahatchi. Anthu amenewa ntchito yawo inali yonyamula makalata komanso zikalata zosiyanasiya za malamulo zimene ankapita nazo kumadera osiyanasiyana a ufumu wa Roma.
Kunja kukada, anthu apaulendowa ankagona m’mbali mwa msewu, mu timatenti tawo timene ankayenda nato. Ena ankagona pamalo ena otchingidwa ndi mpanda koma okhala ndi zipinda zosaoneka bwino. Malo amenewa anali auve komanso osasangalatsa ndipo munthu akagona pamalo amenewa sankatetezeka kwenikweni ku mphepo, mvula kapenanso akuba. Akachita mwayi, amishonale ankagona kwa achibale awo kapena Akhristu anzawo.—Machitidwe 17:7; Aroma 12:13.
Ulendo Wapanyanja Maboti ang’onoang’ono ankanyamula katundu ndi anthu kudutsa pa Nyanja ya Galileya. (Yohane 6:1, 2, 16, 17, 22-24) Ngalawa zikuluzikulu zinkayenda panyanja ya Mediterranean ndipo zinkanyamula katundu wakumadera akutali kwambiri. Ngalawa zimenezi zinkapititsa chakudya ku Roma, kunyamula akuluakulu a boma komanso makalata m’madoko osiyanasiyana.
Masana, oyendetsa ngalawa ankagwiritsa ntchito zinthu zapamtunda kuti adziwe kumene akupita ndipo usiku ankagwiritsa ntchito nyenyezi. Choncho ulendo wapanyanja unali wosavuta kuyambira m’mwezi wa May mpaka cha mu September chifukwa nthawi imeneyi ndi pamene nyengo inkakhalako bwino. Ngozi za ngalawa sizinkati zachitika liti.—Machitidwe 27:39-44; 2 Akorinto 11:25.
Ngakhale kuti anthu ankasankha kuyenda panyanja, si kuti iwo ankachita zimenezi chifukwa chakuti ulendowu unali wosangalatsa kuposa wapamtunda. Ulendo wa pa ngalawa zonyamula katundu unali wowawa. Mwachitsanzo, anthu ankakhala komanso kugona pamwamba pa ngalawa kaya kunja kuche bwanji. Mu zipinda zouma bwino za pansi pa ngalawayo ankaikamo katundu wa mtengo wapatali. Pa nkhani ya zakudya, aliyense ankadya zimene anatenga ngati kamba wapaulendo. Chimene ankapatsidwa ndi madzi akumwa basi. Nthawi zina nyengo sinkakhala yabwino. Chimphepo chamkuntho chomwe nthawi zina sichinkatherapo, chinkachititsa kuti anthu azidwala kwa masiku angapo.
Ngakhale kuti ulendo wapamtunda ndiponso wapanyanja unali wovuta chonchi, amishonale ngati Paulo anafalitsa ‘uthenga wabwino wa ufumu’ kulikonse kumene kunali anthu pa nthawiyo. (Mateyu 24:14) Patangotha zaka 30 zokha kuchokera pamene Yesu anauza ophunzira ake kuti akhale mboni zake, Paulo analemba kuti uthenga wabwino unali kulalikidwa “m’chilengedwe chonse cha pansi pa thambo.”—Akolose 1:23.