Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Muziganizira Makolo Amene Sali Pabanja

Muziganizira Makolo Amene Sali Pabanja

Muziganizira Makolo Amene Sali Pabanja

MAKOLO amene sali pabanja amakhala ndi zochita zambiri ndiponso amatopa kwambiri poyerekeza ndi anthu ena. Iwo amakumana ndi mavuto ambirimbiri. Ndipo amachita zinthu zosiyanasiyana pofuna kusamalira ana awo. Mwachitsanzo, kuwonjezera pa kugwira ntchito yolembedwa kapena kuchita bizinezi, makolo ambiri amene akulera okha ana amafunika kukagula zinthu, kuphika, kuyeretsa pakhomo ndi kulera ana. Amafunikanso kusamalira anawo akadwala kuchita nawo zinthu zina zosangalatsa komanso kuwalimbikitsa. Ndiponso ngati ndi zotheka, makolowo amafunika kupeza nthawi yoti achite zinthu zinazake pawokha.

Masiku ano pali mabanja ambiri amene mulibe bambo kapena mayi ndipo n’zosavuta kuti anthu azinyalanyaza mabanja oterewa. Mayi wina anavomereza mfundo imeneyi ponena kuti: “Ineyo sindinkachita chidwi ndi makolo amene akulera okha ana mpaka pamene ndinayamba kulera ndekha ana anga.” Kodi mungasonyeze bwanji kuti mumaganizira makolo oterewa? Kodi muyenera kuwaderadi nkhawa? Tiyeni tikambirane chifukwa chake tiyenera kuchita zinthu mowaganizira. Tikambirana zifukwa zitatu.

N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuchita Zinthu Mowaganizira?

Makolo ambiri amene akulera okha ana amafuna kuthandizidwa. Mayi wina wamasiye wa zaka 41 amene akulera yekha ana ake awiri ananena kuti: “Nthawi zina sindidziwa kuti ndichite chiyani ndipo zochita zimandichulukira.” Umasiye, kusiyidwa ukwati kapena mavuto ena amachititsa makolo ambiri amene akulera okha ana kumva ngati mmene nakubala wina anamvera. Iye anati: “Tikupempha thandizo ndipo tikulifuna mwamsanga.”

Kuthandiza makolo amene akulera okha ana kumatithandiza kukhala osangalala. Kodi inuyo munayamba mwathandizapo munthu wina kunyamula katundu wolemera kwambiri? Ngati ndi choncho, muyenera kuti munasangalala kwambiri podziwa kuti mwathandiza winawake. Nawonso makolo amene akulera okha ana amakumana ndi mavuto amene nthawi zina amakhala aakulu kwambiri moti sangathane nawo okha. Mukawathandiza, mudzaona kuti zimene lemba la Salimo 41:1 limanena ndi zoona. Lembali limati: “Wodala ndi munthu amene amachita zinthu moganizira munthu wonyozeka.”

Mulungu amasangalala tikamathandiza makolo amene sali pa banja. Lemba la Yakobo 1:27 limati: “Kupembedza koyera ndi kosaipitsidwa kwa Mulungu ndi Atate wathu ndi uku: Kusamalira ana amasiye ndi akazi amasiye m’masautso awo.” Zimenezi zikuphatikizapo kusamalira makolo amene akulera okha ana. * Lemba la Aheberi 13:16 limanena kuti: “Musaiwale kuchita zabwino ndi kugawana zinthu ndi ena, pakuti nsembe zotero Mulungu amakondwera nazo.”

Popeza kuti takambirana zifukwa zitatu zimene tiyenera kuchitira zinthu moganizira makolo amene akulera okha ana, tsopano tiyeni tikambirane mmene tingawathandizire komanso mmene tingadziwire kuti tikuperekadi thandizo lofunika.

Mmene Mungadziwire Zosowa Zawo

Anthu ena amaona kuti ndi bwino kufunsa makolo oterewa kuti: “Kodi mukufuna ndikuthandizeni chiyani?” Komatu nthawi zina munthu akafunsidwa funso limeneli sanena zimene akufuna. Monga taonera kale, lemba la Salimo 41:1 limatilimbikitsa ‘kuchita zinthu moganizira munthu wonyozeka.’ Buku lina limafotokoza kuti mawu achiheberi amene palembali anawamasulira kuti “kuchita zinthu moganizira” angatanthauze “kuganizira mozama ndiponso mofatsa mfundo zosiyanasiyana kenako n’kuchita zinthu mwanzeru.”

Choncho kuti mupeze njira yabwino yowathandizira mufunika kuganizira mofatsa mavuto amene kholo limene likulera lokha ana limakumana nawo. Yesetsani kuzindikira zimene zikuwachitikira, osati kungoyang’ana chabe. Dzifunseni kuti, ‘Kodi zikanakhala kuti ndine, ndikanafuna kuti ena andithandize bwanji?’ Ndi zoona kuti makolo ambiri amene akulera okha ana angakuuzeni kuti ngakhale mutayesetsa bwanji simungamvetse mavuto amene makolo oterewa amakumana nawo kufikira pamene inuyo mutakhalanso kholo lolera lokha ana. Ngakhale zili choncho, kuyesetsa mmene mungathere kuwamvera chisoni kungachititse kuti ‘muzichita zinthu mowaganizira.’

Tsatirani Chitsanzo Chabwino Kwambiri cha Mulungu

Yehova Mulungu ndi amene amachita zinthu mwachikondi kwa makolo amene akulera okha ana kuposa wina aliyense. Malemba ambiri amasonyeza kuti Yehova Mulungu amaganizira komanso kudera nkhawa amayi amasiye ndiponso ana amasiye. Zimenezi zikutanthauza kuti amadera nkhawa makolo amene akulera okha ana. Kuphunzira mmene Mulungu amachitira pothandiza makolo amenewa kungatiphunzitse zambiri zokhudza mmene nafenso tingawathandizire moyenerera. Pali mfundo zinayi zimene tiyenera kuziganizira.

Muziwamvetsera

M’Chilamulo chimene Yehova anapereka kwa Aisiraeli, iye ananena kuti ‘adzamva ndithu kulira’ kwa anthu osauka. (Ekisodo 22:22, 23) Kodi mungatsatire bwanji chitsanzo chimenechi? Nthawi zambiri makolo amene sali pa banja amasungulumwa chifukwa chosowa munthu wina wamkulu womuuza zakukhosi. Mayi wina amene akulera yekha ana ananena modandaula kuti: “Ana anga akagona nthawi zina ndimangolira. Ndimasowa wocheza naye ndipo vuto limeneli nthawi zina limandisowetsa mtendere kwambiri.” Ngati ndi zotheka, kodi mungapeze nthawi kuti ‘mumve kulira’ kwa kholo lamasiye limene likufuna kuuza munthu wina zakukhosi kwake? Kuwamvetsera pa nthawi yoyenera ndiponso pamalo oyenera, kungathandize kwambiri makolo oterewa kuti athe kupirira mavuto amene akukumana nawo.

Muzilankhula mawu olimbikitsa

Yehova anauzira anthu ena kulemba nyimbo zapadera, kapena kuti masalimo, amene Aisiraeli ankaimba polambira. Ndiyeno taganizirani mmene amayi amasiye ndi ana amasiye ku Isiraeli ankalimbikitsidwira akamaimba nyimbo zouziridwa ndi Mulungu zimenezi. Nyimbozi zinkawakumbutsa kuti Yehova ndi “tate” ndi “woweruza “ wawo ndipo zinkawatsimikizira kuti iye ndi wokonzeka kuwathandiza. (Salimo 68:5; 146:9) Nafenso tingauze makolo amene akulera okha ana mawu olimbikitsa amene angamawakumbukirebe ngakhale patapita zaka zambiri. Ngakhale kuti papita zaka 20, Ruth amene akulera yekha ana amakumbukirabe nthawi imene bambo wina anamuuza kuti: “Mukugwira ntchito yotamandika kwambiri yosamalira ana anu awiriwa. Pitirizani, mukuchita bwino kwambiri.” Ruth ananena kuti: “Mawu amenewa anandilimbikitsa kwambiri.” Ndi zoonadi kuti “mawu abwino ndi mankhwala” ndipo angalimbikitse kholo limene likulera lokha ana kuposa mmene timayembekezera. (Miyambo 15:4, Contemporary English Version) Kodi mungaganizire za zinthu zinazake zabwino zimene kholo limene likulera lokha ana likuchita zimene mungaliyamikire?

Muziwapatsa zosowa zawo

M’Chilamulo cha Yehova chimene anapatsa Aisiraeli munali lamulo lothandiza kuti akazi ndi ana amasiye azipeza chakudya m’njira imene singawachotsere ulemu. Lamulo limeneli linathandiza kuti anthu amenewa ‘azidya ndi kukhuta.’ (Deuteronomo 24:19-21; 26:12, 13) Nafenso mwaulemu komanso mwanzeru tingapereke thandizo kwa kholo limene likulera lokha ana. Mwina mungawagulire chakudya kapena zinthu zina ndi zina. Mungawapatsenso zovala zimene kholo lotere kapena ana ake angavale. Kapenanso mungawapatse ndalama kuti agulire zina ndi zina zofunika pa banjapo.

Muzicheza nawo

Yehova analamula kuti akazi ndi ana amasiye azipezeka nawo pa zikondwerero zapachaka zimene mtundu wa Isiraeli unkachita. Kumeneko ankatha kucheza ndi Aisiraeli anzawo. Ndipotu Yehova anawauza kuti: ‘Muzisangalala.’ (Deuteronomo 16:10-15) Mofanana ndi zimenezi, masiku anonso Akhristu akulangizidwa kuti ‘azicherezana’ kutanthauza kuti nthawi zina azikhala ndi nthawi yocheza ndi Akhristu anzawo. (1 Petulo 4:9) Choncho mungachite bwino kuitana banja la kholo limene likulera lokha ana kuti mudzadye nawo chakudya kunyumba kwanu. Sizichita kufunika kuti mukhale ndi zinthu zambiri. Pamene Yesu ankacheza ndi mabwenzi ake kunyumba yawo, iye anawauza kuti: “Zinthu zofunika kwenikweni n’zochepa chabe, mwinanso n’chimodzi chokha basi.”​—Luka 10:42.

Amayamikira Kwambiri Chifukwa Chowaganizira

Mayi wina dzina lake Kathleen, amene analera yekha ana ake atatu ananena kuti sadzaiwala malangizo anzeru akuti: “Musayembekezere chilichonse, koma thokozani pa chilichonse chimene munthu wakuchitirani.” Mofanana ndi mayi ameneyu, makolo ambiri amene akulera okha ana amazindikira kuti ndi udindo wawo kulera ana awo. Choncho sayembekezera kuti ena awachitire zimene akuyenera kuchita okha. Komabe, iwo amayamikira thandizo lililonse limene mungawapatse. Ngati mumachita zinthu mowaganizira makolo oterewa, mungathandize kuti zinthu ziziwayendera bwino ndipo inunso mungakhale wosangalala podziwa kuti Yehova Mulungu ‘adzakubwezerani zimene munachitazo.’​—Miyambo 19:17.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 7 Ngakhale kuti m’Baibulo simupezeka mawu akuti “makolo amene akulera okha ana” kapena “makolo amene sali pa banja,” mawu akuti “mayi wamasiye” ndi “mwana wamasiye” amapezekamo kambirimbiri. Zimenezi zikusonyeza kuti nthawi imene Baibulo linkalembedwa panali makolo ena amene anali kulera okha ana.​—Yesaya 1:17.

[Chithunzi patsamba 24]

Kodi papita nthawi yaitali bwanji kuchokera pamene munaitanira kholo limene silili pabanja limodzi ndi ana ake kuti adzadye nanu chakudya kunyumba kwanu? Kodi mungawaitanenso?