Muzisankha Mwanzeru Anthu Ocheza Nawo
Mfundo Yachinayi
Muzisankha Mwanzeru Anthu Ocheza Nawo
ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA: “Munthu woyenda ndi anthu anzeru adzakhala wanzeru, koma wochita zinthu ndi anthu opusa adzapeza mavuto.”—Miyambo 13:20.
N’CHIFUKWA CHIYANI ZIMENEZI ZIMAKHALA ZOVUTA? Anzathu angachititse kuti tizikhutira kapena tisamakhutire ndi zimene tili nazo. Mmene iwowo amaonera zinthu ndiponso zimene amakonda kukamba, zimakhudza mmene ifeyo timaonera zinthu pa moyo wathu.—1 Akorinto 15:33.
Mwachitsanzo taganizirani nkhani ya m’Baibulo ya amuna 12 amene anatumidwa kukaona mwachinsinsi dziko la Kanani. Ambiri mwa amuna amenewa “anapitiriza kuuza ana a Isiraeli zoipa za dziko limene anakalizondalo.” Koma awiri mwa amunawa ananena zabwino zokhudza dziko la Kanani. Iwo anati linali ‘labwino kwambiri.’ Koma maganizo olakwika a amuna 10 aja anachititsa kuti anthu ambiri akhalenso ndi maganizo olakwika okhudza dzikolo. Nkhaniyi imati: “Khamu lonselo linayamba kudandaula mofuula, . . . Ana onse a Isiraeli anayamba kudandaula.”—Numeri 13:30–14:9.
N’chimodimodzinso masiku ano. Anthu ambiri ndi “okonda kung’ung’udza, okonda kudandaula za moyo wawo.” (Yuda 16) Choncho n’zovuta kuti munthu azikhutira ngati amakonda kucheza ndi anthu amene sakhutira ndi zimene ali nazo.
ZIMENE MUNGACHITE: Ganizirani zimene mumakonda kukambirana mukakhala ndi anzanu. Kodi anzanuwo nthawi zonse amakonda kunena zodzitamandira chifukwa cha zinthu zimene ali nazo? Kapena kodi amakonda kudandaula za zinthu zimene alibe? Nanga inuyo ndinu munthu wotani? Kodi zochita kapena zolankhula zanu zimachititsa kuti anzanu azisirira zinthu zomwe muli nazo, kapena zimawalimbikitsa kuti azikhutira ndi zimene iwowo ali nazo?
Taganizirani chitsanzo cha Davide yemwe ankayembekezera kukhala mfumu, ndi Yonatani yemwe anali mwana wa Mfumu Sauli. Davide anakhala moyo womangothawathawa m’chipululu chifukwa Mfumu Sauli ankafuna kumupha poganiza kuti Davideyo amulanda ufumu. Ngakhale kuti Yonatani ndi amene akanayenera kulowa ufumu, iye sanachitire nsanje Davide ndipo anakhala mmodzi wa anzake a pamtima a Davideyo. Yonatani anazindikira kuti Mulungu ndi amene anasankha Davide kuti adzakhale mfumu kulowa m’malo mwa Sauli. Choncho iye anathandiza Davide ndipo anakhutira ndi mmene zinthu zinalili pa moyo wake.—1 Samueli 19:1, 2; 20:30-33; 23:14-18.
Inunso mumafunika anzanu ngati amenewo, amene amakhutira ndi zimene ali nazo ndiponso omwe amakufunirani zabwino. (Miyambo 17:17) Koma kuti mukhale ndi anzanu amene amakhutira ndi zimene ali nazo ndiponso okufunirani zabwino, pamafunika kuti nanunso mukhale ndi makhalidwe amenewa.—Afilipi 2:3,4.
[Chithunzi patsamba 7]
Kodi anzanu amakupangitsani kukhala okhutira ndi zimene muli nazo, kapena amakupangitsani kuti musamakhutire?