Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Phunzitsani Ana Anu

Ankakondedwa Ndi Mulungu Komanso Anzake

Ankakondedwa Ndi Mulungu Komanso Anzake

MASIKU ano palibe aliyense amene amadziwa dzina lake, koma amangodziwika kuti mwana wamkazi wa Yefita. Tiye tiwerenge m’Baibulo kuti tidziwe zambiri za Yefita ndi mwana wakeyu. Tipeza kuti mwanayu ankakondedwa kwambiri ndi Mulungu komanso anzake.

M’Baibulo nkhani yonena za Yefita ndi mwana wake wamkazi imapezeka pa Oweruza chaputala 11. Yefita anali mtumiki wokhulupirika wa Mulungu ndipo n’zachidziwikire kuti kawirikawiri ankakambirana Malemba ndi mwana wakeyu.

Yefita anakhalako pa nthawi imene Aisiraeli, omwe anali anthu a Mulungu, anali asanapemphe Mulungu kuti awapatse munthu kuti akhale mfumu yawo. Yefita anali munthu wamphamvu ndipo anali wodziwa nkhondo. Choncho Aisiraeli anamupempha kuti awatsogolere pomenyana ndi Aamoni omwe ankakhala pafupi ndi Aisiraeliwo.

Yefita anafuna kuti Mulungu amuthandize kugonjetsa Aamoni ndipo analonjeza kuti Yehova akamuthandiza, adzam’patsa munthu amene adzakhale woyamba kutuluka m’nyumba yake iyeyo akamachokera kunkhondo. Yefita analonjeza kuti munthu ameneyo adzatumikira pachihema cha Mulungu moyo wake wonse. Chihema chinali malo amene anthu ankalambirako Mulungu nthawi imeneyo. Kodi ukudziwa amene anayambirira kukumana naye pochokera kunkhondo?​ *

Anali mwana wake wamkazi. Yefita anamva chisoni kwambiri ndi zimenezi chifukwa iye anali ndi mwana mmodzi yekhayu basi. Koma usaiwale kuti anali atalonjeza Yehova ndipo anafunika kukwaniritsa lonjezolo. Nthawi yomweyo mwanayo ananena kuti: “Bambo, ngati mwatsegula pakamwa panu pamaso pa Yehova, ndichitireni mogwirizana ndi zimene zatuluka pakamwa panu.” Ndiyeno mwanayu anapempha kuti amulole kuti achoke kwa miyezi iwiri kuti apite kumapiri akalire. Kodi iye anafuna kuti apite kukalira chifukwa chiyani? Chifukwa iye ankadziwa kuti, kuti akwaniritse lonjezo la bambo ake anafunika kulolera kukhala wosakwatiwa ndiponso wopanda ana. Ngakhale kuti iye ankafuna kukwatiwa ndiponso kukhala ndi ana, sanaone kuti zofuna zakezi ndiye zofunika kwambiri. Anafuna kumvera bambo ake komanso kukhala wokhulupirika kwa Yehova. Kodi ukuganiza kuti mtsikanayu anasangalatsa Yehova ndiponso bambo ake?​

Yefita anamulola mwana wake kuti achoke panyumba kwa miyezi iwiri ndi atsikana anzake. Atabwerako, bambo ake anakwaniritsa lonjezo lawo mwa kutumiza mwanayu kuchihema cha Mulungu ku Silo kuti akatumikire Mulungu moyo wake wonse. Chaka chilichonse ana aakazi a ku Isiraeli ankapita ku Silo kukamulimbikitsa mwana wamkazi wa Yefita.

Kodi ukudziwa ana amene amamvera makolo awo ndiponso amakonda Yehova?​— Ndibwino kuwadziwa bwino ana amenewo ndiponso kumacheza nawo. Ukatengera chitsanzo cha mwana wamkazi wa Yefita, n’kukhala womvera ndiponso wokhulupirika, udzakhala ndi anzako abwino. Komanso udzasangalatsa makolo ako ndiponso Yehova azikukonda.

^ ndime 6 Ngati mukuwerenga nkhaniyi ndi mwana, mukapeza mzera muime kaye kuti mwanayo anenepo maganizo ake.