Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Munthu wa Kum’mawa kwa Asia Anapezeka ku Italy

Munthu wa Kum’mawa kwa Asia Anapezeka ku Italy

Munthu wa Kum’mawa kwa Asia Anapezeka ku Italy

KODI zinatheka bwanji kuti munthu yemwe kwawo kwenikweni kunali Kum’mawa kwa Asia akapezeke kudera la Ufumu wa Roma, zaka 2,000 zapitazo? Limeneli ndi funso limene akatswiri ofukula zinthu zakale anafuna atadziwa yankho lake atafukula zinthu zina zochititsa chidwi mu 2009, cha kum’mwera kwa Italy.

Pamalo amene anapeza zinthu zakalezi ndi pamanda ena akale a ku Roma omwe anali m’mudzi wa Vagnari. Mudziwu unali pa mtunda wa makilomita 60 kumadzulo kwa mzinda wa Bari. Pamandawo anafukula mafupa a anthu 75. Atayeza mafupawo, anapeza kuti ochuluka mwa anthuwo anali a komweko. Koma mafupa a mmodzi mwa anthu amenewa, anadabwitsa kwambiri akatswiriwa. Kuti adziwe zambiri za munthu ameneyu, iwo anamuyeza tizinthu tina timene timapezeka m’maselo a munthu, timene timatha kusonyeza kumene munthuyo anachokera. Zimene anapeza atayeza mafupa ake, zinasonyeza kuti makolo akuchikazi a munthuyu anali a Kum’mawa kwa Asia. * Mafupa a munthu ameneyu anasonyeza kuti iye anakhalako kale kwambiri, mu nthawi ya atumwi a Yesu kapena m’zaka za m’ma 100 C.E. Malinga ndi zimene akatswiriwa ananena, “aka kanali koyamba kuti mu Ufumu wa Roma mupezeke mafupa a munthu yemwe makolo ake anali a Kum’mawa kwa Asia.” Ndiyeno kodi munthu ameneyu anali ndani?

Akatswiriwo ananenanso kuti: “Munthu atangoimva kumene nkhaniyi, angaganize kuti mwina munthuyu ankakachita malonda ansalu zasilika omwe pa nthawiyo ankachitika kwambiri pakati pa dziko la China ndi Ufumu wa Roma.” Komabe zikuoneka kuti panalibe munthu amene ankayenda ulendo wonse wamakilomita 8,000 kuchokera ku China kukafika ku Italy. M’malomwake amkhalapakati osiyanasiyana ankapatsirana malondawo mpaka kukafika kumene akupita.

Nanga kodi malo amene anapezapo mafupawa akutiuza chiyani? Kale Vagnari linali dera lolamulidwa ndi mfumu ndipo anthu ankagwirako ntchito yosula zitsulo komanso kupanga matailosi adothi. Ambiri mwa anthu ogwira ntchitowa ankakhala akapolo ndipo n’kutheka kuti nayenso munthu ameneyu anali kapolo. Ndipotu mmene anaikidwira m’manda zinasonyeza kuti sanali munthu wolemera. Katundu wake amene anaikidwa naye limodzi m’manda anali poto mmodzi basi ndipo pamwamba pa mtembo wake panaikidwanso munthu wina.

N’chifukwa chiyani tili ndi chidwi ndi nkhani ya munthu ameneyu? M’nthawi ya atumwi, kuti uthenga umene Akhristu ankalalikira ufike kumadera osiyanasiyana, zinkadalira ngati anthu afika kumaderawo. Baibulo limanena kuti Pentekosite wa mu 33 C.E. atachitika, alendo ochokera m’mayiko ena, amene ankabwera ku Yerusalemu, akamabwerera ankafalitsa uthenga wabwino kumadera osiyanasiyana akutali. (Machitidwe 2:1-12, 37-41) Kupezeka kwa mafupa a munthu ameneyu kukusonyeza kuti mwina nthawi imeneyi, anthu ena ankayenda kuchokera Kum’mawa kwa Asia kukafika kumadera ozungulira nyanja ya Mediterranean. *

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Zimene anayezazo sizithandiza kudziwa makolo akuchimuna.

^ ndime 6 Komanso pali umboni wosonyeza kuti anthu ochokera kumayiko a azungu ankakafika Kum’mawa kwa Asia. Werengani nkhani yakuti: “Kodi Amishonale Analalikira Kum’mawa Mpaka Kukafika Kuti?” mu Nsanja ya Olonda ya January 1, 2009.

[Mapu patsamba 29]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

ROMA

Vagnari

Nyanja ya Mediterranean

KUM’MAWA KWA ASIA

NYANJA YA PACIFIC

[Chithunzi patsamba 29]

Mafupa a munthu wa Kum’mawa kwa Asia amene anawapeza pamanda a ku Roma

[Mawu a Chithunzi]

© Su concessione del Ministero per i Beni e le Attività Culturali - Direzione Regionale per i Beni Culturali e Paesaggistici della Puglia - Soprintendenza per i Beni Archeologici della Puglia